Psalms 18 (BOGWICC)
undefined Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide mtumiki wa Yehova. Iye anayimbira Yehova nyimbo iyi pamene Yehovayo anamupulumutsa mʼdzanja la adani ake onse ndiponso mʼdzanja la Sauli. 1 Davide anati: Ine ndimakukondani Inu Yehova, mphamvu zanga. 2 Yehova ndiye thanthwe langa, chitetezo changa ndi mpulumutsi wanga;Mulungu wanga ndi thanthwe langa mʼmene ndimathawiramo.Chishango changa ndi ndodo yachipulumutso changa, ndi linga langa. 3 Ndimayitana Yehova amene ndi woyenera matamando,ndipo ndapulumutsidwa kwa adani anga. 4 Zingwe za imfa zinandizinga;mitsinje yothamanga yachiwonongeko inandiopsa kwambiri. 5 Anandimanga ndi zingwe za ku manda;misampha ya imfa inalimbana nane. 6 Mʼmasautso anga ndinapemphera kwa Yehova;ndinalirira kwa Mulungu wanga kuti andithandize.Ali mʼNyumba yake, anamva mawu anga;kulira kwanga kunafika pamaso pake ndi mʼmakutu mwake. 7 Dziko lapansi linanjenjemera ndi kuchita chivomerezi,ndipo maziko a mapiri anagwedezeka;ananjenjemera chifukwa Iye anakwiya. 8 Mʼmphuno mwake munatuluka utsi;moto wonyeketsa unatuluka mʼkamwa mwake,makala amoto anali lawilawi mʼkamwa mwake. 9 Iye anangʼamba thambo natsika pansi;pansi pa mapazi ake panali mitambo yakuda. 10 Iye anakwera pa Kerubi ndi kuwuluka;nawuluka ndi mphepo mwaliwiro. 11 Iye anapanga mdima kukhala chofunda chake,chophimba chake chomuzungulira chinali mitambo yakuda ya mlengalenga. 12 Mʼkuwala kumene kunali pamaso pake munkachokera matalala,makala amoto ndi ziphaliwali zongʼanima. 13 Yehova anabangula kumwamba ngati bingu,mawu a Wammwambamwamba anamveka ponseponse. 14 Iye anaponya mivi yake nabalalitsa adani ake,ndi zingʼaningʼani zake anawagonjetsa. 15 Zigwa za mʼnyanja zinaonekera poyera;maziko a dziko lapansi anakhala poyera,Yehova atabangula mwaukali,pamene mpweya wamphamvu unatuluka mʼmphuno mwanu. 16 Ali kumwamba, Iye anatambalitsa dzanja lake ndipo anandigwira;anandivuwula mʼmadzi ozama. 17 Anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu,adani anga, amene anali amphamvu kuposa ine. 18 Adaniwo analimbana nane pamene ndinali pa mavuto,koma Yehova anali thandizo langa. 19 Iye anandipititsa kumalo otakasuka;anandipulumutsa chifukwa amakondwera nane. 20 Yehova wandithandiza molingana ndi chilungamo changa;molingana ndi makhalidwe anga abwino, Iye wandipulumutsa. 21 Pakuti ine ndinatsata njira za Yehova;ndilibe mlandu wochoka pamaso Mulungu wanga. 22 Malamulo ake onse ali pamaso panga;sindinasiye malangizo ake. 23 Ndakhala moyo wosalakwa pamaso pakendipo ndakhala ndi kupewa tchimo. 24 Yehova wandipatsa mphotho molingana ndi chilungamo changa,molingana ndi kuyera kwa manja anga pamaso pake. 25 Kwa wokhulupirika, Inu mumaonetsa kukhulupirika kwanu;kwa anthu amakhalidwe abwino, Inu mumaonetsanso makhalidwe abwino, 26 kwa woyera mtima, Inu mumaonetsa kuyera mtima kwanu,koma kwa achinyengo mumaonetsanso kunyansidwa nawo. 27 Inu mumapulumutsa anthu odzichepetsa,koma anthu amtima odzikuza mumawatsitsa. 28 Inu Yehova, sungani nyale yanga kuti iziyakabe;Mulungu wanga wasandutsa mdima wanga kukhala kuwunika. 29 Ndi thandizo lanu nditha kulimbana ndi gulu la ankhondo;ndi Mulungu wanga nditha kuchita zosatheka ndi munthu. 30 Kunena za Mulungu, zochita zake ndi zangwiro;mawu a Yehova alibe cholakwika.Iye ndi chishangokwa onse amene amathawira kwa Iye. 31 Mulungu wina ndi uti wofanana nanu Yehova?Ndipo ndani amene ndi Thanthwe kupatula Mulungu wathu? 32 Ndi Mulungu amene anandipatsa mphamvundi kulungamitsa njira yanga. 33 Iye amasandutsa mapazi anga kukhala ngati ambawala yayikazi;Iye amandithandiza kuyimirira pamwamba pa mapiri. 34 Iye amaphunzitsa manja anga kuchita nkhondo;manja anga amatha kuthyola uta wachitsulo. 35 Inu mumandipatsa chishango chachipambano,ndipo dzanja lanu lamanja limandichirikiza;mumawerama pansi kundikuza. 36 Munakulitsa njira yoyendamo ine,kuti mapazi anga asaguluke. 37 Ndinathamangitsa adani anga ndi kuwapitirira;sindinabwerere mpaka atawonongedwa. 38 Ndinakantha adaniwo kotero kuti sanathenso kudzuka;anagwera pa mapazi anga. 39 Inu munandiveka ndi mphamvu yokachitira nkhondo,munachititsa kuti ndigonjetse adani anga. 40 Inu munachititsa adani anga kutembenuka, kuonetsa misana yawo pothawa,ndipo ine ndinawononga adani angawo. 41 Iwo anafuwula kupempha thandizo, koma panalibe ndi mmodzi yemwe owapulumutsa.Analirira kwa Yehova koma sanawayankhe. 42 Ine ndinawaperesa ngati fumbi lowuluka ndi mphepo.Ndinawapondaponda ngati matope a mʼmisewu. 43 Inu mwandipulumutsa mʼmanja mwa anthu;mwandisandutsa kukhala mtsogoleri wa anthu a mitundu ina.Anthu amene sindikuwadziwa ali pansi pa ulamuliro wanga. 44 Alendo amadzipereka okha pamaso panga;akangomva za ine amandigonjera. 45 Iwo onse anataya mtima;anatuluka mʼmalinga awo akunjenjemera. 46 Yehova ndi wamoyo! Litamandidwe Thanthwe langa!Akuzike Mulungu Mpulumutsi wanga! 47 Iye ndi Mulungu amene amabwezera chilango,amene amagonjetsa anthu a mitundu yonse amene ali pansi pa ulamuliro wanga, 48 amene amandipulumutsa mʼmanja mwa adani anga.Inu munandikuza kuposa adani anga;munandilanditsa mʼmanja mwa anthu ankhanza. 49 Choncho ine ndidzakutamandani pakati pa anthu a mitundu ina, Inu Yehova;ndidzayimba nyimbo zotamanda dzina lanu. 50 Iye amapereka chipambano chachikulu kwa mfumu yake;amaonetsa chikondi chosasinthika kwa wodzozedwa wake,kwa Davide ndi zidzukulu zake kwamuyaya.