2 Chronicles 3 (BOGWICC)

1 Pamenepo Solomoni anayamba kumanga Nyumba ya Yehova mu Yerusalemu pa Phiri la Moriya, pamene Yehova anaonekera Davide abambo ake. Panali pabwalo lopunthirapo tirigu la Arauna Myebusi, malo amene anapereka Davide. 2 Iye anayamba kumanga pa tsiku lachiwiri la mwezi wachiwiri mʼchaka chachinayi cha ulamuliro wake. 3 Maziko amene Solomoni anayika pomanga Nyumba ya Mulungu ndi awa: Mulitali munali mamita 27, mulifupi munali mamita asanu ndi anayi (potsata miyeso yakale). 4 Chipinda cha polowera mulitali mwake chinali mamita asanu ndi anayi ofanana ndi mulifupi mwake mwa nyumbayo. Msinkhu wake unali mamita 54.Iye anakuta nyumbayo mʼkati mwake ndi golide woyengeka bwino. 5 Chipinda chachikulu, khoma lake anakhomera matabwa a payini ndipo analikutira ndi golide wabwino ndi kulikongoletsa ndi zithunzi za kanjedza ndi maunyolo. 6 Iye anakongoletsa Nyumba ya Mulunguyo ndi miyala yokongola. Ndipo golide amene anagwiritsa ntchito anali golide wa ku Paravaimu. 7 Iye anakutira ndi golide mitanda ya ku denga, maferemu a zitseko, makoma ndi zitseko za Nyumba ya Mulungu, ndipo anajambula Akerubi mʼmakoma mwake. 8 Iye anamanga Malo Opatulika Kwambiri ndipo mulitali mwake munali mofanana ndi mulifupi mwa Nyumba mamita asanu ndi anayi. Anakuta mʼkati mwake ndi golide wosalala wolemera matani makumi awiri. 9 Misomali yagolide imalemera magalamu 570. Anakutanso ndi golide zipinda zapamwamba. 10 Ku Malo Opatulika Kwambiri iye anapangako Akerubi awiri achitsulo ndipo anawakuta ndi golide. 11 Kutalika kwa mapiko onse a Akerubi kunali mamita asanu ndi anayi. Phiko la Kerubi woyamba linali loposerapo mamita awiri ndipo limakhudza khoma la Nyumba ya Mulungu, pamene phiko linalo, lotalikanso koposerapo mamita awiri, limakhudza phiko la Kerubi winayo. 12 Chimodzimodzinso phiko la Kerubi wachiwiri linali loposerapo mamita awiri ndipo limakhudza mbali ina ya khoma la Nyumba ya Mulungu, ndipo linalo limene linalinso loposera mamita awiri, limakhudza phiko la Kerubi woyamba uja. 13 Mapiko a Akerubiwa akawatambasula amatalika mamita asanu ndi anayi. Akerubiwa anayimirira pa mapazi awo, kuyangʼana chipinda chachikulu. 14 Solomoni anapanga nsalu zotchingira zobiriwira, zapepo ndi zofiira ndi nsalu zofewa zosalala, atajambulapo Akerubi. 15 Kutsogolo kwa Nyumba ya Mulungu anamangako zipilala ziwiri, zimene zonse pamodzi zinali zotalika mamita khumi ndi asanu ndi theka; chipilala chilichonse chinali ndi mutu woposera mamita awiri. 16 Iye anapanga maunyolo olumikizanalumikizana ndipo anawayika pamwamba pa zipilalazo. Anapanganso makangadza 100 ndipo anawalumikiza ku maunyolo aja. 17 Solomoni anayimika nsanamirazo kutsogolo kwa Nyumba ya Mulungu, imodzi mbali ya kummwera ndi inayo mbali ya kumpoto. Nsanamira ya kummwera anayitcha Yakini ndipo ya kumpoto anayitcha Bowazi.

In Other Versions

2 Chronicles 3 in the ANGEFD

2 Chronicles 3 in the ANTPNG2D

2 Chronicles 3 in the AS21

2 Chronicles 3 in the BAGH

2 Chronicles 3 in the BBPNG

2 Chronicles 3 in the BBT1E

2 Chronicles 3 in the BDS

2 Chronicles 3 in the BEV

2 Chronicles 3 in the BHAD

2 Chronicles 3 in the BIB

2 Chronicles 3 in the BLPT

2 Chronicles 3 in the BNT

2 Chronicles 3 in the BNTABOOT

2 Chronicles 3 in the BNTLV

2 Chronicles 3 in the BOATCB

2 Chronicles 3 in the BOATCB2

2 Chronicles 3 in the BOBCV

2 Chronicles 3 in the BOCNT

2 Chronicles 3 in the BOECS

2 Chronicles 3 in the BOHCB

2 Chronicles 3 in the BOHCV

2 Chronicles 3 in the BOHLNT

2 Chronicles 3 in the BOHNTLTAL

2 Chronicles 3 in the BOICB

2 Chronicles 3 in the BOILNTAP

2 Chronicles 3 in the BOITCV

2 Chronicles 3 in the BOKCV

2 Chronicles 3 in the BOKCV2

2 Chronicles 3 in the BOKHWOG

2 Chronicles 3 in the BOKSSV

2 Chronicles 3 in the BOLCB

2 Chronicles 3 in the BOLCB2

2 Chronicles 3 in the BOMCV

2 Chronicles 3 in the BONAV

2 Chronicles 3 in the BONCB

2 Chronicles 3 in the BONLT

2 Chronicles 3 in the BONUT2

2 Chronicles 3 in the BOPLNT

2 Chronicles 3 in the BOSCB

2 Chronicles 3 in the BOSNC

2 Chronicles 3 in the BOTLNT

2 Chronicles 3 in the BOVCB

2 Chronicles 3 in the BOYCB

2 Chronicles 3 in the BPBB

2 Chronicles 3 in the BPH

2 Chronicles 3 in the BSB

2 Chronicles 3 in the CCB

2 Chronicles 3 in the CUV

2 Chronicles 3 in the CUVS

2 Chronicles 3 in the DBT

2 Chronicles 3 in the DGDNT

2 Chronicles 3 in the DHNT

2 Chronicles 3 in the DNT

2 Chronicles 3 in the ELBE

2 Chronicles 3 in the EMTV

2 Chronicles 3 in the ESV

2 Chronicles 3 in the FBV

2 Chronicles 3 in the FEB

2 Chronicles 3 in the GGMNT

2 Chronicles 3 in the GNT

2 Chronicles 3 in the HARY

2 Chronicles 3 in the HNT

2 Chronicles 3 in the IRVA

2 Chronicles 3 in the IRVB

2 Chronicles 3 in the IRVG

2 Chronicles 3 in the IRVH

2 Chronicles 3 in the IRVK

2 Chronicles 3 in the IRVM

2 Chronicles 3 in the IRVM2

2 Chronicles 3 in the IRVO

2 Chronicles 3 in the IRVP

2 Chronicles 3 in the IRVT

2 Chronicles 3 in the IRVT2

2 Chronicles 3 in the IRVU

2 Chronicles 3 in the ISVN

2 Chronicles 3 in the JSNT

2 Chronicles 3 in the KAPI

2 Chronicles 3 in the KBT1ETNIK

2 Chronicles 3 in the KBV

2 Chronicles 3 in the KJV

2 Chronicles 3 in the KNFD

2 Chronicles 3 in the LBA

2 Chronicles 3 in the LBLA

2 Chronicles 3 in the LNT

2 Chronicles 3 in the LSV

2 Chronicles 3 in the MAAL

2 Chronicles 3 in the MBV

2 Chronicles 3 in the MBV2

2 Chronicles 3 in the MHNT

2 Chronicles 3 in the MKNFD

2 Chronicles 3 in the MNG

2 Chronicles 3 in the MNT

2 Chronicles 3 in the MNT2

2 Chronicles 3 in the MRS1T

2 Chronicles 3 in the NAA

2 Chronicles 3 in the NASB

2 Chronicles 3 in the NBLA

2 Chronicles 3 in the NBS

2 Chronicles 3 in the NBVTP

2 Chronicles 3 in the NET2

2 Chronicles 3 in the NIV11

2 Chronicles 3 in the NNT

2 Chronicles 3 in the NNT2

2 Chronicles 3 in the NNT3

2 Chronicles 3 in the PDDPT

2 Chronicles 3 in the PFNT

2 Chronicles 3 in the RMNT

2 Chronicles 3 in the SBIAS

2 Chronicles 3 in the SBIBS

2 Chronicles 3 in the SBIBS2

2 Chronicles 3 in the SBICS

2 Chronicles 3 in the SBIDS

2 Chronicles 3 in the SBIGS

2 Chronicles 3 in the SBIHS

2 Chronicles 3 in the SBIIS

2 Chronicles 3 in the SBIIS2

2 Chronicles 3 in the SBIIS3

2 Chronicles 3 in the SBIKS

2 Chronicles 3 in the SBIKS2

2 Chronicles 3 in the SBIMS

2 Chronicles 3 in the SBIOS

2 Chronicles 3 in the SBIPS

2 Chronicles 3 in the SBISS

2 Chronicles 3 in the SBITS

2 Chronicles 3 in the SBITS2

2 Chronicles 3 in the SBITS3

2 Chronicles 3 in the SBITS4

2 Chronicles 3 in the SBIUS

2 Chronicles 3 in the SBIVS

2 Chronicles 3 in the SBT

2 Chronicles 3 in the SBT1E

2 Chronicles 3 in the SCHL

2 Chronicles 3 in the SNT

2 Chronicles 3 in the SUSU

2 Chronicles 3 in the SUSU2

2 Chronicles 3 in the SYNO

2 Chronicles 3 in the TBIAOTANT

2 Chronicles 3 in the TBT1E

2 Chronicles 3 in the TBT1E2

2 Chronicles 3 in the TFTIP

2 Chronicles 3 in the TFTU

2 Chronicles 3 in the TGNTATF3T

2 Chronicles 3 in the THAI

2 Chronicles 3 in the TNFD

2 Chronicles 3 in the TNT

2 Chronicles 3 in the TNTIK

2 Chronicles 3 in the TNTIL

2 Chronicles 3 in the TNTIN

2 Chronicles 3 in the TNTIP

2 Chronicles 3 in the TNTIZ

2 Chronicles 3 in the TOMA

2 Chronicles 3 in the TTENT

2 Chronicles 3 in the UBG

2 Chronicles 3 in the UGV

2 Chronicles 3 in the UGV2

2 Chronicles 3 in the UGV3

2 Chronicles 3 in the VBL

2 Chronicles 3 in the VDCC

2 Chronicles 3 in the YALU

2 Chronicles 3 in the YAPE

2 Chronicles 3 in the YBVTP

2 Chronicles 3 in the ZBP