2 Timothy 4 (BOGWICC)
1 Pamaso pa Mulungu ndi pamaso pa Khristu Yesu, amene adzaweruza amoyo ndi akufa omwe pamene adzaonekera ndi ufumu wake, ndikukulamula kuti: 2 Lalikira Mawu; khala wokonzeka pa nthawi yake, ngakhale pamene si pa nthawi yake. Konza zolakwa zawo, dzudzula ndipo limbikitsa moleza mtima kwambiri ndi malangizo osamalitsa. 3 Pakuti idzafika nthawi imene anthu adzakana chiphunzitso choona. Mʼmalo mwake, chifukwa chokhumba kumva zowakomera zokha, adzasonkhanitsa aphunzitsi ambiri omawawuza zimene iwo akufuna kumva. 4 Sadzafuna kumva choona koma adzafuna kumva nthano chabe. 5 Koma iwe, khala tcheru nthawi zonse, pirira mʼzovuta, gwira ntchito ya mlaliki, gwira ntchito zonse za utumiki wako. 6 Pakuti moyo wanga wayamba kale kuthiridwa ngati nsembe, ndipo nthawi yakwana yoti ndinyamuke ulendo wanga. 7 Ndamenya nkhondo yabwino, ndatsiriza bwino mpikisano wa liwiro ndipo ndasunga chikhulupiriro. 8 Tsopano mphotho yanga ikundidikira imene ndi chipewa cha chilungamo, imene Ambuye, woweruza wolungama, adzandipatsa pa tsiku lijalo, osati ine ndekha komanso onse amene akufunitsitsa kubwera kwake. 9 Uyesetse kubwera kuno msanga. 10 Paja Dema anandisiya chifukwa chokonda dziko lapansi lino, ndipo anapita ku Tesalonika. Kresike anapita ku Galatiya ndipo Tito anapita ku Dalimatiya. 11 Ndatsala ndi Luka yekha basi. Mutenge Marko ndipo ubwere naye kuno, chifukwa amandithandiza mu utumiki wanga. 12 Ndatumiza Tukiko ku Efeso. 13 Pobwera, unditengere chofunda pamwamba chimene ndinachisiya kwa Kupro ku Trowa. Unditengerenso mabuku anga, makamaka aja azikopawa. 14 Alekisandro, mmisiri wa zitsulo anandichitira zoyipa kwambiri. Ambuye adzamubwezera pa zimene anachita. 15 Iwenso ukhale naye tcheru chifukwa anatsutsa kwambiri uthenga wathu. 16 Podziteteza koyamba pa mlandu wanga, panalibe ndi mmodzi yemwe amene anandithandiza, koma aliyense anandithawa. Mulungu awakhululukire. 17 Koma Ambuye anayima nane limodzi, ndipo anandipatsa mphamvu, kuti kudzera mwa ine, uthenga ulalikidwe kwambiri, ndikuti anthu a mitundu ina amve. Ndipo ndinalanditsidwa mʼkamwa mwa mkango. 18 Ambuye adzandilanditsa ku chilichonse chofuna kundichita choyipa ndipo adzandisamalira bwino mpaka kundilowetsa chonse mu ufumu wake wakumwamba. Kwa Iye kukhale ulemerero mpaka muyaya. 19 Pereka moni kwa Prisila ndi Akura pamodzi ndi banja lonse la Onesiforo. 20 Erasto anatsalira ku Korinto. Trofimo ndinamusiya akudwala ku Mileto. 21 Uyesetse kubwera kuno nthawi yozizira isanafike. Eubulo akupereka moni, ndiponso Pude, Lino, Klaudiya ndi abale onse nawonso akupereka moni. 22 Ambuye akhale ndi mzimu wako. Chisomo chikhale ndi inu nonse.
In Other Versions
2 Timothy 4 in the ANGEFD
2 Timothy 4 in the ANTPNG2D
2 Timothy 4 in the AS21
2 Timothy 4 in the BAGH
2 Timothy 4 in the BBPNG
2 Timothy 4 in the BBT1E
2 Timothy 4 in the BDS
2 Timothy 4 in the BEV
2 Timothy 4 in the BHAD
2 Timothy 4 in the BIB
2 Timothy 4 in the BLPT
2 Timothy 4 in the BNT
2 Timothy 4 in the BNTABOOT
2 Timothy 4 in the BNTLV
2 Timothy 4 in the BOATCB
2 Timothy 4 in the BOATCB2
2 Timothy 4 in the BOBCV
2 Timothy 4 in the BOCNT
2 Timothy 4 in the BOECS
2 Timothy 4 in the BOHCB
2 Timothy 4 in the BOHCV
2 Timothy 4 in the BOHLNT
2 Timothy 4 in the BOHNTLTAL
2 Timothy 4 in the BOICB
2 Timothy 4 in the BOILNTAP
2 Timothy 4 in the BOITCV
2 Timothy 4 in the BOKCV
2 Timothy 4 in the BOKCV2
2 Timothy 4 in the BOKHWOG
2 Timothy 4 in the BOKSSV
2 Timothy 4 in the BOLCB
2 Timothy 4 in the BOLCB2
2 Timothy 4 in the BOMCV
2 Timothy 4 in the BONAV
2 Timothy 4 in the BONCB
2 Timothy 4 in the BONLT
2 Timothy 4 in the BONUT2
2 Timothy 4 in the BOPLNT
2 Timothy 4 in the BOSCB
2 Timothy 4 in the BOSNC
2 Timothy 4 in the BOTLNT
2 Timothy 4 in the BOVCB
2 Timothy 4 in the BOYCB
2 Timothy 4 in the BPBB
2 Timothy 4 in the BPH
2 Timothy 4 in the BSB
2 Timothy 4 in the CCB
2 Timothy 4 in the CUV
2 Timothy 4 in the CUVS
2 Timothy 4 in the DBT
2 Timothy 4 in the DGDNT
2 Timothy 4 in the DHNT
2 Timothy 4 in the DNT
2 Timothy 4 in the ELBE
2 Timothy 4 in the EMTV
2 Timothy 4 in the ESV
2 Timothy 4 in the FBV
2 Timothy 4 in the FEB
2 Timothy 4 in the GGMNT
2 Timothy 4 in the GNT
2 Timothy 4 in the HARY
2 Timothy 4 in the HNT
2 Timothy 4 in the IRVA
2 Timothy 4 in the IRVB
2 Timothy 4 in the IRVG
2 Timothy 4 in the IRVH
2 Timothy 4 in the IRVK
2 Timothy 4 in the IRVM
2 Timothy 4 in the IRVM2
2 Timothy 4 in the IRVO
2 Timothy 4 in the IRVP
2 Timothy 4 in the IRVT
2 Timothy 4 in the IRVT2
2 Timothy 4 in the IRVU
2 Timothy 4 in the ISVN
2 Timothy 4 in the JSNT
2 Timothy 4 in the KAPI
2 Timothy 4 in the KBT1ETNIK
2 Timothy 4 in the KBV
2 Timothy 4 in the KJV
2 Timothy 4 in the KNFD
2 Timothy 4 in the LBA
2 Timothy 4 in the LBLA
2 Timothy 4 in the LNT
2 Timothy 4 in the LSV
2 Timothy 4 in the MAAL
2 Timothy 4 in the MBV
2 Timothy 4 in the MBV2
2 Timothy 4 in the MHNT
2 Timothy 4 in the MKNFD
2 Timothy 4 in the MNG
2 Timothy 4 in the MNT
2 Timothy 4 in the MNT2
2 Timothy 4 in the MRS1T
2 Timothy 4 in the NAA
2 Timothy 4 in the NASB
2 Timothy 4 in the NBLA
2 Timothy 4 in the NBS
2 Timothy 4 in the NBVTP
2 Timothy 4 in the NET2
2 Timothy 4 in the NIV11
2 Timothy 4 in the NNT
2 Timothy 4 in the NNT2
2 Timothy 4 in the NNT3
2 Timothy 4 in the PDDPT
2 Timothy 4 in the PFNT
2 Timothy 4 in the RMNT
2 Timothy 4 in the SBIAS
2 Timothy 4 in the SBIBS
2 Timothy 4 in the SBIBS2
2 Timothy 4 in the SBICS
2 Timothy 4 in the SBIDS
2 Timothy 4 in the SBIGS
2 Timothy 4 in the SBIHS
2 Timothy 4 in the SBIIS
2 Timothy 4 in the SBIIS2
2 Timothy 4 in the SBIIS3
2 Timothy 4 in the SBIKS
2 Timothy 4 in the SBIKS2
2 Timothy 4 in the SBIMS
2 Timothy 4 in the SBIOS
2 Timothy 4 in the SBIPS
2 Timothy 4 in the SBISS
2 Timothy 4 in the SBITS
2 Timothy 4 in the SBITS2
2 Timothy 4 in the SBITS3
2 Timothy 4 in the SBITS4
2 Timothy 4 in the SBIUS
2 Timothy 4 in the SBIVS
2 Timothy 4 in the SBT
2 Timothy 4 in the SBT1E
2 Timothy 4 in the SCHL
2 Timothy 4 in the SNT
2 Timothy 4 in the SUSU
2 Timothy 4 in the SUSU2
2 Timothy 4 in the SYNO
2 Timothy 4 in the TBIAOTANT
2 Timothy 4 in the TBT1E
2 Timothy 4 in the TBT1E2
2 Timothy 4 in the TFTIP
2 Timothy 4 in the TFTU
2 Timothy 4 in the TGNTATF3T
2 Timothy 4 in the THAI
2 Timothy 4 in the TNFD
2 Timothy 4 in the TNT
2 Timothy 4 in the TNTIK
2 Timothy 4 in the TNTIL
2 Timothy 4 in the TNTIN
2 Timothy 4 in the TNTIP
2 Timothy 4 in the TNTIZ
2 Timothy 4 in the TOMA
2 Timothy 4 in the TTENT
2 Timothy 4 in the UBG
2 Timothy 4 in the UGV
2 Timothy 4 in the UGV2
2 Timothy 4 in the UGV3
2 Timothy 4 in the VBL
2 Timothy 4 in the VDCC
2 Timothy 4 in the YALU
2 Timothy 4 in the YAPE
2 Timothy 4 in the YBVTP
2 Timothy 4 in the ZBP