Numbers 9 (BOGWICC)
1 Yehova anayankhula ndi Mose mʼchipululu cha Sinai pa mwezi woyamba wa chaka chachiwiri atatuluka mu Igupto, nati, 2 “Aisraeli azichita Paska pa nthawi yake yoyikika. 3 Muzichita Paska pa nthawi yake yoyikika, madzulo a tsiku la 14 la mwezi uno, potsata malamulo ndi malangizo ake.” 4 Choncho Mose anawuza Aisraeli kuti azichita Paska, 5 ndipo anachitadi Paskayo mʼchipululu cha Sinai madzulo a tsiku la 14 la mwezi woyamba. Aisraeli anachita zonse monga momwe Yehova analamulira Mose. 6 Koma ena a iwo sanathe kuchita nawo Paska pa tsiku limenelo chifukwa anali odetsedwa chifukwa chokhudza mtembo. Choncho anabwera kwa Mose ndi Aaroni tsiku lomwelo, 7 ndipo anawuza Moseyo kuti, “Ife tadetsedwa chifukwa cha mtembo wa munthu. Nʼchifukwa chiyani taletsedwa kupereka nsembe kwa Yehova pamodzi ndi Aisraeli ena pa nthawi yake?” 8 Mose anawayankha kuti, “Dikirani mpaka nditamva zimene Yehova walamula zokhudza Inu.” 9 Ndipo Yehova anawuza Mose kuti, 10 “Uza Aisraeli kuti, ‘Pamene wina mwa inu kapena zidzukulu zanu adetsedwa chifukwa chokhudza mtembo wa munthu, kapena akakhala pa ulendo, akhoza kuchita nawo Paska ya Yehova. 11 Azichita chikondwererochi madzulo a pa tsiku la 14 la mwezi wachiwiri. Azidya mwana wankhosa wamwamuna pamodzi ndi buledi wopanda yisiti ndi ndiwo zowawa zamasamba. 12 Iwo asasiye nyama ina iliyonse mpaka mmawa. Asaswe mafupa aliwonse. Pamene akuchita chikondwerero cha Paska, atsate malangizo onse. 13 Koma ngati munthu wina ali woyeretsedwa ndipo sali pa ulendo koma alephera kuchita Paska, munthu ameneyo achotsedwe pakati pa anthu a mtundu wake chifukwa sanabweretse chopereka cha Yehova pa nthawi yake. Munthu ameneyo adzalangidwa chifukwa cha tchimo lake. 14 “ ‘Mlendo amene akukhala pakati panu, nafuna kuchita nawo Paska ya Yehova, achite nawo motsata malamulo ndi malangizo ake. Muzikhala ndi malangizo ofanana a Paska; mbadwa kapena mlendo.’ ” 15 Pa tsiku limene anayimika chihema, tenti ya umboni, mtambo unaphimba chihemacho. Kuyambira madzulo mpaka mmawa, mtambo umene unali pamwamba pa chihemacho unkaoneka ngati moto. 16 Zinkachitika motere mosalekeza: mtambo unkakhala pamwamba pa chihema, ndipo usiku unkaoneka ngati moto. 17 Nthawi ina iliyonse mtambo ukachoka pamwamba pa chihema, Aisraeli ankasamukanso, ndipo paliponse pamene mtambo wayima, Aisraeli ankamangapo misasa. 18 Aisraeli ankasamuka pamalopo Yehova akawalamula, ndipo ankamanganso misasa Iyeyo akawalamula. Nthawi yonse imene mtambowo wayima pa chihema, ankakhalabe mʼmisasa yawo. 19 Mtambowo ukakhala pa chihema nthawi yayitali, Aisraeli ankasungabe lamulo la Yehova ndipo iwo sankasamukanso. 20 Nthawi zina mtambowo unkakhala pa chihemapo masiku owerengeka. Aisraeli ankamanga misasa molamulidwa ndi Yehova ndipo ankasamukanso molamulidwa ndi Iyeyo. 21 Nthawi zina mtambo unkakhala kuyambira madzulo mpaka mmawa ndipo unkachoka mmawa mwake, ankasamuka. Kaya ndi masana kapena usiku, pamene mtambo wachoka, ankasamuka. 22 Ngakhale mtambo ukhale pa chihema masiku awiri kapena mwezi kapena chaka, Aisraeli ankakhalabe pa msasa osachoka. Koma ukachoka, ankasamuka. 23 Molamulidwa ndi Yehova ankamanga misasa yawo ndipo ankasamukanso Yehova akawalamula. Ankamvera lamulo la Yehova kudzera mwa Mose.
In Other Versions
Numbers 9 in the ANGEFD
Numbers 9 in the ANTPNG2D
Numbers 9 in the AS21
Numbers 9 in the BAGH
Numbers 9 in the BBPNG
Numbers 9 in the BBT1E
Numbers 9 in the BDS
Numbers 9 in the BEV
Numbers 9 in the BHAD
Numbers 9 in the BIB
Numbers 9 in the BLPT
Numbers 9 in the BNT
Numbers 9 in the BNTABOOT
Numbers 9 in the BNTLV
Numbers 9 in the BOATCB
Numbers 9 in the BOATCB2
Numbers 9 in the BOBCV
Numbers 9 in the BOCNT
Numbers 9 in the BOECS
Numbers 9 in the BOHCB
Numbers 9 in the BOHCV
Numbers 9 in the BOHLNT
Numbers 9 in the BOHNTLTAL
Numbers 9 in the BOICB
Numbers 9 in the BOILNTAP
Numbers 9 in the BOITCV
Numbers 9 in the BOKCV
Numbers 9 in the BOKCV2
Numbers 9 in the BOKHWOG
Numbers 9 in the BOKSSV
Numbers 9 in the BOLCB
Numbers 9 in the BOLCB2
Numbers 9 in the BOMCV
Numbers 9 in the BONAV
Numbers 9 in the BONCB
Numbers 9 in the BONLT
Numbers 9 in the BONUT2
Numbers 9 in the BOPLNT
Numbers 9 in the BOSCB
Numbers 9 in the BOSNC
Numbers 9 in the BOTLNT
Numbers 9 in the BOVCB
Numbers 9 in the BOYCB
Numbers 9 in the BPBB
Numbers 9 in the BPH
Numbers 9 in the BSB
Numbers 9 in the CCB
Numbers 9 in the CUV
Numbers 9 in the CUVS
Numbers 9 in the DBT
Numbers 9 in the DGDNT
Numbers 9 in the DHNT
Numbers 9 in the DNT
Numbers 9 in the ELBE
Numbers 9 in the EMTV
Numbers 9 in the ESV
Numbers 9 in the FBV
Numbers 9 in the FEB
Numbers 9 in the GGMNT
Numbers 9 in the GNT
Numbers 9 in the HARY
Numbers 9 in the HNT
Numbers 9 in the IRVA
Numbers 9 in the IRVB
Numbers 9 in the IRVG
Numbers 9 in the IRVH
Numbers 9 in the IRVK
Numbers 9 in the IRVM
Numbers 9 in the IRVM2
Numbers 9 in the IRVO
Numbers 9 in the IRVP
Numbers 9 in the IRVT
Numbers 9 in the IRVT2
Numbers 9 in the IRVU
Numbers 9 in the ISVN
Numbers 9 in the JSNT
Numbers 9 in the KAPI
Numbers 9 in the KBT1ETNIK
Numbers 9 in the KBV
Numbers 9 in the KJV
Numbers 9 in the KNFD
Numbers 9 in the LBA
Numbers 9 in the LBLA
Numbers 9 in the LNT
Numbers 9 in the LSV
Numbers 9 in the MAAL
Numbers 9 in the MBV
Numbers 9 in the MBV2
Numbers 9 in the MHNT
Numbers 9 in the MKNFD
Numbers 9 in the MNG
Numbers 9 in the MNT
Numbers 9 in the MNT2
Numbers 9 in the MRS1T
Numbers 9 in the NAA
Numbers 9 in the NASB
Numbers 9 in the NBLA
Numbers 9 in the NBS
Numbers 9 in the NBVTP
Numbers 9 in the NET2
Numbers 9 in the NIV11
Numbers 9 in the NNT
Numbers 9 in the NNT2
Numbers 9 in the NNT3
Numbers 9 in the PDDPT
Numbers 9 in the PFNT
Numbers 9 in the RMNT
Numbers 9 in the SBIAS
Numbers 9 in the SBIBS
Numbers 9 in the SBIBS2
Numbers 9 in the SBICS
Numbers 9 in the SBIDS
Numbers 9 in the SBIGS
Numbers 9 in the SBIHS
Numbers 9 in the SBIIS
Numbers 9 in the SBIIS2
Numbers 9 in the SBIIS3
Numbers 9 in the SBIKS
Numbers 9 in the SBIKS2
Numbers 9 in the SBIMS
Numbers 9 in the SBIOS
Numbers 9 in the SBIPS
Numbers 9 in the SBISS
Numbers 9 in the SBITS
Numbers 9 in the SBITS2
Numbers 9 in the SBITS3
Numbers 9 in the SBITS4
Numbers 9 in the SBIUS
Numbers 9 in the SBIVS
Numbers 9 in the SBT
Numbers 9 in the SBT1E
Numbers 9 in the SCHL
Numbers 9 in the SNT
Numbers 9 in the SUSU
Numbers 9 in the SUSU2
Numbers 9 in the SYNO
Numbers 9 in the TBIAOTANT
Numbers 9 in the TBT1E
Numbers 9 in the TBT1E2
Numbers 9 in the TFTIP
Numbers 9 in the TFTU
Numbers 9 in the TGNTATF3T
Numbers 9 in the THAI
Numbers 9 in the TNFD
Numbers 9 in the TNT
Numbers 9 in the TNTIK
Numbers 9 in the TNTIL
Numbers 9 in the TNTIN
Numbers 9 in the TNTIP
Numbers 9 in the TNTIZ
Numbers 9 in the TOMA
Numbers 9 in the TTENT
Numbers 9 in the UBG
Numbers 9 in the UGV
Numbers 9 in the UGV2
Numbers 9 in the UGV3
Numbers 9 in the VBL
Numbers 9 in the VDCC
Numbers 9 in the YALU
Numbers 9 in the YAPE
Numbers 9 in the YBVTP
Numbers 9 in the ZBP