Daniel 1 (BOGWICC)

1 Chaka chachitatu cha ufumu wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda, Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni inabwera ndi kuzinga mzinda wa Yerusalemu ndi kuwuthira nkhondo. 2 Ndipo Ambuye anapereka Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda mʼdzanja lake, pamodzi ndi zina mwa zida zotumikira mʼNyumba ya Mulungu. Iye anazitenga napita nazo ku nyumba ya mulungu wake ku Babuloni ndi kuziyika mʼnyumba yosungiramo chuma cha mulungu wake. 3 Tsono mfumu inalamula Asipenazi, mkulu wa nduna zake kuti abwere nawo ena mwa Aisraeli ochokera mʼbanja laufumu ndi la olemekezeka, 4 achinyamata wopanda chilema, okongola, aluso mu nzeru zonse, okhala ndi chidziwitso, achangu pophunzira, odziwa kutumikira mʼnyumba ya mfumu. Ndipo anati awaphunzitsenso kuwerenga chiyankhulo cha Ababuloni. 5 Ndipo mfumu imawapatsa tsiku ndi tsiku gawo la chakudya ndi vinyo wa ku nyumba yaufumu, ndi kuti awaphunzitse kwa zaka zitatu, ndipo kenaka adzayambe kutumikira mfumu. 6 Pakati pa amenewa panali ena ochokera ku Yuda: Danieli, Hananiya, Misaeli ndi Azariya. 7 Mkulu wa nduna za mfumu anawapatsa mayina atsopano: Danieli anamutcha Belitesezara; Hananiya anamutcha Sadirake; Misaeli anamutcha Mesaki; ndi Azariya anamutcha Abedenego. 8 Koma Danieli anatsimikiza mtima kuti asadzidetse ndi chakudya ndi vinyo wa mfumu, ndipo anapempha chilolezo kwa mkulu wa nduna za mfumu kuti asadzidetse mwa njira imeneyi. 9 Ndipo Mulungu anafewetsa mtima wa ndunayo kuti amukomere mtima ndi kumuchitira chifundo Danieli, 10 koma ndunayo inamuwuza Danieli kuti, “Ine ndikuchita mantha ndi mbuye wanga mfumu, amene wapereka chakudya ndi chakumwa chanu. Kodi akuoneni inu owonda kuposa anzanu a misinkhu yanu pa chifukwa chanji? Mfumu ikhoza kundidula mutu chifukwa cha iwe.” 11 Ndipo Danieli anati kwa kapitawo amene anali mkulu wa nduna za mfumu amene anamuyika kuti ayangʼanire Danieli, Hananiya, Misaeli ndi Azariya, 12 “Chonde mutiyese ife akapolo anu pa masiku khumi: mutipatse masamba okha kuti tidye ndi madzi akumwa. 13 Ndipo mudzafananize maonekedwe athu ndi a anyamata amene akudya chakudya cha mfumu, ndi kuti mudzachite ndi anyamata anu monga momwe mudzawaonere.” 14 Choncho anawavomera ndipo anawayesa pa masiku khumi. 15 Pakutha pa masiku khumi iwo anaoneka athanzi ndi odya bwino kuposa aliyense wa anyamata amene ankadya chakudya cha mfumu aja. 16 Choncho kapitawo anawachotsera chakudya ndi vinyo za ku nyumba yaufumu zija nawapatsa ndiwo zamasamba basi. 17 Kwa anyamata anayiwa Mulungu anapereka chidziwitso ndi kuzindikira bwino mitundu yonse ya zolembedwa ndi za maphunziro. Ndipo Danieli ankatanthauzira masomphenya ndi maloto a mitundu yonse. 18 Ndipo kumapeto kwa masiku amene mfumu inayika kuti adzaonetse anyamatawa ku nyumba yake, mkulu wa nduna za mfumu uja anawapereka iwo kwa Nebukadinezara. 19 Mfumu inayankhula nawo, ndipo panalibe wofanana ndi Danieli; Hananiya Misaeli ndi Azariya; Choncho analowa ndi kukhala otumikira mfumu. 20 Nthawi zonse mfumu ikawafunsa zonse zofuna nzeru ndi chidziwitso, inkapeza kuti iwo anali oposa amatsenga ndi owombeza onse a mu ufumu wake wonse mopitirira muyeso. 21 Ndipo Danieli anali kumeneko mpaka chaka choyamba cha ufumu wa Koresi.

In Other Versions

Daniel 1 in the ANGEFD

Daniel 1 in the ANTPNG2D

Daniel 1 in the AS21

Daniel 1 in the BAGH

Daniel 1 in the BBPNG

Daniel 1 in the BBT1E

Daniel 1 in the BDS

Daniel 1 in the BEV

Daniel 1 in the BHAD

Daniel 1 in the BIB

Daniel 1 in the BLPT

Daniel 1 in the BNT

Daniel 1 in the BNTABOOT

Daniel 1 in the BNTLV

Daniel 1 in the BOATCB

Daniel 1 in the BOATCB2

Daniel 1 in the BOBCV

Daniel 1 in the BOCNT

Daniel 1 in the BOECS

Daniel 1 in the BOHCB

Daniel 1 in the BOHCV

Daniel 1 in the BOHLNT

Daniel 1 in the BOHNTLTAL

Daniel 1 in the BOICB

Daniel 1 in the BOILNTAP

Daniel 1 in the BOITCV

Daniel 1 in the BOKCV

Daniel 1 in the BOKCV2

Daniel 1 in the BOKHWOG

Daniel 1 in the BOKSSV

Daniel 1 in the BOLCB

Daniel 1 in the BOLCB2

Daniel 1 in the BOMCV

Daniel 1 in the BONAV

Daniel 1 in the BONCB

Daniel 1 in the BONLT

Daniel 1 in the BONUT2

Daniel 1 in the BOPLNT

Daniel 1 in the BOSCB

Daniel 1 in the BOSNC

Daniel 1 in the BOTLNT

Daniel 1 in the BOVCB

Daniel 1 in the BOYCB

Daniel 1 in the BPBB

Daniel 1 in the BPH

Daniel 1 in the BSB

Daniel 1 in the CCB

Daniel 1 in the CUV

Daniel 1 in the CUVS

Daniel 1 in the DBT

Daniel 1 in the DGDNT

Daniel 1 in the DHNT

Daniel 1 in the DNT

Daniel 1 in the ELBE

Daniel 1 in the EMTV

Daniel 1 in the ESV

Daniel 1 in the FBV

Daniel 1 in the FEB

Daniel 1 in the GGMNT

Daniel 1 in the GNT

Daniel 1 in the HARY

Daniel 1 in the HNT

Daniel 1 in the IRVA

Daniel 1 in the IRVB

Daniel 1 in the IRVG

Daniel 1 in the IRVH

Daniel 1 in the IRVK

Daniel 1 in the IRVM

Daniel 1 in the IRVM2

Daniel 1 in the IRVO

Daniel 1 in the IRVP

Daniel 1 in the IRVT

Daniel 1 in the IRVT2

Daniel 1 in the IRVU

Daniel 1 in the ISVN

Daniel 1 in the JSNT

Daniel 1 in the KAPI

Daniel 1 in the KBT1ETNIK

Daniel 1 in the KBV

Daniel 1 in the KJV

Daniel 1 in the KNFD

Daniel 1 in the LBA

Daniel 1 in the LBLA

Daniel 1 in the LNT

Daniel 1 in the LSV

Daniel 1 in the MAAL

Daniel 1 in the MBV

Daniel 1 in the MBV2

Daniel 1 in the MHNT

Daniel 1 in the MKNFD

Daniel 1 in the MNG

Daniel 1 in the MNT

Daniel 1 in the MNT2

Daniel 1 in the MRS1T

Daniel 1 in the NAA

Daniel 1 in the NASB

Daniel 1 in the NBLA

Daniel 1 in the NBS

Daniel 1 in the NBVTP

Daniel 1 in the NET2

Daniel 1 in the NIV11

Daniel 1 in the NNT

Daniel 1 in the NNT2

Daniel 1 in the NNT3

Daniel 1 in the PDDPT

Daniel 1 in the PFNT

Daniel 1 in the RMNT

Daniel 1 in the SBIAS

Daniel 1 in the SBIBS

Daniel 1 in the SBIBS2

Daniel 1 in the SBICS

Daniel 1 in the SBIDS

Daniel 1 in the SBIGS

Daniel 1 in the SBIHS

Daniel 1 in the SBIIS

Daniel 1 in the SBIIS2

Daniel 1 in the SBIIS3

Daniel 1 in the SBIKS

Daniel 1 in the SBIKS2

Daniel 1 in the SBIMS

Daniel 1 in the SBIOS

Daniel 1 in the SBIPS

Daniel 1 in the SBISS

Daniel 1 in the SBITS

Daniel 1 in the SBITS2

Daniel 1 in the SBITS3

Daniel 1 in the SBITS4

Daniel 1 in the SBIUS

Daniel 1 in the SBIVS

Daniel 1 in the SBT

Daniel 1 in the SBT1E

Daniel 1 in the SCHL

Daniel 1 in the SNT

Daniel 1 in the SUSU

Daniel 1 in the SUSU2

Daniel 1 in the SYNO

Daniel 1 in the TBIAOTANT

Daniel 1 in the TBT1E

Daniel 1 in the TBT1E2

Daniel 1 in the TFTIP

Daniel 1 in the TFTU

Daniel 1 in the TGNTATF3T

Daniel 1 in the THAI

Daniel 1 in the TNFD

Daniel 1 in the TNT

Daniel 1 in the TNTIK

Daniel 1 in the TNTIL

Daniel 1 in the TNTIN

Daniel 1 in the TNTIP

Daniel 1 in the TNTIZ

Daniel 1 in the TOMA

Daniel 1 in the TTENT

Daniel 1 in the UBG

Daniel 1 in the UGV

Daniel 1 in the UGV2

Daniel 1 in the UGV3

Daniel 1 in the VBL

Daniel 1 in the VDCC

Daniel 1 in the YALU

Daniel 1 in the YAPE

Daniel 1 in the YBVTP

Daniel 1 in the ZBP