Revelation 17 (BOGWICC)
1 Mmodzi wa angelo asanu ndi awiri aja amene anali ndi mbale zisanu ndi ziwiri anadza nati kwa ine, “Bwera ndikuonetse chilango cha mkazi wadama wotchuka uja amene akukhala pambali pa madzi ambiri. 2 Mafumu a dziko lapansi amachita naye chigololo ndipo okhala pa dziko lapansi analedzera ndi vinyo wa zigololo zake.” 3 Kenaka mngeloyo anandinyamula mwa Mzimu Woyera kupita nane ku chipululu. Kumeneko ndinaona mkazi atakhala pa chirombo chofiira chokutidwa ndi mayina a chipongwe ndipo chinali ndi mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi. 4 Mkaziyo anavala zovala za pepo ndi zofiira nadzikongoletsa ndi golide, miyala yapamwamba ndi ngale. Ananyamula chikho chagolide mʼdzanja lake, chodzaza ndi zinthu zonyansa ndi fungo loyipa la zigololo zake. 5 Pa mphumi pake panalembedwa dzina lodabwitsa: BABULONI WAMKULUMAYI WA AKAZI ADAMANDI WAZOYIPITSA ZA DZIKO LAPANSI. 6 Ndinaona kuti mkaziyo anali ataledzera ndi magazi a oyera mtima, magazi a amene anachitira umboni Yesu.Nditamuona mkaziyo ndinadabwa kwambiri. 7 Kenaka mngelo uja anati kwa ine, “Bwanji ukudabwa? Ndikufotokozera chinsinsi cha mkaziyu ndi chinsinsi cha chirombo chimene wakwerapochi chokhala ndi mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi. 8 Chirombo chimene wachionachi chinalipo kale koma tsopano kulibe ndipo chidzatuluka ku chidzenje chakuya ndi kupita kukawonongedwa. Anthu okhala pa dziko lapansi amene mayina awo sanalembedwe mʼbuku lamoyo kuyambira pa kulengedwa kwa dziko lapansi adzadabwa pamene adzaona chirombocho, chifukwa chinalipo kale, tsopano kulibe, komabe chidzabwera. 9 “Zimenezi zikufunika kuganizira mwanzeru. Mitu isanu ndi iwiriyo ndi mapiri asanu ndi awiri pomwe mkazi uja amakhalirapo. Yomweyonso ndi mafumu asanu ndi awiri. 10 Mafumu asanu anagwa, imodzi ilipo ndipo ina sinabwere; koma pamene idzafika, idzayenera kukhala kwa kanthawi kochepa. 11 Chirombo chomwe chinalipo kale ndipo tsopano kulibe ndiyo mfumu yachisanu ndi chitatu. Iyo ndi ya mʼgulu la asanu ndi awiriwo ndipo ikupita kukawonongedwa. 12 “Nyanga khumi unaziona zija ndi mafumu khumi amene sanapatsidwe ulamuliro, koma adzapatsidwa ulamuliro pamodzi ndi chirombo kwa ora limodzi. 13 Mafumuwo ali ndi cholinga chimodzi ndipo adzapereka mphamvu ndi ulamuliro wawo kwa chirombocho. 14 Iwo adzachita nkhondo ndi Mwana Wankhosa, koma Mwana Wankhosayo adzawagonjetsa chifukwa Iye ndi Mbuye wa ambuye ndi Mfumu ya mafumu, ndipo amene adzakhala ndi Iye ndi oyitanidwa ake, osankhidwa ndi otsatira ake okhulupirika.” 15 Kenaka mngeloyo anati kwa ine, “Madzi amene unawaona pamene mkazi wadamayo anakhalapo ndiwo anthu ochuluka, mitundu ndi ziyankhulo. 16 Nyanga khumi ndi chirombo unazionazo zidzadya mkazi wadamayo. Zidzamufwifwitsa ndi kumusiya wamaliseche; zidzadya nyama yake ndi kumutentha ndi moto. 17 Pakuti Mulungu wayika ichi mʼmitima mwawo kuti akwaniritse cholinga chake povomerezana kupereka mphamvu zawo zolamulira kwa chirombo, kufikira Mawu a Mulungu atakwaniritsidwa. 18 Mkazi unamuonayo ndi mzinda waukulu umene ulamulira mafumu a dziko lapansi.”
In Other Versions
Revelation 17 in the ANGEFD
Revelation 17 in the ANTPNG2D
Revelation 17 in the AS21
Revelation 17 in the BAGH
Revelation 17 in the BBPNG
Revelation 17 in the BBT1E
Revelation 17 in the BDS
Revelation 17 in the BEV
Revelation 17 in the BHAD
Revelation 17 in the BIB
Revelation 17 in the BLPT
Revelation 17 in the BNT
Revelation 17 in the BNTABOOT
Revelation 17 in the BNTLV
Revelation 17 in the BOATCB
Revelation 17 in the BOATCB2
Revelation 17 in the BOBCV
Revelation 17 in the BOCNT
Revelation 17 in the BOECS
Revelation 17 in the BOHCB
Revelation 17 in the BOHCV
Revelation 17 in the BOHLNT
Revelation 17 in the BOHNTLTAL
Revelation 17 in the BOICB
Revelation 17 in the BOILNTAP
Revelation 17 in the BOITCV
Revelation 17 in the BOKCV
Revelation 17 in the BOKCV2
Revelation 17 in the BOKHWOG
Revelation 17 in the BOKSSV
Revelation 17 in the BOLCB
Revelation 17 in the BOLCB2
Revelation 17 in the BOMCV
Revelation 17 in the BONAV
Revelation 17 in the BONCB
Revelation 17 in the BONLT
Revelation 17 in the BONUT2
Revelation 17 in the BOPLNT
Revelation 17 in the BOSCB
Revelation 17 in the BOSNC
Revelation 17 in the BOTLNT
Revelation 17 in the BOVCB
Revelation 17 in the BOYCB
Revelation 17 in the BPBB
Revelation 17 in the BPH
Revelation 17 in the BSB
Revelation 17 in the CCB
Revelation 17 in the CUV
Revelation 17 in the CUVS
Revelation 17 in the DBT
Revelation 17 in the DGDNT
Revelation 17 in the DHNT
Revelation 17 in the DNT
Revelation 17 in the ELBE
Revelation 17 in the EMTV
Revelation 17 in the ESV
Revelation 17 in the FBV
Revelation 17 in the FEB
Revelation 17 in the GGMNT
Revelation 17 in the GNT
Revelation 17 in the HARY
Revelation 17 in the HNT
Revelation 17 in the IRVA
Revelation 17 in the IRVB
Revelation 17 in the IRVG
Revelation 17 in the IRVH
Revelation 17 in the IRVK
Revelation 17 in the IRVM
Revelation 17 in the IRVM2
Revelation 17 in the IRVO
Revelation 17 in the IRVP
Revelation 17 in the IRVT
Revelation 17 in the IRVT2
Revelation 17 in the IRVU
Revelation 17 in the ISVN
Revelation 17 in the JSNT
Revelation 17 in the KAPI
Revelation 17 in the KBT1ETNIK
Revelation 17 in the KBV
Revelation 17 in the KJV
Revelation 17 in the KNFD
Revelation 17 in the LBA
Revelation 17 in the LBLA
Revelation 17 in the LNT
Revelation 17 in the LSV
Revelation 17 in the MAAL
Revelation 17 in the MBV
Revelation 17 in the MBV2
Revelation 17 in the MHNT
Revelation 17 in the MKNFD
Revelation 17 in the MNG
Revelation 17 in the MNT
Revelation 17 in the MNT2
Revelation 17 in the MRS1T
Revelation 17 in the NAA
Revelation 17 in the NASB
Revelation 17 in the NBLA
Revelation 17 in the NBS
Revelation 17 in the NBVTP
Revelation 17 in the NET2
Revelation 17 in the NIV11
Revelation 17 in the NNT
Revelation 17 in the NNT2
Revelation 17 in the NNT3
Revelation 17 in the PDDPT
Revelation 17 in the PFNT
Revelation 17 in the RMNT
Revelation 17 in the SBIAS
Revelation 17 in the SBIBS
Revelation 17 in the SBIBS2
Revelation 17 in the SBICS
Revelation 17 in the SBIDS
Revelation 17 in the SBIGS
Revelation 17 in the SBIHS
Revelation 17 in the SBIIS
Revelation 17 in the SBIIS2
Revelation 17 in the SBIIS3
Revelation 17 in the SBIKS
Revelation 17 in the SBIKS2
Revelation 17 in the SBIMS
Revelation 17 in the SBIOS
Revelation 17 in the SBIPS
Revelation 17 in the SBISS
Revelation 17 in the SBITS
Revelation 17 in the SBITS2
Revelation 17 in the SBITS3
Revelation 17 in the SBITS4
Revelation 17 in the SBIUS
Revelation 17 in the SBIVS
Revelation 17 in the SBT
Revelation 17 in the SBT1E
Revelation 17 in the SCHL
Revelation 17 in the SNT
Revelation 17 in the SUSU
Revelation 17 in the SUSU2
Revelation 17 in the SYNO
Revelation 17 in the TBIAOTANT
Revelation 17 in the TBT1E
Revelation 17 in the TBT1E2
Revelation 17 in the TFTIP
Revelation 17 in the TFTU
Revelation 17 in the TGNTATF3T
Revelation 17 in the THAI
Revelation 17 in the TNFD
Revelation 17 in the TNT
Revelation 17 in the TNTIK
Revelation 17 in the TNTIL
Revelation 17 in the TNTIN
Revelation 17 in the TNTIP
Revelation 17 in the TNTIZ
Revelation 17 in the TOMA
Revelation 17 in the TTENT
Revelation 17 in the UBG
Revelation 17 in the UGV
Revelation 17 in the UGV2
Revelation 17 in the UGV3
Revelation 17 in the VBL
Revelation 17 in the VDCC
Revelation 17 in the YALU
Revelation 17 in the YAPE
Revelation 17 in the YBVTP
Revelation 17 in the ZBP