Proverbs 28 (BOGWICC)

1 Munthu woyipa amathawa ngakhale palibe wina womuthamangitsa,koma wolungama ndi wolimba mtima ngati mkango. 2 Pamene mʼdziko muli kuwukirana, dzikolo limakhala ndi olamulira ambiri,koma anthu omvetsa ndi odziwa zinthu bwino ndiwo angakhazikitse bata mʼdzikolo nthawi yayitali. 3 Munthu wosauka amene amapondereza osauka anzakeali ngati mvula yamkuntho imene imawononga mbewu mʼmunda. 4 Amene amakana malamulo amatamanda anthu oyipa,koma amene amasunga malamulo amatsutsana nawo. 5 Anthu oyipa samvetsa za chiweruzo cholungama,koma amene amafuna kuchita zimene Yehova afuna amachimvetsetsa bwino. 6 Munthu wosauka wa makhalidwe abwinoaposa munthu wolemera wa makhalidwe okhotakhota. 7 Amene amasunga malamulo ndi mwana wozindikira zinthu,koma amene amayenda ndi anthu adyera amachititsa manyazi abambo ake. 8 Amene amachulukitsa chuma chake polandira chiwongoladzanja chochulukaamakundikira chumacho anthu ena, amene adzachitira chifundo anthu osauka. 9 Wokana kumvera malamulongakhale pemphero lake lomwe limamunyansa Yehova. 10 Amene amatsogolera anthu olungama kuti ayende mʼnjira yoyipaadzagwera mu msampha wake womwe,koma anthu opanda cholakwa adzalandira cholowa chabwino. 11 Munthu wolemera amadziyesa kuti ndi wanzeru,koma munthu wosauka amene ali ndi nzeru zodziwa zinthu amamutulukira. 12 Pamene olungama apambana pamakhala chikondwerero chachikulu;koma pamene anthu oyipa apatsidwa ulamuliro, anthu amabisala. 13 Wobisa machimo ake sadzaona mwayi,koma aliyense amene awulula ndi kuleka machimowo, adzalandira chifundo. 14 Ndi wodala munthu amene amaopa Yehova nthawi zonse,koma amene aumitsa mtima wake adzagwa mʼmavuto. 15 Ngati mkango wobuma kapena chimbalangondo cholusandi mmenenso amakhalira munthu woyipa akamalamulira anthu osauka. 16 Wolamulira amene samvetsa zinthu ndiye amakhala wankhanzakoma amene amadana ndi phindu lopeza mwachinyengo adzakhala ndi moyo wautali. 17 Munthu amene wapalamula mlandu wopha munthuadzakhala wothawathawa mpaka imfa yake;wina aliyense asamuthandize. 18 Amene amayenda mokhulupirika adzapulumutsidwakoma amene njira zake ndi zokhotakhota adzagwa mʼdzenje. 19 Amene amalima mʼmunda mwake adzakhala ndi chakudya chochuluka,koma amene amangosewera adzakhala mʼmphawi. 20 Munthu wokhulupirika adzadalitsika kwambiri,koma wofuna kulemera mofulumira adzalangidwa. 21 Kukondera si kwabwino,ena amachita zolakwazo chifukwa cha kachidutswa ka buledi. 22 Munthu wowumira amafunitsitsa kulemerakoma sazindikira kuti umphawi udzamugwera. 23 Amene amadzudzula mnzake potsiriza pakemnzakeyo adzamukonda kwambiri, kupambana amene amanena mawu oshashalika. 24 Amene amabera abambo ake kapena amayi akenamanena kuti “kumeneko sikulakwa,”ndi mnzake wa munthu amene amasakaza. 25 Munthu wadyera amayambitsa mikangano,koma amene amadalira Yehova adzalemera. 26 Amene amadzidalira yekha ndi chitsiru,koma amene amatsata nzeru za ena adzapulumuka. 27 Amene amapereka kwa osauka sadzasowa kanthu,koma amene amatsinzina maso ake adzatembereredwa kwambiri. 28 Pamene anthu oyipa apatsidwa ulamuliro anthu amabisala,koma anthu oyipa akawonongeka olungama amapeza bwino.

In Other Versions

Proverbs 28 in the ANGEFD

Proverbs 28 in the ANTPNG2D

Proverbs 28 in the AS21

Proverbs 28 in the BAGH

Proverbs 28 in the BBPNG

Proverbs 28 in the BBT1E

Proverbs 28 in the BDS

Proverbs 28 in the BEV

Proverbs 28 in the BHAD

Proverbs 28 in the BIB

Proverbs 28 in the BLPT

Proverbs 28 in the BNT

Proverbs 28 in the BNTABOOT

Proverbs 28 in the BNTLV

Proverbs 28 in the BOATCB

Proverbs 28 in the BOATCB2

Proverbs 28 in the BOBCV

Proverbs 28 in the BOCNT

Proverbs 28 in the BOECS

Proverbs 28 in the BOHCB

Proverbs 28 in the BOHCV

Proverbs 28 in the BOHLNT

Proverbs 28 in the BOHNTLTAL

Proverbs 28 in the BOICB

Proverbs 28 in the BOILNTAP

Proverbs 28 in the BOITCV

Proverbs 28 in the BOKCV

Proverbs 28 in the BOKCV2

Proverbs 28 in the BOKHWOG

Proverbs 28 in the BOKSSV

Proverbs 28 in the BOLCB

Proverbs 28 in the BOLCB2

Proverbs 28 in the BOMCV

Proverbs 28 in the BONAV

Proverbs 28 in the BONCB

Proverbs 28 in the BONLT

Proverbs 28 in the BONUT2

Proverbs 28 in the BOPLNT

Proverbs 28 in the BOSCB

Proverbs 28 in the BOSNC

Proverbs 28 in the BOTLNT

Proverbs 28 in the BOVCB

Proverbs 28 in the BOYCB

Proverbs 28 in the BPBB

Proverbs 28 in the BPH

Proverbs 28 in the BSB

Proverbs 28 in the CCB

Proverbs 28 in the CUV

Proverbs 28 in the CUVS

Proverbs 28 in the DBT

Proverbs 28 in the DGDNT

Proverbs 28 in the DHNT

Proverbs 28 in the DNT

Proverbs 28 in the ELBE

Proverbs 28 in the EMTV

Proverbs 28 in the ESV

Proverbs 28 in the FBV

Proverbs 28 in the FEB

Proverbs 28 in the GGMNT

Proverbs 28 in the GNT

Proverbs 28 in the HARY

Proverbs 28 in the HNT

Proverbs 28 in the IRVA

Proverbs 28 in the IRVB

Proverbs 28 in the IRVG

Proverbs 28 in the IRVH

Proverbs 28 in the IRVK

Proverbs 28 in the IRVM

Proverbs 28 in the IRVM2

Proverbs 28 in the IRVO

Proverbs 28 in the IRVP

Proverbs 28 in the IRVT

Proverbs 28 in the IRVT2

Proverbs 28 in the IRVU

Proverbs 28 in the ISVN

Proverbs 28 in the JSNT

Proverbs 28 in the KAPI

Proverbs 28 in the KBT1ETNIK

Proverbs 28 in the KBV

Proverbs 28 in the KJV

Proverbs 28 in the KNFD

Proverbs 28 in the LBA

Proverbs 28 in the LBLA

Proverbs 28 in the LNT

Proverbs 28 in the LSV

Proverbs 28 in the MAAL

Proverbs 28 in the MBV

Proverbs 28 in the MBV2

Proverbs 28 in the MHNT

Proverbs 28 in the MKNFD

Proverbs 28 in the MNG

Proverbs 28 in the MNT

Proverbs 28 in the MNT2

Proverbs 28 in the MRS1T

Proverbs 28 in the NAA

Proverbs 28 in the NASB

Proverbs 28 in the NBLA

Proverbs 28 in the NBS

Proverbs 28 in the NBVTP

Proverbs 28 in the NET2

Proverbs 28 in the NIV11

Proverbs 28 in the NNT

Proverbs 28 in the NNT2

Proverbs 28 in the NNT3

Proverbs 28 in the PDDPT

Proverbs 28 in the PFNT

Proverbs 28 in the RMNT

Proverbs 28 in the SBIAS

Proverbs 28 in the SBIBS

Proverbs 28 in the SBIBS2

Proverbs 28 in the SBICS

Proverbs 28 in the SBIDS

Proverbs 28 in the SBIGS

Proverbs 28 in the SBIHS

Proverbs 28 in the SBIIS

Proverbs 28 in the SBIIS2

Proverbs 28 in the SBIIS3

Proverbs 28 in the SBIKS

Proverbs 28 in the SBIKS2

Proverbs 28 in the SBIMS

Proverbs 28 in the SBIOS

Proverbs 28 in the SBIPS

Proverbs 28 in the SBISS

Proverbs 28 in the SBITS

Proverbs 28 in the SBITS2

Proverbs 28 in the SBITS3

Proverbs 28 in the SBITS4

Proverbs 28 in the SBIUS

Proverbs 28 in the SBIVS

Proverbs 28 in the SBT

Proverbs 28 in the SBT1E

Proverbs 28 in the SCHL

Proverbs 28 in the SNT

Proverbs 28 in the SUSU

Proverbs 28 in the SUSU2

Proverbs 28 in the SYNO

Proverbs 28 in the TBIAOTANT

Proverbs 28 in the TBT1E

Proverbs 28 in the TBT1E2

Proverbs 28 in the TFTIP

Proverbs 28 in the TFTU

Proverbs 28 in the TGNTATF3T

Proverbs 28 in the THAI

Proverbs 28 in the TNFD

Proverbs 28 in the TNT

Proverbs 28 in the TNTIK

Proverbs 28 in the TNTIL

Proverbs 28 in the TNTIN

Proverbs 28 in the TNTIP

Proverbs 28 in the TNTIZ

Proverbs 28 in the TOMA

Proverbs 28 in the TTENT

Proverbs 28 in the UBG

Proverbs 28 in the UGV

Proverbs 28 in the UGV2

Proverbs 28 in the UGV3

Proverbs 28 in the VBL

Proverbs 28 in the VDCC

Proverbs 28 in the YALU

Proverbs 28 in the YAPE

Proverbs 28 in the YBVTP

Proverbs 28 in the ZBP