1 Chronicles 18 (BOGWICC)

1 Patapita nthawi, Davide anagonjetsa Afilisti ndipo anakhala pansi pa ulamuliro wake. Iye analanda Gati ndi midzi yake yozungulira mʼmanja mwa Afilistiwo. 2 Davide anagonjetsanso Amowabu, nakhala pansi pa ulamuliro wake ndipo ankapereka msonkho kwa iye. 3 Komanso Davide anagonjetsa Hadadezeri mfumu ya Zoba, mpaka ku Hamati, pamene anapita kukakhazikitsa ulamuliro wake mʼmbali mwa mtsinje wa Yufurate. 4 Davide analanda magaleta 1,000, anthu okwera magaleta 7,000 pamodzi ndi asilikali oyenda pansi 20,000. Iye anadula mitsempha ya akavalo onse okoka magaleta, koma anasiyapo akavalo 100 okha. 5 Aramu wa ku Damasiko atabwera kudzathandiza Hadadezeri mfumu ya ku Zoba, Davide anakantha asilikali 22,000. 6 Iye anakhazikitsa maboma mu ufumu wa Aramu wa ku Damasiko, ndipo Aaramu anakhala pansi pa ulamuliro wake ndipo ankapereka msonkho. Yehova ankamupatsa chipambano Davide kulikonse kumene ankapita. 7 Davide anatenga zishango zagolide zimene ankanyamula akuluakulu ankhondo a Hadadezeri ndi kubwera nazo ku Yerusalemu. 8 Kuchokera ku Teba ndi Kuni, mizinda ya Hadadezeri, Davide anatengako mkuwa wambiri umene Solomoni anapangira chimbiya, zipilala ndi zida zosiyanasiyana zamkuwa. 9 Tou, mfumu ya Hamati atamva kuti Davide wagonjetsa gulu lonse lankhondo la Hadadezeri mfumu ya Zoba, 10 anatumiza mwana wake Hadoramu kwa mfumu Davide kukamulonjera ndi kukamuyamikira chifukwa cha kupambana kwake pa nkhondo yake ndi Hadadezeriyo, amene analinso pa nkhondo ndi Tou. Hadoramu anabweretsa ziwiya zosiyanasiyana zagolide, zasiliva ndi zamkuwa. 11 Mfumu Davide inapereka zinthu zimenezi kwa Yehova, monga anachitira ndi siliva ndi golide zochokera ku mayiko ena onse monga Edomu ndi Mowabu, Aamoni ndi Afilisti, ndi Aamaleki. 12 Abisai mwana wa Zeruya anakantha Aedomu 18,000 mu Chigwa cha Mchere. 13 Iye anayika maboma ku Edomu, ndipo Aedomu onse anakhala pansi pa Davide. Yehova ankapambanitsa Davide kulikonse kumene ankapita. 14 Davide analamulira dziko lonse la Israeli ndipo ankachita zonse mwachilungamo ndi molondola pamaso pa anthu ake onse. 15 Yowabu, mwana wa Zeruya anali mkulu wa ankhondo; Yehosafati mwana wa Ahiludi anali mlembi wa zochitika; 16 Zadoki, mwana wa Ahitubi ndi Ahimeleki mwana wa Abiatara anali ansembe; Savisa anali mlembi; 17 Benaya mwana wa Yehoyada anali mtsogoleri wa Akereti ndi Apeleti, ndipo ana a Davide anali alangizi a mfumu.

In Other Versions

1 Chronicles 18 in the ANGEFD

1 Chronicles 18 in the ANTPNG2D

1 Chronicles 18 in the AS21

1 Chronicles 18 in the BAGH

1 Chronicles 18 in the BBPNG

1 Chronicles 18 in the BBT1E

1 Chronicles 18 in the BDS

1 Chronicles 18 in the BEV

1 Chronicles 18 in the BHAD

1 Chronicles 18 in the BIB

1 Chronicles 18 in the BLPT

1 Chronicles 18 in the BNT

1 Chronicles 18 in the BNTABOOT

1 Chronicles 18 in the BNTLV

1 Chronicles 18 in the BOATCB

1 Chronicles 18 in the BOATCB2

1 Chronicles 18 in the BOBCV

1 Chronicles 18 in the BOCNT

1 Chronicles 18 in the BOECS

1 Chronicles 18 in the BOHCB

1 Chronicles 18 in the BOHCV

1 Chronicles 18 in the BOHLNT

1 Chronicles 18 in the BOHNTLTAL

1 Chronicles 18 in the BOICB

1 Chronicles 18 in the BOILNTAP

1 Chronicles 18 in the BOITCV

1 Chronicles 18 in the BOKCV

1 Chronicles 18 in the BOKCV2

1 Chronicles 18 in the BOKHWOG

1 Chronicles 18 in the BOKSSV

1 Chronicles 18 in the BOLCB

1 Chronicles 18 in the BOLCB2

1 Chronicles 18 in the BOMCV

1 Chronicles 18 in the BONAV

1 Chronicles 18 in the BONCB

1 Chronicles 18 in the BONLT

1 Chronicles 18 in the BONUT2

1 Chronicles 18 in the BOPLNT

1 Chronicles 18 in the BOSCB

1 Chronicles 18 in the BOSNC

1 Chronicles 18 in the BOTLNT

1 Chronicles 18 in the BOVCB

1 Chronicles 18 in the BOYCB

1 Chronicles 18 in the BPBB

1 Chronicles 18 in the BPH

1 Chronicles 18 in the BSB

1 Chronicles 18 in the CCB

1 Chronicles 18 in the CUV

1 Chronicles 18 in the CUVS

1 Chronicles 18 in the DBT

1 Chronicles 18 in the DGDNT

1 Chronicles 18 in the DHNT

1 Chronicles 18 in the DNT

1 Chronicles 18 in the ELBE

1 Chronicles 18 in the EMTV

1 Chronicles 18 in the ESV

1 Chronicles 18 in the FBV

1 Chronicles 18 in the FEB

1 Chronicles 18 in the GGMNT

1 Chronicles 18 in the GNT

1 Chronicles 18 in the HARY

1 Chronicles 18 in the HNT

1 Chronicles 18 in the IRVA

1 Chronicles 18 in the IRVB

1 Chronicles 18 in the IRVG

1 Chronicles 18 in the IRVH

1 Chronicles 18 in the IRVK

1 Chronicles 18 in the IRVM

1 Chronicles 18 in the IRVM2

1 Chronicles 18 in the IRVO

1 Chronicles 18 in the IRVP

1 Chronicles 18 in the IRVT

1 Chronicles 18 in the IRVT2

1 Chronicles 18 in the IRVU

1 Chronicles 18 in the ISVN

1 Chronicles 18 in the JSNT

1 Chronicles 18 in the KAPI

1 Chronicles 18 in the KBT1ETNIK

1 Chronicles 18 in the KBV

1 Chronicles 18 in the KJV

1 Chronicles 18 in the KNFD

1 Chronicles 18 in the LBA

1 Chronicles 18 in the LBLA

1 Chronicles 18 in the LNT

1 Chronicles 18 in the LSV

1 Chronicles 18 in the MAAL

1 Chronicles 18 in the MBV

1 Chronicles 18 in the MBV2

1 Chronicles 18 in the MHNT

1 Chronicles 18 in the MKNFD

1 Chronicles 18 in the MNG

1 Chronicles 18 in the MNT

1 Chronicles 18 in the MNT2

1 Chronicles 18 in the MRS1T

1 Chronicles 18 in the NAA

1 Chronicles 18 in the NASB

1 Chronicles 18 in the NBLA

1 Chronicles 18 in the NBS

1 Chronicles 18 in the NBVTP

1 Chronicles 18 in the NET2

1 Chronicles 18 in the NIV11

1 Chronicles 18 in the NNT

1 Chronicles 18 in the NNT2

1 Chronicles 18 in the NNT3

1 Chronicles 18 in the PDDPT

1 Chronicles 18 in the PFNT

1 Chronicles 18 in the RMNT

1 Chronicles 18 in the SBIAS

1 Chronicles 18 in the SBIBS

1 Chronicles 18 in the SBIBS2

1 Chronicles 18 in the SBICS

1 Chronicles 18 in the SBIDS

1 Chronicles 18 in the SBIGS

1 Chronicles 18 in the SBIHS

1 Chronicles 18 in the SBIIS

1 Chronicles 18 in the SBIIS2

1 Chronicles 18 in the SBIIS3

1 Chronicles 18 in the SBIKS

1 Chronicles 18 in the SBIKS2

1 Chronicles 18 in the SBIMS

1 Chronicles 18 in the SBIOS

1 Chronicles 18 in the SBIPS

1 Chronicles 18 in the SBISS

1 Chronicles 18 in the SBITS

1 Chronicles 18 in the SBITS2

1 Chronicles 18 in the SBITS3

1 Chronicles 18 in the SBITS4

1 Chronicles 18 in the SBIUS

1 Chronicles 18 in the SBIVS

1 Chronicles 18 in the SBT

1 Chronicles 18 in the SBT1E

1 Chronicles 18 in the SCHL

1 Chronicles 18 in the SNT

1 Chronicles 18 in the SUSU

1 Chronicles 18 in the SUSU2

1 Chronicles 18 in the SYNO

1 Chronicles 18 in the TBIAOTANT

1 Chronicles 18 in the TBT1E

1 Chronicles 18 in the TBT1E2

1 Chronicles 18 in the TFTIP

1 Chronicles 18 in the TFTU

1 Chronicles 18 in the TGNTATF3T

1 Chronicles 18 in the THAI

1 Chronicles 18 in the TNFD

1 Chronicles 18 in the TNT

1 Chronicles 18 in the TNTIK

1 Chronicles 18 in the TNTIL

1 Chronicles 18 in the TNTIN

1 Chronicles 18 in the TNTIP

1 Chronicles 18 in the TNTIZ

1 Chronicles 18 in the TOMA

1 Chronicles 18 in the TTENT

1 Chronicles 18 in the UBG

1 Chronicles 18 in the UGV

1 Chronicles 18 in the UGV2

1 Chronicles 18 in the UGV3

1 Chronicles 18 in the VBL

1 Chronicles 18 in the VDCC

1 Chronicles 18 in the YALU

1 Chronicles 18 in the YAPE

1 Chronicles 18 in the YBVTP

1 Chronicles 18 in the ZBP