Revelation 14 (BOGWICC)
1 Kenaka ndinaona patsogolo panga panali Mwana Wankhosa, atayimirira pa Phiri la Ziyoni, ndipo Iye anali pamodzi ndi anthu 144,000 amene pa mphumi pawo panalembedwa dzina la Mwana Wankhosayo ndi la Atate ake. 2 Ndipo ndinamva liwu lochokera kumwamba ngati mkokomo wa madzi ambiri, ndiponso ngati kugunda kwamphamvu kwa bingu. Liwu limene ndinamvalo linali ngati a anthu akuyimba azeze awo. 3 Anthuwo ankayimba nyimbo yatsopano patsogolo pa mpando waufumu ndi zamoyo zinayi zija ndi akuluakulu aja. Palibe ndi mmodzi yemwe amene anatha kuphunzira nyimboyo kupatula anthu 144,000 aja amene anawomboledwa pa dziko lapansi. 4 Awa ndiwo amene sanadzidetse koma anadzisunga ndipo sanadziyipitse ndi akazi. Anthu amenewa ndiwo ankatsatira Mwana Wankhosa kulikonse kumene ankapita. Ndiwo amene anagulidwa pakati pa anthu a dziko lapansi kuti akhale oyambirira kuperekedwa kwa Mulungu ndi kwa Mwana Wankhosa. 5 Iwo sananenepo bodza ndipo alibe cholakwa. 6 Kenaka ndinaona mngelo wina akuwuluka mu mlengalenga ndipo anali ndi Uthenga Wabwino wamuyaya woti akalalikire kwa anthu okhala pa dziko lapansi, kwa a mtundu uliwonse, a fuko lililonse, a chiyankhulo chilichonse ndi kwa anthu onse. 7 Mngeloyo anayankhula mokweza mawu kuti, “Wopani Mulungu ndi kumutamanda, chifukwa nthawi yoweruza anthu yafika. Mumupembedze Iye amene analenga thambo, dziko lapansi, nyanja ndi akasupe amadzi.” 8 Mngelo wachiwiri anatsatana naye ndipo anati, “Wagwa! Wagwa Babuloni womveka uja, amene anachititsa anthu a mitundu yonse kumwa vinyo wa zilakolako zake zachigololo.” 9 Mngelo wachitatu anatsatana nawo ndi mawu ofuwula anati, “Ngati wina apembedza chirombo chija ndi fano lake ndi kulembedwa chizindikiro pa mphumi kapena pa dzanja, 10 nayenso adzamwa vinyo waukali wa Mulungu, umene wathiridwa popanda kuchepetsa mphamvu zake mʼchikho cha ukali wa Mulungu. Munthuyo adzazunzidwa ndi moto wamiyala yasulufure pamaso pa angelo oyera ndi pa Mwana Wankhosa. 11 Ndipo utsi wa moto wowazunzawo udzakwera kumwamba mpaka muyaya. Sikudzakhala kupumula usana ndi usiku kwa amene anapembedza chirombo chija ndi fano lake kapena kwa aliyense amene analembedwa chizindikiro cha dzina lake lija.” 12 Pamenepa ndi pofunika kupirira kwa anthu oyera mtima amene amasunga malamulo a Mulungu ndi kukhalabe okhulupirika kwa Yesu. 13 Kenaka ndinamva mawu kuchokera kumwamba akuti, “Lemba kuti, Odala anthu amene akufa ali mwa Ambuye kuyambira tsopano mpaka mʼtsogolo.”“Inde,” akutero Mzimu, “akapumule ntchito zawo zotopetsa pakuti ntchito zawo zidzawatsata.” 14 Ndinayangʼana patsogolo panga ndinaona mtambo woyera patakhalapo wina ngati Mwana wa Munthu, kumutu atavala chipewa chaufumu chagolide ndipo mʼdzanja mwake munali chikwakwa chakunthwa. 15 Tsono mngelo wina anatuluka mʼNyumba ya Mulungu nafuwula mwamphamvu kwa uja wokhala pa mtamboyu. Mngeloyo anati, “Tenga chikwakwa chako ndipo kolola, pakuti nthawi yokolola ya dziko la pansi yakwana” 16 Choncho wokhala pa mtambo uja anayamba kukolola dzinthu pa dziko lapansi ndi chikwakwa chakecho. 17 Mngelo wina anatuluka mʼNyumba ya Mulungu kumwamba ndipo nayenso anali ndi chikwakwa chakunthwa. 18 Kenaka mngelo winanso amene amalamulira moto, anatuluka kuchokera ku guwa lansembe nayitana mwamphamvu mngelo uja amene anali ndi chikwakwa chakunthwa chija, nati, “Tenga chikwakwa chako chakunthwacho yamba kudula mphesa za mʼmunda wamphesa wa pa dziko lapansi, pakuti mphesa zapsa kale.” 19 Pamenepo mngeloyo anayambadi kugwiritsa ntchito chikwakwa chake nadula mphesa za dziko lapansi, naziponya mʼchopondera mphesa chachikulu cha ukali woopsa wa Mulungu. 20 Mphesazo zinapondedwa mʼchopondera mphesa kunja kwa mzinda. Mʼchopondera mphesamo munatuluka magazi amene anayenderera ngati mtsinje, kuzama kwake mita ndi theka ndipo kutalika kwake makilomita 300.
In Other Versions
Revelation 14 in the ANGEFD
Revelation 14 in the ANTPNG2D
Revelation 14 in the AS21
Revelation 14 in the BAGH
Revelation 14 in the BBPNG
Revelation 14 in the BBT1E
Revelation 14 in the BDS
Revelation 14 in the BEV
Revelation 14 in the BHAD
Revelation 14 in the BIB
Revelation 14 in the BLPT
Revelation 14 in the BNT
Revelation 14 in the BNTABOOT
Revelation 14 in the BNTLV
Revelation 14 in the BOATCB
Revelation 14 in the BOATCB2
Revelation 14 in the BOBCV
Revelation 14 in the BOCNT
Revelation 14 in the BOECS
Revelation 14 in the BOHCB
Revelation 14 in the BOHCV
Revelation 14 in the BOHLNT
Revelation 14 in the BOHNTLTAL
Revelation 14 in the BOICB
Revelation 14 in the BOILNTAP
Revelation 14 in the BOITCV
Revelation 14 in the BOKCV
Revelation 14 in the BOKCV2
Revelation 14 in the BOKHWOG
Revelation 14 in the BOKSSV
Revelation 14 in the BOLCB
Revelation 14 in the BOLCB2
Revelation 14 in the BOMCV
Revelation 14 in the BONAV
Revelation 14 in the BONCB
Revelation 14 in the BONLT
Revelation 14 in the BONUT2
Revelation 14 in the BOPLNT
Revelation 14 in the BOSCB
Revelation 14 in the BOSNC
Revelation 14 in the BOTLNT
Revelation 14 in the BOVCB
Revelation 14 in the BOYCB
Revelation 14 in the BPBB
Revelation 14 in the BPH
Revelation 14 in the BSB
Revelation 14 in the CCB
Revelation 14 in the CUV
Revelation 14 in the CUVS
Revelation 14 in the DBT
Revelation 14 in the DGDNT
Revelation 14 in the DHNT
Revelation 14 in the DNT
Revelation 14 in the ELBE
Revelation 14 in the EMTV
Revelation 14 in the ESV
Revelation 14 in the FBV
Revelation 14 in the FEB
Revelation 14 in the GGMNT
Revelation 14 in the GNT
Revelation 14 in the HARY
Revelation 14 in the HNT
Revelation 14 in the IRVA
Revelation 14 in the IRVB
Revelation 14 in the IRVG
Revelation 14 in the IRVH
Revelation 14 in the IRVK
Revelation 14 in the IRVM
Revelation 14 in the IRVM2
Revelation 14 in the IRVO
Revelation 14 in the IRVP
Revelation 14 in the IRVT
Revelation 14 in the IRVT2
Revelation 14 in the IRVU
Revelation 14 in the ISVN
Revelation 14 in the JSNT
Revelation 14 in the KAPI
Revelation 14 in the KBT1ETNIK
Revelation 14 in the KBV
Revelation 14 in the KJV
Revelation 14 in the KNFD
Revelation 14 in the LBA
Revelation 14 in the LBLA
Revelation 14 in the LNT
Revelation 14 in the LSV
Revelation 14 in the MAAL
Revelation 14 in the MBV
Revelation 14 in the MBV2
Revelation 14 in the MHNT
Revelation 14 in the MKNFD
Revelation 14 in the MNG
Revelation 14 in the MNT
Revelation 14 in the MNT2
Revelation 14 in the MRS1T
Revelation 14 in the NAA
Revelation 14 in the NASB
Revelation 14 in the NBLA
Revelation 14 in the NBS
Revelation 14 in the NBVTP
Revelation 14 in the NET2
Revelation 14 in the NIV11
Revelation 14 in the NNT
Revelation 14 in the NNT2
Revelation 14 in the NNT3
Revelation 14 in the PDDPT
Revelation 14 in the PFNT
Revelation 14 in the RMNT
Revelation 14 in the SBIAS
Revelation 14 in the SBIBS
Revelation 14 in the SBIBS2
Revelation 14 in the SBICS
Revelation 14 in the SBIDS
Revelation 14 in the SBIGS
Revelation 14 in the SBIHS
Revelation 14 in the SBIIS
Revelation 14 in the SBIIS2
Revelation 14 in the SBIIS3
Revelation 14 in the SBIKS
Revelation 14 in the SBIKS2
Revelation 14 in the SBIMS
Revelation 14 in the SBIOS
Revelation 14 in the SBIPS
Revelation 14 in the SBISS
Revelation 14 in the SBITS
Revelation 14 in the SBITS2
Revelation 14 in the SBITS3
Revelation 14 in the SBITS4
Revelation 14 in the SBIUS
Revelation 14 in the SBIVS
Revelation 14 in the SBT
Revelation 14 in the SBT1E
Revelation 14 in the SCHL
Revelation 14 in the SNT
Revelation 14 in the SUSU
Revelation 14 in the SUSU2
Revelation 14 in the SYNO
Revelation 14 in the TBIAOTANT
Revelation 14 in the TBT1E
Revelation 14 in the TBT1E2
Revelation 14 in the TFTIP
Revelation 14 in the TFTU
Revelation 14 in the TGNTATF3T
Revelation 14 in the THAI
Revelation 14 in the TNFD
Revelation 14 in the TNT
Revelation 14 in the TNTIK
Revelation 14 in the TNTIL
Revelation 14 in the TNTIN
Revelation 14 in the TNTIP
Revelation 14 in the TNTIZ
Revelation 14 in the TOMA
Revelation 14 in the TTENT
Revelation 14 in the UBG
Revelation 14 in the UGV
Revelation 14 in the UGV2
Revelation 14 in the UGV3
Revelation 14 in the VBL
Revelation 14 in the VDCC
Revelation 14 in the YALU
Revelation 14 in the YAPE
Revelation 14 in the YBVTP
Revelation 14 in the ZBP