Psalms 87 (BOGWICC)
undefined Salimo la Ana a Kora. 1 Iye wakhazikitsa maziko ake pa phiri loyera; 2 Yehova amakonda zipata za Ziyonikupambana malo onse okhalamo a Yakobo. 3 Za ulemerero wako zimakambidwa,Iwe mzinda wa Mulungu:Sela 4 “Ndidzanena za Rahabe ndi Babulonipakati pa iwo amene amandidziwa.Dzikonso la Filisitiya, Turo pamodzi ndi Kusi,ndipo ndidzati, ‘Uyu anabadwira mʼZiyoni.’ ” 5 Ndithudi, za Ziyoni adzanena kuti,“Uyu ndi uyo anabadwira mwa iye,ndipo Wammwambamwamba adzakhazikitsa iyeyo.” 6 Yehova adzalemba mʼbuku la kawundula wa anthu a mitundu ina:“Uyu anabadwira mʼZiyoni.”Sela 7 Oyimba ndi ovina omwe adzati,“Akasupe anga onse ali mwa iwe.”