Numbers 8 (BOGWICC)

1 Yehova anawuza Mose kuti, 2 “Yankhula ndi Aaroni kuti pamene uyimika nyale zisanu ndi ziwiri, nyalezo ziziyaka kutsogolo kwa choyikapo nyale.” 3 Aaroni anachitadi zomwezo. Anayimika nyale ndi kuziyangʼanitsa kumene kunali choyikapo nyale monga Yehova analamulira Mose. 4 Choyikapo nyalecho chinapangidwa motere: chinasulidwa kuchokera ku golide, kuyambira pa tsinde pake mpaka ku maluwa ake. Choyikapo nyalecho chinapangidwa monga momwe Yehova anaonetsera Mose. 5 Yehova anawuza Mose kuti, 6 “Tenga Alevi pakati pa Aisraeli ndipo uwayeretse. 7 Powayeretsa uchite izi: uwawaze madzi oyeretsa ndipo amete thupi lawo lonse ndi kuchapa zovala zawo kuti adziyeretse. 8 Atenge ngʼombe yayimuna yayingʼono ndi chopereka cha chakudya cha ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta. Atengenso ngʼombe ina yayimuna, yayingʼono, ya chopereka chopepesera machimo. 9 Ubwere nawo Aleviwo kutsogolo kwa tenti ya msonkhano ndipo usonkhanitse gulu la Aisraeli. 10 Ubwere nawo pamaso pa Yehova, ndipo Aisraeli asanjike manja awo pa iwo. 11 Aaroni apereke Alevi aja pamaso pa Yehova ngati chopereka choweyula kuchokera kwa Aisraeli kuti akhale okonzeka kugwira ntchito ya Yehova. 12 “Alevi akatsiriza kusanjika manja awo pa mitu ya ngʼombe zazimuna, imodzi ikhale ya nsembe yopepesera machimo ndipo inayo ikhale ya nsembe yopsereza ya kwa Yehova, kupepesera machimo a Alevi. 13 Uyimiritse Aleviwo pamaso pa Aaroni ndi ana ake aamuna ndipo uwapereke ngati nsembe yoweyula kwa Yehova. 14 Pochita zimenezi mudzapatula Alevi pakati pa Aisraeli ndipo Aleviwo adzakhala anga. 15 “Utatha kuyeretsa ndi kupereka Aleviwo monga nsembe yoweyula, apite kukagwira ntchito yawo ku tenti ya msonkhano. 16 Iwo ndiwo Aisraeli amene aperekedwa kwathunthu kwa Ine. Ndawatenga kuti akhale anga mʼmalo mwa mwana wamwamuna aliyense woyamba kubadwa wa Mwisraeli aliyense wamkazi. 17 Mwana aliyense wamwamuna woyamba kubadwa mu Israeli, kaya wa munthu kapena wa ziweto, ndi wanga. Pamene ndinakantha ana oyamba kubadwa ku Igupto, ndinawapatulira kwa Ine mwini. 18 Ndipo ndatenga Alevi mʼmalo mwa ana aamuna onse oyamba kubadwa mu Israeli. 19 Mwa Aisraeli onse, ndapereka Alevi kuti akhale mphatso kwa Aaroni ndi ana ake aamuna kugwira ntchito ya ku tenti ya msonkhano mʼmalo mwa Aisraeli onse kuti azikapereka nsembe yopepesera machimo, kuti mliri usadzaphe Aisraeli pamene ayandikira ku malo wopatulika.” 20 Mose, Aaroni pamodzi ndi gulu lonse la Israeli anachita kwa Alevi monga momwe Yehova analamulira Mose. 21 Alevi anadziyeretsa ndi kuchapa zovala zawo. Kenaka Aaroni anawapereka ngati nsembe yoweyula pamaso pa Yehova ndi kuchita nsembe yopepesera machimo yowayeretsa. 22 Zitatha zimenezi, Alevi anapita kukagwira ntchito yawo ku tenti ya msonkhano motsogozedwa ndi Aaroni ndi ana ake aamuna. Anachita kwa Alevi monga momwe Yehova analamulira Mose. 23 Yehova anawuza Mose kuti, 24 “Ntchito za Alevi ndi izi: Amuna a zaka 24 kapena kuposera pamenepa ndiye azibwera kudzagwira ntchito ku tenti ya msonkhano. 25 Koma akakwana zaka makumi asanu, apume pa ntchito yawo ya tsiku ndi tsiku ndi kulekeratu kugwira ntchitoyo. 26 Atha kuthandiza abale awo kugwira ntchito za ku tenti ya msonkhano, koma iwowo asamagwire ntchitoyo. Mmenemu ndimo ugawire ntchito yomwe azigwira Alevi.”

In Other Versions

Numbers 8 in the ANGEFD

Numbers 8 in the ANTPNG2D

Numbers 8 in the AS21

Numbers 8 in the BAGH

Numbers 8 in the BBPNG

Numbers 8 in the BBT1E

Numbers 8 in the BDS

Numbers 8 in the BEV

Numbers 8 in the BHAD

Numbers 8 in the BIB

Numbers 8 in the BLPT

Numbers 8 in the BNT

Numbers 8 in the BNTABOOT

Numbers 8 in the BNTLV

Numbers 8 in the BOATCB

Numbers 8 in the BOATCB2

Numbers 8 in the BOBCV

Numbers 8 in the BOCNT

Numbers 8 in the BOECS

Numbers 8 in the BOHCB

Numbers 8 in the BOHCV

Numbers 8 in the BOHLNT

Numbers 8 in the BOHNTLTAL

Numbers 8 in the BOICB

Numbers 8 in the BOILNTAP

Numbers 8 in the BOITCV

Numbers 8 in the BOKCV

Numbers 8 in the BOKCV2

Numbers 8 in the BOKHWOG

Numbers 8 in the BOKSSV

Numbers 8 in the BOLCB

Numbers 8 in the BOLCB2

Numbers 8 in the BOMCV

Numbers 8 in the BONAV

Numbers 8 in the BONCB

Numbers 8 in the BONLT

Numbers 8 in the BONUT2

Numbers 8 in the BOPLNT

Numbers 8 in the BOSCB

Numbers 8 in the BOSNC

Numbers 8 in the BOTLNT

Numbers 8 in the BOVCB

Numbers 8 in the BOYCB

Numbers 8 in the BPBB

Numbers 8 in the BPH

Numbers 8 in the BSB

Numbers 8 in the CCB

Numbers 8 in the CUV

Numbers 8 in the CUVS

Numbers 8 in the DBT

Numbers 8 in the DGDNT

Numbers 8 in the DHNT

Numbers 8 in the DNT

Numbers 8 in the ELBE

Numbers 8 in the EMTV

Numbers 8 in the ESV

Numbers 8 in the FBV

Numbers 8 in the FEB

Numbers 8 in the GGMNT

Numbers 8 in the GNT

Numbers 8 in the HARY

Numbers 8 in the HNT

Numbers 8 in the IRVA

Numbers 8 in the IRVB

Numbers 8 in the IRVG

Numbers 8 in the IRVH

Numbers 8 in the IRVK

Numbers 8 in the IRVM

Numbers 8 in the IRVM2

Numbers 8 in the IRVO

Numbers 8 in the IRVP

Numbers 8 in the IRVT

Numbers 8 in the IRVT2

Numbers 8 in the IRVU

Numbers 8 in the ISVN

Numbers 8 in the JSNT

Numbers 8 in the KAPI

Numbers 8 in the KBT1ETNIK

Numbers 8 in the KBV

Numbers 8 in the KJV

Numbers 8 in the KNFD

Numbers 8 in the LBA

Numbers 8 in the LBLA

Numbers 8 in the LNT

Numbers 8 in the LSV

Numbers 8 in the MAAL

Numbers 8 in the MBV

Numbers 8 in the MBV2

Numbers 8 in the MHNT

Numbers 8 in the MKNFD

Numbers 8 in the MNG

Numbers 8 in the MNT

Numbers 8 in the MNT2

Numbers 8 in the MRS1T

Numbers 8 in the NAA

Numbers 8 in the NASB

Numbers 8 in the NBLA

Numbers 8 in the NBS

Numbers 8 in the NBVTP

Numbers 8 in the NET2

Numbers 8 in the NIV11

Numbers 8 in the NNT

Numbers 8 in the NNT2

Numbers 8 in the NNT3

Numbers 8 in the PDDPT

Numbers 8 in the PFNT

Numbers 8 in the RMNT

Numbers 8 in the SBIAS

Numbers 8 in the SBIBS

Numbers 8 in the SBIBS2

Numbers 8 in the SBICS

Numbers 8 in the SBIDS

Numbers 8 in the SBIGS

Numbers 8 in the SBIHS

Numbers 8 in the SBIIS

Numbers 8 in the SBIIS2

Numbers 8 in the SBIIS3

Numbers 8 in the SBIKS

Numbers 8 in the SBIKS2

Numbers 8 in the SBIMS

Numbers 8 in the SBIOS

Numbers 8 in the SBIPS

Numbers 8 in the SBISS

Numbers 8 in the SBITS

Numbers 8 in the SBITS2

Numbers 8 in the SBITS3

Numbers 8 in the SBITS4

Numbers 8 in the SBIUS

Numbers 8 in the SBIVS

Numbers 8 in the SBT

Numbers 8 in the SBT1E

Numbers 8 in the SCHL

Numbers 8 in the SNT

Numbers 8 in the SUSU

Numbers 8 in the SUSU2

Numbers 8 in the SYNO

Numbers 8 in the TBIAOTANT

Numbers 8 in the TBT1E

Numbers 8 in the TBT1E2

Numbers 8 in the TFTIP

Numbers 8 in the TFTU

Numbers 8 in the TGNTATF3T

Numbers 8 in the THAI

Numbers 8 in the TNFD

Numbers 8 in the TNT

Numbers 8 in the TNTIK

Numbers 8 in the TNTIL

Numbers 8 in the TNTIN

Numbers 8 in the TNTIP

Numbers 8 in the TNTIZ

Numbers 8 in the TOMA

Numbers 8 in the TTENT

Numbers 8 in the UBG

Numbers 8 in the UGV

Numbers 8 in the UGV2

Numbers 8 in the UGV3

Numbers 8 in the VBL

Numbers 8 in the VDCC

Numbers 8 in the YALU

Numbers 8 in the YAPE

Numbers 8 in the YBVTP

Numbers 8 in the ZBP