2 Corinthians 1 (BOGWICC)

1 Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwachifuniro cha Mulungu, pamodzi ndi mʼbale wathu Timoteyo,Kulembera mpingo wa Mulungu mu Korinto, pamodzi ndi oyera mtima onse mu Akaya monse. 2 Mukhale ndi chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu. 3 Alemekezeke Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu, Atate achifundo chonse, Mulungu wachitonthozo chonse. 4 Iye amatitonthoza ife mʼmavuto athu onse, kuti ifenso tithe kutonthoza amene ali pavuto lililonse ndi chitonthozo chimene ife tilandira kwa Mulungu. 5 Pakuti monga momwe tili mʼmasautso pamodzi ndi Khristu, momwemonso Khristu amatitonthoza kwambiri. 6 Ngati ife tikusautsidwa, nʼchifukwa choti inu mutonthozedwe ndi kupulumutsidwa. Ngati ife tikutonthozedwa nʼchifukwa choti inu mutonthozedwe, ndi chitonthozo chimene chimabweretsa mwa inu kupirira kosawiringula pa zosautsa zomwe timasauka nazo ife. 7 Ndipo chiyembekezo chathu pa inu nʼcholimba chifukwa tikudziwa kuti monga momwe mumamva zowawa pamodzi nafe, momwemonso mumatonthozedwa nafe pamodzi. 8 Abale, sitikufuna kuti mukhale osadziwa za masautso amene tinakumana nawo mʼchigawo cha Asiya. Tinapanikizidwa koopsa kuposa muyeso woti nʼkutha kupirira, mwakuti sitinkadziwa kuti nʼkukhalabe ndi moyo. 9 Zoonadi, tinamva mʼmitima mwathu chilango cha imfa. Koma izi zimachitika kuti tisangodzidalira mwa ife tokha koma Mulungu yemwe amaukitsa akufa. 10 Mulungu watilanditsa ku zoopsa zotere za imfa, ndipo adzatilanditsanso. Ife tayika chiyembekezo chathu pa Iyeyo kuti adzapitiriza kutilanditsabe. 11 Mutithandize potipempherera. Pamenepo ambiri adzathokoza mʼmalo mwathu, chifukwa cha chisomo chake poyankha mapemphero a anthu ambiri. 12 Tsono chonyadira chathu nʼchakuti, chikumbumtima chathu chimatitsimikizira kuti timakhala bwino mʼdziko lapansi, makamaka pa ubale wathu ndi inu. Takhala moona mtima ndi oyera mtima. Sitinachite chomwechi mwa nzeru ya dziko lapansi koma monga mwa chisomo cha Mulungu. 13 Pakuti sitikukulemberani zoti simungawerenge kapena kumvetsetsa. 14 Monga mwamva pangʼono chabe, ndikuyembekeza kuti mudzamvetsa kwenikweni, kuti mutha kutinyadira monga ife tidzakunyadirani, pa tsiku la Ambuye Yesu. 15 Popeza ndinatsimikiza mtima za ichi, nʼchifukwa chake ndinafuna kuti poyamba, ndidzakuchezereni kuti mupindule pawiri. 16 Ndinafuna kuti ndidzakuchezereni pa ulendo wanga wopita ku Makedoniya ndi kudzakuonaninso pochokera ku Makedoniyako kuti inu mudzandithandize pa ulendo wanga wopita ku Yudeya. 17 Kodi pamene ndinkakonzekera zimenezi, mukuganiza kuti ndinkachita mwachibwana? Kapena kuti ndinkaganiza ngati mwa dziko lapansi; kuti ndikhoza kumanena kuti, “Inde, Inde,” nthawi yomweyo nʼkumatinso “Ayi, Ayi?” 18 Koma zoona monga Mulungu ali wokhulupirika, uthenga wathu kwa inu siwakuti, “Inde” nʼkutinso “Ayi.” 19 Pakuti Yesu Khristu mwana wa Mulungu amene ine, Silivano ndi Timoteyo tinamulalikira pakati panu sali “Inde” yemweyonso “Ayi.” Koma nthawi zonse mwa Iye muli “Inde.” 20 Pakuti ngakhale malonjezo a Mulungu atachuluka chotani, onsewo ndi “Inde” mwa Khristu. Kotero kuti mwa Iye, ife timati “Ameni” kuchitira Mulungu ulemu. 21 Tsono ndi Mulungu amene anachititsa kuti inu ndi ife tiyime molimba mwa Khristu. Anatidzoza ife, 22 nayikanso Mzimu wake mʼmitima mwathu kutitsimikizira za mʼtsogolo. 23 Mulungu ndi mboni yanga kuti sindinabwererenso ku Korinto kuno kuti ndisakumvetseni chisoni. 24 Sikuti ife tikufuna kukhala olamulira chikhulupiriro chanu, koma timagwira nanu ntchito pamodzi kuti mukhale achimwemwe, chifukwa ndinu okhazikika kwambiri mʼchikhulupiriro.

In Other Versions

2 Corinthians 1 in the ANGEFD

2 Corinthians 1 in the ANTPNG2D

2 Corinthians 1 in the AS21

2 Corinthians 1 in the BAGH

2 Corinthians 1 in the BBPNG

2 Corinthians 1 in the BBT1E

2 Corinthians 1 in the BDS

2 Corinthians 1 in the BEV

2 Corinthians 1 in the BHAD

2 Corinthians 1 in the BIB

2 Corinthians 1 in the BLPT

2 Corinthians 1 in the BNT

2 Corinthians 1 in the BNTABOOT

2 Corinthians 1 in the BNTLV

2 Corinthians 1 in the BOATCB

2 Corinthians 1 in the BOATCB2

2 Corinthians 1 in the BOBCV

2 Corinthians 1 in the BOCNT

2 Corinthians 1 in the BOECS

2 Corinthians 1 in the BOHCB

2 Corinthians 1 in the BOHCV

2 Corinthians 1 in the BOHLNT

2 Corinthians 1 in the BOHNTLTAL

2 Corinthians 1 in the BOICB

2 Corinthians 1 in the BOILNTAP

2 Corinthians 1 in the BOITCV

2 Corinthians 1 in the BOKCV

2 Corinthians 1 in the BOKCV2

2 Corinthians 1 in the BOKHWOG

2 Corinthians 1 in the BOKSSV

2 Corinthians 1 in the BOLCB

2 Corinthians 1 in the BOLCB2

2 Corinthians 1 in the BOMCV

2 Corinthians 1 in the BONAV

2 Corinthians 1 in the BONCB

2 Corinthians 1 in the BONLT

2 Corinthians 1 in the BONUT2

2 Corinthians 1 in the BOPLNT

2 Corinthians 1 in the BOSCB

2 Corinthians 1 in the BOSNC

2 Corinthians 1 in the BOTLNT

2 Corinthians 1 in the BOVCB

2 Corinthians 1 in the BOYCB

2 Corinthians 1 in the BPBB

2 Corinthians 1 in the BPH

2 Corinthians 1 in the BSB

2 Corinthians 1 in the CCB

2 Corinthians 1 in the CUV

2 Corinthians 1 in the CUVS

2 Corinthians 1 in the DBT

2 Corinthians 1 in the DGDNT

2 Corinthians 1 in the DHNT

2 Corinthians 1 in the DNT

2 Corinthians 1 in the ELBE

2 Corinthians 1 in the EMTV

2 Corinthians 1 in the ESV

2 Corinthians 1 in the FBV

2 Corinthians 1 in the FEB

2 Corinthians 1 in the GGMNT

2 Corinthians 1 in the GNT

2 Corinthians 1 in the HARY

2 Corinthians 1 in the HNT

2 Corinthians 1 in the IRVA

2 Corinthians 1 in the IRVB

2 Corinthians 1 in the IRVG

2 Corinthians 1 in the IRVH

2 Corinthians 1 in the IRVK

2 Corinthians 1 in the IRVM

2 Corinthians 1 in the IRVM2

2 Corinthians 1 in the IRVO

2 Corinthians 1 in the IRVP

2 Corinthians 1 in the IRVT

2 Corinthians 1 in the IRVT2

2 Corinthians 1 in the IRVU

2 Corinthians 1 in the ISVN

2 Corinthians 1 in the JSNT

2 Corinthians 1 in the KAPI

2 Corinthians 1 in the KBT1ETNIK

2 Corinthians 1 in the KBV

2 Corinthians 1 in the KJV

2 Corinthians 1 in the KNFD

2 Corinthians 1 in the LBA

2 Corinthians 1 in the LBLA

2 Corinthians 1 in the LNT

2 Corinthians 1 in the LSV

2 Corinthians 1 in the MAAL

2 Corinthians 1 in the MBV

2 Corinthians 1 in the MBV2

2 Corinthians 1 in the MHNT

2 Corinthians 1 in the MKNFD

2 Corinthians 1 in the MNG

2 Corinthians 1 in the MNT

2 Corinthians 1 in the MNT2

2 Corinthians 1 in the MRS1T

2 Corinthians 1 in the NAA

2 Corinthians 1 in the NASB

2 Corinthians 1 in the NBLA

2 Corinthians 1 in the NBS

2 Corinthians 1 in the NBVTP

2 Corinthians 1 in the NET2

2 Corinthians 1 in the NIV11

2 Corinthians 1 in the NNT

2 Corinthians 1 in the NNT2

2 Corinthians 1 in the NNT3

2 Corinthians 1 in the PDDPT

2 Corinthians 1 in the PFNT

2 Corinthians 1 in the RMNT

2 Corinthians 1 in the SBIAS

2 Corinthians 1 in the SBIBS

2 Corinthians 1 in the SBIBS2

2 Corinthians 1 in the SBICS

2 Corinthians 1 in the SBIDS

2 Corinthians 1 in the SBIGS

2 Corinthians 1 in the SBIHS

2 Corinthians 1 in the SBIIS

2 Corinthians 1 in the SBIIS2

2 Corinthians 1 in the SBIIS3

2 Corinthians 1 in the SBIKS

2 Corinthians 1 in the SBIKS2

2 Corinthians 1 in the SBIMS

2 Corinthians 1 in the SBIOS

2 Corinthians 1 in the SBIPS

2 Corinthians 1 in the SBISS

2 Corinthians 1 in the SBITS

2 Corinthians 1 in the SBITS2

2 Corinthians 1 in the SBITS3

2 Corinthians 1 in the SBITS4

2 Corinthians 1 in the SBIUS

2 Corinthians 1 in the SBIVS

2 Corinthians 1 in the SBT

2 Corinthians 1 in the SBT1E

2 Corinthians 1 in the SCHL

2 Corinthians 1 in the SNT

2 Corinthians 1 in the SUSU

2 Corinthians 1 in the SUSU2

2 Corinthians 1 in the SYNO

2 Corinthians 1 in the TBIAOTANT

2 Corinthians 1 in the TBT1E

2 Corinthians 1 in the TBT1E2

2 Corinthians 1 in the TFTIP

2 Corinthians 1 in the TFTU

2 Corinthians 1 in the TGNTATF3T

2 Corinthians 1 in the THAI

2 Corinthians 1 in the TNFD

2 Corinthians 1 in the TNT

2 Corinthians 1 in the TNTIK

2 Corinthians 1 in the TNTIL

2 Corinthians 1 in the TNTIN

2 Corinthians 1 in the TNTIP

2 Corinthians 1 in the TNTIZ

2 Corinthians 1 in the TOMA

2 Corinthians 1 in the TTENT

2 Corinthians 1 in the UBG

2 Corinthians 1 in the UGV

2 Corinthians 1 in the UGV2

2 Corinthians 1 in the UGV3

2 Corinthians 1 in the VBL

2 Corinthians 1 in the VDCC

2 Corinthians 1 in the YALU

2 Corinthians 1 in the YAPE

2 Corinthians 1 in the YBVTP

2 Corinthians 1 in the ZBP