1 Corinthians 4 (BOGWICC)

1 Choncho tsono anthu atione ife monga atumiki a Khristu, ndiponso ngati osunga zinsinsi za Mulungu. 2 Chofunika kwambiri nʼchakuti amene apatsidwa udindo oyangʼanira aonetse kukhulupirika. 3 Ine ndilibe nazo kanthu ngati ndiweruzidwa ndi inu kapena khothi lina lililonse. Ndithu, inenso sindidziweruza ndekha. 4 Chikumbumtima changa sichikunditsutsa, koma sikuti ndine wolungama. Wondiweruza ine ndi Ambuye. 5 Chomwecho musaweruze nthawi yoweruza isanakwane. Dikirani mpaka Ambuye atabwera. Iye adzaonetsa poyera zimene zabisika mu mdima ndipo adzaonetsa maganizo a mʼmitima ya anthu. Pa nthawi imeneyo aliyense adzalandira kwa Mulungu chiyamiko. 6 Tsono abale, ndapereka chitsanzo cha ine mwini ndi Apolo kuti mupindule. Phunzirani kwa ife tanthauzo la mawu akuti, “Musamapitirire zimene Malemba akunena,” kuti musamanyade pamene wina aposa mnzake. 7 Pakuti ndani amakusiyanitsani ndi wina aliyense? Nʼchiyani muli nacho chimene simunalandire? Ndipo ngati munalandira, bwanji mumadzitukumula ngati kuti simunalandire? 8 Inu muli nazo kale zonse zimene mufuna! Inu mwalemera kale! Inu mwayamba kale kulamulira ife! Ndilakalaka mukanakhaladi mafumu kuti ife tikhale nawo mafumu pamodzi ndi inu. 9 Pakuti kwa ine zikuoneka ngati kuti Mulungu watiyika ife atumwi pachionetsero, kumapeto kwa mndandanda, monga anthu oweruzidwa kuti akaphedwe mʼmabwalo. Ife tayikidwa kuti tionekere ku dziko lonse, kwa angelo ndi anthu. 10 Ife ndife opusa chifukwa cha Khristu, koma inu ndinu anzeru mwa Khristu! Ife ndife ofowoka koma inu ndinu amphamvu! Inu ndinu olemekezeka koma ife ndife opeputsidwa! 11 Mpaka pano tili ndi njala ndi ludzu, tili ndi sanza, tikuzunzidwa, tilibe nyumba. 12 Timagwira ntchito molimbika ndi manja athu. Akamatitemberera, ife timadalitsa; tikasautsidwa, ife timapirira. 13 Pamene atilalatira timayankha mwachifundo. Mpaka pano takhala ngati zinyalala za dziko, monga zakudzala za dziko lapansi. 14 Sindikulemba izi kuti ndikuchititseni manyazi, koma kukuchenjezani monga ana anga okondedwa. 15 Ngakhale muli ndi anthu 10,000 okutsogolerani mwa Khristu, mulibe abambo ambiri, popeza mwa Khristu Yesu, ine ndakhala abambo anu kudzera mu Uthenga Wabwino. 16 Chifukwa chake ndikukupemphani kuti munditsanze ine. 17 Chifukwa cha ichi ndikutumiza kwa inu Timoteyo, mwana wanga amene ndimamukonda, amene ndi wokhulupirika mwa Ambuye. Adzakukumbutsani inuyo za moyo wanga mwa Khristu Yesu, umene ukugwirizana ndi zimene ndimaphunzitsa paliponse mu mpingo uliwonse. 18 Ena mwa inu mukudzitukumula, ngati kuti sindingabwere kwanu. 19 Koma ndibwera kwanuko posachedwapa, ngati Ambuye alola, ndipo ndi pamene ndidzadziwe osati zimene anthu odzitukumulawa akuyankhula, koma kuti mphamvu zawo nʼzotani. 20 Pakuti ufumu wa Mulungu si mawu chabe koma mphamvu. 21 Kodi musankha chiyani? Kodi ndidzabwere ndi chikwapu, kapena mu chikondi ndiponso mwa mzimu wofatsa?

In Other Versions

1 Corinthians 4 in the ANGEFD

1 Corinthians 4 in the ANTPNG2D

1 Corinthians 4 in the AS21

1 Corinthians 4 in the BAGH

1 Corinthians 4 in the BBPNG

1 Corinthians 4 in the BBT1E

1 Corinthians 4 in the BDS

1 Corinthians 4 in the BEV

1 Corinthians 4 in the BHAD

1 Corinthians 4 in the BIB

1 Corinthians 4 in the BLPT

1 Corinthians 4 in the BNT

1 Corinthians 4 in the BNTABOOT

1 Corinthians 4 in the BNTLV

1 Corinthians 4 in the BOATCB

1 Corinthians 4 in the BOATCB2

1 Corinthians 4 in the BOBCV

1 Corinthians 4 in the BOCNT

1 Corinthians 4 in the BOECS

1 Corinthians 4 in the BOHCB

1 Corinthians 4 in the BOHCV

1 Corinthians 4 in the BOHLNT

1 Corinthians 4 in the BOHNTLTAL

1 Corinthians 4 in the BOICB

1 Corinthians 4 in the BOILNTAP

1 Corinthians 4 in the BOITCV

1 Corinthians 4 in the BOKCV

1 Corinthians 4 in the BOKCV2

1 Corinthians 4 in the BOKHWOG

1 Corinthians 4 in the BOKSSV

1 Corinthians 4 in the BOLCB

1 Corinthians 4 in the BOLCB2

1 Corinthians 4 in the BOMCV

1 Corinthians 4 in the BONAV

1 Corinthians 4 in the BONCB

1 Corinthians 4 in the BONLT

1 Corinthians 4 in the BONUT2

1 Corinthians 4 in the BOPLNT

1 Corinthians 4 in the BOSCB

1 Corinthians 4 in the BOSNC

1 Corinthians 4 in the BOTLNT

1 Corinthians 4 in the BOVCB

1 Corinthians 4 in the BOYCB

1 Corinthians 4 in the BPBB

1 Corinthians 4 in the BPH

1 Corinthians 4 in the BSB

1 Corinthians 4 in the CCB

1 Corinthians 4 in the CUV

1 Corinthians 4 in the CUVS

1 Corinthians 4 in the DBT

1 Corinthians 4 in the DGDNT

1 Corinthians 4 in the DHNT

1 Corinthians 4 in the DNT

1 Corinthians 4 in the ELBE

1 Corinthians 4 in the EMTV

1 Corinthians 4 in the ESV

1 Corinthians 4 in the FBV

1 Corinthians 4 in the FEB

1 Corinthians 4 in the GGMNT

1 Corinthians 4 in the GNT

1 Corinthians 4 in the HARY

1 Corinthians 4 in the HNT

1 Corinthians 4 in the IRVA

1 Corinthians 4 in the IRVB

1 Corinthians 4 in the IRVG

1 Corinthians 4 in the IRVH

1 Corinthians 4 in the IRVK

1 Corinthians 4 in the IRVM

1 Corinthians 4 in the IRVM2

1 Corinthians 4 in the IRVO

1 Corinthians 4 in the IRVP

1 Corinthians 4 in the IRVT

1 Corinthians 4 in the IRVT2

1 Corinthians 4 in the IRVU

1 Corinthians 4 in the ISVN

1 Corinthians 4 in the JSNT

1 Corinthians 4 in the KAPI

1 Corinthians 4 in the KBT1ETNIK

1 Corinthians 4 in the KBV

1 Corinthians 4 in the KJV

1 Corinthians 4 in the KNFD

1 Corinthians 4 in the LBA

1 Corinthians 4 in the LBLA

1 Corinthians 4 in the LNT

1 Corinthians 4 in the LSV

1 Corinthians 4 in the MAAL

1 Corinthians 4 in the MBV

1 Corinthians 4 in the MBV2

1 Corinthians 4 in the MHNT

1 Corinthians 4 in the MKNFD

1 Corinthians 4 in the MNG

1 Corinthians 4 in the MNT

1 Corinthians 4 in the MNT2

1 Corinthians 4 in the MRS1T

1 Corinthians 4 in the NAA

1 Corinthians 4 in the NASB

1 Corinthians 4 in the NBLA

1 Corinthians 4 in the NBS

1 Corinthians 4 in the NBVTP

1 Corinthians 4 in the NET2

1 Corinthians 4 in the NIV11

1 Corinthians 4 in the NNT

1 Corinthians 4 in the NNT2

1 Corinthians 4 in the NNT3

1 Corinthians 4 in the PDDPT

1 Corinthians 4 in the PFNT

1 Corinthians 4 in the RMNT

1 Corinthians 4 in the SBIAS

1 Corinthians 4 in the SBIBS

1 Corinthians 4 in the SBIBS2

1 Corinthians 4 in the SBICS

1 Corinthians 4 in the SBIDS

1 Corinthians 4 in the SBIGS

1 Corinthians 4 in the SBIHS

1 Corinthians 4 in the SBIIS

1 Corinthians 4 in the SBIIS2

1 Corinthians 4 in the SBIIS3

1 Corinthians 4 in the SBIKS

1 Corinthians 4 in the SBIKS2

1 Corinthians 4 in the SBIMS

1 Corinthians 4 in the SBIOS

1 Corinthians 4 in the SBIPS

1 Corinthians 4 in the SBISS

1 Corinthians 4 in the SBITS

1 Corinthians 4 in the SBITS2

1 Corinthians 4 in the SBITS3

1 Corinthians 4 in the SBITS4

1 Corinthians 4 in the SBIUS

1 Corinthians 4 in the SBIVS

1 Corinthians 4 in the SBT

1 Corinthians 4 in the SBT1E

1 Corinthians 4 in the SCHL

1 Corinthians 4 in the SNT

1 Corinthians 4 in the SUSU

1 Corinthians 4 in the SUSU2

1 Corinthians 4 in the SYNO

1 Corinthians 4 in the TBIAOTANT

1 Corinthians 4 in the TBT1E

1 Corinthians 4 in the TBT1E2

1 Corinthians 4 in the TFTIP

1 Corinthians 4 in the TFTU

1 Corinthians 4 in the TGNTATF3T

1 Corinthians 4 in the THAI

1 Corinthians 4 in the TNFD

1 Corinthians 4 in the TNT

1 Corinthians 4 in the TNTIK

1 Corinthians 4 in the TNTIL

1 Corinthians 4 in the TNTIN

1 Corinthians 4 in the TNTIP

1 Corinthians 4 in the TNTIZ

1 Corinthians 4 in the TOMA

1 Corinthians 4 in the TTENT

1 Corinthians 4 in the UBG

1 Corinthians 4 in the UGV

1 Corinthians 4 in the UGV2

1 Corinthians 4 in the UGV3

1 Corinthians 4 in the VBL

1 Corinthians 4 in the VDCC

1 Corinthians 4 in the YALU

1 Corinthians 4 in the YAPE

1 Corinthians 4 in the YBVTP

1 Corinthians 4 in the ZBP