2 Kings 1 (BOGWICC)
1 Atamwalira Ahabu, Mowabu anawukira Israeli. 2 Ndipo Ahaziya anagwa kuchokera pa khonde la chipinda chake chammwamba ku Samariya, ndipo anavulala kwambiri. Choncho iye anatuma amithenga nawawuza kuti, “Pitani mukafunse kwa Baala-zebubu, mulungu wa ku Ekroni, ngati ndichire matendawa.” 3 Koma mngelo wa Yehova anawuza Eliya wa ku Tisibe kuti, “Nyamuka, pita ukakumane ndi amithenga a mfumu ya ku Samariya ndipo ukawafunse kuti, ‘Kodi popeza kulibe Mulungu ku Israeli, nʼchifukwa chake inu mukupita kukafunsa nzeru kwa Baala-zebubu, mulungu wa ku Ekroni?’ 4 Tsono Yehova akuti, ‘Iweyo sudzadzuka pa bedi wagonapo. Udzafa ndithu!’ ” Ndipo Eliya ananyamuka. 5 Amithenga aja atabwerera kwa mfumu, mfumuyo inawafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mwabwerera?” 6 Iwo anayankha kuti, “Munthu wina anabwera kudzakumana nafe, ndipo anatiwuza kuti, bwererani kwa mfumu imene inakutumani ndipo mukayiwuze kuti, ‘Yehova akuti, kodi popeza kulibe Mulungu ku Israeli, nʼchifukwa chake mukupita kukafunsa nzeru kwa Baala-zebubu, mulungu wa ku Ekroni? Tsono sudzadzuka pa bedi wagonapo. Udzafa ndithu!’ ” 7 Mfumu inafunsa amithengawo kuti, “Kodi munthu amene anabwera kudzakumana nanuyo ndi kukuwuzani zimenezi amaoneka bwanji?” 8 Iwo anayankha kuti, “Munthuyo anavala zovala zaubweya ndi lamba wachikopa mʼchiwuno mwake.”Mfumu inati, “Munthu ameneyo ndi Eliya wa ku Tisibe.” 9 Pamenepo mfumu inatuma mtsogoleri wa ankhondo ndi anthu ake makumi asanu kwa Eliya. Mtsogoleriyo anapita kwa Eliya, amene anali atakhala pamwamba pa phiri, ndipo anati, “Munthu wa Mulungu, mfumu ikuti, ‘Tsikani!’ ” 10 Eliya anayankha mtsogoleriyo kuti, “Ngati ndine munthu wa Mulungu, moto utsike kuchokera kumwamba, ukupsereze iwe pamodzi ndi anthu makumi asanu akowo!” Pomwepo moto unatsikadi kuchokera kumwamba ndipo unapsereza mtsogoleriyo pamodzi ndi anthu akewo. 11 Zitachitika izi, mfumu inatumanso mtsogoleri wina pamodzi ndi asilikali ake makumi asanu. Mtsogoleriyo anati kwa Eliya, “Munthu wa Mulungu, zimene mfumu ikunena ndi izi, ‘Tsikani msangamsanga!’ ” 12 Eliya anayankha kuti, “Ngati ndine munthu wa Mulungu, moto utsike kuchokera kumwamba, ukupsereze iwe pamodzi ndi anthu ako makumi asanuwo!” Pomwepo moto unatsikadi kuchokera kumwamba ndipo unapsereza mtsogoleriyo pamodzi ndi anthu akewo. 13 Ndipo mfumu inatumanso mtsogoleri wachitatu pamodzi ndi asilikali ake makumi asanu. Mtsogoleri wachitatuyu anakwera pa phiripo ndi kugwada pamaso pa Eliya. Iye anayankhula mopemba kuti, “Munthu wa Mulungu, chonde musandiwononge ineyo pamodzi ndi atumiki makumi asanu anuwa! 14 Taonani, moto unatsika kuchokera kumwamba ndi kupsereza atsogoleri awiri pamodzi ndi anthu awo onse. Koma tsopano musawononge moyo wanga!” 15 Mngelo wa Yehova anati kwa Eliya, “Pita naye, usamuope.” Choncho Eliya ananyamuka natsika naye limodzi kupita kwa mfumu. 16 Eliya anawuza mfumu kuti, “Yehova akuti, ‘Chifukwa chiyani munatumiza amithenga kwa Baala-zebubu, mulungu wa ku Ekroni, kukafunsa ngati muti muchire? Kodi mu Israeli mulibe Mulungu woti nʼkukuyankhani funso lanu? Choncho, popeza mwachita izi, simudzadzuka pamene mwagonapo; mudzafa ndithu.’ ” 17 Motero Ahaziya anafadi, monga mwa mawu a Yehova amene Eliya anayankhula.Tsono popeza Ahaziya analibe mwana, Yoramu analowa ufumu mʼmalo mwake mʼchaka chachiwiri cha Yehoramu mwana wa Yehosafati mfumu ya ku Yuda. 18 Ntchito zina zonse zimene Ahaziya anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a ku Israeli?
In Other Versions
2 Kings 1 in the ANGEFD
2 Kings 1 in the ANTPNG2D
2 Kings 1 in the AS21
2 Kings 1 in the BAGH
2 Kings 1 in the BBPNG
2 Kings 1 in the BBT1E
2 Kings 1 in the BDS
2 Kings 1 in the BEV
2 Kings 1 in the BHAD
2 Kings 1 in the BIB
2 Kings 1 in the BLPT
2 Kings 1 in the BNT
2 Kings 1 in the BNTABOOT
2 Kings 1 in the BNTLV
2 Kings 1 in the BOATCB
2 Kings 1 in the BOATCB2
2 Kings 1 in the BOBCV
2 Kings 1 in the BOCNT
2 Kings 1 in the BOECS
2 Kings 1 in the BOHCB
2 Kings 1 in the BOHCV
2 Kings 1 in the BOHLNT
2 Kings 1 in the BOHNTLTAL
2 Kings 1 in the BOICB
2 Kings 1 in the BOILNTAP
2 Kings 1 in the BOITCV
2 Kings 1 in the BOKCV
2 Kings 1 in the BOKCV2
2 Kings 1 in the BOKHWOG
2 Kings 1 in the BOKSSV
2 Kings 1 in the BOLCB
2 Kings 1 in the BOLCB2
2 Kings 1 in the BOMCV
2 Kings 1 in the BONAV
2 Kings 1 in the BONCB
2 Kings 1 in the BONLT
2 Kings 1 in the BONUT2
2 Kings 1 in the BOPLNT
2 Kings 1 in the BOSCB
2 Kings 1 in the BOSNC
2 Kings 1 in the BOTLNT
2 Kings 1 in the BOVCB
2 Kings 1 in the BOYCB
2 Kings 1 in the BPBB
2 Kings 1 in the BPH
2 Kings 1 in the BSB
2 Kings 1 in the CCB
2 Kings 1 in the CUV
2 Kings 1 in the CUVS
2 Kings 1 in the DBT
2 Kings 1 in the DGDNT
2 Kings 1 in the DHNT
2 Kings 1 in the DNT
2 Kings 1 in the ELBE
2 Kings 1 in the EMTV
2 Kings 1 in the ESV
2 Kings 1 in the FBV
2 Kings 1 in the FEB
2 Kings 1 in the GGMNT
2 Kings 1 in the GNT
2 Kings 1 in the HARY
2 Kings 1 in the HNT
2 Kings 1 in the IRVA
2 Kings 1 in the IRVB
2 Kings 1 in the IRVG
2 Kings 1 in the IRVH
2 Kings 1 in the IRVK
2 Kings 1 in the IRVM
2 Kings 1 in the IRVM2
2 Kings 1 in the IRVO
2 Kings 1 in the IRVP
2 Kings 1 in the IRVT
2 Kings 1 in the IRVT2
2 Kings 1 in the IRVU
2 Kings 1 in the ISVN
2 Kings 1 in the JSNT
2 Kings 1 in the KAPI
2 Kings 1 in the KBT1ETNIK
2 Kings 1 in the KBV
2 Kings 1 in the KJV
2 Kings 1 in the KNFD
2 Kings 1 in the LBA
2 Kings 1 in the LBLA
2 Kings 1 in the LNT
2 Kings 1 in the LSV
2 Kings 1 in the MAAL
2 Kings 1 in the MBV
2 Kings 1 in the MBV2
2 Kings 1 in the MHNT
2 Kings 1 in the MKNFD
2 Kings 1 in the MNG
2 Kings 1 in the MNT
2 Kings 1 in the MNT2
2 Kings 1 in the MRS1T
2 Kings 1 in the NAA
2 Kings 1 in the NASB
2 Kings 1 in the NBLA
2 Kings 1 in the NBS
2 Kings 1 in the NBVTP
2 Kings 1 in the NET2
2 Kings 1 in the NIV11
2 Kings 1 in the NNT
2 Kings 1 in the NNT2
2 Kings 1 in the NNT3
2 Kings 1 in the PDDPT
2 Kings 1 in the PFNT
2 Kings 1 in the RMNT
2 Kings 1 in the SBIAS
2 Kings 1 in the SBIBS
2 Kings 1 in the SBIBS2
2 Kings 1 in the SBICS
2 Kings 1 in the SBIDS
2 Kings 1 in the SBIGS
2 Kings 1 in the SBIHS
2 Kings 1 in the SBIIS
2 Kings 1 in the SBIIS2
2 Kings 1 in the SBIIS3
2 Kings 1 in the SBIKS
2 Kings 1 in the SBIKS2
2 Kings 1 in the SBIMS
2 Kings 1 in the SBIOS
2 Kings 1 in the SBIPS
2 Kings 1 in the SBISS
2 Kings 1 in the SBITS
2 Kings 1 in the SBITS2
2 Kings 1 in the SBITS3
2 Kings 1 in the SBITS4
2 Kings 1 in the SBIUS
2 Kings 1 in the SBIVS
2 Kings 1 in the SBT
2 Kings 1 in the SBT1E
2 Kings 1 in the SCHL
2 Kings 1 in the SNT
2 Kings 1 in the SUSU
2 Kings 1 in the SUSU2
2 Kings 1 in the SYNO
2 Kings 1 in the TBIAOTANT
2 Kings 1 in the TBT1E
2 Kings 1 in the TBT1E2
2 Kings 1 in the TFTIP
2 Kings 1 in the TFTU
2 Kings 1 in the TGNTATF3T
2 Kings 1 in the THAI
2 Kings 1 in the TNFD
2 Kings 1 in the TNT
2 Kings 1 in the TNTIK
2 Kings 1 in the TNTIL
2 Kings 1 in the TNTIN
2 Kings 1 in the TNTIP
2 Kings 1 in the TNTIZ
2 Kings 1 in the TOMA
2 Kings 1 in the TTENT
2 Kings 1 in the UBG
2 Kings 1 in the UGV
2 Kings 1 in the UGV2
2 Kings 1 in the UGV3
2 Kings 1 in the VBL
2 Kings 1 in the VDCC
2 Kings 1 in the YALU
2 Kings 1 in the YAPE
2 Kings 1 in the YBVTP
2 Kings 1 in the ZBP