1 Samuel 3 (BOGWICC)

1 Samueli ankatumikira Yehova moyangʼaniridwa ndi Eli. Masiku amenewo mawu a Yehova sankamveka pafupipafupi. Kuona zinthu mʼmasomphenya sikunkachitikanso kawirikawiri. 2 Tsiku lina Eli, amene maso anali ofowoka ndi kuti sankatha kuona bwino, anagona pa malo ake. 3 Nthawiyi nʼkuti nyale ya Mulungu isanazimitsidwe. Samueli anali gone mu Nyumba ya Yehova, kumene kunali Bokosi la Chipangano cha Mulungu. 4 Yehova anayitana Samueli.Iye anayankha kuti, “Wawa.” 5 Ndipo iyeyo anathamangira kwa Eli ndipo anati, “Ndabwera ndamva kuyitana.”Koma Eli anati, “Ine sindinakuyitane, bwerera kagone.” Ndipo iye anapita kukagona. 6 Yehova anayitananso, “Samueli!” Ndipo Samueli anadzuka ndi kupita kwa Eli nati, “Ndabwera popeza ndamva mukundiyitana.”Eli nati, “Mwana wanga, ine sindinakuyitane, bwerera kagone.” 7 Nthawiyi nʼkuti Samueli asanadziwe Yehova ndipo Mawu a Yehova nʼkuti asanawululidwe kwa iye. 8 Yehova anayitananso Samueli kachitatu ndipo Samueli anadzuka ndikupita kwa Eli ndipo anati, “Ndabwera popeza mwandiyitana ndithu.”Apo Eli anazindikira kuti Yehova ndiye ankayitana mnyamatayo. 9 Tsono Eli anamuwuza Samueli kuti, “Pita ukagone ndipo akakuyitananso ukanene kuti, ‘Yankhulani Yehova, pakuti mtumiki wanu ndikumvetsera.’ ” Choncho Samueli anapita ndi kukagona pamalo pake. 10 Yehova anabwera ndi kuyima pomwepo, ndi kuyitana monga nthawi zina zija, “Samueli! Samueli!”Ndipo Samueli anayankha, “Yankhulani, pakuti mtumiki wanu akumvetsera.” 11 Ndipo Yehova anati kwa Samueli, “Taona, patsala pangʼono kuti ndichite chinthu china mu Israeli chimene chidzadabwitsa aliyense amene adzamve. 12 Tsiku limenelo ndidzachitadi zonse zimene ndinayankhula zokhudza banja la Eli kuyambira poyamba mpaka pomaliza. 13 Pakuti ndinamudziwitsa kuti Ine ndikhoza kulanga banja lake kwamuyaya chifukwa cha zoyipa zimene ana ake ankadziyipitsa nazo. Iye ankadziwa zimenezi koma osawaletsa. 14 Nʼchifukwa chake ndinalumbira kuti, ‘Zoyipa zimene banja la Eli linandichita sizidzafafanizidwa mpaka muyaya ngakhale adzapereke nsembe kapena zopereka zina.’ ” 15 Samueli anagona mpaka mmawa. Atadzuka anatsekula zitseko za Nyumba ya Yehova. Iye anachita mantha kumuwuza Eli za masomphenya ake. 16 Koma Eli anamuyitana nati, “Samueli mwana wanga.”Samueli anayankha kuti, “Wawa.” 17 Tsono Eli anafunsa kuti, “Yehova wakuwuza chiyani? Usandibisire. Mulungu akulange ndithu ngati undibisira chilichonse cha zimene wakuwuza.” 18 Choncho Samueli anamuwuza zonse, sanamubisire kalikonse. Ndipo Eli anati, “Iye ndi Yehova, mulekeni achite chimene chamukomera.” 19 Yehova anali ndi Samueli pamene amakula, ndipo zonse zimene ankayankhula zinkachitikadi. 20 Ndipo Aisraeli onse kuyambira ku dera la Dani mpaka ku Beeriseba anazindikira kuti Yehova analozadi chala pa Samueli kuti akhale mneneri wake. 21 Yehova anapitiriza kuoneka ku Silo, ndipo kumeneko anadziwulula yekha kwa Samueli mwa mawu ake.

In Other Versions

1 Samuel 3 in the ANGEFD

1 Samuel 3 in the ANTPNG2D

1 Samuel 3 in the AS21

1 Samuel 3 in the BAGH

1 Samuel 3 in the BBPNG

1 Samuel 3 in the BBT1E

1 Samuel 3 in the BDS

1 Samuel 3 in the BEV

1 Samuel 3 in the BHAD

1 Samuel 3 in the BIB

1 Samuel 3 in the BLPT

1 Samuel 3 in the BNT

1 Samuel 3 in the BNTABOOT

1 Samuel 3 in the BNTLV

1 Samuel 3 in the BOATCB

1 Samuel 3 in the BOATCB2

1 Samuel 3 in the BOBCV

1 Samuel 3 in the BOCNT

1 Samuel 3 in the BOECS

1 Samuel 3 in the BOHCB

1 Samuel 3 in the BOHCV

1 Samuel 3 in the BOHLNT

1 Samuel 3 in the BOHNTLTAL

1 Samuel 3 in the BOICB

1 Samuel 3 in the BOILNTAP

1 Samuel 3 in the BOITCV

1 Samuel 3 in the BOKCV

1 Samuel 3 in the BOKCV2

1 Samuel 3 in the BOKHWOG

1 Samuel 3 in the BOKSSV

1 Samuel 3 in the BOLCB

1 Samuel 3 in the BOLCB2

1 Samuel 3 in the BOMCV

1 Samuel 3 in the BONAV

1 Samuel 3 in the BONCB

1 Samuel 3 in the BONLT

1 Samuel 3 in the BONUT2

1 Samuel 3 in the BOPLNT

1 Samuel 3 in the BOSCB

1 Samuel 3 in the BOSNC

1 Samuel 3 in the BOTLNT

1 Samuel 3 in the BOVCB

1 Samuel 3 in the BOYCB

1 Samuel 3 in the BPBB

1 Samuel 3 in the BPH

1 Samuel 3 in the BSB

1 Samuel 3 in the CCB

1 Samuel 3 in the CUV

1 Samuel 3 in the CUVS

1 Samuel 3 in the DBT

1 Samuel 3 in the DGDNT

1 Samuel 3 in the DHNT

1 Samuel 3 in the DNT

1 Samuel 3 in the ELBE

1 Samuel 3 in the EMTV

1 Samuel 3 in the ESV

1 Samuel 3 in the FBV

1 Samuel 3 in the FEB

1 Samuel 3 in the GGMNT

1 Samuel 3 in the GNT

1 Samuel 3 in the HARY

1 Samuel 3 in the HNT

1 Samuel 3 in the IRVA

1 Samuel 3 in the IRVB

1 Samuel 3 in the IRVG

1 Samuel 3 in the IRVH

1 Samuel 3 in the IRVK

1 Samuel 3 in the IRVM

1 Samuel 3 in the IRVM2

1 Samuel 3 in the IRVO

1 Samuel 3 in the IRVP

1 Samuel 3 in the IRVT

1 Samuel 3 in the IRVT2

1 Samuel 3 in the IRVU

1 Samuel 3 in the ISVN

1 Samuel 3 in the JSNT

1 Samuel 3 in the KAPI

1 Samuel 3 in the KBT1ETNIK

1 Samuel 3 in the KBV

1 Samuel 3 in the KJV

1 Samuel 3 in the KNFD

1 Samuel 3 in the LBA

1 Samuel 3 in the LBLA

1 Samuel 3 in the LNT

1 Samuel 3 in the LSV

1 Samuel 3 in the MAAL

1 Samuel 3 in the MBV

1 Samuel 3 in the MBV2

1 Samuel 3 in the MHNT

1 Samuel 3 in the MKNFD

1 Samuel 3 in the MNG

1 Samuel 3 in the MNT

1 Samuel 3 in the MNT2

1 Samuel 3 in the MRS1T

1 Samuel 3 in the NAA

1 Samuel 3 in the NASB

1 Samuel 3 in the NBLA

1 Samuel 3 in the NBS

1 Samuel 3 in the NBVTP

1 Samuel 3 in the NET2

1 Samuel 3 in the NIV11

1 Samuel 3 in the NNT

1 Samuel 3 in the NNT2

1 Samuel 3 in the NNT3

1 Samuel 3 in the PDDPT

1 Samuel 3 in the PFNT

1 Samuel 3 in the RMNT

1 Samuel 3 in the SBIAS

1 Samuel 3 in the SBIBS

1 Samuel 3 in the SBIBS2

1 Samuel 3 in the SBICS

1 Samuel 3 in the SBIDS

1 Samuel 3 in the SBIGS

1 Samuel 3 in the SBIHS

1 Samuel 3 in the SBIIS

1 Samuel 3 in the SBIIS2

1 Samuel 3 in the SBIIS3

1 Samuel 3 in the SBIKS

1 Samuel 3 in the SBIKS2

1 Samuel 3 in the SBIMS

1 Samuel 3 in the SBIOS

1 Samuel 3 in the SBIPS

1 Samuel 3 in the SBISS

1 Samuel 3 in the SBITS

1 Samuel 3 in the SBITS2

1 Samuel 3 in the SBITS3

1 Samuel 3 in the SBITS4

1 Samuel 3 in the SBIUS

1 Samuel 3 in the SBIVS

1 Samuel 3 in the SBT

1 Samuel 3 in the SBT1E

1 Samuel 3 in the SCHL

1 Samuel 3 in the SNT

1 Samuel 3 in the SUSU

1 Samuel 3 in the SUSU2

1 Samuel 3 in the SYNO

1 Samuel 3 in the TBIAOTANT

1 Samuel 3 in the TBT1E

1 Samuel 3 in the TBT1E2

1 Samuel 3 in the TFTIP

1 Samuel 3 in the TFTU

1 Samuel 3 in the TGNTATF3T

1 Samuel 3 in the THAI

1 Samuel 3 in the TNFD

1 Samuel 3 in the TNT

1 Samuel 3 in the TNTIK

1 Samuel 3 in the TNTIL

1 Samuel 3 in the TNTIN

1 Samuel 3 in the TNTIP

1 Samuel 3 in the TNTIZ

1 Samuel 3 in the TOMA

1 Samuel 3 in the TTENT

1 Samuel 3 in the UBG

1 Samuel 3 in the UGV

1 Samuel 3 in the UGV2

1 Samuel 3 in the UGV3

1 Samuel 3 in the VBL

1 Samuel 3 in the VDCC

1 Samuel 3 in the YALU

1 Samuel 3 in the YAPE

1 Samuel 3 in the YBVTP

1 Samuel 3 in the ZBP