2 Thessalonians 3 (BOGWICC)
1 Potsiriza, abale, mutipempherere kuti uthenga wa Ambuye ufalikire msanga ndi kulemekezedwa monga momwe munachitira inu. 2 Ndipo pempherani kuti tilanditsidwe mʼmanja mwa anthu ovuta ndi oyipa, pakuti si onse amene ali nacho chikhulupiriro. 3 Koma Ambuye ndi wokhulupirika, ndipo adzakulimbikitsani ndi kukutetezani kwa woyipayo. 4 Tili ndi chikhulupiriro mwa Ambuye kuti mukuchita zonse ndipo mudzapitirira kuchita zimene tinakulamulirani. 5 Ambuye atsogolere mitima yanu kuti mudziwe chikondi cha Mulungu ndiponso kupirira kumene Khristu amapereka. 6 Abale, tikukulamulani mʼdzina la Ambuye Yesu Khristu, kuti mupewe mʼbale aliyense amene ndi waulesi ndi wachisokonezo, wosafuna kutsata zimene tinakuphunzitsani. 7 Pakuti inu mukudziwa zimene muyenera kuchita pofuna kutitsatira. Ife sitinali alesi pamene tinali nanu 8 ndipo sitinadye chakudya cha aliyense osalipira. Komatu tinkagwira ntchito mwamphamvu usiku ndi usana kuti tisakhale cholemetsa kwa aliyense. 9 Sitinachite zimenezi chifukwa choti tinalibe mphamvu zolamula kuti mutithandize koma kuti tikhale chitsanzo choti mutsatire. 10 Pakuti ngakhale pamene tinali nanu, tinakupatsani lamulo lakuti, “Munthu wosafuna kugwira ntchito, asadye.” 11 Ife tikumva kuti pakati panu pali ena amene ndi alesi. Iwo safuna kugwira ntchito, koma amangolowerera pa za eni. 12 Mʼdzina la Ambuye Yesu Khristu, tikuwalamula ndi kuwakakamiza kuti azigwira ntchito mwabata ndi kumadya chakudya chodzigwirira ntchito okha. 13 Koma inu abale, musatope nʼkuchita zabwino. 14 Ngati wina aliyense akana kumvera malangizo athu a mʼkalatayi, mumuonetsetse ameneyo ndipo musayanjane naye kuti achite manyazi. 15 Komatu musamutenge kukhala mdani, koma muchenjezeni ngati mʼbale. 16 Tsopano Ambuye mwini mtendere akupatseni mtendere nthawi zonse mwa njira iliyonse. Ambuye akhale ndi inu nonse. 17 Ine Paulo, ndikulemba malonje awa ndi dzanja langa, chimene ndi chizindikiro chodziwika mʼmakalata anga onse. Umo ndi mmene ndimalembera. 18 Chisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse.
In Other Versions
2 Thessalonians 3 in the ANGEFD
2 Thessalonians 3 in the ANTPNG2D
2 Thessalonians 3 in the BBPNG
2 Thessalonians 3 in the BBT1E
2 Thessalonians 3 in the BNTABOOT
2 Thessalonians 3 in the BNTLV
2 Thessalonians 3 in the BOATCB
2 Thessalonians 3 in the BOATCB2
2 Thessalonians 3 in the BOBCV
2 Thessalonians 3 in the BOCNT
2 Thessalonians 3 in the BOECS
2 Thessalonians 3 in the BOHCB
2 Thessalonians 3 in the BOHCV
2 Thessalonians 3 in the BOHLNT
2 Thessalonians 3 in the BOHNTLTAL
2 Thessalonians 3 in the BOICB
2 Thessalonians 3 in the BOILNTAP
2 Thessalonians 3 in the BOITCV
2 Thessalonians 3 in the BOKCV
2 Thessalonians 3 in the BOKCV2
2 Thessalonians 3 in the BOKHWOG
2 Thessalonians 3 in the BOKSSV
2 Thessalonians 3 in the BOLCB
2 Thessalonians 3 in the BOLCB2
2 Thessalonians 3 in the BOMCV
2 Thessalonians 3 in the BONAV
2 Thessalonians 3 in the BONCB
2 Thessalonians 3 in the BONLT
2 Thessalonians 3 in the BONUT2
2 Thessalonians 3 in the BOPLNT
2 Thessalonians 3 in the BOSCB
2 Thessalonians 3 in the BOSNC
2 Thessalonians 3 in the BOTLNT
2 Thessalonians 3 in the BOVCB
2 Thessalonians 3 in the BOYCB
2 Thessalonians 3 in the DGDNT
2 Thessalonians 3 in the GGMNT
2 Thessalonians 3 in the IRVM2
2 Thessalonians 3 in the IRVT2
2 Thessalonians 3 in the KBT1ETNIK
2 Thessalonians 3 in the MKNFD
2 Thessalonians 3 in the MRS1T
2 Thessalonians 3 in the NBVTP
2 Thessalonians 3 in the NIV11
2 Thessalonians 3 in the PDDPT
2 Thessalonians 3 in the SBIAS
2 Thessalonians 3 in the SBIBS
2 Thessalonians 3 in the SBIBS2
2 Thessalonians 3 in the SBICS
2 Thessalonians 3 in the SBIDS
2 Thessalonians 3 in the SBIGS
2 Thessalonians 3 in the SBIHS
2 Thessalonians 3 in the SBIIS
2 Thessalonians 3 in the SBIIS2
2 Thessalonians 3 in the SBIIS3
2 Thessalonians 3 in the SBIKS
2 Thessalonians 3 in the SBIKS2
2 Thessalonians 3 in the SBIMS
2 Thessalonians 3 in the SBIOS
2 Thessalonians 3 in the SBIPS
2 Thessalonians 3 in the SBISS
2 Thessalonians 3 in the SBITS
2 Thessalonians 3 in the SBITS2
2 Thessalonians 3 in the SBITS3
2 Thessalonians 3 in the SBITS4
2 Thessalonians 3 in the SBIUS
2 Thessalonians 3 in the SBIVS
2 Thessalonians 3 in the SBT1E
2 Thessalonians 3 in the SUSU2
2 Thessalonians 3 in the TBIAOTANT
2 Thessalonians 3 in the TBT1E
2 Thessalonians 3 in the TBT1E2
2 Thessalonians 3 in the TFTIP
2 Thessalonians 3 in the TGNTATF3T
2 Thessalonians 3 in the TNTIK
2 Thessalonians 3 in the TNTIL
2 Thessalonians 3 in the TNTIN
2 Thessalonians 3 in the TNTIP
2 Thessalonians 3 in the TNTIZ
2 Thessalonians 3 in the TTENT