1 Chronicles 23 (BOGWICC)

1 Davide atakalamba, ali ndi zaka zambiri, anayika Solomoni mwana wake kukhala mfumu ya Israeli. 2 Iye anasonkhanitsanso pamodzi atsogoleri onse a Israeli, pamodzi ndi ansembe ndi Alevi. 3 Anawerenga Alevi kuyambira a zaka makumi atatu ndi kupitirirapo, ndipo chiwerengero cha amuna onse chinali 38,000. 4 Davide anati, “Mwa amenewa, amuna 24,000 aziyangʼanira ntchito za mʼNyumba ya Mulungu ndipo 6,000 akhale akuluakulu ndi oweruza. 5 Amuna 4,000 akhale alonda a pa zipata ndipo 4,000 azitamanda Yehova ndi zipangizo zoyimbira zimene ndazipereka ndi cholinga chimenecho.” 6 Davide anagawa Aleviwo mʼmagulumagulu motsatira ana a Levi awa: Geresoni, Kohati ndi Merari. 7 Ana a Geresoni:Ladani ndi Simei. 8 Ana a Ladani:Mtsogoleri Yehieli, Zetamu ndi Yoweli. Onse analipo atatu. 9 Ana a Simei:Selomoti, Haziyeli ndi Harani. Onse analipo atatu.Awa anali atsogoleri a mabanja a Ladani. 10 Ndipo ana a Simei anali:Yahati, Zina, Yeusi ndi Beriya.Awa anali ana a Semei. Onse analipo anayi. 11 Mtsogoleri anali Yahati, ndipo Ziza anali wachiwiri, koma Yeusi ndi Beriya analibe ana aamuna ambiri. Kotero iwo anawerengedwa ngati banja limodzi ndipo anapatsidwa ntchito imodzinso yofanana. 12 Ana a Kohati:Amramu, Izihari, Hebroni ndi Uzieli. Onse analipo anayi. 13 Ana a Amramu:Aaroni ndi Mose.Aaroni ndi zidzukulu zake anapatulidwa kwamuyaya kuti azipereka zinthu zopatulika kwambiri monga nsembe pamaso pa Yehova, komanso kuti azitumikira pamaso pake ndi kumadalitsa anthu mʼdzina lake kwamuyaya. 14 Ana a Mose munthu wa Mulungu anawerengedwa ngati gawo la fuko la Levi. 15 Ana a Mose:Geresomu ndi Eliezara. 16 Zidzukulu za Geresomu:Mtsogoleri anali Subaeli. 17 Zidzukulu za Eliezara:Mtsogoleri anali Rehabiya.Eliezara analibe ana ena aamuna, koma ana a Rehabiya anali ochuluka kwambiri. 18 Ana a Izihari:Mtsogoleri anali Selomiti. 19 Ana a Hebroni:Mtsogoleri anali Yeriya, wachiwiri anali Amariya, Yahazieli anali wachitatu ndipo Yekameamu anali wachinayi. 20 Ana a Uzieli:Mtsogoleri anali Mika ndipo wachiwiri anali Isiya. 21 Ana a Merari:Mahili ndi Musi.Ana a Mahili:Eliezara ndi Kisi. 22 Eliezara anamwalira wopanda ana aamuna. Iye anali ndi ana aakazi okhaokha. Abale awo, ana a Kisi, ndiwo amene anawakwatira. 23 Ana a Musi:Mahili, Ederi ndi Yeremoti. Onse analipo atatu. 24 Izi zinali zidzukulu za Levi mwa mabanja awo, atsogoleri a mabanja monga momwe analembedwera mayina awo ndi monga momwenso anawerengedwera, banja lililonse pa lokha. Awa ndi anthu ogwira ntchito oyambira zaka makumi awiri zobadwa kapena kupitirirapo, amene amatumikira mʼNyumba ya Yehova. 25 Popeza Davide anati, “Pakuti Yehova Mulungu wa Israeli, wapereka mpumulo kwa anthu ake ndipo wabwera kudzakhala mu Yerusalemu kwamuyaya, 26 sikofunikiranso kuti Alevi azinyamula tenti kapena zipangizo za chipembedzo.” 27 Potsata malangizo otsiriza a Davide, Alevi anawerengedwa kuyambira amuna a zaka makumi awiri zakubadwa kapena kupitirirapo. 28 Ntchito ya Alevi inali kuthandiza zidzukulu za Aaroni pa ntchito yotumikira mʼNyumba ya Yehova monga kuyangʼanira mabwalo, zipinda zamʼmbali, kuyeretsa zinthu zonse zachipembedzo, ndiponso kuchita ntchito zina za mʼnyumba ya Mulungu. 29 Iwo amayangʼanira buledi amene amayikidwa pa tebulo, ufa wa nsembe yachakudya, timitanda ta buledi wopanda yisiti: kuphika ndi kusakaniza, ndiponso miyeso yonse ndi kukula kwake. 30 Iwo amayimiriranso mmawa uliwonse kuthokoza ndi kutamanda Yehova. Amachitanso chomwecho madzulo, 31 ndiponso popereka nsembe zopsereza kwa Yehova pa Sabata ndi pa chikondwerero cha Mwezi Watsopano, ndi pa nthawi yosankhidwa ya Chikondwerero. Iwo amatumikira pamaso pa Yehova nthawi zonse mwa chiwerengero chawo ndi momwe analangizidwira. 32 Ndipo kotero Alevi anachita ntchito yawo ya ku tenti ya msonkhano ya ku Malo Opatulika ndiponso molamulidwa ndi abale awo, zidzukulu za Aaroni, pa ntchito ya mʼNyumba ya Yehova.

In Other Versions

1 Chronicles 23 in the ANGEFD

1 Chronicles 23 in the ANTPNG2D

1 Chronicles 23 in the AS21

1 Chronicles 23 in the BAGH

1 Chronicles 23 in the BBPNG

1 Chronicles 23 in the BBT1E

1 Chronicles 23 in the BDS

1 Chronicles 23 in the BEV

1 Chronicles 23 in the BHAD

1 Chronicles 23 in the BIB

1 Chronicles 23 in the BLPT

1 Chronicles 23 in the BNT

1 Chronicles 23 in the BNTABOOT

1 Chronicles 23 in the BNTLV

1 Chronicles 23 in the BOATCB

1 Chronicles 23 in the BOATCB2

1 Chronicles 23 in the BOBCV

1 Chronicles 23 in the BOCNT

1 Chronicles 23 in the BOECS

1 Chronicles 23 in the BOHCB

1 Chronicles 23 in the BOHCV

1 Chronicles 23 in the BOHLNT

1 Chronicles 23 in the BOHNTLTAL

1 Chronicles 23 in the BOICB

1 Chronicles 23 in the BOILNTAP

1 Chronicles 23 in the BOITCV

1 Chronicles 23 in the BOKCV

1 Chronicles 23 in the BOKCV2

1 Chronicles 23 in the BOKHWOG

1 Chronicles 23 in the BOKSSV

1 Chronicles 23 in the BOLCB

1 Chronicles 23 in the BOLCB2

1 Chronicles 23 in the BOMCV

1 Chronicles 23 in the BONAV

1 Chronicles 23 in the BONCB

1 Chronicles 23 in the BONLT

1 Chronicles 23 in the BONUT2

1 Chronicles 23 in the BOPLNT

1 Chronicles 23 in the BOSCB

1 Chronicles 23 in the BOSNC

1 Chronicles 23 in the BOTLNT

1 Chronicles 23 in the BOVCB

1 Chronicles 23 in the BOYCB

1 Chronicles 23 in the BPBB

1 Chronicles 23 in the BPH

1 Chronicles 23 in the BSB

1 Chronicles 23 in the CCB

1 Chronicles 23 in the CUV

1 Chronicles 23 in the CUVS

1 Chronicles 23 in the DBT

1 Chronicles 23 in the DGDNT

1 Chronicles 23 in the DHNT

1 Chronicles 23 in the DNT

1 Chronicles 23 in the ELBE

1 Chronicles 23 in the EMTV

1 Chronicles 23 in the ESV

1 Chronicles 23 in the FBV

1 Chronicles 23 in the FEB

1 Chronicles 23 in the GGMNT

1 Chronicles 23 in the GNT

1 Chronicles 23 in the HARY

1 Chronicles 23 in the HNT

1 Chronicles 23 in the IRVA

1 Chronicles 23 in the IRVB

1 Chronicles 23 in the IRVG

1 Chronicles 23 in the IRVH

1 Chronicles 23 in the IRVK

1 Chronicles 23 in the IRVM

1 Chronicles 23 in the IRVM2

1 Chronicles 23 in the IRVO

1 Chronicles 23 in the IRVP

1 Chronicles 23 in the IRVT

1 Chronicles 23 in the IRVT2

1 Chronicles 23 in the IRVU

1 Chronicles 23 in the ISVN

1 Chronicles 23 in the JSNT

1 Chronicles 23 in the KAPI

1 Chronicles 23 in the KBT1ETNIK

1 Chronicles 23 in the KBV

1 Chronicles 23 in the KJV

1 Chronicles 23 in the KNFD

1 Chronicles 23 in the LBA

1 Chronicles 23 in the LBLA

1 Chronicles 23 in the LNT

1 Chronicles 23 in the LSV

1 Chronicles 23 in the MAAL

1 Chronicles 23 in the MBV

1 Chronicles 23 in the MBV2

1 Chronicles 23 in the MHNT

1 Chronicles 23 in the MKNFD

1 Chronicles 23 in the MNG

1 Chronicles 23 in the MNT

1 Chronicles 23 in the MNT2

1 Chronicles 23 in the MRS1T

1 Chronicles 23 in the NAA

1 Chronicles 23 in the NASB

1 Chronicles 23 in the NBLA

1 Chronicles 23 in the NBS

1 Chronicles 23 in the NBVTP

1 Chronicles 23 in the NET2

1 Chronicles 23 in the NIV11

1 Chronicles 23 in the NNT

1 Chronicles 23 in the NNT2

1 Chronicles 23 in the NNT3

1 Chronicles 23 in the PDDPT

1 Chronicles 23 in the PFNT

1 Chronicles 23 in the RMNT

1 Chronicles 23 in the SBIAS

1 Chronicles 23 in the SBIBS

1 Chronicles 23 in the SBIBS2

1 Chronicles 23 in the SBICS

1 Chronicles 23 in the SBIDS

1 Chronicles 23 in the SBIGS

1 Chronicles 23 in the SBIHS

1 Chronicles 23 in the SBIIS

1 Chronicles 23 in the SBIIS2

1 Chronicles 23 in the SBIIS3

1 Chronicles 23 in the SBIKS

1 Chronicles 23 in the SBIKS2

1 Chronicles 23 in the SBIMS

1 Chronicles 23 in the SBIOS

1 Chronicles 23 in the SBIPS

1 Chronicles 23 in the SBISS

1 Chronicles 23 in the SBITS

1 Chronicles 23 in the SBITS2

1 Chronicles 23 in the SBITS3

1 Chronicles 23 in the SBITS4

1 Chronicles 23 in the SBIUS

1 Chronicles 23 in the SBIVS

1 Chronicles 23 in the SBT

1 Chronicles 23 in the SBT1E

1 Chronicles 23 in the SCHL

1 Chronicles 23 in the SNT

1 Chronicles 23 in the SUSU

1 Chronicles 23 in the SUSU2

1 Chronicles 23 in the SYNO

1 Chronicles 23 in the TBIAOTANT

1 Chronicles 23 in the TBT1E

1 Chronicles 23 in the TBT1E2

1 Chronicles 23 in the TFTIP

1 Chronicles 23 in the TFTU

1 Chronicles 23 in the TGNTATF3T

1 Chronicles 23 in the THAI

1 Chronicles 23 in the TNFD

1 Chronicles 23 in the TNT

1 Chronicles 23 in the TNTIK

1 Chronicles 23 in the TNTIL

1 Chronicles 23 in the TNTIN

1 Chronicles 23 in the TNTIP

1 Chronicles 23 in the TNTIZ

1 Chronicles 23 in the TOMA

1 Chronicles 23 in the TTENT

1 Chronicles 23 in the UBG

1 Chronicles 23 in the UGV

1 Chronicles 23 in the UGV2

1 Chronicles 23 in the UGV3

1 Chronicles 23 in the VBL

1 Chronicles 23 in the VDCC

1 Chronicles 23 in the YALU

1 Chronicles 23 in the YAPE

1 Chronicles 23 in the YBVTP

1 Chronicles 23 in the ZBP