Psalms 100 (BOGWICC)
undefined Salimo. Nyimbo yothokoza. 1 Fuwulani kwa Yehova mwachimwemwe, inu dziko lonse lapansi. 2 Mulambireni Yehova mosangalala;bwerani pamaso pake ndi nyimbo zachikondwerero. 3 Dziwani kuti Yehova ndi Mulungu.Iye ndiye amene anatipanga ndipo ife ndife ake;ndife anthu ake, nkhosa za pabusa pake. 4 Lowani ku zipata zake ndi chiyamikondi ku mabwalo ake ndi matamando;muyamikeni ndi kutamanda dzina lake. 5 Pakuti Yehova ndi wabwino ndipo chikondi chake ndi chamuyaya;kukhulupirika kwake nʼkokhazikika pa mibado ndi mibado.