Zechariah 8 (BOGWICC)
1 Awa ndi mawu amene Yehova Wamphamvuzonse ananena. 2 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ine ndikuchitira nsanje yayikulu Ziyoni. Mtima wanga ukupweteka chifukwa cha nsanje pa iyeyo.” 3 Yehova akuti, “Ndidzabwerera ku Ziyoni ndi kukakhala ku Yerusalemu. Pamenepo Yerusalemu adzatchedwa Mzinda wa Choonadi ndipo phiri la Yehova Wamphamvuzonse lidzatchedwa Phiri Lopatulika.” 4 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Abambo ndi amayi okalamba adzakhalanso mʼmisewu ya mu Yerusalemu, aliyense ali ndi ndodo mʼmanja mwake chifukwa cha kuchuluka kwa masiku ake. 5 Ndipo misewu ya mu mzindamo idzadzaza ndi anyamata ndi atsikana akusewera.” 6 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ngati zikuoneka kuti nʼzosatheka kwa anthu otsala pa nthawi ino, kodi zidzakhala zosathekanso kwa Ine?” akutero Yehova Wamphamvuzonse. 7 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Taonani ndidzapulumutsa anthu anga kuchokera ku mayiko a kummawa ndi kumadzulo. 8 Ndidzawabweretsa kuti adzakhale mu Yerusalemu; adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wawo, wokhulupirika ndi wolungama pakati pawo.” 9 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Inu amene tsopano mukumva mawu awa amene akuyankhula aneneri amene analipo pamene ankayika maziko a nyumba ya Yehova Wamphamvuzonse, ‘limbani mtima kuti mumange Nyumba ya Yehova.’ 10 Mpaka nthawi imeneyi panalibe munthu wolandira malipiro pa ntchito kapena ndalama zolipirira nyama zogwira ntchito. Panalibe munthu amene ankadzigwirira ntchito mwamtendere chifukwa choopa adani ake, pakuti Ine ndinkawayambanitsa. 11 Koma tsopano sindidzachitira otsala mwa anthu awa zomwe ndinachita kale,” akutero Yehova Wamphamvuzonse. 12 “Pakuti mbewu zidzamera bwino, mpesa udzabala zipatso zake, nthaka idzatulutsa zomera zake, ndi thambo lidzagwetsa mame. Ndidzapereka zonse kukhala cholowa cha otsala mwa anthu awa. 13 Monga mwakhala muli chinthu chotembereredwa pakati pa mitundu ina ya anthu, inu Yuda ndi Israeli, choncho ndidzakupulumutsani, ndipo mudzakhala dalitso. Musachite mantha, koma limbani mtima.” 14 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Monga ndinatsimikiza mtima kubweretsa choyipa pa inu, komanso osakuchitirani chisoni pamene makolo anu anandikwiyitsa,” akutero Yehova, 15 “Choncho tsopano ndatsimikiza mtima kuchitiranso zabwino Yerusalemu ndi Yuda. Musachite mantha. 16 Zinthu zoti muchite ndi izi: Muziwuzana zoona zokhazokha, muziweruza moona ndi mwachilungamo mʼmabwalo anu; 17 musamachitire mnzanu chiwembu, musamakonde kulumbira zonama. Zonsezi Ine ndimadana nazo,” akutero Yehova. 18 Yehova Wamphamvuzonse anayankhulanso nane. 19 Ndipo ananena kuti, “Kusala zakudya kwa pa mwezi wachinayi, chisanu, chisanu ndi chiwiri ndi wakhumi, kudzakhala nthawi yachimwemwe, ya chisangalalo ndi nthawi ya madyerero chikondwerero kwa Yuda. Nʼchifukwa chake muzikonda choonadi ndi mtendere.” 20 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Anthu a mitundu yambiri ndi anthu okhala mʼmizinda yambiri adzabwerabe, 21 ndipo nzika za mzinda wina zidzapita ku mzinda wina, kukanena kuti, ‘Tiyeni mwamsanga tikapemphe madalitso kwa Yehova ndi kukapembedza Yehova Wamphamvuzonse. Inenso ndikupita kumeneko.’ 22 Anthu ambiri ndiponso a ku mayiko amphamvu adzabwera ku Yerusalemu kudzapembedza Yehova Wamphamvuzonse ndi kudzapempha madalitso.” 23 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Masiku amenewo anthu khumi ochokera ku mitundu ya anthu a ziyankhulo zosiyana adzagwira mkanjo wa Myuda ndi kunena kuti, ‘Tipite nawo, chifukwa tamva kuti Mulungu ali nanu.’ ”
In Other Versions
Zechariah 8 in the ANGEFD
Zechariah 8 in the ANTPNG2D
Zechariah 8 in the AS21
Zechariah 8 in the BAGH
Zechariah 8 in the BBPNG
Zechariah 8 in the BBT1E
Zechariah 8 in the BDS
Zechariah 8 in the BEV
Zechariah 8 in the BHAD
Zechariah 8 in the BIB
Zechariah 8 in the BLPT
Zechariah 8 in the BNT
Zechariah 8 in the BNTABOOT
Zechariah 8 in the BNTLV
Zechariah 8 in the BOATCB
Zechariah 8 in the BOATCB2
Zechariah 8 in the BOBCV
Zechariah 8 in the BOCNT
Zechariah 8 in the BOECS
Zechariah 8 in the BOHCB
Zechariah 8 in the BOHCV
Zechariah 8 in the BOHLNT
Zechariah 8 in the BOHNTLTAL
Zechariah 8 in the BOICB
Zechariah 8 in the BOILNTAP
Zechariah 8 in the BOITCV
Zechariah 8 in the BOKCV
Zechariah 8 in the BOKCV2
Zechariah 8 in the BOKHWOG
Zechariah 8 in the BOKSSV
Zechariah 8 in the BOLCB
Zechariah 8 in the BOLCB2
Zechariah 8 in the BOMCV
Zechariah 8 in the BONAV
Zechariah 8 in the BONCB
Zechariah 8 in the BONLT
Zechariah 8 in the BONUT2
Zechariah 8 in the BOPLNT
Zechariah 8 in the BOSCB
Zechariah 8 in the BOSNC
Zechariah 8 in the BOTLNT
Zechariah 8 in the BOVCB
Zechariah 8 in the BOYCB
Zechariah 8 in the BPBB
Zechariah 8 in the BPH
Zechariah 8 in the BSB
Zechariah 8 in the CCB
Zechariah 8 in the CUV
Zechariah 8 in the CUVS
Zechariah 8 in the DBT
Zechariah 8 in the DGDNT
Zechariah 8 in the DHNT
Zechariah 8 in the DNT
Zechariah 8 in the ELBE
Zechariah 8 in the EMTV
Zechariah 8 in the ESV
Zechariah 8 in the FBV
Zechariah 8 in the FEB
Zechariah 8 in the GGMNT
Zechariah 8 in the GNT
Zechariah 8 in the HARY
Zechariah 8 in the HNT
Zechariah 8 in the IRVA
Zechariah 8 in the IRVB
Zechariah 8 in the IRVG
Zechariah 8 in the IRVH
Zechariah 8 in the IRVK
Zechariah 8 in the IRVM
Zechariah 8 in the IRVM2
Zechariah 8 in the IRVO
Zechariah 8 in the IRVP
Zechariah 8 in the IRVT
Zechariah 8 in the IRVT2
Zechariah 8 in the IRVU
Zechariah 8 in the ISVN
Zechariah 8 in the JSNT
Zechariah 8 in the KAPI
Zechariah 8 in the KBT1ETNIK
Zechariah 8 in the KBV
Zechariah 8 in the KJV
Zechariah 8 in the KNFD
Zechariah 8 in the LBA
Zechariah 8 in the LBLA
Zechariah 8 in the LNT
Zechariah 8 in the LSV
Zechariah 8 in the MAAL
Zechariah 8 in the MBV
Zechariah 8 in the MBV2
Zechariah 8 in the MHNT
Zechariah 8 in the MKNFD
Zechariah 8 in the MNG
Zechariah 8 in the MNT
Zechariah 8 in the MNT2
Zechariah 8 in the MRS1T
Zechariah 8 in the NAA
Zechariah 8 in the NASB
Zechariah 8 in the NBLA
Zechariah 8 in the NBS
Zechariah 8 in the NBVTP
Zechariah 8 in the NET2
Zechariah 8 in the NIV11
Zechariah 8 in the NNT
Zechariah 8 in the NNT2
Zechariah 8 in the NNT3
Zechariah 8 in the PDDPT
Zechariah 8 in the PFNT
Zechariah 8 in the RMNT
Zechariah 8 in the SBIAS
Zechariah 8 in the SBIBS
Zechariah 8 in the SBIBS2
Zechariah 8 in the SBICS
Zechariah 8 in the SBIDS
Zechariah 8 in the SBIGS
Zechariah 8 in the SBIHS
Zechariah 8 in the SBIIS
Zechariah 8 in the SBIIS2
Zechariah 8 in the SBIIS3
Zechariah 8 in the SBIKS
Zechariah 8 in the SBIKS2
Zechariah 8 in the SBIMS
Zechariah 8 in the SBIOS
Zechariah 8 in the SBIPS
Zechariah 8 in the SBISS
Zechariah 8 in the SBITS
Zechariah 8 in the SBITS2
Zechariah 8 in the SBITS3
Zechariah 8 in the SBITS4
Zechariah 8 in the SBIUS
Zechariah 8 in the SBIVS
Zechariah 8 in the SBT
Zechariah 8 in the SBT1E
Zechariah 8 in the SCHL
Zechariah 8 in the SNT
Zechariah 8 in the SUSU
Zechariah 8 in the SUSU2
Zechariah 8 in the SYNO
Zechariah 8 in the TBIAOTANT
Zechariah 8 in the TBT1E
Zechariah 8 in the TBT1E2
Zechariah 8 in the TFTIP
Zechariah 8 in the TFTU
Zechariah 8 in the TGNTATF3T
Zechariah 8 in the THAI
Zechariah 8 in the TNFD
Zechariah 8 in the TNT
Zechariah 8 in the TNTIK
Zechariah 8 in the TNTIL
Zechariah 8 in the TNTIN
Zechariah 8 in the TNTIP
Zechariah 8 in the TNTIZ
Zechariah 8 in the TOMA
Zechariah 8 in the TTENT
Zechariah 8 in the UBG
Zechariah 8 in the UGV
Zechariah 8 in the UGV2
Zechariah 8 in the UGV3
Zechariah 8 in the VBL
Zechariah 8 in the VDCC
Zechariah 8 in the YALU
Zechariah 8 in the YAPE
Zechariah 8 in the YBVTP
Zechariah 8 in the ZBP