Deuteronomy 25 (BOGWICC)
1 Anthu akasemphana mawu, ayenera kupita ku bwalo la milandu ndipo woweruza adzaweruza mlanduwo. Adzamasula wosalakwa nalanga wolakwa. 2 Munthu akapezeka wolakwa ayenera kukwapulidwa, woweruza amugoneke pansi wolakwayo ndipo akwapulidwe pamaso pake zikoti zochuluka molingana ndi mlandu wake, 3 koma asamukwapule zikoti zopitirira makumi anayi. Akakwapulidwa kupitirira apo ndiye kuti mʼbale wanuyo anyozeka pamaso panu. 4 Musamange ngʼombe pakamwa pamene ikupuntha tirigu. 5 Ngati abale akukhala pamodzi ndipo wina mwa iwo akamwalira wosasiya mwana wamwamuna, mkazi wamasiyeyo asakakwatiwe ndi mlendo. Mʼbale wake wa mwamuna wakeyo amukwatire kukwaniritsa chimene akuyenera kuchita kwa mlamu wakeyo. 6 Mwana wamwamuna woyamba amene mayiyo angabereke ayenera kutenga dzina la mwamuna wake womwalirayo kuti dzina lake lisafafanizike mu Israeli. 7 Komabe, ngati munthu sakufuna kukwatira mkazi wa mʼbale wakeyo, mkaziyo ayenera kupita kwa akuluakulu ku chipata cha mzinda ndi kukanena kuti, “Mʼbale wake wa mwamuna wanga akukana kupitiriza dzina la mʼbale wake mu Israeli. Iye akukana kulowa chokolo.” 8 Pamenepo akuluakulu a mu mzinda wawowo adzamuyitanitsa nakamba naye. Ngati alimbikirabe kunena kuti, “Ine sindikufuna kumukwatira mkaziyu,” 9 mkazi wamasiye wa mʼbale wakeyo adzapita kwa iye pamaso pa akuluakuluwo namuvula nsapato imodzi, adzamulavulire kumaso nʼkunena kuti, “Izi ndi zimene amachitira munthu amene safuna kupitiriza mbiri ya banja la mʼbale wake.” 10 Mbiri ya banja la munthu ameneyo idzadziwika mu Israeli kuti ndi Banja la Wovulidwa nsapato. 11 Ngati anthu awiri akuchita ndewu ndipo mkazi wa mmodzi wa iwo abwera kudzaleretsa mwamuna wake kwa mnzakeyo natambasula dzanja lake kugwira ku maliseche kwa winayo, 12 muyenera kumudula dzanja, osamumvera chisoni. 13 Musamakhale ndi miyeso iwiri yosiyana mʼthumba mwanu, wolemera ndi wopepuka. 14 Musamakhale ndi milingo iwiri yosiyana mʼnyumba mwanu, waukulu ndi waungʼono. 15 Muyenera kukhala ndi miyeso ndi milingo yoyenera ndi yosanyenga kuti mukhalitse mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani. 16 Pakuti Yehova Mulungu wanu amanyansidwa ndi aliyense wochita za chinyengo zoterezi. 17 Kumbukirani zimene Aamaleki anakuchitirani pamene munali pa ulendo wochokera ku Igupto. 18 Pamene munali otopa ndi ofowoka, iwo anakumana nanu pa ulendo wanu ndi kukantha onse otsalira mʼmbuyo ndipo iwo sanaope Mulungu. 19 Pamene Yehova Mulungu wanu akupumulitsani kwa adani onse okuzungulirani mʼdziko limene akupatsani inu ngati cholowa chanu, mudzawafafanize Aamaleki, asadzawakumbukirenso pa dziko lapansi. Musadzayiwale chimenechi!
In Other Versions
Deuteronomy 25 in the ANGEFD
Deuteronomy 25 in the ANTPNG2D
Deuteronomy 25 in the AS21
Deuteronomy 25 in the BAGH
Deuteronomy 25 in the BBPNG
Deuteronomy 25 in the BBT1E
Deuteronomy 25 in the BDS
Deuteronomy 25 in the BEV
Deuteronomy 25 in the BHAD
Deuteronomy 25 in the BIB
Deuteronomy 25 in the BLPT
Deuteronomy 25 in the BNT
Deuteronomy 25 in the BNTABOOT
Deuteronomy 25 in the BNTLV
Deuteronomy 25 in the BOATCB
Deuteronomy 25 in the BOATCB2
Deuteronomy 25 in the BOBCV
Deuteronomy 25 in the BOCNT
Deuteronomy 25 in the BOECS
Deuteronomy 25 in the BOHCB
Deuteronomy 25 in the BOHCV
Deuteronomy 25 in the BOHLNT
Deuteronomy 25 in the BOHNTLTAL
Deuteronomy 25 in the BOICB
Deuteronomy 25 in the BOILNTAP
Deuteronomy 25 in the BOITCV
Deuteronomy 25 in the BOKCV
Deuteronomy 25 in the BOKCV2
Deuteronomy 25 in the BOKHWOG
Deuteronomy 25 in the BOKSSV
Deuteronomy 25 in the BOLCB
Deuteronomy 25 in the BOLCB2
Deuteronomy 25 in the BOMCV
Deuteronomy 25 in the BONAV
Deuteronomy 25 in the BONCB
Deuteronomy 25 in the BONLT
Deuteronomy 25 in the BONUT2
Deuteronomy 25 in the BOPLNT
Deuteronomy 25 in the BOSCB
Deuteronomy 25 in the BOSNC
Deuteronomy 25 in the BOTLNT
Deuteronomy 25 in the BOVCB
Deuteronomy 25 in the BOYCB
Deuteronomy 25 in the BPBB
Deuteronomy 25 in the BPH
Deuteronomy 25 in the BSB
Deuteronomy 25 in the CCB
Deuteronomy 25 in the CUV
Deuteronomy 25 in the CUVS
Deuteronomy 25 in the DBT
Deuteronomy 25 in the DGDNT
Deuteronomy 25 in the DHNT
Deuteronomy 25 in the DNT
Deuteronomy 25 in the ELBE
Deuteronomy 25 in the EMTV
Deuteronomy 25 in the ESV
Deuteronomy 25 in the FBV
Deuteronomy 25 in the FEB
Deuteronomy 25 in the GGMNT
Deuteronomy 25 in the GNT
Deuteronomy 25 in the HARY
Deuteronomy 25 in the HNT
Deuteronomy 25 in the IRVA
Deuteronomy 25 in the IRVB
Deuteronomy 25 in the IRVG
Deuteronomy 25 in the IRVH
Deuteronomy 25 in the IRVK
Deuteronomy 25 in the IRVM
Deuteronomy 25 in the IRVM2
Deuteronomy 25 in the IRVO
Deuteronomy 25 in the IRVP
Deuteronomy 25 in the IRVT
Deuteronomy 25 in the IRVT2
Deuteronomy 25 in the IRVU
Deuteronomy 25 in the ISVN
Deuteronomy 25 in the JSNT
Deuteronomy 25 in the KAPI
Deuteronomy 25 in the KBT1ETNIK
Deuteronomy 25 in the KBV
Deuteronomy 25 in the KJV
Deuteronomy 25 in the KNFD
Deuteronomy 25 in the LBA
Deuteronomy 25 in the LBLA
Deuteronomy 25 in the LNT
Deuteronomy 25 in the LSV
Deuteronomy 25 in the MAAL
Deuteronomy 25 in the MBV
Deuteronomy 25 in the MBV2
Deuteronomy 25 in the MHNT
Deuteronomy 25 in the MKNFD
Deuteronomy 25 in the MNG
Deuteronomy 25 in the MNT
Deuteronomy 25 in the MNT2
Deuteronomy 25 in the MRS1T
Deuteronomy 25 in the NAA
Deuteronomy 25 in the NASB
Deuteronomy 25 in the NBLA
Deuteronomy 25 in the NBS
Deuteronomy 25 in the NBVTP
Deuteronomy 25 in the NET2
Deuteronomy 25 in the NIV11
Deuteronomy 25 in the NNT
Deuteronomy 25 in the NNT2
Deuteronomy 25 in the NNT3
Deuteronomy 25 in the PDDPT
Deuteronomy 25 in the PFNT
Deuteronomy 25 in the RMNT
Deuteronomy 25 in the SBIAS
Deuteronomy 25 in the SBIBS
Deuteronomy 25 in the SBIBS2
Deuteronomy 25 in the SBICS
Deuteronomy 25 in the SBIDS
Deuteronomy 25 in the SBIGS
Deuteronomy 25 in the SBIHS
Deuteronomy 25 in the SBIIS
Deuteronomy 25 in the SBIIS2
Deuteronomy 25 in the SBIIS3
Deuteronomy 25 in the SBIKS
Deuteronomy 25 in the SBIKS2
Deuteronomy 25 in the SBIMS
Deuteronomy 25 in the SBIOS
Deuteronomy 25 in the SBIPS
Deuteronomy 25 in the SBISS
Deuteronomy 25 in the SBITS
Deuteronomy 25 in the SBITS2
Deuteronomy 25 in the SBITS3
Deuteronomy 25 in the SBITS4
Deuteronomy 25 in the SBIUS
Deuteronomy 25 in the SBIVS
Deuteronomy 25 in the SBT
Deuteronomy 25 in the SBT1E
Deuteronomy 25 in the SCHL
Deuteronomy 25 in the SNT
Deuteronomy 25 in the SUSU
Deuteronomy 25 in the SUSU2
Deuteronomy 25 in the SYNO
Deuteronomy 25 in the TBIAOTANT
Deuteronomy 25 in the TBT1E
Deuteronomy 25 in the TBT1E2
Deuteronomy 25 in the TFTIP
Deuteronomy 25 in the TFTU
Deuteronomy 25 in the TGNTATF3T
Deuteronomy 25 in the THAI
Deuteronomy 25 in the TNFD
Deuteronomy 25 in the TNT
Deuteronomy 25 in the TNTIK
Deuteronomy 25 in the TNTIL
Deuteronomy 25 in the TNTIN
Deuteronomy 25 in the TNTIP
Deuteronomy 25 in the TNTIZ
Deuteronomy 25 in the TOMA
Deuteronomy 25 in the TTENT
Deuteronomy 25 in the UBG
Deuteronomy 25 in the UGV
Deuteronomy 25 in the UGV2
Deuteronomy 25 in the UGV3
Deuteronomy 25 in the VBL
Deuteronomy 25 in the VDCC
Deuteronomy 25 in the YALU
Deuteronomy 25 in the YAPE
Deuteronomy 25 in the YBVTP
Deuteronomy 25 in the ZBP