1 Samuel 7 (BOGWICC)
1 Choncho anthu a ku Kiriati-Yearimu anabwera ndi kudzatenga Bokosi la Yehova. Iwo anapita nalo ku nyumba ya Abinadabu ya ku phiri ndipo anapatula Eliezara mwana wake kuti aziyangʼanira Bokosi la Yehovalo. 2 Zaka makumi awiri zinapita kuyambira pamene Bokosi la Yehova linakhala ku Kiriati-Yearimu, ndipo anthu a Israeli onse analira kupempha Yehova kuti awathandize. 3 Ndipo Samueli anati kwa nyumba yonse ya Israeli, “Ngati mukubwerera kwa Yehova ndi mtima wanu wonse, muchotse milungu yachilendo ndi Asiteroti pakati panu ndipo mitima yanu ikhazikike pa Yehova ndi kutumikira Iye yekha. Mukatero Iye adzakupulumutsani mʼmanja mwa Afilisti.” 4 Choncho Aisraeli anachotsa milungu yawo ya Baala ndi Asitoreti ndi kutumikira Yehova yekha. 5 Kenaka Samueli anati, “Sonkhanitsani Aisraeli onse ku Mizipa ndipo ine ndidzakupemphererani kwa Yehova.” 6 Choncho anasonkhana ku Mizipa, ndipo anatunga madzi ndi kuwathira pansi pamaso pa Yehova. Pa tsiku limenelo anasala kudya namanena kuti, “Ife tachimwira Yehova.” Ndipo Samueli anali mtsogoleri wa Israeli ku Mizipa. 7 Afilisti anamva kuti Aisraeli asonkhana ku Mizipa, choncho akalonga awo anabwera kudzawathira nkhondo. Ndipo Aisraeli atamva anachita mantha chifukwa cha Afilisti. 8 Choncho anati kwa Samueli, “Musasiye kutipempherera kwa Yehova Mulungu wathu, kuti atipulumutse mʼdzanja la Afilistiwa.” 9 Ndipo Samueli anatenga mwana wankhosa wamkazi woyamwa ndi kumupereka monga nsembe yopsereza kwa Yehova. Iye anapemphera kwa Yehova mʼmalo mwa Aisraeli, ndipo Yehova anamuyankha. 10 Samueli akupereka nsembe yopsereza, Afilisti anayandikira kuti ayambe kuwathira nkhondo Aisraeli. Koma tsiku limenelo Yehova anawaopseza Afilisti aja ndi mawu aakulu ngati bingu. Choncho anasokonezeka motero kuti Aisraeli anawagonjetsa. 11 Aisraeli anatuluka ku Mizipa kuthamangitsa Afilisti aja nʼkumawapha mʼnjira yonse mpaka kumunsi kwa Beti-Kari. 12 Kenaka Samueli anatenga mwala nawuyika pakati pa Mizipa ndi Seni. Iye anawutcha Ebenezeri, popeza anati, “Yehova watithandiza mpaka pano.” 13 Kotero Afilisti anagonjetsedwa ndipo sanadzalowenso mʼdziko la Israeli.Yehova analimbana ndi Afilisti masiku onse a Samueli. 14 Mizinda yonse imene Afilisti analanda kuchokera ku Ekroni mpaka ku Gati inabwezedwa kwa Aisraeli. Choncho Aisraeli anapulumutsa dziko lawo. Ndipo panalinso mtendere pakati pa Aisraeli ndi Aamori. 15 Samueli anatsogolera Aisraeli moyo wake wonse. 16 Chaka ndi chaka Samueli ankakonza ulendo wozungulira kuchokera ku Beteli mpaka ku Giligala ndi Mizipa, kuweruza milandu ya Aisraeli mʼmadera onsewa. 17 Koma pambuyo pake ankabwerera ku Rama, kumene kunali nyumba yake. Ankaweruza Aisraeli kumeneko. Ndipo iye anamanga guwa lansembe la Yehova kumeneko.
In Other Versions
1 Samuel 7 in the ANGEFD
1 Samuel 7 in the ANTPNG2D
1 Samuel 7 in the AS21
1 Samuel 7 in the BAGH
1 Samuel 7 in the BBPNG
1 Samuel 7 in the BBT1E
1 Samuel 7 in the BDS
1 Samuel 7 in the BEV
1 Samuel 7 in the BHAD
1 Samuel 7 in the BIB
1 Samuel 7 in the BLPT
1 Samuel 7 in the BNT
1 Samuel 7 in the BNTABOOT
1 Samuel 7 in the BNTLV
1 Samuel 7 in the BOATCB
1 Samuel 7 in the BOATCB2
1 Samuel 7 in the BOBCV
1 Samuel 7 in the BOCNT
1 Samuel 7 in the BOECS
1 Samuel 7 in the BOHCB
1 Samuel 7 in the BOHCV
1 Samuel 7 in the BOHLNT
1 Samuel 7 in the BOHNTLTAL
1 Samuel 7 in the BOICB
1 Samuel 7 in the BOILNTAP
1 Samuel 7 in the BOITCV
1 Samuel 7 in the BOKCV
1 Samuel 7 in the BOKCV2
1 Samuel 7 in the BOKHWOG
1 Samuel 7 in the BOKSSV
1 Samuel 7 in the BOLCB
1 Samuel 7 in the BOLCB2
1 Samuel 7 in the BOMCV
1 Samuel 7 in the BONAV
1 Samuel 7 in the BONCB
1 Samuel 7 in the BONLT
1 Samuel 7 in the BONUT2
1 Samuel 7 in the BOPLNT
1 Samuel 7 in the BOSCB
1 Samuel 7 in the BOSNC
1 Samuel 7 in the BOTLNT
1 Samuel 7 in the BOVCB
1 Samuel 7 in the BOYCB
1 Samuel 7 in the BPBB
1 Samuel 7 in the BPH
1 Samuel 7 in the BSB
1 Samuel 7 in the CCB
1 Samuel 7 in the CUV
1 Samuel 7 in the CUVS
1 Samuel 7 in the DBT
1 Samuel 7 in the DGDNT
1 Samuel 7 in the DHNT
1 Samuel 7 in the DNT
1 Samuel 7 in the ELBE
1 Samuel 7 in the EMTV
1 Samuel 7 in the ESV
1 Samuel 7 in the FBV
1 Samuel 7 in the FEB
1 Samuel 7 in the GGMNT
1 Samuel 7 in the GNT
1 Samuel 7 in the HARY
1 Samuel 7 in the HNT
1 Samuel 7 in the IRVA
1 Samuel 7 in the IRVB
1 Samuel 7 in the IRVG
1 Samuel 7 in the IRVH
1 Samuel 7 in the IRVK
1 Samuel 7 in the IRVM
1 Samuel 7 in the IRVM2
1 Samuel 7 in the IRVO
1 Samuel 7 in the IRVP
1 Samuel 7 in the IRVT
1 Samuel 7 in the IRVT2
1 Samuel 7 in the IRVU
1 Samuel 7 in the ISVN
1 Samuel 7 in the JSNT
1 Samuel 7 in the KAPI
1 Samuel 7 in the KBT1ETNIK
1 Samuel 7 in the KBV
1 Samuel 7 in the KJV
1 Samuel 7 in the KNFD
1 Samuel 7 in the LBA
1 Samuel 7 in the LBLA
1 Samuel 7 in the LNT
1 Samuel 7 in the LSV
1 Samuel 7 in the MAAL
1 Samuel 7 in the MBV
1 Samuel 7 in the MBV2
1 Samuel 7 in the MHNT
1 Samuel 7 in the MKNFD
1 Samuel 7 in the MNG
1 Samuel 7 in the MNT
1 Samuel 7 in the MNT2
1 Samuel 7 in the MRS1T
1 Samuel 7 in the NAA
1 Samuel 7 in the NASB
1 Samuel 7 in the NBLA
1 Samuel 7 in the NBS
1 Samuel 7 in the NBVTP
1 Samuel 7 in the NET2
1 Samuel 7 in the NIV11
1 Samuel 7 in the NNT
1 Samuel 7 in the NNT2
1 Samuel 7 in the NNT3
1 Samuel 7 in the PDDPT
1 Samuel 7 in the PFNT
1 Samuel 7 in the RMNT
1 Samuel 7 in the SBIAS
1 Samuel 7 in the SBIBS
1 Samuel 7 in the SBIBS2
1 Samuel 7 in the SBICS
1 Samuel 7 in the SBIDS
1 Samuel 7 in the SBIGS
1 Samuel 7 in the SBIHS
1 Samuel 7 in the SBIIS
1 Samuel 7 in the SBIIS2
1 Samuel 7 in the SBIIS3
1 Samuel 7 in the SBIKS
1 Samuel 7 in the SBIKS2
1 Samuel 7 in the SBIMS
1 Samuel 7 in the SBIOS
1 Samuel 7 in the SBIPS
1 Samuel 7 in the SBISS
1 Samuel 7 in the SBITS
1 Samuel 7 in the SBITS2
1 Samuel 7 in the SBITS3
1 Samuel 7 in the SBITS4
1 Samuel 7 in the SBIUS
1 Samuel 7 in the SBIVS
1 Samuel 7 in the SBT
1 Samuel 7 in the SBT1E
1 Samuel 7 in the SCHL
1 Samuel 7 in the SNT
1 Samuel 7 in the SUSU
1 Samuel 7 in the SUSU2
1 Samuel 7 in the SYNO
1 Samuel 7 in the TBIAOTANT
1 Samuel 7 in the TBT1E
1 Samuel 7 in the TBT1E2
1 Samuel 7 in the TFTIP
1 Samuel 7 in the TFTU
1 Samuel 7 in the TGNTATF3T
1 Samuel 7 in the THAI
1 Samuel 7 in the TNFD
1 Samuel 7 in the TNT
1 Samuel 7 in the TNTIK
1 Samuel 7 in the TNTIL
1 Samuel 7 in the TNTIN
1 Samuel 7 in the TNTIP
1 Samuel 7 in the TNTIZ
1 Samuel 7 in the TOMA
1 Samuel 7 in the TTENT
1 Samuel 7 in the UBG
1 Samuel 7 in the UGV
1 Samuel 7 in the UGV2
1 Samuel 7 in the UGV3
1 Samuel 7 in the VBL
1 Samuel 7 in the VDCC
1 Samuel 7 in the YALU
1 Samuel 7 in the YAPE
1 Samuel 7 in the YBVTP
1 Samuel 7 in the ZBP