1 Chronicles 19 (BOGWICC)

1 Patapita nthawi Nahasi mfumu ya Aamoni inamwalira, ndipo mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake. 2 Davide anaganiza kuti, “Ine ndidzachitira chifundo Hanuni mwana wa Nahasi chifukwa abambo ake anandichitira zabwino.” Choncho Davide anatumiza anthu kuti akamupepesere kwa Hanuni chifukwa cha imfa ya abambo ake.Anthu amene Davide anawatuma atafika kwa Hanuni mʼdziko la Aamoni kudzamupepesa, 3 atsogoleri a ankhondo a Aamoni anawuza Hanuni kuti, “Kodi mukuganiza kuti Davide akupereka ulemu kwa abambo anu potumiza anthuwa kwa inu kudzapepesa? Kodi anthuwa sanawatumize kuti adzaone dziko lathu ndi kuchita ukazitape ndi cholinga chofuna kuwulanda?” 4 Choncho Hanuni anagwira anthu amene Davide anawatuma aja ndipo anawameta ndi kudula zovala zawo pakati mʼchiwuno mpaka matako kuonekera ndipo anawabweza kwawo. 5 Munthu wina atafika ndi kufotokozera Davide za anthuwo, iye anatuma amithenga kukakumana nawo, chifukwa anali ndi manyazi kwambiri. Mfumu inati, “Mukhale ku Yeriko mpaka ndevu zanu zitakula, ndipo kenaka mubwere kuno.” 6 Aamoni atazindikira kuti amukwiyitsa kwambiri Davide, Hanuni ndi Aamoni anatumiza siliva wolemera makilogalamu 34,000 kuti akalipirire magaleta ndi okwerapo ake a ku Mesopotamiya; Aramu-Maaka ndi Zoba. 7 Iwo analipira magaleta okwanira 32,000, pamodzi ndi mfumu ya ku Maaka ndi ankhondo ake. Amenewa anabwera ndi kudzamanga misasa yawo pafupi ndi Medeba. Nawonso Aamoni anabwera kuchokera ku mizinda yawo ndipo anapita kukachita nkhondo. 8 Davide atamva zimenezi, anatumiza Yowabu ndi gulu lonse la ankhondo amphamvu. 9 Aamoni anatuluka ndi kukhala mʼmizere ya nkhondo pa chipata cha mzinda wawo, pamene mafumu amene anabwera nawo anali kwa wokha, ku malo wopanda mitengo. 10 Yowabu ataona kuti kunali mizere ya ankhondo kutsogolo kwake ndi kumbuyo kwake; iye anasankha ena mwa ankhondo a Israeli odziwa kuchita bwino nkhondo ndipo anawayika kuti amenyane ndi Aaramu. 11 Iye anayika ankhondo ena otsalawo mʼmanja mwa Abisai mʼbale wake ndipo anawayika kuti amenyane ndi Aamoni. 12 Yowabu anati, “Ngati Aaramu andipose mphamvu, iwe ubwere udzandipulumutse; koma ngati Aamoni akupose mphamvu, ine ndidzabwera kudzakupulumutsa. 13 Limba mtima ndipo timenyane nawo mopanda mantha chifukwa cha anthu athu ndi mizinda ya Mulungu wathu. Yehova achite chomukomera pamaso pake.” 14 Choncho Yowabu ndi ankhondo amene anali naye anapita kukamenyana ndi Aaramu, ndipo iwo anathawa pamaso pake. 15 Aamoni atazindikira kuti Aaramu akuthawa, iwo anathawanso pamaso pa Abisai mʼbale wake ndi kulowa mu mzinda. Motero Yowabu anabwerera ku Yerusalemu. 16 Aaramu ataona kuti agonjetsedwa ndi Aisraeli, anatumiza amithenga kukayitana Aaramu amene anali ku tsidya la Mtsinje, pamodzi ndi mtsogoleri wa ankhondo wa Hadadezeri, Sofaki akuwatsogolera. 17 Davide atawuzidwa zimenezi, iye anasonkhanitsa Aisraeli onse ndi kuwoloka Yorodani. Iyeyo anapita kukakumana nawo ndipo anakhala mʼmizere yankhondo moyangʼanana ndipo iwo anamenyana naye. 18 Koma iwo anathawa pamaso pa Aisraeli, ndipo Davide anapha anthu okwera pa magaleta 7,000 ndi ankhondo oyenda pansi 40,000. Iye anaphanso Sofaki, mtsogoleri wawo wankhondo. 19 Mafumu amene ali pansi pa Hadadezeri ataona kuti agonjetsedwa ndi Aisraeli, anachita mtendere ndi Davide ndipo anakhala pansi pa ulamuliro wake.Motero Aaramu anaopa kuthandizanso Aamoni.

In Other Versions

1 Chronicles 19 in the ANGEFD

1 Chronicles 19 in the ANTPNG2D

1 Chronicles 19 in the AS21

1 Chronicles 19 in the BAGH

1 Chronicles 19 in the BBPNG

1 Chronicles 19 in the BBT1E

1 Chronicles 19 in the BDS

1 Chronicles 19 in the BEV

1 Chronicles 19 in the BHAD

1 Chronicles 19 in the BIB

1 Chronicles 19 in the BLPT

1 Chronicles 19 in the BNT

1 Chronicles 19 in the BNTABOOT

1 Chronicles 19 in the BNTLV

1 Chronicles 19 in the BOATCB

1 Chronicles 19 in the BOATCB2

1 Chronicles 19 in the BOBCV

1 Chronicles 19 in the BOCNT

1 Chronicles 19 in the BOECS

1 Chronicles 19 in the BOHCB

1 Chronicles 19 in the BOHCV

1 Chronicles 19 in the BOHLNT

1 Chronicles 19 in the BOHNTLTAL

1 Chronicles 19 in the BOICB

1 Chronicles 19 in the BOILNTAP

1 Chronicles 19 in the BOITCV

1 Chronicles 19 in the BOKCV

1 Chronicles 19 in the BOKCV2

1 Chronicles 19 in the BOKHWOG

1 Chronicles 19 in the BOKSSV

1 Chronicles 19 in the BOLCB

1 Chronicles 19 in the BOLCB2

1 Chronicles 19 in the BOMCV

1 Chronicles 19 in the BONAV

1 Chronicles 19 in the BONCB

1 Chronicles 19 in the BONLT

1 Chronicles 19 in the BONUT2

1 Chronicles 19 in the BOPLNT

1 Chronicles 19 in the BOSCB

1 Chronicles 19 in the BOSNC

1 Chronicles 19 in the BOTLNT

1 Chronicles 19 in the BOVCB

1 Chronicles 19 in the BOYCB

1 Chronicles 19 in the BPBB

1 Chronicles 19 in the BPH

1 Chronicles 19 in the BSB

1 Chronicles 19 in the CCB

1 Chronicles 19 in the CUV

1 Chronicles 19 in the CUVS

1 Chronicles 19 in the DBT

1 Chronicles 19 in the DGDNT

1 Chronicles 19 in the DHNT

1 Chronicles 19 in the DNT

1 Chronicles 19 in the ELBE

1 Chronicles 19 in the EMTV

1 Chronicles 19 in the ESV

1 Chronicles 19 in the FBV

1 Chronicles 19 in the FEB

1 Chronicles 19 in the GGMNT

1 Chronicles 19 in the GNT

1 Chronicles 19 in the HARY

1 Chronicles 19 in the HNT

1 Chronicles 19 in the IRVA

1 Chronicles 19 in the IRVB

1 Chronicles 19 in the IRVG

1 Chronicles 19 in the IRVH

1 Chronicles 19 in the IRVK

1 Chronicles 19 in the IRVM

1 Chronicles 19 in the IRVM2

1 Chronicles 19 in the IRVO

1 Chronicles 19 in the IRVP

1 Chronicles 19 in the IRVT

1 Chronicles 19 in the IRVT2

1 Chronicles 19 in the IRVU

1 Chronicles 19 in the ISVN

1 Chronicles 19 in the JSNT

1 Chronicles 19 in the KAPI

1 Chronicles 19 in the KBT1ETNIK

1 Chronicles 19 in the KBV

1 Chronicles 19 in the KJV

1 Chronicles 19 in the KNFD

1 Chronicles 19 in the LBA

1 Chronicles 19 in the LBLA

1 Chronicles 19 in the LNT

1 Chronicles 19 in the LSV

1 Chronicles 19 in the MAAL

1 Chronicles 19 in the MBV

1 Chronicles 19 in the MBV2

1 Chronicles 19 in the MHNT

1 Chronicles 19 in the MKNFD

1 Chronicles 19 in the MNG

1 Chronicles 19 in the MNT

1 Chronicles 19 in the MNT2

1 Chronicles 19 in the MRS1T

1 Chronicles 19 in the NAA

1 Chronicles 19 in the NASB

1 Chronicles 19 in the NBLA

1 Chronicles 19 in the NBS

1 Chronicles 19 in the NBVTP

1 Chronicles 19 in the NET2

1 Chronicles 19 in the NIV11

1 Chronicles 19 in the NNT

1 Chronicles 19 in the NNT2

1 Chronicles 19 in the NNT3

1 Chronicles 19 in the PDDPT

1 Chronicles 19 in the PFNT

1 Chronicles 19 in the RMNT

1 Chronicles 19 in the SBIAS

1 Chronicles 19 in the SBIBS

1 Chronicles 19 in the SBIBS2

1 Chronicles 19 in the SBICS

1 Chronicles 19 in the SBIDS

1 Chronicles 19 in the SBIGS

1 Chronicles 19 in the SBIHS

1 Chronicles 19 in the SBIIS

1 Chronicles 19 in the SBIIS2

1 Chronicles 19 in the SBIIS3

1 Chronicles 19 in the SBIKS

1 Chronicles 19 in the SBIKS2

1 Chronicles 19 in the SBIMS

1 Chronicles 19 in the SBIOS

1 Chronicles 19 in the SBIPS

1 Chronicles 19 in the SBISS

1 Chronicles 19 in the SBITS

1 Chronicles 19 in the SBITS2

1 Chronicles 19 in the SBITS3

1 Chronicles 19 in the SBITS4

1 Chronicles 19 in the SBIUS

1 Chronicles 19 in the SBIVS

1 Chronicles 19 in the SBT

1 Chronicles 19 in the SBT1E

1 Chronicles 19 in the SCHL

1 Chronicles 19 in the SNT

1 Chronicles 19 in the SUSU

1 Chronicles 19 in the SUSU2

1 Chronicles 19 in the SYNO

1 Chronicles 19 in the TBIAOTANT

1 Chronicles 19 in the TBT1E

1 Chronicles 19 in the TBT1E2

1 Chronicles 19 in the TFTIP

1 Chronicles 19 in the TFTU

1 Chronicles 19 in the TGNTATF3T

1 Chronicles 19 in the THAI

1 Chronicles 19 in the TNFD

1 Chronicles 19 in the TNT

1 Chronicles 19 in the TNTIK

1 Chronicles 19 in the TNTIL

1 Chronicles 19 in the TNTIN

1 Chronicles 19 in the TNTIP

1 Chronicles 19 in the TNTIZ

1 Chronicles 19 in the TOMA

1 Chronicles 19 in the TTENT

1 Chronicles 19 in the UBG

1 Chronicles 19 in the UGV

1 Chronicles 19 in the UGV2

1 Chronicles 19 in the UGV3

1 Chronicles 19 in the VBL

1 Chronicles 19 in the VDCC

1 Chronicles 19 in the YALU

1 Chronicles 19 in the YAPE

1 Chronicles 19 in the YBVTP

1 Chronicles 19 in the ZBP