Exodus 33 (BOGWICC)

1 Ndipo Yehova anati, “Chokani pa malo ano, iwe ndi anthu amene unawatulutsa mʼdziko la Igupto. Pitani ku dziko limene ine ndinalonjeza ndi lumbiro kwa Abrahamu, Isake ndi Yakobo kuti, ‘Ine ndidzalipereka kwa zidzukulu zanu.’ 2 Ndipo ndidzatumiza mngelo patsogolo panu kuthamangitsa Akanaani, Aamori, Ahiti, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi. 3 Pitani ku dziko loyenda mkaka ndi uchi. Koma ine sindidzapita nanu, chifukwa anthu inu ndinu nkhutukumve ndipo nditha kukuwonongani mʼnjiramo.” 4 Anthu atamva mawu owopsawa, anayamba kulira ndipo palibe anavala zodzikometsera. 5 Pakuti Yehova anali atanena kwa Mose kuti, “Awuze Aisraeli kuti, ‘Inu ndinu nkhutukumve.’ Ngati ine ndipita ndi inu kwa kanthawi, nditha kukuwonongani. Tsopano vulani zodzikometsera zanu ndipo ine ndidzaganiza choti ndichite nanu.” 6 Kotero Aisraeli anavula zodzikometsera zawo pa phiri la Horebu. 7 Tsono Mose ankatenga tenti ndi kukayimanga kunja kwa msasa chapatalipo, ndipo ankayitcha “tenti ya msonkhano.” Aliyense wofuna kukafunsa kanthu kwa Yehova amapita ku tenti ya msonkhano kunja kwa msasa. 8 Ndipo nthawi ina iliyonse imene Mose amapita ku tenti anthu onse amanyamuka ndi kuyimirira pa makomo amatenti awo, kumuyangʼana Mose mpaka atalowa mu tentimo. 9 Mose akamalowa mu tenti, chipilala cha mtambo chimatsika ndi kukhala pa khomo pamene Yehova amayankhula ndi Mose. 10 Nthawi zonse anthu akaona chipilala cha mtambo chitayima pa khomo la tentiyo amayimirira ndi kupembedza, aliyense ali pa khomo la tenti yake. 11 Yehova amayankhula ndi Mose maso ndi maso ngati mmene munthu amayankhulira ndi bwenzi lake. Kenaka Mose amabwerera ku msasa koma womuthandiza wake, Yoswa, mwana wa Nuni samachoka pa tentiyo. 12 Mose anati kwa Yehova, “Inu mwakhala mukundiwuza kuti, ‘Tsogolera anthu awa,’ koma simunandiwuze amene mudzamutuma kuti apite pamodzi nane. Inu mwanena kuti, ‘Ndikukudziwa bwino kwambiri ndipo wapeza chisomo pamaso panga.’ 13 Ngati mwakondwera nane ndiphunzitseni njira zanu kuti ndikudziweni ndi kupitiriza kupeza chisomo pamaso panu. Kumbukirani kuti mtundu uwu ndi anthu anu.” 14 Yehova anayankha kuti, “Ine ndemwe ndidzapita pamodzi ndi iwe, ndipo ndidzakupatsa mpumulo.” 15 Kenaka Mose anati kwa Yehova, “Ngati inu simupita nafe, musatitumize kuti tipite, kutichotsa pano. 16 Kodi wina adzadziwa bwanji kuti inu mwandikomera mtima pamodzi ndi anthu awa ngati simupita nafe? Kodi nʼchiyani chomwe chidzatisiyanitse pakati pa anthu onse amene ali pa dziko lapansi?” 17 Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Ine ndidzachita zimene iwe wandipempha chifukwa Ine ndikukondwera nawe, ndikukudziwa bwino lomwe.” 18 Kenaka Mose anati, “Tsopano ndionetseni ulemerero wanu.” 19 Ndipo Yehova anati, “Ine ndidzakuonetsa ulemerero wanga wonse ndipo ndidzatchula dzina langa lakuti Yehova pamaso pako. Ine ndidzachitira chifundo amene ndikufuna kumuchitira chifundo ndipo ndidzakomera mtima amene ndikufuna kumukomera mtima.” 20 Iye anati, “Koma iwe sungaone nkhope yanga, pakuti palibe munthu amene amaona Ine nakhala ndi moyo.” 21 Ndipo Yehova anati, “Pali malo pafupi ndi ine pomwe ungathe kuyima pa thanthwe. 22 Pamene ulemerero wanga udutsa, ndidzakuyika mʼphanga la thanthwe ndi kukuphimba ndi dzanja langa mpaka nditadutsa. 23 Kenaka ine ndidzachotsa dzanja langa ndipo iwe udzaona msana wanga, koma nkhope yanga sidzaoneka.”

In Other Versions

Exodus 33 in the ANGEFD

Exodus 33 in the ANTPNG2D

Exodus 33 in the AS21

Exodus 33 in the BAGH

Exodus 33 in the BBPNG

Exodus 33 in the BBT1E

Exodus 33 in the BDS

Exodus 33 in the BEV

Exodus 33 in the BHAD

Exodus 33 in the BIB

Exodus 33 in the BLPT

Exodus 33 in the BNT

Exodus 33 in the BNTABOOT

Exodus 33 in the BNTLV

Exodus 33 in the BOATCB

Exodus 33 in the BOATCB2

Exodus 33 in the BOBCV

Exodus 33 in the BOCNT

Exodus 33 in the BOECS

Exodus 33 in the BOHCB

Exodus 33 in the BOHCV

Exodus 33 in the BOHLNT

Exodus 33 in the BOHNTLTAL

Exodus 33 in the BOICB

Exodus 33 in the BOILNTAP

Exodus 33 in the BOITCV

Exodus 33 in the BOKCV

Exodus 33 in the BOKCV2

Exodus 33 in the BOKHWOG

Exodus 33 in the BOKSSV

Exodus 33 in the BOLCB

Exodus 33 in the BOLCB2

Exodus 33 in the BOMCV

Exodus 33 in the BONAV

Exodus 33 in the BONCB

Exodus 33 in the BONLT

Exodus 33 in the BONUT2

Exodus 33 in the BOPLNT

Exodus 33 in the BOSCB

Exodus 33 in the BOSNC

Exodus 33 in the BOTLNT

Exodus 33 in the BOVCB

Exodus 33 in the BOYCB

Exodus 33 in the BPBB

Exodus 33 in the BPH

Exodus 33 in the BSB

Exodus 33 in the CCB

Exodus 33 in the CUV

Exodus 33 in the CUVS

Exodus 33 in the DBT

Exodus 33 in the DGDNT

Exodus 33 in the DHNT

Exodus 33 in the DNT

Exodus 33 in the ELBE

Exodus 33 in the EMTV

Exodus 33 in the ESV

Exodus 33 in the FBV

Exodus 33 in the FEB

Exodus 33 in the GGMNT

Exodus 33 in the GNT

Exodus 33 in the HARY

Exodus 33 in the HNT

Exodus 33 in the IRVA

Exodus 33 in the IRVB

Exodus 33 in the IRVG

Exodus 33 in the IRVH

Exodus 33 in the IRVK

Exodus 33 in the IRVM

Exodus 33 in the IRVM2

Exodus 33 in the IRVO

Exodus 33 in the IRVP

Exodus 33 in the IRVT

Exodus 33 in the IRVT2

Exodus 33 in the IRVU

Exodus 33 in the ISVN

Exodus 33 in the JSNT

Exodus 33 in the KAPI

Exodus 33 in the KBT1ETNIK

Exodus 33 in the KBV

Exodus 33 in the KJV

Exodus 33 in the KNFD

Exodus 33 in the LBA

Exodus 33 in the LBLA

Exodus 33 in the LNT

Exodus 33 in the LSV

Exodus 33 in the MAAL

Exodus 33 in the MBV

Exodus 33 in the MBV2

Exodus 33 in the MHNT

Exodus 33 in the MKNFD

Exodus 33 in the MNG

Exodus 33 in the MNT

Exodus 33 in the MNT2

Exodus 33 in the MRS1T

Exodus 33 in the NAA

Exodus 33 in the NASB

Exodus 33 in the NBLA

Exodus 33 in the NBS

Exodus 33 in the NBVTP

Exodus 33 in the NET2

Exodus 33 in the NIV11

Exodus 33 in the NNT

Exodus 33 in the NNT2

Exodus 33 in the NNT3

Exodus 33 in the PDDPT

Exodus 33 in the PFNT

Exodus 33 in the RMNT

Exodus 33 in the SBIAS

Exodus 33 in the SBIBS

Exodus 33 in the SBIBS2

Exodus 33 in the SBICS

Exodus 33 in the SBIDS

Exodus 33 in the SBIGS

Exodus 33 in the SBIHS

Exodus 33 in the SBIIS

Exodus 33 in the SBIIS2

Exodus 33 in the SBIIS3

Exodus 33 in the SBIKS

Exodus 33 in the SBIKS2

Exodus 33 in the SBIMS

Exodus 33 in the SBIOS

Exodus 33 in the SBIPS

Exodus 33 in the SBISS

Exodus 33 in the SBITS

Exodus 33 in the SBITS2

Exodus 33 in the SBITS3

Exodus 33 in the SBITS4

Exodus 33 in the SBIUS

Exodus 33 in the SBIVS

Exodus 33 in the SBT

Exodus 33 in the SBT1E

Exodus 33 in the SCHL

Exodus 33 in the SNT

Exodus 33 in the SUSU

Exodus 33 in the SUSU2

Exodus 33 in the SYNO

Exodus 33 in the TBIAOTANT

Exodus 33 in the TBT1E

Exodus 33 in the TBT1E2

Exodus 33 in the TFTIP

Exodus 33 in the TFTU

Exodus 33 in the TGNTATF3T

Exodus 33 in the THAI

Exodus 33 in the TNFD

Exodus 33 in the TNT

Exodus 33 in the TNTIK

Exodus 33 in the TNTIL

Exodus 33 in the TNTIN

Exodus 33 in the TNTIP

Exodus 33 in the TNTIZ

Exodus 33 in the TOMA

Exodus 33 in the TTENT

Exodus 33 in the UBG

Exodus 33 in the UGV

Exodus 33 in the UGV2

Exodus 33 in the UGV3

Exodus 33 in the VBL

Exodus 33 in the VDCC

Exodus 33 in the YALU

Exodus 33 in the YAPE

Exodus 33 in the YBVTP

Exodus 33 in the ZBP