2 Peter 3 (BOGWICC)

1 Inu okondedwa, iyi ndi kalata yanga yachiwiri kwa inu. Ine ndalemba makalata onse awiri kuti ndikukumbutseni ndi kukutsitsimutsani ndi cholinga choti muzilingalira moyenera. 2 Ndikufuna kuti mukumbukire mawu amene anayankhulidwa kale ndi aneneri oyera mtima ndiponso lamulo limene Ambuye ndi Mpulumutsi wathu analipereka kudzera mwa atumwi. 3 Poyamba mudziwe kuti mʼmasiku otsiriza kudzafika anthu onyoza, adzanyoza ndi kutsata zilakolako zawo zoyipa. 4 Iwo adzati, “Kodi suja Ambuye analonjeza kuti adzabweranso? Nanga ali kuti? Lija nʼkale anamwalira makolo athu, koma zinthu zonse zili monga anazilengera poyamba paja.” 5 Koma iwo akuyiwala dala kuti Mulungu atanena mawu, kumwamba kunakhalapo ndipo analenga dziko lapansi ndi madzi. 6 Ndi madzinso achigumula, dziko lapansi la masiku amenewo linawonongedwa. 7 Dziko la kumwamba ndi lapansi la masiku ano akulisunga ndi mawu omwewo kuti adzalitentha ndi moto. Akuzisunga mpaka tsiku limene adzaweruza ndi kuwononga anthu onse osapembedza Mulungu. 8 Koma abale okondedwa, musayiwale chinthu chimodzi ichi: Kuti pamaso pa Ambuye tsiku limodzi lili ngati zaka 1,000, ndipo zaka 1,000 zili ngati tsiku limodzi! 9 Ambuye sazengereza kuchita zimene analonjeza, monga ena amaganizira. Iwo akukulezerani mtima, sakufuna kuti aliyense awonongeke, koma akufuna kuti aliyense alape. 10 Koma tsiku la Ambuye lidzafika ngati mbala. Pa tsikuli zinthu zakumwamba zidzachoka ndi phokoso lalikulu. Zinthu zonse zidzawonongedwa ndi moto, ndipo dziko lapansi ndi zonse zili mʼmenemo zidzapsa. 11 Popeza kuti zinthu zonse zidzawonongedwa motere, kodi inu muyenera kukhala anthu otani? Muyenera kukhala moyo wachiyero ndi opembedza Mulungu 12 pamene mukuyembekezera tsiku la Mulungu ndi kufulumiza kufika kwake. Pa tsiku limeneli zinthu zakumwamba zidzawonongedwa ndi moto, ndipo zidzasungunuka ndi kutentha. 13 Koma ife tikudikira kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano, zimene Mulungu analonjeza, mʼmene chilungamo chidzakhalamo. 14 Chomwecho okondedwa, popeza inu mukudikira zimenezi, chitani changu kuti mukhale wopanda chilema kuti mukhale pa mtendere ndi Iye. 15 Zindikirani kuti kuleza mtima kwa Ambuye kukutanthauza chipulumutso, monga momwe mʼbale wathu wokondedwa Paulo anakulemberaninso ndi nzeru zimene Mulungu anamupatsa. 16 Iye walemba chimodzimodzi makalata ake onse, kuyankhula za zinthu izi. Mʼmakalata ake mumakhala zinthu zina zovuta kuzimvetsa, zimene anthu osadziwa ndi osakhazikika amazipotoza, monga amachita ndi malemba ena onse, potero akudziwononga okha. 17 Nʼchifukwa chake, abale okondedwa, popeza mukuzidziwa kale zimenezi, chenjerani kuti musatengeke ndi zolakwa za anthu osaweruzika, mungagwe ndi kuchoka pamalo otetezedwa. 18 Koma kulani mu chisomo ndi mʼchidziwitso cha Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu. Kwa Iye kukhale ulemerero tsopano mpaka muyaya. Ameni.

In Other Versions

2 Peter 3 in the ANGEFD

2 Peter 3 in the ANTPNG2D

2 Peter 3 in the AS21

2 Peter 3 in the BAGH

2 Peter 3 in the BBPNG

2 Peter 3 in the BBT1E

2 Peter 3 in the BDS

2 Peter 3 in the BEV

2 Peter 3 in the BHAD

2 Peter 3 in the BIB

2 Peter 3 in the BLPT

2 Peter 3 in the BNT

2 Peter 3 in the BNTABOOT

2 Peter 3 in the BNTLV

2 Peter 3 in the BOATCB

2 Peter 3 in the BOATCB2

2 Peter 3 in the BOBCV

2 Peter 3 in the BOCNT

2 Peter 3 in the BOECS

2 Peter 3 in the BOHCB

2 Peter 3 in the BOHCV

2 Peter 3 in the BOHLNT

2 Peter 3 in the BOHNTLTAL

2 Peter 3 in the BOICB

2 Peter 3 in the BOILNTAP

2 Peter 3 in the BOITCV

2 Peter 3 in the BOKCV

2 Peter 3 in the BOKCV2

2 Peter 3 in the BOKHWOG

2 Peter 3 in the BOKSSV

2 Peter 3 in the BOLCB

2 Peter 3 in the BOLCB2

2 Peter 3 in the BOMCV

2 Peter 3 in the BONAV

2 Peter 3 in the BONCB

2 Peter 3 in the BONLT

2 Peter 3 in the BONUT2

2 Peter 3 in the BOPLNT

2 Peter 3 in the BOSCB

2 Peter 3 in the BOSNC

2 Peter 3 in the BOTLNT

2 Peter 3 in the BOVCB

2 Peter 3 in the BOYCB

2 Peter 3 in the BPBB

2 Peter 3 in the BPH

2 Peter 3 in the BSB

2 Peter 3 in the CCB

2 Peter 3 in the CUV

2 Peter 3 in the CUVS

2 Peter 3 in the DBT

2 Peter 3 in the DGDNT

2 Peter 3 in the DHNT

2 Peter 3 in the DNT

2 Peter 3 in the ELBE

2 Peter 3 in the EMTV

2 Peter 3 in the ESV

2 Peter 3 in the FBV

2 Peter 3 in the FEB

2 Peter 3 in the GGMNT

2 Peter 3 in the GNT

2 Peter 3 in the HARY

2 Peter 3 in the HNT

2 Peter 3 in the IRVA

2 Peter 3 in the IRVB

2 Peter 3 in the IRVG

2 Peter 3 in the IRVH

2 Peter 3 in the IRVK

2 Peter 3 in the IRVM

2 Peter 3 in the IRVM2

2 Peter 3 in the IRVO

2 Peter 3 in the IRVP

2 Peter 3 in the IRVT

2 Peter 3 in the IRVT2

2 Peter 3 in the IRVU

2 Peter 3 in the ISVN

2 Peter 3 in the JSNT

2 Peter 3 in the KAPI

2 Peter 3 in the KBT1ETNIK

2 Peter 3 in the KBV

2 Peter 3 in the KJV

2 Peter 3 in the KNFD

2 Peter 3 in the LBA

2 Peter 3 in the LBLA

2 Peter 3 in the LNT

2 Peter 3 in the LSV

2 Peter 3 in the MAAL

2 Peter 3 in the MBV

2 Peter 3 in the MBV2

2 Peter 3 in the MHNT

2 Peter 3 in the MKNFD

2 Peter 3 in the MNG

2 Peter 3 in the MNT

2 Peter 3 in the MNT2

2 Peter 3 in the MRS1T

2 Peter 3 in the NAA

2 Peter 3 in the NASB

2 Peter 3 in the NBLA

2 Peter 3 in the NBS

2 Peter 3 in the NBVTP

2 Peter 3 in the NET2

2 Peter 3 in the NIV11

2 Peter 3 in the NNT

2 Peter 3 in the NNT2

2 Peter 3 in the NNT3

2 Peter 3 in the PDDPT

2 Peter 3 in the PFNT

2 Peter 3 in the RMNT

2 Peter 3 in the SBIAS

2 Peter 3 in the SBIBS

2 Peter 3 in the SBIBS2

2 Peter 3 in the SBICS

2 Peter 3 in the SBIDS

2 Peter 3 in the SBIGS

2 Peter 3 in the SBIHS

2 Peter 3 in the SBIIS

2 Peter 3 in the SBIIS2

2 Peter 3 in the SBIIS3

2 Peter 3 in the SBIKS

2 Peter 3 in the SBIKS2

2 Peter 3 in the SBIMS

2 Peter 3 in the SBIOS

2 Peter 3 in the SBIPS

2 Peter 3 in the SBISS

2 Peter 3 in the SBITS

2 Peter 3 in the SBITS2

2 Peter 3 in the SBITS3

2 Peter 3 in the SBITS4

2 Peter 3 in the SBIUS

2 Peter 3 in the SBIVS

2 Peter 3 in the SBT

2 Peter 3 in the SBT1E

2 Peter 3 in the SCHL

2 Peter 3 in the SNT

2 Peter 3 in the SUSU

2 Peter 3 in the SUSU2

2 Peter 3 in the SYNO

2 Peter 3 in the TBIAOTANT

2 Peter 3 in the TBT1E

2 Peter 3 in the TBT1E2

2 Peter 3 in the TFTIP

2 Peter 3 in the TFTU

2 Peter 3 in the TGNTATF3T

2 Peter 3 in the THAI

2 Peter 3 in the TNFD

2 Peter 3 in the TNT

2 Peter 3 in the TNTIK

2 Peter 3 in the TNTIL

2 Peter 3 in the TNTIN

2 Peter 3 in the TNTIP

2 Peter 3 in the TNTIZ

2 Peter 3 in the TOMA

2 Peter 3 in the TTENT

2 Peter 3 in the UBG

2 Peter 3 in the UGV

2 Peter 3 in the UGV2

2 Peter 3 in the UGV3

2 Peter 3 in the VBL

2 Peter 3 in the VDCC

2 Peter 3 in the YALU

2 Peter 3 in the YAPE

2 Peter 3 in the YBVTP

2 Peter 3 in the ZBP