2 Corinthians 5 (BOGWICC)

1 Popeza tikudziwa kuti ngati msasa wa dziko lapansi umene tikukhalamo uwonongeka, tili ndi nyumba yochokera kwa Mulungu, nyumba yamuyaya yakumwamba, osati yomangidwa ndi manja a anthu. 2 Pakali pano tibuwula, ndi kulakalaka kuvala nyumba yathu ya kumwambayo, 3 chifukwa tikavala, sitidzapezekanso amaliseche. 4 Pamene tili mu msasa uno, timalemedwa ndipo timabuwula, chifukwa sitifuna kukhala amaliseche koma ovala nyumba yathu ya kumwamba, kuti chimene chili chakufa chimezedwe ndi moyo. 5 Tsono ndi Mulungu amene anatikonzeratu ife kuti tilandire zimenezi. Iye anatipatsa Mzimu ngati chikole, kutsimikizira zimene zikubwera. 6 Nʼchifukwa chake nthawi zonse timalimba mtima, ndipo timadziwa kuti pamene tikukhala mʼthupi, ndiye kuti tili kutali ndi Ambuye. 7 Ife timakhala mwachikhulupiriro, osati mwa zooneka ndi maso. 8 Inde, ife tikulimba mtima, ndipo tikanakonda kulekana nalo thupi lathu ndi kukhala ndi Ambuye. 9 Choncho timayesetsa kukondweretsa Ambuye, ngakhale tikhale mʼthupi, kapena tichokemo. 10 Pakuti tonsefe tiyenera kukaonekera pa mpando woweruza wa Khristu, kuti aliyense wa ife akalandire zomuyenera molingana ndi zimene anachita ali mʼthupi; zabwino kapena zoyipa. 11 Tsono popeza tikudziwa tanthauzo la kuopa Ambuye, ife timayesetsa kukopa anthu. Mulungu amatidziwa bwino lomwe, ndipo tikukhulupirira kuti inunso mumatidziwa bwino mʼmitima mwanu. 12 Sitikudzichitiranso tokha umboni kwa inu, koma tikukupatsani mwayi oti muzitinyadira. Tikufuna kuti muwayankhe amene amanyadira zinthu zooneka ndi maso osati zimene zili mu mtima. 13 Ngati ndife amisala, monga amanenera ena, nʼchifukwa chofuna kuti Mulungu alemekezedwe. Ngati si ife amisala, nʼkuti inu muthandizike. 14 Pakuti chikondi cha Khristu ndicho chimatikakamiza, chifukwa tikutsimikiza kuti mmodzi anafera anthu onse, kotero kuti anthu onse anafanso. 15 Ndipo Iye anafera anthu onse kuti amene ali ndi moyo, asakhale ndi moyo wofuna kudzikondweretsa okha, koma azikondweretsa amene anawafera naukitsidwa chifukwa cha iwowo. 16 Choncho, kuyambira tsopano mpaka mʼtsogolo ife sitiganizirapo za munthu aliyense monga mwanzeru za umunthu, ngakhale kuti poyamba tinkaganiza za Khristu mʼnjira imeneyi, koma tsopano sititeronso. 17 Nʼchifukwa chake, ngati munthu aliyense ali mwa Khristu, ndi wolengedwa kwatsopano; zinthu zakale zapita taonani, zakhala zatsopano. 18 Zonsezi zichokera kwa Mulungu amene anatiyanjanitsa ndi Iye mwini kudzera mwa Khristu ndipo anatipatsa ife utumiki wa chiyanjanitso. 19 Mulungu ankayanjanitsa dziko lapansi kwa Iye mwini kudzera mwa Khristu, osawerengera anthu monga mwa zochimwa zawo. Ndipo watisungitsa ife uthenga uwu wa chiyanjanitso. 20 Choncho ife ndi akazembe a Khristu, monga ngati Mulungu akudandaulira anthu kudzera mwa ife. Ife tikukupemphani inu mʼmalo mwa Khristu kuti, yanjanitsidwani ndi Mulungu. 21 Chifukwa cha ife, Mulungu anasandutsa wopanda tchimoyo kukhala tchimo, kuti mwa Iye ife tikakhale chilungamo cha Mulungu.

In Other Versions

2 Corinthians 5 in the ANGEFD

2 Corinthians 5 in the ANTPNG2D

2 Corinthians 5 in the AS21

2 Corinthians 5 in the BAGH

2 Corinthians 5 in the BBPNG

2 Corinthians 5 in the BBT1E

2 Corinthians 5 in the BDS

2 Corinthians 5 in the BEV

2 Corinthians 5 in the BHAD

2 Corinthians 5 in the BIB

2 Corinthians 5 in the BLPT

2 Corinthians 5 in the BNT

2 Corinthians 5 in the BNTABOOT

2 Corinthians 5 in the BNTLV

2 Corinthians 5 in the BOATCB

2 Corinthians 5 in the BOATCB2

2 Corinthians 5 in the BOBCV

2 Corinthians 5 in the BOCNT

2 Corinthians 5 in the BOECS

2 Corinthians 5 in the BOHCB

2 Corinthians 5 in the BOHCV

2 Corinthians 5 in the BOHLNT

2 Corinthians 5 in the BOHNTLTAL

2 Corinthians 5 in the BOICB

2 Corinthians 5 in the BOILNTAP

2 Corinthians 5 in the BOITCV

2 Corinthians 5 in the BOKCV

2 Corinthians 5 in the BOKCV2

2 Corinthians 5 in the BOKHWOG

2 Corinthians 5 in the BOKSSV

2 Corinthians 5 in the BOLCB

2 Corinthians 5 in the BOLCB2

2 Corinthians 5 in the BOMCV

2 Corinthians 5 in the BONAV

2 Corinthians 5 in the BONCB

2 Corinthians 5 in the BONLT

2 Corinthians 5 in the BONUT2

2 Corinthians 5 in the BOPLNT

2 Corinthians 5 in the BOSCB

2 Corinthians 5 in the BOSNC

2 Corinthians 5 in the BOTLNT

2 Corinthians 5 in the BOVCB

2 Corinthians 5 in the BOYCB

2 Corinthians 5 in the BPBB

2 Corinthians 5 in the BPH

2 Corinthians 5 in the BSB

2 Corinthians 5 in the CCB

2 Corinthians 5 in the CUV

2 Corinthians 5 in the CUVS

2 Corinthians 5 in the DBT

2 Corinthians 5 in the DGDNT

2 Corinthians 5 in the DHNT

2 Corinthians 5 in the DNT

2 Corinthians 5 in the ELBE

2 Corinthians 5 in the EMTV

2 Corinthians 5 in the ESV

2 Corinthians 5 in the FBV

2 Corinthians 5 in the FEB

2 Corinthians 5 in the GGMNT

2 Corinthians 5 in the GNT

2 Corinthians 5 in the HARY

2 Corinthians 5 in the HNT

2 Corinthians 5 in the IRVA

2 Corinthians 5 in the IRVB

2 Corinthians 5 in the IRVG

2 Corinthians 5 in the IRVH

2 Corinthians 5 in the IRVK

2 Corinthians 5 in the IRVM

2 Corinthians 5 in the IRVM2

2 Corinthians 5 in the IRVO

2 Corinthians 5 in the IRVP

2 Corinthians 5 in the IRVT

2 Corinthians 5 in the IRVT2

2 Corinthians 5 in the IRVU

2 Corinthians 5 in the ISVN

2 Corinthians 5 in the JSNT

2 Corinthians 5 in the KAPI

2 Corinthians 5 in the KBT1ETNIK

2 Corinthians 5 in the KBV

2 Corinthians 5 in the KJV

2 Corinthians 5 in the KNFD

2 Corinthians 5 in the LBA

2 Corinthians 5 in the LBLA

2 Corinthians 5 in the LNT

2 Corinthians 5 in the LSV

2 Corinthians 5 in the MAAL

2 Corinthians 5 in the MBV

2 Corinthians 5 in the MBV2

2 Corinthians 5 in the MHNT

2 Corinthians 5 in the MKNFD

2 Corinthians 5 in the MNG

2 Corinthians 5 in the MNT

2 Corinthians 5 in the MNT2

2 Corinthians 5 in the MRS1T

2 Corinthians 5 in the NAA

2 Corinthians 5 in the NASB

2 Corinthians 5 in the NBLA

2 Corinthians 5 in the NBS

2 Corinthians 5 in the NBVTP

2 Corinthians 5 in the NET2

2 Corinthians 5 in the NIV11

2 Corinthians 5 in the NNT

2 Corinthians 5 in the NNT2

2 Corinthians 5 in the NNT3

2 Corinthians 5 in the PDDPT

2 Corinthians 5 in the PFNT

2 Corinthians 5 in the RMNT

2 Corinthians 5 in the SBIAS

2 Corinthians 5 in the SBIBS

2 Corinthians 5 in the SBIBS2

2 Corinthians 5 in the SBICS

2 Corinthians 5 in the SBIDS

2 Corinthians 5 in the SBIGS

2 Corinthians 5 in the SBIHS

2 Corinthians 5 in the SBIIS

2 Corinthians 5 in the SBIIS2

2 Corinthians 5 in the SBIIS3

2 Corinthians 5 in the SBIKS

2 Corinthians 5 in the SBIKS2

2 Corinthians 5 in the SBIMS

2 Corinthians 5 in the SBIOS

2 Corinthians 5 in the SBIPS

2 Corinthians 5 in the SBISS

2 Corinthians 5 in the SBITS

2 Corinthians 5 in the SBITS2

2 Corinthians 5 in the SBITS3

2 Corinthians 5 in the SBITS4

2 Corinthians 5 in the SBIUS

2 Corinthians 5 in the SBIVS

2 Corinthians 5 in the SBT

2 Corinthians 5 in the SBT1E

2 Corinthians 5 in the SCHL

2 Corinthians 5 in the SNT

2 Corinthians 5 in the SUSU

2 Corinthians 5 in the SUSU2

2 Corinthians 5 in the SYNO

2 Corinthians 5 in the TBIAOTANT

2 Corinthians 5 in the TBT1E

2 Corinthians 5 in the TBT1E2

2 Corinthians 5 in the TFTIP

2 Corinthians 5 in the TFTU

2 Corinthians 5 in the TGNTATF3T

2 Corinthians 5 in the THAI

2 Corinthians 5 in the TNFD

2 Corinthians 5 in the TNT

2 Corinthians 5 in the TNTIK

2 Corinthians 5 in the TNTIL

2 Corinthians 5 in the TNTIN

2 Corinthians 5 in the TNTIP

2 Corinthians 5 in the TNTIZ

2 Corinthians 5 in the TOMA

2 Corinthians 5 in the TTENT

2 Corinthians 5 in the UBG

2 Corinthians 5 in the UGV

2 Corinthians 5 in the UGV2

2 Corinthians 5 in the UGV3

2 Corinthians 5 in the VBL

2 Corinthians 5 in the VDCC

2 Corinthians 5 in the YALU

2 Corinthians 5 in the YAPE

2 Corinthians 5 in the YBVTP

2 Corinthians 5 in the ZBP