Deuteronomy 3 (BOGWICC)

1 Kenaka tinakhota ndi kumayenda mokwera mtunda ndi njira yolowera ku Basani. Ndipo Ogi mfumu ya ku Basani ndi gulu lake lonse lankhondo anakumana nafe ndipo anamenyana nafe ku Ederi. 2 Yehova anati kwa ine, “Usachite naye mantha pakuti ndamupereka mʼmanja mwako pamodzi ndi gulu lake lonse lankhondo ndi dziko lake lomwe. Ndipo uchite kwa iye zimene unachita Sihoni mfumu ya Aamori, amene ankalamulira ku Hesiboni.” 3 Choncho Yehova Mulungu wathu anapereka mʼmanja mwathu Ogi mfumu ya ku Basani ndi gulu lake lonse lankhondo. Tinawakantha onsewo osasiya ndi mmodzi yemwe. 4 Pa nthawi imeneyo tinatenga mizinda yake yonse. Pa mizinda 60, panalibe ndi umodzi womwe umene sitinawalande, mʼdera lonse la ufumu wa Ogi ku Basani chimene ndi chigawo cha Arigobu. 5 Mizinda yonseyi inali yotetezedwa ndi malinga ataliatali wokhala ndi zitseko ndi zitsulo, komabe panali midzi ina yambiri imene inalibe malinga. 6 Tinawawonongeratu monga momwe tinachitira Sihoni, mfumu ya ku Hesiboni. Tinawononga mzinda uliwonse, amayi, amuna ndi ana omwe. 7 Koma tinafunkha ziweto ndi katundu wawo yense. 8 Choncho pa nthawi imeneyi tinalanda kwa mafumu awiri Aamori, dera la kummawa kwa Yorodani, kuyambira ku khwawa la Arinoni mpaka ku Phiri la Herimoni. 9 (Asidoni amatcha Herimoni kuti Siriyoni, pamene Aamori amalitcha Seniri). 10 Tinalanda mizinda yonse ya ku mapiri, ku Giliyadi, Basani mpaka ku Saleka ndi Ederi, mizinda ya mu ufumu wa Ogi wa ku Basani. 11 (Ogi, mfumu ya ku Basani, anali yekhayo amene anatsala mwa mtundu wa anthu ataliatali a Chirefai. Bedi lake linali lachitsulo ndipo lalitali kuposa mamita anayi. Mulifupi mwake munali mamita awiri. Bedilo likanalipo ku Raba kwa Aamori). 12 Dziko limene tinalanda nthawi imeneyo, ndinapatsa fuko la Rubeni ndi fuko la Gadi dera la kumpoto kwa Aroeri cha mʼmphepete mwa khwawa la Arinoni kuphatikizapo theka la dziko lamapiri la Giliyadi ndi mizinda yake. 13 Theka la fuko la Manase ndinalipatsa dziko lonse lotsala la Giliyadi ndi Basani yense yemwe ndi dera la ufumu wa Ogi. (Chigawo chonse cha Arigobu mu Basani chinkadziwika kuti ndi dziko la Arefai. 14 Yairi, mdzukulu wa Manase, anatenga chigawo chonse cha Arigobu mpaka ku malire a Agesuri ndi Amaakati. Anatcha chigawochi dzina lake, moti mpaka lero Basani amatchedwa Havoti Yairi). 15 Ndipo ndinapereka Giliyadi kwa Makiri. 16 Koma kwa fuko la Rubeni ndi fuko la Gadi ndinapereka chigawo chochokera ku Giliyadi kutsetsereka mpaka ku khwawa la Arinoni (pakati pa khwawalo ndiye panali malire) ndi kupitirira mpaka ku mtsinje wa Yaboki umene ndi malire Aamoni. 17 Malire ake a chakumadzulo anali Yorodani ku Araba, kuchokera ku Kinereti mpaka ku Nyanja ya Araba (Nyanja ya Mchere), mʼmunsi mwa matsitso a Pisiga. 18 Ndinakulamulirani nthawi imene ija kuti, “Yehova Mulungu wanu wakupatsani dziko ili kuti likhale lanu. Koma amuna amphamvu onse ali ndi zida zankhondo, awoloke kutsogolera abale anu Aisraeli. 19 Koma akazi anu, ana anu ndi ziweto zanu (ndikudziwa kuti muli ndi ziweto zambiri) zikhoza kumakhalabe mʼmizinda imene ndakupatsani, 20 mpaka Yehova atapereka mpumulo kwa abale anu, nawonso atatenga dziko limene Yehova Mulungu wanu akuwapatsa patsidya pa Yorodani, monga wachitira ndi inu. Kenaka, aliyense wa inu akhoza kudzabwerera ku dziko limene ndinakupatsani.” 21 Nthawi imeneyo ndinamulamula Yoswa kuti, “Waona wekha ndi maso ako zonse zimene Yehova Mulungu wako anachitira mafumu awiriwa. Yehova adzachita zomwezo ndi mafumu ena onse kumene mukupitako. 22 Musawaope chifukwa Yehova Mulungu mwini adzakumenyerani nkhondo.” 23 Nthawi imeneyo ndinachonderera Yehova kuti, 24 “Ambuye Mulungu, mwayamba tsopano kuonetsa mtumiki wanu ukulu wanu ndi dzanja lanu lamphamvu. Ndi mulungu uti ali kumwamba kapena pa dziko lapansi amene angachite ntchito zozizwitsa zimene mumachita? 25 Mundilole ndipite ndi kukaona dziko labwinolo kutsidya kwa Yorodani dziko la mapiri abwinowo ndi Lebanoni.” 26 Koma chifukwa cha inu, Yehova anakwiya nane osandimvera. Yehova anati, “Basi pakwana, usayankhulenso ndi ine zimenezi. 27 Pita pamwamba pa phiri la Pisiga ndipo uyangʼane kumadzulo, kumpoto, kummwera ndi kummawa. Ulione dzikolo ndi maso ako pakuti suwoloka Yorodaniyu. 28 Koma langiza Yoswa ndipo umulimbikitse ndi kumupatsa mphamvu pakuti adzatsogolera anthu awa kuwoloka ndipo adzawathandiza kuti atenge dziko limene ulioneli.” 29 Ndipo tinakhala mʼchigwa pafupi ndi Beti-Peori.

In Other Versions

Deuteronomy 3 in the ANGEFD

Deuteronomy 3 in the ANTPNG2D

Deuteronomy 3 in the AS21

Deuteronomy 3 in the BAGH

Deuteronomy 3 in the BBPNG

Deuteronomy 3 in the BBT1E

Deuteronomy 3 in the BDS

Deuteronomy 3 in the BEV

Deuteronomy 3 in the BHAD

Deuteronomy 3 in the BIB

Deuteronomy 3 in the BLPT

Deuteronomy 3 in the BNT

Deuteronomy 3 in the BNTABOOT

Deuteronomy 3 in the BNTLV

Deuteronomy 3 in the BOATCB

Deuteronomy 3 in the BOATCB2

Deuteronomy 3 in the BOBCV

Deuteronomy 3 in the BOCNT

Deuteronomy 3 in the BOECS

Deuteronomy 3 in the BOHCB

Deuteronomy 3 in the BOHCV

Deuteronomy 3 in the BOHLNT

Deuteronomy 3 in the BOHNTLTAL

Deuteronomy 3 in the BOICB

Deuteronomy 3 in the BOILNTAP

Deuteronomy 3 in the BOITCV

Deuteronomy 3 in the BOKCV

Deuteronomy 3 in the BOKCV2

Deuteronomy 3 in the BOKHWOG

Deuteronomy 3 in the BOKSSV

Deuteronomy 3 in the BOLCB

Deuteronomy 3 in the BOLCB2

Deuteronomy 3 in the BOMCV

Deuteronomy 3 in the BONAV

Deuteronomy 3 in the BONCB

Deuteronomy 3 in the BONLT

Deuteronomy 3 in the BONUT2

Deuteronomy 3 in the BOPLNT

Deuteronomy 3 in the BOSCB

Deuteronomy 3 in the BOSNC

Deuteronomy 3 in the BOTLNT

Deuteronomy 3 in the BOVCB

Deuteronomy 3 in the BOYCB

Deuteronomy 3 in the BPBB

Deuteronomy 3 in the BPH

Deuteronomy 3 in the BSB

Deuteronomy 3 in the CCB

Deuteronomy 3 in the CUV

Deuteronomy 3 in the CUVS

Deuteronomy 3 in the DBT

Deuteronomy 3 in the DGDNT

Deuteronomy 3 in the DHNT

Deuteronomy 3 in the DNT

Deuteronomy 3 in the ELBE

Deuteronomy 3 in the EMTV

Deuteronomy 3 in the ESV

Deuteronomy 3 in the FBV

Deuteronomy 3 in the FEB

Deuteronomy 3 in the GGMNT

Deuteronomy 3 in the GNT

Deuteronomy 3 in the HARY

Deuteronomy 3 in the HNT

Deuteronomy 3 in the IRVA

Deuteronomy 3 in the IRVB

Deuteronomy 3 in the IRVG

Deuteronomy 3 in the IRVH

Deuteronomy 3 in the IRVK

Deuteronomy 3 in the IRVM

Deuteronomy 3 in the IRVM2

Deuteronomy 3 in the IRVO

Deuteronomy 3 in the IRVP

Deuteronomy 3 in the IRVT

Deuteronomy 3 in the IRVT2

Deuteronomy 3 in the IRVU

Deuteronomy 3 in the ISVN

Deuteronomy 3 in the JSNT

Deuteronomy 3 in the KAPI

Deuteronomy 3 in the KBT1ETNIK

Deuteronomy 3 in the KBV

Deuteronomy 3 in the KJV

Deuteronomy 3 in the KNFD

Deuteronomy 3 in the LBA

Deuteronomy 3 in the LBLA

Deuteronomy 3 in the LNT

Deuteronomy 3 in the LSV

Deuteronomy 3 in the MAAL

Deuteronomy 3 in the MBV

Deuteronomy 3 in the MBV2

Deuteronomy 3 in the MHNT

Deuteronomy 3 in the MKNFD

Deuteronomy 3 in the MNG

Deuteronomy 3 in the MNT

Deuteronomy 3 in the MNT2

Deuteronomy 3 in the MRS1T

Deuteronomy 3 in the NAA

Deuteronomy 3 in the NASB

Deuteronomy 3 in the NBLA

Deuteronomy 3 in the NBS

Deuteronomy 3 in the NBVTP

Deuteronomy 3 in the NET2

Deuteronomy 3 in the NIV11

Deuteronomy 3 in the NNT

Deuteronomy 3 in the NNT2

Deuteronomy 3 in the NNT3

Deuteronomy 3 in the PDDPT

Deuteronomy 3 in the PFNT

Deuteronomy 3 in the RMNT

Deuteronomy 3 in the SBIAS

Deuteronomy 3 in the SBIBS

Deuteronomy 3 in the SBIBS2

Deuteronomy 3 in the SBICS

Deuteronomy 3 in the SBIDS

Deuteronomy 3 in the SBIGS

Deuteronomy 3 in the SBIHS

Deuteronomy 3 in the SBIIS

Deuteronomy 3 in the SBIIS2

Deuteronomy 3 in the SBIIS3

Deuteronomy 3 in the SBIKS

Deuteronomy 3 in the SBIKS2

Deuteronomy 3 in the SBIMS

Deuteronomy 3 in the SBIOS

Deuteronomy 3 in the SBIPS

Deuteronomy 3 in the SBISS

Deuteronomy 3 in the SBITS

Deuteronomy 3 in the SBITS2

Deuteronomy 3 in the SBITS3

Deuteronomy 3 in the SBITS4

Deuteronomy 3 in the SBIUS

Deuteronomy 3 in the SBIVS

Deuteronomy 3 in the SBT

Deuteronomy 3 in the SBT1E

Deuteronomy 3 in the SCHL

Deuteronomy 3 in the SNT

Deuteronomy 3 in the SUSU

Deuteronomy 3 in the SUSU2

Deuteronomy 3 in the SYNO

Deuteronomy 3 in the TBIAOTANT

Deuteronomy 3 in the TBT1E

Deuteronomy 3 in the TBT1E2

Deuteronomy 3 in the TFTIP

Deuteronomy 3 in the TFTU

Deuteronomy 3 in the TGNTATF3T

Deuteronomy 3 in the THAI

Deuteronomy 3 in the TNFD

Deuteronomy 3 in the TNT

Deuteronomy 3 in the TNTIK

Deuteronomy 3 in the TNTIL

Deuteronomy 3 in the TNTIN

Deuteronomy 3 in the TNTIP

Deuteronomy 3 in the TNTIZ

Deuteronomy 3 in the TOMA

Deuteronomy 3 in the TTENT

Deuteronomy 3 in the UBG

Deuteronomy 3 in the UGV

Deuteronomy 3 in the UGV2

Deuteronomy 3 in the UGV3

Deuteronomy 3 in the VBL

Deuteronomy 3 in the VDCC

Deuteronomy 3 in the YALU

Deuteronomy 3 in the YAPE

Deuteronomy 3 in the YBVTP

Deuteronomy 3 in the ZBP