2 Chronicles 21 (BOGWICC)
1 Yehosafati anamwalira nayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu mzinda wa Davide. Ndipo Yehoramu mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake. 2 Abale ake a Yehoramu, ana aamuna a Yehosafati, anali Azariya, Yehieli, Zekariya, Azariyahu, Mikayeli ndi Sefatiya. Onsewa anali ana a Yehosafati mfumu ya Israeli. 3 Abambo awo anawapatsa mphatso zambiri za siliva, golide ndi zinthu zina zamtengowapatali komanso mizinda yotetezedwa ya Yuda. Koma iye anapereka ufumu kwa Yehoramu chifukwa anali mwana wake woyamba kubadwa. 4 Yehoramu atakhazikika pa ufumu wa abambo ake, iye anapha abale ake ndi lupanga pamodzi ndi atsogoleri ena a Israeli. 5 Yehoramu anali wa zaka 32 pamene anakhala mfumu, ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka zisanu ndi zitatu. 6 Iye anayenda mʼnjira za mafumu a Israeli, monga mmene linachitira banja la Ahabu, pakuti anakwatira mwana wa Ahabu. Ndipo anachita zoyipa pamaso pa Yehova. 7 Komabe, chifukwa cha pangano limene Yehova anachita ndi Davide, Yehova sanafune kuwononga banja la Davide. Iye analonjeza kusungira nyale Davide ndi zidzukulu zake mpaka muyaya. 8 Pa nthawi ya Yehoramu, Edomu anawukira Yuda ndipo anadzisankhira mfumu. 9 Choncho Yehoramu anapita kumeneko pamodzi ndi atsogoleri ake ndi magaleta ake onse. Aedomu anamuzungulira pamodzi ndi atsogoleri ake koma iye ananyamuka ndi kuthawa usiku. 10 Mpaka lero lino Edomu ndi wowukira ulamuliro wa Yuda.Pa nthawi yomweyi, mzinda wa Libina unawukiranso chifukwa Yehoramu anasiya Yehova, Mulungu wa makolo ake. 11 Iye anamanganso malo opembedzerapo mafano mʼmapiri a Yuda ndipo anachititsa anthu a mu Yerusalemu kukhala osakhulupirika. Choncho anasocheretsa anthu a ku Yuda. 12 Yehoramu analandira kalata yochokera kwa mneneri Eliya yonena kuti,“Yehova Mulungu wa Davide abambo ako akuti, ‘Iwe sunayende mʼnjira ya Yehosafati abambo ako kapena Asa mfumu ya Yuda. 13 Koma wayenda mʼnjira za mafumu a Israeli ndipo watsogolera anthu a ku Yuda ndi Yerusalemu kukhala osakhulupirika, monga linachitira banja la Ahabu. Waphanso abale ako, abale a banja la abambo ako, anthu amene anali abwino kuposa iweyo. 14 Kotero tsono Yehova ali pafupi kukantha anthu ako, ana ako, akazi ako ndi zinthu zako zonse, ndi chilango chachikulu. 15 Ndipo iwe udzadwala nthenda yoopsa yamʼmimba, mpaka nthendayo idzachititsa matumbo ako kutuluka.’ ” 16 Yehova anamuutsira Yehoramuyo mkwiyo wa Afilisti ndi Aarabu amene amakhala pafupi ndi Akusi. 17 Iwo anathira nkhondo Yuda. Analowanso ndi kutenga katundu yense amene anamupeza mʼnyumba ya mfumu pamodzi ndi ana ake ndi akazi ake. Palibe mwana amene anatsala kupatula mwana wake wamngʼono kwambiri, Ahaziya. 18 Izi zonse zitachitika, Yehova anakantha Yehoramu ndi nthenda yamʼmimba imene inali yosachiritsika. 19 Patapita nthawi, kumapeto kwa chaka chachiwiri, matumbo ake anatuluka chifukwa cha nthendayo, ndipo anafa imfa yopweteka kwambiri. Anthu ake sanasonkhe moto kumuchitira ulemu, monga anachitira ndi makolo ake. 20 Yehoramu anali wa zaka 32 pamene anakhala mfumu. Iyeyo analamulira mu Yerusalemu zaka zisanu ndi zitatu. Ndipo anamwalira popanda odandawula, nayikidwa mʼmanda mu mzinda wa Davide, koma osati mʼmanda a mafumu.
In Other Versions
2 Chronicles 21 in the ANGEFD
2 Chronicles 21 in the ANTPNG2D
2 Chronicles 21 in the AS21
2 Chronicles 21 in the BAGH
2 Chronicles 21 in the BBPNG
2 Chronicles 21 in the BBT1E
2 Chronicles 21 in the BDS
2 Chronicles 21 in the BEV
2 Chronicles 21 in the BHAD
2 Chronicles 21 in the BIB
2 Chronicles 21 in the BLPT
2 Chronicles 21 in the BNT
2 Chronicles 21 in the BNTABOOT
2 Chronicles 21 in the BNTLV
2 Chronicles 21 in the BOATCB
2 Chronicles 21 in the BOATCB2
2 Chronicles 21 in the BOBCV
2 Chronicles 21 in the BOCNT
2 Chronicles 21 in the BOECS
2 Chronicles 21 in the BOHCB
2 Chronicles 21 in the BOHCV
2 Chronicles 21 in the BOHLNT
2 Chronicles 21 in the BOHNTLTAL
2 Chronicles 21 in the BOICB
2 Chronicles 21 in the BOILNTAP
2 Chronicles 21 in the BOITCV
2 Chronicles 21 in the BOKCV
2 Chronicles 21 in the BOKCV2
2 Chronicles 21 in the BOKHWOG
2 Chronicles 21 in the BOKSSV
2 Chronicles 21 in the BOLCB
2 Chronicles 21 in the BOLCB2
2 Chronicles 21 in the BOMCV
2 Chronicles 21 in the BONAV
2 Chronicles 21 in the BONCB
2 Chronicles 21 in the BONLT
2 Chronicles 21 in the BONUT2
2 Chronicles 21 in the BOPLNT
2 Chronicles 21 in the BOSCB
2 Chronicles 21 in the BOSNC
2 Chronicles 21 in the BOTLNT
2 Chronicles 21 in the BOVCB
2 Chronicles 21 in the BOYCB
2 Chronicles 21 in the BPBB
2 Chronicles 21 in the BPH
2 Chronicles 21 in the BSB
2 Chronicles 21 in the CCB
2 Chronicles 21 in the CUV
2 Chronicles 21 in the CUVS
2 Chronicles 21 in the DBT
2 Chronicles 21 in the DGDNT
2 Chronicles 21 in the DHNT
2 Chronicles 21 in the DNT
2 Chronicles 21 in the ELBE
2 Chronicles 21 in the EMTV
2 Chronicles 21 in the ESV
2 Chronicles 21 in the FBV
2 Chronicles 21 in the FEB
2 Chronicles 21 in the GGMNT
2 Chronicles 21 in the GNT
2 Chronicles 21 in the HARY
2 Chronicles 21 in the HNT
2 Chronicles 21 in the IRVA
2 Chronicles 21 in the IRVB
2 Chronicles 21 in the IRVG
2 Chronicles 21 in the IRVH
2 Chronicles 21 in the IRVK
2 Chronicles 21 in the IRVM
2 Chronicles 21 in the IRVM2
2 Chronicles 21 in the IRVO
2 Chronicles 21 in the IRVP
2 Chronicles 21 in the IRVT
2 Chronicles 21 in the IRVT2
2 Chronicles 21 in the IRVU
2 Chronicles 21 in the ISVN
2 Chronicles 21 in the JSNT
2 Chronicles 21 in the KAPI
2 Chronicles 21 in the KBT1ETNIK
2 Chronicles 21 in the KBV
2 Chronicles 21 in the KJV
2 Chronicles 21 in the KNFD
2 Chronicles 21 in the LBA
2 Chronicles 21 in the LBLA
2 Chronicles 21 in the LNT
2 Chronicles 21 in the LSV
2 Chronicles 21 in the MAAL
2 Chronicles 21 in the MBV
2 Chronicles 21 in the MBV2
2 Chronicles 21 in the MHNT
2 Chronicles 21 in the MKNFD
2 Chronicles 21 in the MNG
2 Chronicles 21 in the MNT
2 Chronicles 21 in the MNT2
2 Chronicles 21 in the MRS1T
2 Chronicles 21 in the NAA
2 Chronicles 21 in the NASB
2 Chronicles 21 in the NBLA
2 Chronicles 21 in the NBS
2 Chronicles 21 in the NBVTP
2 Chronicles 21 in the NET2
2 Chronicles 21 in the NIV11
2 Chronicles 21 in the NNT
2 Chronicles 21 in the NNT2
2 Chronicles 21 in the NNT3
2 Chronicles 21 in the PDDPT
2 Chronicles 21 in the PFNT
2 Chronicles 21 in the RMNT
2 Chronicles 21 in the SBIAS
2 Chronicles 21 in the SBIBS
2 Chronicles 21 in the SBIBS2
2 Chronicles 21 in the SBICS
2 Chronicles 21 in the SBIDS
2 Chronicles 21 in the SBIGS
2 Chronicles 21 in the SBIHS
2 Chronicles 21 in the SBIIS
2 Chronicles 21 in the SBIIS2
2 Chronicles 21 in the SBIIS3
2 Chronicles 21 in the SBIKS
2 Chronicles 21 in the SBIKS2
2 Chronicles 21 in the SBIMS
2 Chronicles 21 in the SBIOS
2 Chronicles 21 in the SBIPS
2 Chronicles 21 in the SBISS
2 Chronicles 21 in the SBITS
2 Chronicles 21 in the SBITS2
2 Chronicles 21 in the SBITS3
2 Chronicles 21 in the SBITS4
2 Chronicles 21 in the SBIUS
2 Chronicles 21 in the SBIVS
2 Chronicles 21 in the SBT
2 Chronicles 21 in the SBT1E
2 Chronicles 21 in the SCHL
2 Chronicles 21 in the SNT
2 Chronicles 21 in the SUSU
2 Chronicles 21 in the SUSU2
2 Chronicles 21 in the SYNO
2 Chronicles 21 in the TBIAOTANT
2 Chronicles 21 in the TBT1E
2 Chronicles 21 in the TBT1E2
2 Chronicles 21 in the TFTIP
2 Chronicles 21 in the TFTU
2 Chronicles 21 in the TGNTATF3T
2 Chronicles 21 in the THAI
2 Chronicles 21 in the TNFD
2 Chronicles 21 in the TNT
2 Chronicles 21 in the TNTIK
2 Chronicles 21 in the TNTIL
2 Chronicles 21 in the TNTIN
2 Chronicles 21 in the TNTIP
2 Chronicles 21 in the TNTIZ
2 Chronicles 21 in the TOMA
2 Chronicles 21 in the TTENT
2 Chronicles 21 in the UBG
2 Chronicles 21 in the UGV
2 Chronicles 21 in the UGV2
2 Chronicles 21 in the UGV3
2 Chronicles 21 in the VBL
2 Chronicles 21 in the VDCC
2 Chronicles 21 in the YALU
2 Chronicles 21 in the YAPE
2 Chronicles 21 in the YBVTP
2 Chronicles 21 in the ZBP