1 John 5 (BOGWICC)
1 Aliyense amene amakhulupirira kuti Yesu ndi Khristu, iyeyo ndi mwana wa Mulungu, ndipo aliyense amene amakonda Atate amakondanso Mwana wake. 2 Chodziwira kuti timakonda ana a Mulungu nʼchakuti timakonda Mulungu ndi kusunga malamulo ake. 3 Pakuti kukonda Mulungu ndiye kusunga malamulo ake. Ndipo malamulo ake siwolemetsa, 4 chifukwa aliyense amene ndi mwana wa Mulungu amagonjetsa dziko lapansi. Chikhulupiriro chathu ndicho timagonjetsera dziko lapansi. 5 Ndani amagonjetsa dziko lapansi? Yekhayo amene amakhulupirira kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu. 6 Uyu ndiye anabwera mwa madzi ndi magazi, ndiye Yesu Khristu. Sanabwere mwa madzi okha, koma mwa madzi ndi magazi. Ndipo ndi Mzimu Woyera amene akuchitira umboni, chifukwa Mzimu Woyera ndi choonadi. 7 Pakuti pali atatu amene amachitira umboni. 8 Mzimu Woyera, madzi ndi magazi; ndipo atatu amavomerezana. 9 Timalandira umboni wa anthu, koma umboni wa Mulungu ndi wopambana. Umboniwo ndi umene anachitira Mwana wake. 10 Aliyense amene amakhulupirira Mwana wa Mulungu ali nawo umboniwu mu mtima mwake, koma aliyense amene sanakhulupirire Mulungu amayesa kuti Mulunguyo ndi wonama, chifukwa sanakhulupirire umboni umene Mulungu anachitira wa Mwana wake. 11 Ndipo umboniwo ndi uwu: Mulungu anatipatsa moyo wosatha, ndipo moyowu uli mwa Mwana wake. 12 Iye amene ali ndi Mwana ali ndi moyo, amene alibe Mwana wa Mulungu alibe moyo. 13 Ine ndikulemba zimenezi kwa inu, amene mwakhulupirira dzina la Mwana wa Mulungu kuti mudziwe kuti muli ndi moyo wosatha. 14 Ife timalimba mtima tikamafika pamaso pa Mulungu, popeza kuti ngati tipempha kanthu kalikonse monga mwa chifuniro chake, amatimvera. 15 Ndipo ngati tikudziwa kuti amatimvera, chilichonse chimene timapempha, tikudziwanso kuti tili nacho chimene tamupempha Iye. 16 Ngati wina aona mʼbale wake akuchita tchimo losadzetsa imfa, apemphere ndipo Mulungu adzamupatsa moyo mʼbale wakeyo. Ndikunena za ochita tchimo losadzetsa imfa. Pali tchimo lodzetsa imfa. Ine sindikunena kuti apemphere ayi. 17 Chilichonse chosalungama ndi tchimo ndipo pali tchimo losadzetsa imfa. 18 Tikudziwa kuti aliyense amene ndi mwana wa Mulungu sachimwirachimwirabe. Yesu, Mwana wa Mulungu, amamusunga ndipo woyipa uja sangamukhudze. 19 Tikudziwa kuti ndife ana a Mulungu ndi kuti dziko lonse lapansi lili pansi pa ulamuliro wa woyipayo. 20 Tikudziwa kuti Mwana wa Mulungu anafika ndipo anatipatsa nzeru, kuti timudziwe Iye amene ali woona. Ndipo ife tili mwa Iye amene ndi woona, Mwana wake, Yesu Khristu. Iye ndi Mulungu woona ndi moyo wosatha. 21 Ana okondedwa, dzisungeni bwino, osapembedza mafano.
In Other Versions
1 John 5 in the ANGEFD
1 John 5 in the ANTPNG2D
1 John 5 in the AS21
1 John 5 in the BAGH
1 John 5 in the BBPNG
1 John 5 in the BBT1E
1 John 5 in the BDS
1 John 5 in the BEV
1 John 5 in the BHAD
1 John 5 in the BIB
1 John 5 in the BLPT
1 John 5 in the BNT
1 John 5 in the BNTABOOT
1 John 5 in the BNTLV
1 John 5 in the BOATCB
1 John 5 in the BOATCB2
1 John 5 in the BOBCV
1 John 5 in the BOCNT
1 John 5 in the BOECS
1 John 5 in the BOHCB
1 John 5 in the BOHCV
1 John 5 in the BOHLNT
1 John 5 in the BOHNTLTAL
1 John 5 in the BOICB
1 John 5 in the BOILNTAP
1 John 5 in the BOITCV
1 John 5 in the BOKCV
1 John 5 in the BOKCV2
1 John 5 in the BOKHWOG
1 John 5 in the BOKSSV
1 John 5 in the BOLCB
1 John 5 in the BOLCB2
1 John 5 in the BOMCV
1 John 5 in the BONAV
1 John 5 in the BONCB
1 John 5 in the BONLT
1 John 5 in the BONUT2
1 John 5 in the BOPLNT
1 John 5 in the BOSCB
1 John 5 in the BOSNC
1 John 5 in the BOTLNT
1 John 5 in the BOVCB
1 John 5 in the BOYCB
1 John 5 in the BPBB
1 John 5 in the BPH
1 John 5 in the BSB
1 John 5 in the CCB
1 John 5 in the CUV
1 John 5 in the CUVS
1 John 5 in the DBT
1 John 5 in the DGDNT
1 John 5 in the DHNT
1 John 5 in the DNT
1 John 5 in the ELBE
1 John 5 in the EMTV
1 John 5 in the ESV
1 John 5 in the FBV
1 John 5 in the FEB
1 John 5 in the GGMNT
1 John 5 in the GNT
1 John 5 in the HARY
1 John 5 in the HNT
1 John 5 in the IRVA
1 John 5 in the IRVB
1 John 5 in the IRVG
1 John 5 in the IRVH
1 John 5 in the IRVK
1 John 5 in the IRVM
1 John 5 in the IRVM2
1 John 5 in the IRVO
1 John 5 in the IRVP
1 John 5 in the IRVT
1 John 5 in the IRVT2
1 John 5 in the IRVU
1 John 5 in the ISVN
1 John 5 in the JSNT
1 John 5 in the KAPI
1 John 5 in the KBT1ETNIK
1 John 5 in the KBV
1 John 5 in the KJV
1 John 5 in the KNFD
1 John 5 in the LBA
1 John 5 in the LBLA
1 John 5 in the LNT
1 John 5 in the LSV
1 John 5 in the MAAL
1 John 5 in the MBV
1 John 5 in the MBV2
1 John 5 in the MHNT
1 John 5 in the MKNFD
1 John 5 in the MNG
1 John 5 in the MNT
1 John 5 in the MNT2
1 John 5 in the MRS1T
1 John 5 in the NAA
1 John 5 in the NASB
1 John 5 in the NBLA
1 John 5 in the NBS
1 John 5 in the NBVTP
1 John 5 in the NET2
1 John 5 in the NIV11
1 John 5 in the NNT
1 John 5 in the NNT2
1 John 5 in the NNT3
1 John 5 in the PDDPT
1 John 5 in the PFNT
1 John 5 in the RMNT
1 John 5 in the SBIAS
1 John 5 in the SBIBS
1 John 5 in the SBIBS2
1 John 5 in the SBICS
1 John 5 in the SBIDS
1 John 5 in the SBIGS
1 John 5 in the SBIHS
1 John 5 in the SBIIS
1 John 5 in the SBIIS2
1 John 5 in the SBIIS3
1 John 5 in the SBIKS
1 John 5 in the SBIKS2
1 John 5 in the SBIMS
1 John 5 in the SBIOS
1 John 5 in the SBIPS
1 John 5 in the SBISS
1 John 5 in the SBITS
1 John 5 in the SBITS2
1 John 5 in the SBITS3
1 John 5 in the SBITS4
1 John 5 in the SBIUS
1 John 5 in the SBIVS
1 John 5 in the SBT
1 John 5 in the SBT1E
1 John 5 in the SCHL
1 John 5 in the SNT
1 John 5 in the SUSU
1 John 5 in the SUSU2
1 John 5 in the SYNO
1 John 5 in the TBIAOTANT
1 John 5 in the TBT1E
1 John 5 in the TBT1E2
1 John 5 in the TFTIP
1 John 5 in the TFTU
1 John 5 in the TGNTATF3T
1 John 5 in the THAI
1 John 5 in the TNFD
1 John 5 in the TNT
1 John 5 in the TNTIK
1 John 5 in the TNTIL
1 John 5 in the TNTIN
1 John 5 in the TNTIP
1 John 5 in the TNTIZ
1 John 5 in the TOMA
1 John 5 in the TTENT
1 John 5 in the UBG
1 John 5 in the UGV
1 John 5 in the UGV2
1 John 5 in the UGV3
1 John 5 in the VBL
1 John 5 in the VDCC
1 John 5 in the YALU
1 John 5 in the YAPE
1 John 5 in the YBVTP
1 John 5 in the ZBP