1 Corinthians 6 (BOGWICC)
1 Pamene wina wa inu ali ndi mlandu ndi mnzake, nʼchifukwa chiyani amatengera nkhaniyo kwa anthu akunja kuti akawaweruze mʼmalo mopita nayo kwa oyera mtima? 2 Kodi inu simukudziwa kuti anthu a Mulungu adzaweruza dziko lapansi? Ndipo ngati inu mungaweruze dziko lapansi, kodi sindinu oyenera kuweruza milandu ingʼonoyingʼono? 3 Kodi simukudziwa kuti mudzaweruza angelo? Nanga bwanji zinthu za mʼmoyo uno! 4 Nʼchifukwa chake, ngati pali milandu pa zinthu zotere, sankhani anthu ena kuti akhale oweruza ngakhale alibe udindo mu mpingo. 5 Ndikunena izi kuti ndikuchititseni manyazi. Moti nʼkutheka kuti pakati panu palibe wina wanzeru zokwanira kuti aziweruza mlandu pakati pa Akhristu? 6 Koma mʼmalo mwake mʼbale atengera ku bwalo la mlandu mʼbale mnzake kukaweruzidwa. Zonsezi pamaso pa akunja! 7 Chokha choti mwakasumirana chikuonetseratu kuti mwagonjetsedwa kale. Bwanji osangolola kuti ena akulakwireni? Bwanji osangolola kuti ena akubereni? 8 Mʼmalo mwake, inuyo ndiye mumabera ena ndi kuwalakwira, ndipo mumachita izi kwa abale anu. 9 Kodi simukudziwa kuti munthu woyipa sadzalowa mu ufumu wa Mulungu? Musanyengedwe: achigololo, kapena opembedza mafano, kapena achiwerewere, kapena amuna adama, kapena ogonana ndi amuna okhaokha; 10 kapena akuba, kapena aumbombo, kapena oledzera, kapena achipongwe, kapena opeza ndalama mwachinyengo sadzalowa mu ufumu wa Mulungu. 11 Ndipo umu ndi mmene ena mwa inu munalili. Koma munatsukidwa, munayeretsedwa, munalungamitsidwa mʼdzina la Ambuye Yesu Khristu ndi Mzimu wa Mulungu wathu. 12 Inu mumati, “Ine ndili ndi ufulu wochita chilichonse.” Komatu si zonse zimene nʼzothandiza. “Ndili ndi ufulu wochita chilichonse.” Koma sindidzagonjetsedwa ndi chilichonse. 13 Inu mumati, “Chakudya, kwake nʼkulowa mʼmimba ndipo mimba ntchito yake nʼkulandira chakudyacho.” Koma Mulungu adzawononga zonsezi. Thupi silochitira chigololo, koma la Ambuye, ndipo Ambuye ndiye mwini thupilo. 14 Mwamphamvu zake Mulungu anaukitsa Ambuye kwa akufa, ndipo ifenso adzatiukitsa. 15 Kodi simukudziwa kuti matupi anuwo ndi ziwalo za Khristu mwini? Kodi tsono ndingatenge ziwalo za Khristu nʼkuzisandutsa ziwalo za mkazi wadama? Zosatheka! 16 Kodi simukudziwa kuti amene amadzipereka kwa mkazi wadama, iyeyo ndi mkaziyo amasanduka thupi limodzi? Paja kunalembedwa kuti, “Awiriwo adzakhala thupi limodzi.” 17 Koma amene amadzipereka kwa Ambuye, iyeyo ndi Ambuye amakhala mzimu umodzi. 18 Thawani dama. Machimo onse amene munthu amachita amakhala kunja kwa thupi lake, koma amene amachita machimo okhudza chigololo, amachimwira thupi lake lomwe. 19 Kodi simukudziwa kuti thupi lanu ndi Nyumba ya Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene mwalandira kuchokera kwa Mulungu? Inu simuli panokha ayi. 20 Ndinu ochita kugulidwa. Nʼchifukwa chake lemekezani Mulungu mʼthupi lanu.
In Other Versions
1 Corinthians 6 in the ANGEFD
1 Corinthians 6 in the ANTPNG2D
1 Corinthians 6 in the AS21
1 Corinthians 6 in the BAGH
1 Corinthians 6 in the BBPNG
1 Corinthians 6 in the BBT1E
1 Corinthians 6 in the BDS
1 Corinthians 6 in the BEV
1 Corinthians 6 in the BHAD
1 Corinthians 6 in the BIB
1 Corinthians 6 in the BLPT
1 Corinthians 6 in the BNT
1 Corinthians 6 in the BNTABOOT
1 Corinthians 6 in the BNTLV
1 Corinthians 6 in the BOATCB
1 Corinthians 6 in the BOATCB2
1 Corinthians 6 in the BOBCV
1 Corinthians 6 in the BOCNT
1 Corinthians 6 in the BOECS
1 Corinthians 6 in the BOHCB
1 Corinthians 6 in the BOHCV
1 Corinthians 6 in the BOHLNT
1 Corinthians 6 in the BOHNTLTAL
1 Corinthians 6 in the BOICB
1 Corinthians 6 in the BOILNTAP
1 Corinthians 6 in the BOITCV
1 Corinthians 6 in the BOKCV
1 Corinthians 6 in the BOKCV2
1 Corinthians 6 in the BOKHWOG
1 Corinthians 6 in the BOKSSV
1 Corinthians 6 in the BOLCB
1 Corinthians 6 in the BOLCB2
1 Corinthians 6 in the BOMCV
1 Corinthians 6 in the BONAV
1 Corinthians 6 in the BONCB
1 Corinthians 6 in the BONLT
1 Corinthians 6 in the BONUT2
1 Corinthians 6 in the BOPLNT
1 Corinthians 6 in the BOSCB
1 Corinthians 6 in the BOSNC
1 Corinthians 6 in the BOTLNT
1 Corinthians 6 in the BOVCB
1 Corinthians 6 in the BOYCB
1 Corinthians 6 in the BPBB
1 Corinthians 6 in the BPH
1 Corinthians 6 in the BSB
1 Corinthians 6 in the CCB
1 Corinthians 6 in the CUV
1 Corinthians 6 in the CUVS
1 Corinthians 6 in the DBT
1 Corinthians 6 in the DGDNT
1 Corinthians 6 in the DHNT
1 Corinthians 6 in the DNT
1 Corinthians 6 in the ELBE
1 Corinthians 6 in the EMTV
1 Corinthians 6 in the ESV
1 Corinthians 6 in the FBV
1 Corinthians 6 in the FEB
1 Corinthians 6 in the GGMNT
1 Corinthians 6 in the GNT
1 Corinthians 6 in the HARY
1 Corinthians 6 in the HNT
1 Corinthians 6 in the IRVA
1 Corinthians 6 in the IRVB
1 Corinthians 6 in the IRVG
1 Corinthians 6 in the IRVH
1 Corinthians 6 in the IRVK
1 Corinthians 6 in the IRVM
1 Corinthians 6 in the IRVM2
1 Corinthians 6 in the IRVO
1 Corinthians 6 in the IRVP
1 Corinthians 6 in the IRVT
1 Corinthians 6 in the IRVT2
1 Corinthians 6 in the IRVU
1 Corinthians 6 in the ISVN
1 Corinthians 6 in the JSNT
1 Corinthians 6 in the KAPI
1 Corinthians 6 in the KBT1ETNIK
1 Corinthians 6 in the KBV
1 Corinthians 6 in the KJV
1 Corinthians 6 in the KNFD
1 Corinthians 6 in the LBA
1 Corinthians 6 in the LBLA
1 Corinthians 6 in the LNT
1 Corinthians 6 in the LSV
1 Corinthians 6 in the MAAL
1 Corinthians 6 in the MBV
1 Corinthians 6 in the MBV2
1 Corinthians 6 in the MHNT
1 Corinthians 6 in the MKNFD
1 Corinthians 6 in the MNG
1 Corinthians 6 in the MNT
1 Corinthians 6 in the MNT2
1 Corinthians 6 in the MRS1T
1 Corinthians 6 in the NAA
1 Corinthians 6 in the NASB
1 Corinthians 6 in the NBLA
1 Corinthians 6 in the NBS
1 Corinthians 6 in the NBVTP
1 Corinthians 6 in the NET2
1 Corinthians 6 in the NIV11
1 Corinthians 6 in the NNT
1 Corinthians 6 in the NNT2
1 Corinthians 6 in the NNT3
1 Corinthians 6 in the PDDPT
1 Corinthians 6 in the PFNT
1 Corinthians 6 in the RMNT
1 Corinthians 6 in the SBIAS
1 Corinthians 6 in the SBIBS
1 Corinthians 6 in the SBIBS2
1 Corinthians 6 in the SBICS
1 Corinthians 6 in the SBIDS
1 Corinthians 6 in the SBIGS
1 Corinthians 6 in the SBIHS
1 Corinthians 6 in the SBIIS
1 Corinthians 6 in the SBIIS2
1 Corinthians 6 in the SBIIS3
1 Corinthians 6 in the SBIKS
1 Corinthians 6 in the SBIKS2
1 Corinthians 6 in the SBIMS
1 Corinthians 6 in the SBIOS
1 Corinthians 6 in the SBIPS
1 Corinthians 6 in the SBISS
1 Corinthians 6 in the SBITS
1 Corinthians 6 in the SBITS2
1 Corinthians 6 in the SBITS3
1 Corinthians 6 in the SBITS4
1 Corinthians 6 in the SBIUS
1 Corinthians 6 in the SBIVS
1 Corinthians 6 in the SBT
1 Corinthians 6 in the SBT1E
1 Corinthians 6 in the SCHL
1 Corinthians 6 in the SNT
1 Corinthians 6 in the SUSU
1 Corinthians 6 in the SUSU2
1 Corinthians 6 in the SYNO
1 Corinthians 6 in the TBIAOTANT
1 Corinthians 6 in the TBT1E
1 Corinthians 6 in the TBT1E2
1 Corinthians 6 in the TFTIP
1 Corinthians 6 in the TFTU
1 Corinthians 6 in the TGNTATF3T
1 Corinthians 6 in the THAI
1 Corinthians 6 in the TNFD
1 Corinthians 6 in the TNT
1 Corinthians 6 in the TNTIK
1 Corinthians 6 in the TNTIL
1 Corinthians 6 in the TNTIN
1 Corinthians 6 in the TNTIP
1 Corinthians 6 in the TNTIZ
1 Corinthians 6 in the TOMA
1 Corinthians 6 in the TTENT
1 Corinthians 6 in the UBG
1 Corinthians 6 in the UGV
1 Corinthians 6 in the UGV2
1 Corinthians 6 in the UGV3
1 Corinthians 6 in the VBL
1 Corinthians 6 in the VDCC
1 Corinthians 6 in the YALU
1 Corinthians 6 in the YAPE
1 Corinthians 6 in the YBVTP
1 Corinthians 6 in the ZBP