Ezekiel 47 (BOGWICC)

1 Munthuyo anabwerera nane ku chipata cha Nyumba ya Mulungu. Ndinaona madzi akutuluka kunsi kwa chiwundo cha Nyumba ya Mulungu chakummawa; poti Nyumba ya Mulungu inayangʼana kummawa. Madziwo ankachokera kunsi kwa mbali yakummwera ya Nyumba ya Mulungu; kummwera kwa guwa lansembe. 2 Ananditulutsira pa chipata chakumpoto ndipo anazungulira nane panja mpaka ku chipata chakunja choyangʼana kummawa. Ndipo ndinaona madzi akutuluka chakummwera kwa chipatacho. 3 Munthuyo anapita chakummawa ali ndi chingwe choyezera mʼdzanja lake. Iye anayeza mamita 500, ndipo pambuyo pake analowa nane mʼmadziwo amene ankalekeza mʼkakolo. 4 Anayezanso mamita 500 ndipo analowa nane mʼmadzi amene amalekeza mʼmawondo. Iye anayezanso mamita 500 ndipo analowa nane mʼmadzi amene amalekeza mʼchiwuno. 5 Munthuyo anayezanso mamita 500, ndipo madziwo anasanduka mtsinje woti sindikanatha kuwoloka, pakuti madziwo anakwera, ndipo anali ozama ofunika kusambira pofuna kuwoloka. 6 Munthuyo anandifunsa kuti: “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuziona zimenezi?”Kenaka anabwerera nane ku gombe la mtsinjewo. 7 Nditafika pa gombepo, ndinaona mitengo yambiri ku mbali iliyonse ya mtsinjewo. 8 Tsono munthuyo anandiwuza kuti, “Madziwa akupita ku chigawo chakummawa ndi kutsikira ku chigwa cha Araba. Kenaka akathira mʼNyanja Yakufa, ndipo akakalowa mʼnyanjayo, madzi a nyanjayo adzasanduka okoma. 9 Kulikonse kumene mtsinjewo ukuyenda cholengedwa chilichonse chidzakhala ndi moyo. Nsombanso zidzakhala zambiri. Paja madzi amenewa amapita kumeneko kuti akakometse madzi ena. Choncho kulikonse kumene madziwa akuyenda chilichonse chidzakhala ndi moyo. 10 Asodzi adzayima mʼmbali mwa Nyanja Yakufa. Pakuti kuchokera ku Eni-Gedi mpaka ku Eni Egilaimu kudzakhala malo oponyako makoka. Kudzakhala nsomba zamitundumitundu, monga nsomba za ku Nyanja Yayikulu. 11 Koma mathawale ake ndi maiwe ake sadzakhala ndi madzi abwino; adzakhala ndi madzi a mchere. 12 Mʼmbali zonse za mtsinje mudzamera mitengo ya zipatso zakudya za mtundu uliwonse. Masamba ake sadzafota kapena kulephera kubereka zipatso. Izidzabereka mwezi uliwonse, chifukwa madzi ake adzakhala ochokera ku Nyumba ya Mulungu. Zipatso zake anthu azidzadya ndipo masamba ake azidzachitira mankhwala.” 13 Ambuye Yehova akuti, “Nawa malire amene mudzatsate powagawira dziko mafuko khumi ndi awiri a Israeli aja. Yosefe adzalandire zigawo ziwiri. 14 Mudzawagawire dzikolo mofanana. Paja ndinalumbira kwa makolo anu kuti dzikoli lidzakhala lanulanu. 15 “Malire a dzikolo adzakhala motere: Mbali ya kumpoto adzachokera ku Nyanja Yayikulu kutsata msewu wa ku Hetiloni mpaka ku chipata cha Hamoti ndi kupitirira ku Zedadi, 16 Berota ndi Sibraimu (mizinda imene ili pakati pa malire a Damasiko ndi Hamati mpaka kukafika ku Hazeri Hatikoni mzinda umene uli mʼmalire mwa Haurani. 17 Motero malire akumpoto adzachokera ku nyanja mpaka ku mzinda wa Hazari-Enoni, mʼmalire akumpoto a Damasiko ndi chakumpoto kwa malire a Hamati. Awa adzakhala malire a kumpoto. 18 Mbali ya kummawa malire adzayenda pakati pa Haurani ndi Damasiko, mbali ya ku Yorodani pakati pa Giliyadi ndi dziko la Israeli, ku nyanja ya kummawa mpaka ku mzinda wa Tamara. Awa adzakhala malire akummawa. 19 Mbali yakummwera malire adzayenda kuchokera ku dziwe la mzinda wa Tamara mpaka ku madzi a ku Meriba Kadesi. Kenaka ndi kutsata chigwa cha ku Igupto mpaka ku Nyanja Yayikulu. Awa adzakhala malire akummwera. 20 Mbali ya kumadzulo, malire adzakhala Nyanja Yayikulu mpaka pa malo oyangʼanana ndi Lebo Hamati. Awa adzakhala malire akumadzulo.” 21 “Mugawane dziko limeneli pakati panu potsata mafuko a Israeli. 22 Muligawe kuti likhale cholowa chanu ndiponso cholowa cha alendo amene akukhala pakati panu, nakhala ndi ana pakati panu. Inu muwatenge monga mbadwa za mu Israeli. Adzapatsidwe cholowa chawo pamodzi ndi inu pakati pa mafuko a Israeli. 23 Mu fuko lililonse kumene mlendoyo akukhala mumupatse cholowa chake.” Ndikutero Ine Ambuye Yehova.

In Other Versions

Ezekiel 47 in the ANGEFD

Ezekiel 47 in the ANTPNG2D

Ezekiel 47 in the AS21

Ezekiel 47 in the BAGH

Ezekiel 47 in the BBPNG

Ezekiel 47 in the BBT1E

Ezekiel 47 in the BDS

Ezekiel 47 in the BEV

Ezekiel 47 in the BHAD

Ezekiel 47 in the BIB

Ezekiel 47 in the BLPT

Ezekiel 47 in the BNT

Ezekiel 47 in the BNTABOOT

Ezekiel 47 in the BNTLV

Ezekiel 47 in the BOATCB

Ezekiel 47 in the BOATCB2

Ezekiel 47 in the BOBCV

Ezekiel 47 in the BOCNT

Ezekiel 47 in the BOECS

Ezekiel 47 in the BOHCB

Ezekiel 47 in the BOHCV

Ezekiel 47 in the BOHLNT

Ezekiel 47 in the BOHNTLTAL

Ezekiel 47 in the BOICB

Ezekiel 47 in the BOILNTAP

Ezekiel 47 in the BOITCV

Ezekiel 47 in the BOKCV

Ezekiel 47 in the BOKCV2

Ezekiel 47 in the BOKHWOG

Ezekiel 47 in the BOKSSV

Ezekiel 47 in the BOLCB

Ezekiel 47 in the BOLCB2

Ezekiel 47 in the BOMCV

Ezekiel 47 in the BONAV

Ezekiel 47 in the BONCB

Ezekiel 47 in the BONLT

Ezekiel 47 in the BONUT2

Ezekiel 47 in the BOPLNT

Ezekiel 47 in the BOSCB

Ezekiel 47 in the BOSNC

Ezekiel 47 in the BOTLNT

Ezekiel 47 in the BOVCB

Ezekiel 47 in the BOYCB

Ezekiel 47 in the BPBB

Ezekiel 47 in the BPH

Ezekiel 47 in the BSB

Ezekiel 47 in the CCB

Ezekiel 47 in the CUV

Ezekiel 47 in the CUVS

Ezekiel 47 in the DBT

Ezekiel 47 in the DGDNT

Ezekiel 47 in the DHNT

Ezekiel 47 in the DNT

Ezekiel 47 in the ELBE

Ezekiel 47 in the EMTV

Ezekiel 47 in the ESV

Ezekiel 47 in the FBV

Ezekiel 47 in the FEB

Ezekiel 47 in the GGMNT

Ezekiel 47 in the GNT

Ezekiel 47 in the HARY

Ezekiel 47 in the HNT

Ezekiel 47 in the IRVA

Ezekiel 47 in the IRVB

Ezekiel 47 in the IRVG

Ezekiel 47 in the IRVH

Ezekiel 47 in the IRVK

Ezekiel 47 in the IRVM

Ezekiel 47 in the IRVM2

Ezekiel 47 in the IRVO

Ezekiel 47 in the IRVP

Ezekiel 47 in the IRVT

Ezekiel 47 in the IRVT2

Ezekiel 47 in the IRVU

Ezekiel 47 in the ISVN

Ezekiel 47 in the JSNT

Ezekiel 47 in the KAPI

Ezekiel 47 in the KBT1ETNIK

Ezekiel 47 in the KBV

Ezekiel 47 in the KJV

Ezekiel 47 in the KNFD

Ezekiel 47 in the LBA

Ezekiel 47 in the LBLA

Ezekiel 47 in the LNT

Ezekiel 47 in the LSV

Ezekiel 47 in the MAAL

Ezekiel 47 in the MBV

Ezekiel 47 in the MBV2

Ezekiel 47 in the MHNT

Ezekiel 47 in the MKNFD

Ezekiel 47 in the MNG

Ezekiel 47 in the MNT

Ezekiel 47 in the MNT2

Ezekiel 47 in the MRS1T

Ezekiel 47 in the NAA

Ezekiel 47 in the NASB

Ezekiel 47 in the NBLA

Ezekiel 47 in the NBS

Ezekiel 47 in the NBVTP

Ezekiel 47 in the NET2

Ezekiel 47 in the NIV11

Ezekiel 47 in the NNT

Ezekiel 47 in the NNT2

Ezekiel 47 in the NNT3

Ezekiel 47 in the PDDPT

Ezekiel 47 in the PFNT

Ezekiel 47 in the RMNT

Ezekiel 47 in the SBIAS

Ezekiel 47 in the SBIBS

Ezekiel 47 in the SBIBS2

Ezekiel 47 in the SBICS

Ezekiel 47 in the SBIDS

Ezekiel 47 in the SBIGS

Ezekiel 47 in the SBIHS

Ezekiel 47 in the SBIIS

Ezekiel 47 in the SBIIS2

Ezekiel 47 in the SBIIS3

Ezekiel 47 in the SBIKS

Ezekiel 47 in the SBIKS2

Ezekiel 47 in the SBIMS

Ezekiel 47 in the SBIOS

Ezekiel 47 in the SBIPS

Ezekiel 47 in the SBISS

Ezekiel 47 in the SBITS

Ezekiel 47 in the SBITS2

Ezekiel 47 in the SBITS3

Ezekiel 47 in the SBITS4

Ezekiel 47 in the SBIUS

Ezekiel 47 in the SBIVS

Ezekiel 47 in the SBT

Ezekiel 47 in the SBT1E

Ezekiel 47 in the SCHL

Ezekiel 47 in the SNT

Ezekiel 47 in the SUSU

Ezekiel 47 in the SUSU2

Ezekiel 47 in the SYNO

Ezekiel 47 in the TBIAOTANT

Ezekiel 47 in the TBT1E

Ezekiel 47 in the TBT1E2

Ezekiel 47 in the TFTIP

Ezekiel 47 in the TFTU

Ezekiel 47 in the TGNTATF3T

Ezekiel 47 in the THAI

Ezekiel 47 in the TNFD

Ezekiel 47 in the TNT

Ezekiel 47 in the TNTIK

Ezekiel 47 in the TNTIL

Ezekiel 47 in the TNTIN

Ezekiel 47 in the TNTIP

Ezekiel 47 in the TNTIZ

Ezekiel 47 in the TOMA

Ezekiel 47 in the TTENT

Ezekiel 47 in the UBG

Ezekiel 47 in the UGV

Ezekiel 47 in the UGV2

Ezekiel 47 in the UGV3

Ezekiel 47 in the VBL

Ezekiel 47 in the VDCC

Ezekiel 47 in the YALU

Ezekiel 47 in the YAPE

Ezekiel 47 in the YBVTP

Ezekiel 47 in the ZBP