Philemon 1 (BOGWICC)
1 Kuchokera kwa Paulo, amene ndili mʼndende chifukwa cha Khristu Yesu ndi Timoteyo mʼbale wathu.Kulembera Filemoni, bwenzi lathu lokondedwa ndi mtumiki mnzathu. 2 Kwa Apiya mlongo wathu, Arkipo msilikali mnzathu, ndiponso mpingo umene umasonkhana mʼnyumba mwanu. 3 Chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu zikhale ndi inu. 4 Ine ndimayamika Mulungu wanga nthawi zonse ndikakukumbukira iwe mʼmapemphero anga. 5 Pakuti ndamva za chikondi chako, za chikhulupiriro chako mwa Ambuye Yesu ndiponso za chikondi chako pa oyera mtima onse. 6 Ine ndikupemphera kuti mgwirizano wako ndi ife mʼchikhulupiriro ukhale opindulitsa pozamitsa nzeru zako zozindikira zinthu zilizonse zabwino zimene timagawana chifukwa cha Khristu. 7 Mʼbale, chikondi chako chandipatsa chimwemwe chachikulu ndi chilimbikitso, chifukwa umatsitsimutsa mitima ya anthu a Ambuye. 8 Tsopano ngakhale kuti mwa Khristu nditha kulimba mtima ndi kulamulira kuti uchite zimene uyenera kuchita, 9 komabe ndikupempha mwachikondi. Ine Paulo, munthu wokalamba, ndipo tsopano ndili mʼndende chifukwa cha Khristu Yesu, 10 ndikukupempha chifukwa cha mwana wanga Onesimo, amene ndamubala ndili mu unyolo. 11 Anali wopanda phindu kwa iwe, koma tsopano wasanduka wa phindu kwa iwe ndi kwa inenso. 12 Ine ndikumutumizanso kwa iwe tsopano, koma potero ndikukhala ngati ndikutumiza mtima wanga weniweni. 13 Ndikanakonda ndikanakhala naye kuno kuti iyeyo azinditumikira mʼmalo mwako pamene ndili mu unyolo chifukwa cha Uthenga Wabwino. 14 Koma sindikufuna kuchita kanthu osakufunsa, nʼcholinga chakuti chilichonse chabwino ungandichitire chikhale mwakufuna kwako osati mokakamiza. 15 Mwina chifukwa chimene unasiyana naye kwa kanthawi ndi chakuti ukhale nayenso nthawi zonse. 16 Osati ngati kapolo, koma woposa kapolo, ngati mʼbale wokondedwa. Iyeyu ndi wokondedwa kwambiri kwa ine koma kwa iweyo ndi wokondedwa koposa, ngati munthu komanso ngati mʼbale mwa Ambuye. 17 Tsono ngati umati ndine mnzako, umulandire iyeyu monga momwe ukanandilandirira ineyo. 18 Ngati anakulakwira kapena kukongola kanthu kalikonse, ndidzalipira ineyo. 19 Ine, Paulo ndikulemba zimenezi ndi dzanja langa. Ine ndidzalipira. Nʼkosafunika kukukumbutsa kuti iweyo ngongole yako kwa ine ndi moyo wakowo. 20 Mʼbale, ndikufuna kuti ndipindule nawe mwa Ambuye; tsono tsitsimutsa mtima wanga mwa Khristu. 21 Ine ndili ndi chitsimikizo cha kumvera kwako pamene ndikukulembera kalatayi. Ndikulemba ndikudziwa kuti udzachita ngakhale kuposa zimene ndakupemphazi. 22 Chinthu chinanso ndi ichi: undikonzere malo, chifukwa ndikukhulupirira kuti Mulungu adzamvera mapemphero anu ndi kundibwezera kwa inu. 23 Epafra, wamʼndende mnzanga chifukwa cha Khristu Yesu akupereka moni. 24 Atumiki anzanga awa, Marko, Aristariko, Dema ndi Luka, akuperekanso moni. 25 Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu chikhale ndi mzimu wako.
In Other Versions
Philemon 1 in the ANGEFD
Philemon 1 in the ANTPNG2D
Philemon 1 in the AS21
Philemon 1 in the BAGH
Philemon 1 in the BBPNG
Philemon 1 in the BBT1E
Philemon 1 in the BDS
Philemon 1 in the BEV
Philemon 1 in the BHAD
Philemon 1 in the BIB
Philemon 1 in the BLPT
Philemon 1 in the BNT
Philemon 1 in the BNTABOOT
Philemon 1 in the BNTLV
Philemon 1 in the BOATCB
Philemon 1 in the BOATCB2
Philemon 1 in the BOBCV
Philemon 1 in the BOCNT
Philemon 1 in the BOECS
Philemon 1 in the BOHCB
Philemon 1 in the BOHCV
Philemon 1 in the BOHLNT
Philemon 1 in the BOHNTLTAL
Philemon 1 in the BOICB
Philemon 1 in the BOILNTAP
Philemon 1 in the BOITCV
Philemon 1 in the BOKCV
Philemon 1 in the BOKCV2
Philemon 1 in the BOKHWOG
Philemon 1 in the BOKSSV
Philemon 1 in the BOLCB
Philemon 1 in the BOLCB2
Philemon 1 in the BOMCV
Philemon 1 in the BONAV
Philemon 1 in the BONCB
Philemon 1 in the BONLT
Philemon 1 in the BONUT2
Philemon 1 in the BOPLNT
Philemon 1 in the BOSCB
Philemon 1 in the BOSNC
Philemon 1 in the BOTLNT
Philemon 1 in the BOVCB
Philemon 1 in the BOYCB
Philemon 1 in the BPBB
Philemon 1 in the BPH
Philemon 1 in the BSB
Philemon 1 in the CCB
Philemon 1 in the CUV
Philemon 1 in the CUVS
Philemon 1 in the DBT
Philemon 1 in the DGDNT
Philemon 1 in the DHNT
Philemon 1 in the DNT
Philemon 1 in the ELBE
Philemon 1 in the EMTV
Philemon 1 in the ESV
Philemon 1 in the FBV
Philemon 1 in the FEB
Philemon 1 in the GGMNT
Philemon 1 in the GNT
Philemon 1 in the HARY
Philemon 1 in the HNT
Philemon 1 in the IRVA
Philemon 1 in the IRVB
Philemon 1 in the IRVG
Philemon 1 in the IRVH
Philemon 1 in the IRVK
Philemon 1 in the IRVM
Philemon 1 in the IRVM2
Philemon 1 in the IRVO
Philemon 1 in the IRVP
Philemon 1 in the IRVT
Philemon 1 in the IRVT2
Philemon 1 in the IRVU
Philemon 1 in the ISVN
Philemon 1 in the JSNT
Philemon 1 in the KAPI
Philemon 1 in the KBT1ETNIK
Philemon 1 in the KBV
Philemon 1 in the KJV
Philemon 1 in the KNFD
Philemon 1 in the LBA
Philemon 1 in the LBLA
Philemon 1 in the LNT
Philemon 1 in the LSV
Philemon 1 in the MAAL
Philemon 1 in the MBV
Philemon 1 in the MBV2
Philemon 1 in the MHNT
Philemon 1 in the MKNFD
Philemon 1 in the MNG
Philemon 1 in the MNT
Philemon 1 in the MNT2
Philemon 1 in the MRS1T
Philemon 1 in the NAA
Philemon 1 in the NASB
Philemon 1 in the NBLA
Philemon 1 in the NBS
Philemon 1 in the NBVTP
Philemon 1 in the NET2
Philemon 1 in the NIV11
Philemon 1 in the NNT
Philemon 1 in the NNT2
Philemon 1 in the NNT3
Philemon 1 in the PDDPT
Philemon 1 in the PFNT
Philemon 1 in the RMNT
Philemon 1 in the SBIAS
Philemon 1 in the SBIBS
Philemon 1 in the SBIBS2
Philemon 1 in the SBICS
Philemon 1 in the SBIDS
Philemon 1 in the SBIGS
Philemon 1 in the SBIHS
Philemon 1 in the SBIIS
Philemon 1 in the SBIIS2
Philemon 1 in the SBIIS3
Philemon 1 in the SBIKS
Philemon 1 in the SBIKS2
Philemon 1 in the SBIMS
Philemon 1 in the SBIOS
Philemon 1 in the SBIPS
Philemon 1 in the SBISS
Philemon 1 in the SBITS
Philemon 1 in the SBITS2
Philemon 1 in the SBITS3
Philemon 1 in the SBITS4
Philemon 1 in the SBIUS
Philemon 1 in the SBIVS
Philemon 1 in the SBT
Philemon 1 in the SBT1E
Philemon 1 in the SCHL
Philemon 1 in the SNT
Philemon 1 in the SUSU
Philemon 1 in the SUSU2
Philemon 1 in the SYNO
Philemon 1 in the TBIAOTANT
Philemon 1 in the TBT1E
Philemon 1 in the TBT1E2
Philemon 1 in the TFTIP
Philemon 1 in the TFTU
Philemon 1 in the TGNTATF3T
Philemon 1 in the THAI
Philemon 1 in the TNFD
Philemon 1 in the TNT
Philemon 1 in the TNTIK
Philemon 1 in the TNTIL
Philemon 1 in the TNTIN
Philemon 1 in the TNTIP
Philemon 1 in the TNTIZ
Philemon 1 in the TOMA
Philemon 1 in the TTENT
Philemon 1 in the UBG
Philemon 1 in the UGV
Philemon 1 in the UGV2
Philemon 1 in the UGV3
Philemon 1 in the VBL
Philemon 1 in the VDCC
Philemon 1 in the YALU
Philemon 1 in the YAPE
Philemon 1 in the YBVTP
Philemon 1 in the ZBP