Numbers 2 (BOGWICC)

1 Yehova anati kwa Mose ndi Aaroni: 2 “Aisraeli azimanga misasa yawo mozungulira tenti ya msonkhano motalikira pangʼono. Munthu aliyense amange pamene pali mbendera ya fuko lake.” 3 Kummawa, kotulukira dzuwa, magulu a msasa wa Yuda amange pamene pali mbendera yawo. Mtsogoleri wa Ayudawo ndi Naasoni mwana wa Aminadabu. 4 Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 74,600. 5 Fuko la Isakara lidzamanga pafupi ndi Yuda. Mtsogoleri wa gulu la Isakara ndi Netanieli mwana wa Zuwara. 6 Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 54,400. 7 Lotsatira lidzakhala fuko la Zebuloni. Mtsogoleri wa gulu la Zebuloni ndi Eliabu mwana wa Heloni. 8 Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 57,400. 9 Anthu onse aamuna mʼmisasa ya Yuda, chiwerengero chawo ndi 186,400 monga mwa magulu awo. Iwowo ndiwo aziyamba kusamuka. 10 Kummwera kudzakhala magulu a msasa wa Rubeni pamene pali mbendera yawo. Mtsogoleri wa gulu la Rubeni ndi Elizuri mwana wa Sedeuri. 11 Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 46,500. 12 Fuko la Simeoni lidzamanga pafupi ndi Rubeni. Mtsogoleri wa gulu la Simeoni ndi Selumieli mwana wa Zurisadai. 13 Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 59,300. 14 Lotsatira lidzakhala fuko la Gadi. Mtsogoleri wa gulu la Gadi ndi Eliyasafu mwana wa Deuweli. 15 Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 45,650. 16 Anthu onse aamuna mu msasa wa Rubeni, chiwerengero chawo monga mwa magulu awo, ndi 151,450. Iwowo azikhala achiwiri posamuka. 17 Tsono tenti ya msonkhano ndi msasa wa Alevi zidzakhala pakati pa misasayo. Iwo adzasamuka monga momwe anamangira misasa yawo, aliyense pa malo ake pamene pali mbendera yake. 18 Kumadzulo kudzakhala magulu a msasa wa Efereimu pamene pali mbendera yawo. Mtsogoleri wa Aefereimuwo ndi Elisama mwana wa Amihudi. 19 Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 40,500. 20 Fuko la Manase lidzakhala pafupi ndi Efereimu. Mtsogoleri wa Amanase ndi Gamalieli mwana wa Pedazuri. 21 Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 32,200. 22 Lotsatira lidzakhala fuko la Benjamini. Mtsogoleri wa Abenjamini ndi Abidani mwana wa Gideoni. 23 Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 35,400. 24 Anthu onse aamuna mu msasa wa Efereimu, chiwerengero chawo ndi 108,100 monga mwa magulu awo. Iwowo azikhala achitatu posamuka. 25 Kumpoto kudzakhala msasa wa magulu a Dani pamene pali mbendera yawo. Mtsogoleri wa Adani ndi Ahiyezeri mwana wa Amisadai. 26 Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 62,700. 27 Fuko la Aseri lidzamanga pafupi ndi iwowo. Mtsogoleri wa Aaseri ndi Pagieli mwana wa Okirani. 28 Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 41,500. 29 Lotsatira lidzakhala fuko la Nafutali. Mtsogoleri wa Anafutali ndi Ahira mwana wa Enani. 30 Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 53,400. 31 Anthu onse aamuna mu msasa wa Dani chiwerengero chawo ndi 157,600. Iwo azidzanyamuka pomaliza, ndi mbendera zawo. 32 Amenewa ndi Aisraeli monga mwa mabanja a makolo awo. Chiwerengero cha Aisraeli onse mʼmisasa chinali 603,550, mwa magulu awo. 33 Koma Alevi sanawawerenge pamodzi ndi Aisraeli enawo monga momwe Yehova analamulira Mose. 34 Choncho Aisraeli anachita zonse zomwe Yehova analamulira Mose. Umo ndi momwe amamangira misasa yawo pamene panali mbendera zawo, ndipo ankasamuka monga mwa mafuko a makolo awo.

In Other Versions

Numbers 2 in the ANGEFD

Numbers 2 in the ANTPNG2D

Numbers 2 in the AS21

Numbers 2 in the BAGH

Numbers 2 in the BBPNG

Numbers 2 in the BBT1E

Numbers 2 in the BDS

Numbers 2 in the BEV

Numbers 2 in the BHAD

Numbers 2 in the BIB

Numbers 2 in the BLPT

Numbers 2 in the BNT

Numbers 2 in the BNTABOOT

Numbers 2 in the BNTLV

Numbers 2 in the BOATCB

Numbers 2 in the BOATCB2

Numbers 2 in the BOBCV

Numbers 2 in the BOCNT

Numbers 2 in the BOECS

Numbers 2 in the BOHCB

Numbers 2 in the BOHCV

Numbers 2 in the BOHLNT

Numbers 2 in the BOHNTLTAL

Numbers 2 in the BOICB

Numbers 2 in the BOILNTAP

Numbers 2 in the BOITCV

Numbers 2 in the BOKCV

Numbers 2 in the BOKCV2

Numbers 2 in the BOKHWOG

Numbers 2 in the BOKSSV

Numbers 2 in the BOLCB

Numbers 2 in the BOLCB2

Numbers 2 in the BOMCV

Numbers 2 in the BONAV

Numbers 2 in the BONCB

Numbers 2 in the BONLT

Numbers 2 in the BONUT2

Numbers 2 in the BOPLNT

Numbers 2 in the BOSCB

Numbers 2 in the BOSNC

Numbers 2 in the BOTLNT

Numbers 2 in the BOVCB

Numbers 2 in the BOYCB

Numbers 2 in the BPBB

Numbers 2 in the BPH

Numbers 2 in the BSB

Numbers 2 in the CCB

Numbers 2 in the CUV

Numbers 2 in the CUVS

Numbers 2 in the DBT

Numbers 2 in the DGDNT

Numbers 2 in the DHNT

Numbers 2 in the DNT

Numbers 2 in the ELBE

Numbers 2 in the EMTV

Numbers 2 in the ESV

Numbers 2 in the FBV

Numbers 2 in the FEB

Numbers 2 in the GGMNT

Numbers 2 in the GNT

Numbers 2 in the HARY

Numbers 2 in the HNT

Numbers 2 in the IRVA

Numbers 2 in the IRVB

Numbers 2 in the IRVG

Numbers 2 in the IRVH

Numbers 2 in the IRVK

Numbers 2 in the IRVM

Numbers 2 in the IRVM2

Numbers 2 in the IRVO

Numbers 2 in the IRVP

Numbers 2 in the IRVT

Numbers 2 in the IRVT2

Numbers 2 in the IRVU

Numbers 2 in the ISVN

Numbers 2 in the JSNT

Numbers 2 in the KAPI

Numbers 2 in the KBT1ETNIK

Numbers 2 in the KBV

Numbers 2 in the KJV

Numbers 2 in the KNFD

Numbers 2 in the LBA

Numbers 2 in the LBLA

Numbers 2 in the LNT

Numbers 2 in the LSV

Numbers 2 in the MAAL

Numbers 2 in the MBV

Numbers 2 in the MBV2

Numbers 2 in the MHNT

Numbers 2 in the MKNFD

Numbers 2 in the MNG

Numbers 2 in the MNT

Numbers 2 in the MNT2

Numbers 2 in the MRS1T

Numbers 2 in the NAA

Numbers 2 in the NASB

Numbers 2 in the NBLA

Numbers 2 in the NBS

Numbers 2 in the NBVTP

Numbers 2 in the NET2

Numbers 2 in the NIV11

Numbers 2 in the NNT

Numbers 2 in the NNT2

Numbers 2 in the NNT3

Numbers 2 in the PDDPT

Numbers 2 in the PFNT

Numbers 2 in the RMNT

Numbers 2 in the SBIAS

Numbers 2 in the SBIBS

Numbers 2 in the SBIBS2

Numbers 2 in the SBICS

Numbers 2 in the SBIDS

Numbers 2 in the SBIGS

Numbers 2 in the SBIHS

Numbers 2 in the SBIIS

Numbers 2 in the SBIIS2

Numbers 2 in the SBIIS3

Numbers 2 in the SBIKS

Numbers 2 in the SBIKS2

Numbers 2 in the SBIMS

Numbers 2 in the SBIOS

Numbers 2 in the SBIPS

Numbers 2 in the SBISS

Numbers 2 in the SBITS

Numbers 2 in the SBITS2

Numbers 2 in the SBITS3

Numbers 2 in the SBITS4

Numbers 2 in the SBIUS

Numbers 2 in the SBIVS

Numbers 2 in the SBT

Numbers 2 in the SBT1E

Numbers 2 in the SCHL

Numbers 2 in the SNT

Numbers 2 in the SUSU

Numbers 2 in the SUSU2

Numbers 2 in the SYNO

Numbers 2 in the TBIAOTANT

Numbers 2 in the TBT1E

Numbers 2 in the TBT1E2

Numbers 2 in the TFTIP

Numbers 2 in the TFTU

Numbers 2 in the TGNTATF3T

Numbers 2 in the THAI

Numbers 2 in the TNFD

Numbers 2 in the TNT

Numbers 2 in the TNTIK

Numbers 2 in the TNTIL

Numbers 2 in the TNTIN

Numbers 2 in the TNTIP

Numbers 2 in the TNTIZ

Numbers 2 in the TOMA

Numbers 2 in the TTENT

Numbers 2 in the UBG

Numbers 2 in the UGV

Numbers 2 in the UGV2

Numbers 2 in the UGV3

Numbers 2 in the VBL

Numbers 2 in the VDCC

Numbers 2 in the YALU

Numbers 2 in the YAPE

Numbers 2 in the YBVTP

Numbers 2 in the ZBP