Proverbs 17 (BOGWICC)
1 Nʼkwabwino kudya mkute koma pali mtendere,kuposa kuchita madyerero mʼnyumba mʼmene muli mikangano. 2 Kapolo wanzeru adzalamulira mwana wochititsa manyazi,ndipo kapoloyo adzagawana nawo cholowa ngati mmodzi mwa abale. 3 Siliva amamuyesa mʼngʼanjo ndipo golide amamuyesa mʼngʼanjo,koma Yehova amayesa mitima. 4 Munthu woyipa amamvera malangizo oyipa;munthu wabodza amatchera khutu mawu osakaza. 5 Iye amene amalalatira mʼmphawi amanyoza mlengi wake;amene amakondwerera tsoka la mnzake sadzakhala osalangidwa. 6 Zidzukulu ndiye ulemu wa anthu okalamba,ndipo makolo ndiye ulemerero wa ana. 7 Kuyankhula bwino sikuyenerana ndi chitsiru,nanji kuyankhula bodza kungayenerane kodi ndi mfumu? 8 Chiphuphu chili ngati mankhwala amwayi kwa wochiperekayo;kulikonse kumene amapita zinthu zimamuyendera. 9 Iye amene amakhululukira zolakwa za wina, amafunitsitsa chikondi;wobwerezabwereza nkhani amapha chibwenzi. 10 Munthu wanzeru amamva kamodzi kokha,munthu wopanda nzeru ndi samvamkunkhu. 11 Munthu woyipa maganizo ake ali pa kuwukira basi;ndipo bwana adzamutumizira wamthenga wankhanza. 12 Nʼkwabwino kukumana ndi chimbalangondo cholandidwa ana akekusiyana ndi kukumana ndi chitsiru mu uchitsiru wake. 13 Ngati munthu abwezera choyipa kusinthana ndi zabwino,ndiye choyipa sichidzachoka mʼnyumba mwake. 14 Chiyambi cha mikangano chili ngati kukhamulira madzi,choncho uzichokapo mkangano usanayambe. 15 Kumasula munthu wolakwa kapena kumanga munthu wosalakwa,zonse ziwirizi Yehova zimamunyansa. 16 Ndalama zogulira nzeru zili ndi phindu lanji mʼmanja mwa chitsirupoti iyeyo mutu wake sumayenda bwino? 17 Bwenzi lako limakukonda nthawi zonse,ndipo mʼbale wako anabadwa kuti azikuthandiza pamavuto. 18 Munthu wopanda nzeru amavomereza zopereka chikolendipo iyeyo amasanduka chikole cha mnansi wake. 19 Wokonda zolakwa amakonda mkangano,ndipo wokonda kuyankhula zonyada amadziyitanira chiwonongeko. 20 Munthu wamtima woyipa zinthu sizimuyendera bwino;ndipo woyankhula zachinyengo amagwa mʼmavuto. 21 Mwana wopusa amamvetsa chisoni abambo ake,abambo a chitsiru sakhala ndi chimwemwe. 22 Mtima wosangalala uli ngati mankhwala abwino,koma mtima wokhumudwa umafowoketsa mafupa. 23 Munthu woyipa amalandira chiphuphu chamserikuti apotoze chiweruzo cholungama. 24 Munthu wozindikira zinthu, maso ake amakhala pa nzeru,koma chitsiru chimwazamwaza maso ake pa dziko lonse lapansi. 25 Mwana wopusa amamvetsa chisoni abambo akendipo amapweteketsa mtima amayi ake. 26 Sibwino kulipitsa munthu wosalakwa,kapena kulanga anthu osalakwa. 27 Munthu wosunga pakamwa ndiye wodziwa zinthu,ndipo wodekha mtima ndiye womvetsa bwino zinthu. 28 Ngakhale chitsiru chimakhala ngati chanzeru chikakhala chete;ndipo chikatseka pakamwa chimakhala ngati munthu wochenjera.
In Other Versions
Proverbs 17 in the ANGEFD
Proverbs 17 in the ANTPNG2D
Proverbs 17 in the AS21
Proverbs 17 in the BAGH
Proverbs 17 in the BBPNG
Proverbs 17 in the BBT1E
Proverbs 17 in the BDS
Proverbs 17 in the BEV
Proverbs 17 in the BHAD
Proverbs 17 in the BIB
Proverbs 17 in the BLPT
Proverbs 17 in the BNT
Proverbs 17 in the BNTABOOT
Proverbs 17 in the BNTLV
Proverbs 17 in the BOATCB
Proverbs 17 in the BOATCB2
Proverbs 17 in the BOBCV
Proverbs 17 in the BOCNT
Proverbs 17 in the BOECS
Proverbs 17 in the BOHCB
Proverbs 17 in the BOHCV
Proverbs 17 in the BOHLNT
Proverbs 17 in the BOHNTLTAL
Proverbs 17 in the BOICB
Proverbs 17 in the BOILNTAP
Proverbs 17 in the BOITCV
Proverbs 17 in the BOKCV
Proverbs 17 in the BOKCV2
Proverbs 17 in the BOKHWOG
Proverbs 17 in the BOKSSV
Proverbs 17 in the BOLCB
Proverbs 17 in the BOLCB2
Proverbs 17 in the BOMCV
Proverbs 17 in the BONAV
Proverbs 17 in the BONCB
Proverbs 17 in the BONLT
Proverbs 17 in the BONUT2
Proverbs 17 in the BOPLNT
Proverbs 17 in the BOSCB
Proverbs 17 in the BOSNC
Proverbs 17 in the BOTLNT
Proverbs 17 in the BOVCB
Proverbs 17 in the BOYCB
Proverbs 17 in the BPBB
Proverbs 17 in the BPH
Proverbs 17 in the BSB
Proverbs 17 in the CCB
Proverbs 17 in the CUV
Proverbs 17 in the CUVS
Proverbs 17 in the DBT
Proverbs 17 in the DGDNT
Proverbs 17 in the DHNT
Proverbs 17 in the DNT
Proverbs 17 in the ELBE
Proverbs 17 in the EMTV
Proverbs 17 in the ESV
Proverbs 17 in the FBV
Proverbs 17 in the FEB
Proverbs 17 in the GGMNT
Proverbs 17 in the GNT
Proverbs 17 in the HARY
Proverbs 17 in the HNT
Proverbs 17 in the IRVA
Proverbs 17 in the IRVB
Proverbs 17 in the IRVG
Proverbs 17 in the IRVH
Proverbs 17 in the IRVK
Proverbs 17 in the IRVM
Proverbs 17 in the IRVM2
Proverbs 17 in the IRVO
Proverbs 17 in the IRVP
Proverbs 17 in the IRVT
Proverbs 17 in the IRVT2
Proverbs 17 in the IRVU
Proverbs 17 in the ISVN
Proverbs 17 in the JSNT
Proverbs 17 in the KAPI
Proverbs 17 in the KBT1ETNIK
Proverbs 17 in the KBV
Proverbs 17 in the KJV
Proverbs 17 in the KNFD
Proverbs 17 in the LBA
Proverbs 17 in the LBLA
Proverbs 17 in the LNT
Proverbs 17 in the LSV
Proverbs 17 in the MAAL
Proverbs 17 in the MBV
Proverbs 17 in the MBV2
Proverbs 17 in the MHNT
Proverbs 17 in the MKNFD
Proverbs 17 in the MNG
Proverbs 17 in the MNT
Proverbs 17 in the MNT2
Proverbs 17 in the MRS1T
Proverbs 17 in the NAA
Proverbs 17 in the NASB
Proverbs 17 in the NBLA
Proverbs 17 in the NBS
Proverbs 17 in the NBVTP
Proverbs 17 in the NET2
Proverbs 17 in the NIV11
Proverbs 17 in the NNT
Proverbs 17 in the NNT2
Proverbs 17 in the NNT3
Proverbs 17 in the PDDPT
Proverbs 17 in the PFNT
Proverbs 17 in the RMNT
Proverbs 17 in the SBIAS
Proverbs 17 in the SBIBS
Proverbs 17 in the SBIBS2
Proverbs 17 in the SBICS
Proverbs 17 in the SBIDS
Proverbs 17 in the SBIGS
Proverbs 17 in the SBIHS
Proverbs 17 in the SBIIS
Proverbs 17 in the SBIIS2
Proverbs 17 in the SBIIS3
Proverbs 17 in the SBIKS
Proverbs 17 in the SBIKS2
Proverbs 17 in the SBIMS
Proverbs 17 in the SBIOS
Proverbs 17 in the SBIPS
Proverbs 17 in the SBISS
Proverbs 17 in the SBITS
Proverbs 17 in the SBITS2
Proverbs 17 in the SBITS3
Proverbs 17 in the SBITS4
Proverbs 17 in the SBIUS
Proverbs 17 in the SBIVS
Proverbs 17 in the SBT
Proverbs 17 in the SBT1E
Proverbs 17 in the SCHL
Proverbs 17 in the SNT
Proverbs 17 in the SUSU
Proverbs 17 in the SUSU2
Proverbs 17 in the SYNO
Proverbs 17 in the TBIAOTANT
Proverbs 17 in the TBT1E
Proverbs 17 in the TBT1E2
Proverbs 17 in the TFTIP
Proverbs 17 in the TFTU
Proverbs 17 in the TGNTATF3T
Proverbs 17 in the THAI
Proverbs 17 in the TNFD
Proverbs 17 in the TNT
Proverbs 17 in the TNTIK
Proverbs 17 in the TNTIL
Proverbs 17 in the TNTIN
Proverbs 17 in the TNTIP
Proverbs 17 in the TNTIZ
Proverbs 17 in the TOMA
Proverbs 17 in the TTENT
Proverbs 17 in the UBG
Proverbs 17 in the UGV
Proverbs 17 in the UGV2
Proverbs 17 in the UGV3
Proverbs 17 in the VBL
Proverbs 17 in the VDCC
Proverbs 17 in the YALU
Proverbs 17 in the YAPE
Proverbs 17 in the YBVTP
Proverbs 17 in the ZBP