Psalms 111 (BOGWICC)
1 Tamandani Yehova. Ndidzathokoza Yehova ndi mtima wanga wonsemʼbwalo la anthu olungama mtima ndi pa msonkhano. 2 Ntchito za Yehova nʼzazikulu;onse amene amakondwera nazo amazilingalira. 3 Zochita zake ndi za ulemerero ndi zaufumu,ndipo chilungamo chake ndi chosatha. 4 Iye wachititsa kuti zodabwitsa zake zikumbukirike;Yehova ndi wokoma mtima ndi wachifundo. 5 Amapereka chakudya kwa amene amamuopa Iye;amakumbukira pangano lake kwamuyaya. 6 Waonetsa anthu ake mphamvu ya ntchito zake,kuwapatsa mayiko a anthu a mitundu ina. 7 Ntchito za manja ake ndi zokhulupirika ndi zolungama;malangizo ake onse ndi odalirika. 8 Malamulo ndi okhazikika ku nthawi za nthawi,ochitidwa mokhulupirika ndi molungama. 9 Iyeyo amawombola anthu ake;anakhazikitsa pangano lake kwamuyayadzina lake ndi loyera ndi loopsa. 10 Kuopa Yehova ndicho chiyambi cha nzeru;onse amene amatsatira malangizo ake amamvetsa bwino zinthu.Iye ndi wotamandika mpaka muyaya.