Revelation 19 (BOGWICC)
1 Zitatha izi, ndinamva chimene chinamveka ngati phokoso la gulu lalikulu mmwamba likufuwula kuti,“Haleluya!Chipulumutso ndi ulemerero ndi mphamvu ndi za Mulungu wathu, 2 pakuti chiweruzo chake ndi choona ndi cha chilungamo.Iye waweruza mkazi wadama wotchuka ujaamene anayipitsa dziko lonse lapansi ndi zigololo zake.Iye wabwezera pa mkaziyo magazi a atumiki ake.” 3 Ndipo anafuwulanso kuti,“Haleluya!Utsi wochokera kwa mkazi wadamayo udzakwera kumwamba mpaka muyaya.” 4 Akuluakulu 24 aja ndi zamoyo zinayi zija anadzigwetsa pansi kupembedza Mulungu amene anakhala pa mpando waufumu. Ndipo anafuwula kuti,“Ameni, Haleluya!” 5 Kenaka mawu anachoka ku mpando waufumu kuti,“Lemekezani Mulungu wathuinu nonse atumiki ake,inu amene mumamuopa,nonse angʼono ndi akulu!” 6 Kenaka ndinamva chimene chinamveka ngati gulu lalikulu, ngati mkokomo wamadzi othamanga ndipo ngati kugunda kwakukulu kwa bingu, ndipo anati,“Haleluya!Pakuti Ambuye Mulungu wathu Wamphamvuzonse akulamulira. 7 Tiyeni tisangalale ndi kukondwerandi kumutamanda!Pakuti nthawi ya ukwati wa Mwana Wankhosa yafika,ndipo Mkwatibwi wakonzekeratu. 8 Wapatsidwa nsalu yoyera kwambiri, yowala ndi yosadakuti avale.”(Nsalu yoyera kwambiri ikuyimira ntchito zolungama za oyera mtima). 9 Kenaka mngelo anandiwuza kuti, “Lemba kuti, Odala amene ayitanidwa ku phwando la ukwati wa Mwana Wankhosa.” Ndipo anatinso, “Awa ndiwo mawu woona a Mulungu.” 10 Pamenepo ndinadzigwetsa pa mapazi ake kumupembedza. Koma anandiwuza kuti, “Usatero ayi, ine ndine mtumiki mnzako ngati iwe yemwe, ndiponso ngati abale ako amene asunga umboni wa Yesu. Pembedza Mulungu. Pakuti umboni wa Yesu ndiye mzimu wa uneneri.” 11 Ndinaona kumwamba kutatsekuka ndipo patsogolo panga panali kavalo woyera, amene anakwerapo dzina lake linali Wokhulupirika ndiponso Woona. Poweruza ndi kuchita nkhondo, amachita molungama. 12 Maso ake anali ngati malawi amoto, ndipo pamutu pake panali zipewa zaufumu zambiri. Anali ndi dzina lolembedwa, lodziwika ndi Iye yekha, osati wina aliyense. 13 Iye anavala mkanjo woviyika mʼmagazi, ndipo dzina lake ndi Mawu a Mulungu. 14 Magulu ankhondo akumwamba ankamutsatira atakwera pa akavalo oyera, ndipo iwowo atavala nsalu zoyera kwambiri ndi zosada. 15 Mʼkamwa mwake munatuluka lupanga lakuthwa limene anati akaphe nalo mitundu ya anthu. Iye adzalamulira ndi ndodo yachitsulo. Iye anaponda choponderamo mphesa cha ukali wa Mulungu Wamphamvuzonse. 16 Pa chovala ndi pa ntchafu pake panalembedwa dzina ili:MFUMU YA MAFUMU NDI MBUYE WA AMBUYE. 17 Ndipo ndinaona mngelo atayimirira pa dzuwa amene anafuwula ndi mawu okweza kwa mbalame zonse zowuluka mlengalenga kuti, “Bwerani, sonkhanani pamodzi ku phwando lalikulu la Mulungu. 18 Kuti mudye mnofu wa mafumu, wa akulu a ankhondo, ndi wa anthu amphamvu, wa akavalo ndi okwerapo awo, ndi wa anthu onse, mfulu ndi akapolo, angʼono ndi aakulu.” 19 Kenaka ndinaona chirombo chija ndi mafumu a dziko lapansi ndi magulu ankhondo atasonkhana pamodzi kuti achite nkhondo ndi wokwera pa kavalo ndi ankhondo ake. 20 Koma chirombocho chinagwidwa pamodzi ndi mneneri wonyenga uja amene anachita zizindikiro zodabwitsa pamaso pake. Ndi zizindikirozi anasocheretsa amene analembedwa chizindikiro cha chirombocho napembedza fano lake. Onse awiri anaponyedwa amoyo mʼnyanja yamoto yasulufule wotentha. 21 Ena onse anaphedwa ndi lupanga lija linatuluka mʼkamwa mwa wokwera pa kavalo uja, ndipo mbalame zonse zinadya mokwanira mnofu wa anthu akufawo.
In Other Versions
Revelation 19 in the ANGEFD
Revelation 19 in the ANTPNG2D
Revelation 19 in the AS21
Revelation 19 in the BAGH
Revelation 19 in the BBPNG
Revelation 19 in the BBT1E
Revelation 19 in the BDS
Revelation 19 in the BEV
Revelation 19 in the BHAD
Revelation 19 in the BIB
Revelation 19 in the BLPT
Revelation 19 in the BNT
Revelation 19 in the BNTABOOT
Revelation 19 in the BNTLV
Revelation 19 in the BOATCB
Revelation 19 in the BOATCB2
Revelation 19 in the BOBCV
Revelation 19 in the BOCNT
Revelation 19 in the BOECS
Revelation 19 in the BOHCB
Revelation 19 in the BOHCV
Revelation 19 in the BOHLNT
Revelation 19 in the BOHNTLTAL
Revelation 19 in the BOICB
Revelation 19 in the BOILNTAP
Revelation 19 in the BOITCV
Revelation 19 in the BOKCV
Revelation 19 in the BOKCV2
Revelation 19 in the BOKHWOG
Revelation 19 in the BOKSSV
Revelation 19 in the BOLCB
Revelation 19 in the BOLCB2
Revelation 19 in the BOMCV
Revelation 19 in the BONAV
Revelation 19 in the BONCB
Revelation 19 in the BONLT
Revelation 19 in the BONUT2
Revelation 19 in the BOPLNT
Revelation 19 in the BOSCB
Revelation 19 in the BOSNC
Revelation 19 in the BOTLNT
Revelation 19 in the BOVCB
Revelation 19 in the BOYCB
Revelation 19 in the BPBB
Revelation 19 in the BPH
Revelation 19 in the BSB
Revelation 19 in the CCB
Revelation 19 in the CUV
Revelation 19 in the CUVS
Revelation 19 in the DBT
Revelation 19 in the DGDNT
Revelation 19 in the DHNT
Revelation 19 in the DNT
Revelation 19 in the ELBE
Revelation 19 in the EMTV
Revelation 19 in the ESV
Revelation 19 in the FBV
Revelation 19 in the FEB
Revelation 19 in the GGMNT
Revelation 19 in the GNT
Revelation 19 in the HARY
Revelation 19 in the HNT
Revelation 19 in the IRVA
Revelation 19 in the IRVB
Revelation 19 in the IRVG
Revelation 19 in the IRVH
Revelation 19 in the IRVK
Revelation 19 in the IRVM
Revelation 19 in the IRVM2
Revelation 19 in the IRVO
Revelation 19 in the IRVP
Revelation 19 in the IRVT
Revelation 19 in the IRVT2
Revelation 19 in the IRVU
Revelation 19 in the ISVN
Revelation 19 in the JSNT
Revelation 19 in the KAPI
Revelation 19 in the KBT1ETNIK
Revelation 19 in the KBV
Revelation 19 in the KJV
Revelation 19 in the KNFD
Revelation 19 in the LBA
Revelation 19 in the LBLA
Revelation 19 in the LNT
Revelation 19 in the LSV
Revelation 19 in the MAAL
Revelation 19 in the MBV
Revelation 19 in the MBV2
Revelation 19 in the MHNT
Revelation 19 in the MKNFD
Revelation 19 in the MNG
Revelation 19 in the MNT
Revelation 19 in the MNT2
Revelation 19 in the MRS1T
Revelation 19 in the NAA
Revelation 19 in the NASB
Revelation 19 in the NBLA
Revelation 19 in the NBS
Revelation 19 in the NBVTP
Revelation 19 in the NET2
Revelation 19 in the NIV11
Revelation 19 in the NNT
Revelation 19 in the NNT2
Revelation 19 in the NNT3
Revelation 19 in the PDDPT
Revelation 19 in the PFNT
Revelation 19 in the RMNT
Revelation 19 in the SBIAS
Revelation 19 in the SBIBS
Revelation 19 in the SBIBS2
Revelation 19 in the SBICS
Revelation 19 in the SBIDS
Revelation 19 in the SBIGS
Revelation 19 in the SBIHS
Revelation 19 in the SBIIS
Revelation 19 in the SBIIS2
Revelation 19 in the SBIIS3
Revelation 19 in the SBIKS
Revelation 19 in the SBIKS2
Revelation 19 in the SBIMS
Revelation 19 in the SBIOS
Revelation 19 in the SBIPS
Revelation 19 in the SBISS
Revelation 19 in the SBITS
Revelation 19 in the SBITS2
Revelation 19 in the SBITS3
Revelation 19 in the SBITS4
Revelation 19 in the SBIUS
Revelation 19 in the SBIVS
Revelation 19 in the SBT
Revelation 19 in the SBT1E
Revelation 19 in the SCHL
Revelation 19 in the SNT
Revelation 19 in the SUSU
Revelation 19 in the SUSU2
Revelation 19 in the SYNO
Revelation 19 in the TBIAOTANT
Revelation 19 in the TBT1E
Revelation 19 in the TBT1E2
Revelation 19 in the TFTIP
Revelation 19 in the TFTU
Revelation 19 in the TGNTATF3T
Revelation 19 in the THAI
Revelation 19 in the TNFD
Revelation 19 in the TNT
Revelation 19 in the TNTIK
Revelation 19 in the TNTIL
Revelation 19 in the TNTIN
Revelation 19 in the TNTIP
Revelation 19 in the TNTIZ
Revelation 19 in the TOMA
Revelation 19 in the TTENT
Revelation 19 in the UBG
Revelation 19 in the UGV
Revelation 19 in the UGV2
Revelation 19 in the UGV3
Revelation 19 in the VBL
Revelation 19 in the VDCC
Revelation 19 in the YALU
Revelation 19 in the YAPE
Revelation 19 in the YBVTP
Revelation 19 in the ZBP