Revelation 13 (BOGWICC)
1 Ndipo ndinaona chirombo chikutuluka mʼnyanja. Chinali ndi nyanga khumi ndi mitu isanu ndi iwiri. Pa nyanga iliyonse chinavala chipewa chaufumu, ndipo pa mutu uliwonse panali dzina lonyoza Mulungu. 2 Chirombo chimene ndinachionacho chinali ngati kambuku, mapazi ake ngati chimbalangondo, kukamwa kwake ngati kwa mkango. Chinjoka chija chinapatsa chirombocho mphamvu zake, mpando wake waufumu ndiponso ulamuliro waukulu. 3 Umodzi wa mitu wa chirombocho unkaoneka ngati uli ndi bala losati nʼkupola, koma nʼkuti balalo litapola. Dziko lonse linadabwa ndipo linatsatira chirombocho. 4 Anthu anapembedza chinjoka chija chifukwa chinapereka ulamuliro wake kwa chirombocho. Nachonso chirombo chija anachipembedza nʼkumafunsa kuti, “Ndani angafanane ndi chirombochi? Ndani angachite nacho nkhondo?” 5 Chirombo chija chinaloledwa kuyankhula mawu onyada ndi achipongwe kwa Mulungu. Chinapatsidwa mphamvu zolamulira pa miyezi 42. 6 Ndipo chinayamba kuyankhula mawu achipongwe onyoza Mulungu, dzina lake, malo okhalamo ndi onse amene amakhala kumwamba. 7 Chinaloledwa kuchita nkhondo ndi oyera mtima ndi kuwagonjetsa. Ndipo chinapatsidwanso mphamvu zolamulira anthu a fuko lililonse, mtundu uliwonse ndi chiyankhulo chilichonse. 8 Anthu onse okhala pa dziko lapansi adzapembedza chirombocho, aliyense amene chilengedwere cha dziko lapansi dzina lake silinalembedwe mʼbuku la amoyo la Mwana Wankhosa anaphedwa uja. 9 Iye amene ali ndi makutu, amve. 10 “Woyenera kupita ku ukapolo,adzapita ku ukapolo.Woyenera kufa ndi lupanga,adzafa ndi lupanga.”Pamenepa kwa anthu a Mulungu pakufunika kupirira ndi kukhulupirika. 11 Kenaka ndinaona chirombo china chikutuluka mʼnthaka. Chinali ndi nyanga ziwiri ngati mwana wankhosa koma kuyankhula kwake ngati chinjoka. 12 Chinalamulira ndi mphamvu zonse za chirombo choyamba chija, ndipo chinachititsa kuti dziko lapansi ndi anthu okhalamo alambire chirombo choyamba chija, chimene bala lake losati nʼkupola linali litapola. 13 Ndipo chinachita zizindikiro zazikulu zodabwitsa, mpaka kumagwetsa moto pa dziko lapansi kuchokera kumwamba anthu akuona. 14 Chifukwa cha zizindikiro zimene chinaloledwa kuchita mʼmalo mwa chirombo choyamba chija, chimene bala lake linapola, chinanyenga anthu okhala pa dziko lapansi. Chinalamula anthu kuti apange fano mopereka ulemu kwa chirombo chimene chinavulazidwa ndi lupanga, koma nʼkukhalabe ndi moyo. 15 Chirombo cha chiwirichi chinapatsidwa mphamvu zakupereka mpweya kwa fano la chirombo choyamba chija kuti liyankhule ndi kuphetsa aliyense wokana kupembedza fanolo. 16 Chinakakamiza aliyense, wamngʼono, wamkulu, wolemera, wosauka, mfulu ndi kapolo kuti alembedwe chizindikiro pa dzanja lamanja kapena pa mphumi. 17 Chinkachita zimenezi kuti wina aliyense asaloledwe kugula kapena kugulitsa kanthu ngati alibe chizindikiro chimenechi, chimene ndi dzina la chirombocho kapena nambala yotanthauza dzina lake. 18 Pano pafunika nzeru. Munthu amene ali ndi nzeru atanthauze nambala ya chirombocho, pakuti nambalayo ikutanthauza munthu. Nambala yake ndi 666.
In Other Versions
Revelation 13 in the ANGEFD
Revelation 13 in the ANTPNG2D
Revelation 13 in the AS21
Revelation 13 in the BAGH
Revelation 13 in the BBPNG
Revelation 13 in the BBT1E
Revelation 13 in the BDS
Revelation 13 in the BEV
Revelation 13 in the BHAD
Revelation 13 in the BIB
Revelation 13 in the BLPT
Revelation 13 in the BNT
Revelation 13 in the BNTABOOT
Revelation 13 in the BNTLV
Revelation 13 in the BOATCB
Revelation 13 in the BOATCB2
Revelation 13 in the BOBCV
Revelation 13 in the BOCNT
Revelation 13 in the BOECS
Revelation 13 in the BOHCB
Revelation 13 in the BOHCV
Revelation 13 in the BOHLNT
Revelation 13 in the BOHNTLTAL
Revelation 13 in the BOICB
Revelation 13 in the BOILNTAP
Revelation 13 in the BOITCV
Revelation 13 in the BOKCV
Revelation 13 in the BOKCV2
Revelation 13 in the BOKHWOG
Revelation 13 in the BOKSSV
Revelation 13 in the BOLCB
Revelation 13 in the BOLCB2
Revelation 13 in the BOMCV
Revelation 13 in the BONAV
Revelation 13 in the BONCB
Revelation 13 in the BONLT
Revelation 13 in the BONUT2
Revelation 13 in the BOPLNT
Revelation 13 in the BOSCB
Revelation 13 in the BOSNC
Revelation 13 in the BOTLNT
Revelation 13 in the BOVCB
Revelation 13 in the BOYCB
Revelation 13 in the BPBB
Revelation 13 in the BPH
Revelation 13 in the BSB
Revelation 13 in the CCB
Revelation 13 in the CUV
Revelation 13 in the CUVS
Revelation 13 in the DBT
Revelation 13 in the DGDNT
Revelation 13 in the DHNT
Revelation 13 in the DNT
Revelation 13 in the ELBE
Revelation 13 in the EMTV
Revelation 13 in the ESV
Revelation 13 in the FBV
Revelation 13 in the FEB
Revelation 13 in the GGMNT
Revelation 13 in the GNT
Revelation 13 in the HARY
Revelation 13 in the HNT
Revelation 13 in the IRVA
Revelation 13 in the IRVB
Revelation 13 in the IRVG
Revelation 13 in the IRVH
Revelation 13 in the IRVK
Revelation 13 in the IRVM
Revelation 13 in the IRVM2
Revelation 13 in the IRVO
Revelation 13 in the IRVP
Revelation 13 in the IRVT
Revelation 13 in the IRVT2
Revelation 13 in the IRVU
Revelation 13 in the ISVN
Revelation 13 in the JSNT
Revelation 13 in the KAPI
Revelation 13 in the KBT1ETNIK
Revelation 13 in the KBV
Revelation 13 in the KJV
Revelation 13 in the KNFD
Revelation 13 in the LBA
Revelation 13 in the LBLA
Revelation 13 in the LNT
Revelation 13 in the LSV
Revelation 13 in the MAAL
Revelation 13 in the MBV
Revelation 13 in the MBV2
Revelation 13 in the MHNT
Revelation 13 in the MKNFD
Revelation 13 in the MNG
Revelation 13 in the MNT
Revelation 13 in the MNT2
Revelation 13 in the MRS1T
Revelation 13 in the NAA
Revelation 13 in the NASB
Revelation 13 in the NBLA
Revelation 13 in the NBS
Revelation 13 in the NBVTP
Revelation 13 in the NET2
Revelation 13 in the NIV11
Revelation 13 in the NNT
Revelation 13 in the NNT2
Revelation 13 in the NNT3
Revelation 13 in the PDDPT
Revelation 13 in the PFNT
Revelation 13 in the RMNT
Revelation 13 in the SBIAS
Revelation 13 in the SBIBS
Revelation 13 in the SBIBS2
Revelation 13 in the SBICS
Revelation 13 in the SBIDS
Revelation 13 in the SBIGS
Revelation 13 in the SBIHS
Revelation 13 in the SBIIS
Revelation 13 in the SBIIS2
Revelation 13 in the SBIIS3
Revelation 13 in the SBIKS
Revelation 13 in the SBIKS2
Revelation 13 in the SBIMS
Revelation 13 in the SBIOS
Revelation 13 in the SBIPS
Revelation 13 in the SBISS
Revelation 13 in the SBITS
Revelation 13 in the SBITS2
Revelation 13 in the SBITS3
Revelation 13 in the SBITS4
Revelation 13 in the SBIUS
Revelation 13 in the SBIVS
Revelation 13 in the SBT
Revelation 13 in the SBT1E
Revelation 13 in the SCHL
Revelation 13 in the SNT
Revelation 13 in the SUSU
Revelation 13 in the SUSU2
Revelation 13 in the SYNO
Revelation 13 in the TBIAOTANT
Revelation 13 in the TBT1E
Revelation 13 in the TBT1E2
Revelation 13 in the TFTIP
Revelation 13 in the TFTU
Revelation 13 in the TGNTATF3T
Revelation 13 in the THAI
Revelation 13 in the TNFD
Revelation 13 in the TNT
Revelation 13 in the TNTIK
Revelation 13 in the TNTIL
Revelation 13 in the TNTIN
Revelation 13 in the TNTIP
Revelation 13 in the TNTIZ
Revelation 13 in the TOMA
Revelation 13 in the TTENT
Revelation 13 in the UBG
Revelation 13 in the UGV
Revelation 13 in the UGV2
Revelation 13 in the UGV3
Revelation 13 in the VBL
Revelation 13 in the VDCC
Revelation 13 in the YALU
Revelation 13 in the YAPE
Revelation 13 in the YBVTP
Revelation 13 in the ZBP