Psalms 47 (BOGWICC)
undefined Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la ana a Kora. 1 Ombani mʼmanja, inu anthu onse;fuwulani kwa Mulungu ndi mawu achimwemwe. 2 Ndi woopsadi Yehova Wammwambamwamba;Mfumu yayikulu ya dziko lonse lapansi! 3 Iye anatigonjetsera mitundu yambirimbiri ya anthu;anayika anthu pansi pa mapazi athu. 4 Iye anatisankhira cholowa chathu,chonyaditsa cha Yakobo, amene anamukonda. Sela 5 Mulungu wakwera, anthu akumufuwulira mwachimwemwe,Yehova wakwera, akumuyimbira malipenga. 6 Imbani matamando kwa Mulungu, imbani matamando;imbani matamando kwa mfumu yathu, imbani matamando. 7 Pakuti Mulungu ndi mfumu ya dziko lonse lapansi;imbirani Iye salimo la matamando. 8 Mulungu akulamulira mitundu ya anthu;Mulungu wakhala pa mpando wake waufumu woyera. 9 Anthu otchuka mwa anthu a mitundu ina asonkhanamonga anthu a Mulungu wa Abrahamu,pakuti mafumu a dziko lapansi ndi ake a Mulungu;Iye wakwezedwa kwakukulu.