Ezekiel 5 (BOGWICC)
1 Tsiku lina Yehova anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, tsopano tenga lupanga lakuthwa ndipo uligwiritse ntchito ngati lumo lometera. Umete tsitsi ndi ndevu zako. Kenaka utenge sikelo ndipo ugawe tsitsilo patatu. 2 Kuzinga mzinda kuja kukatha, chimodzi cha zigawo zitatu za tsitsilo uchitenthe pakati pa mzinda. Chigawo chachiwiri uchiduledule ndi lupanga, poyenda muzungulire mzinda wonsewo. Chigawo chachitatu uchimwazire ku mphepo, ndidzachitsata nditasolola lupanga. 3 Koma utengeko tsitsi pangʼono, ulimange mu mpindiro wa mkanjo wako. 4 Pa tsitsi limeneli utapepo lina, uliponye pa moto ndi kulitentha. Moto udzayambira pamenepo mpaka ku nyumba yonse ya Israeli.” 5 Ambuye Yehova akunena kuti, “Uyu ndi Yerusalemu amene ndamuyika pakati pa mitundu ya anthu, ndipo mayiko onse amuzungulira. 6 Koma anthu a Yerusalemu aphwanya malamulo anga pochita zoyipa kuposa anthu a mitundu ina. Iwo anandipandukira kupambana anthu ena amene awazungulira. Iwo anakana malamulo anga ndipo sanasunge malangizo anga. 7 “Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti: Popeza mwakhala osamvera kupambana anthu a mitundu ina amene akuzungulirani, popeza simunatsate malamulo anga kapena kusunga malangizo anga, mʼmalo mwake mwakhala mukutsata makhalidwe a anthu a mitundu ina amene akuzungulirani. 8 “Tsono Ambuye Yehova akuti: Ine mwini ndikutsutsana nawe, Yerusalemu, choncho Ine ndidzakulangani. Ine ndidzakulangani anthu a mitundu ina akuona. 9 Chifukwa cha ntchito zanu zonyansa ndidzakulangani ndi chilango chimene sindinakulangeni nacho nʼkale lomwe ndipo sindidzakulangani ndi chofanana nacho mʼtsogolomo. 10 Tsono pakati panu makolo adzadya ana awo, ndipo ana adzadya makolo awo. Ndidzakulanga ndipo otsala onse ndidzawabalalitsa ku mphepo zonse zinayi. 11 Ndithu, pali Ine, akutero Ambuye Yehova Wamoyo, pakuti mwayipitsa Nyumba yanga ndi mafano ano oyipa ndi miyambo yanu yonyansa, Inenso ndidzakulangani. Sindidzakulekererani kapena kukumverani chisoni. 12 Chimodzi mwa zigawo zitatu za anthu ako chidzafa ndi mliri, kapena chidzawonongeka ndi njala; chigawo china chidzaphedwa ndi lupanga kunja kwa mzinda, ndipo chigawo china ndidzachibalalitsira ku mphepo zonse zinayi pochita kuchithamangitsa. 13 “Ndi mmene udzachitire mkwiyo wanga. Ndikadzatsiriza kuwalanga, pamenepo mtima wanga udzakhala pansi. Adzadziwa kuti Ine Yehova ndinawayankhula mwa nsanje ndikadzawalanga. 14 “Ndidzakusandutsa iwe bwinja ndi chinthu chonyozeka pakati pa anthu a mitundu ina amene akuzungulira, ndi kwa onse odutsapo 15 Udzakhala chinthu chonyozeka ndi chonyogodoledwa. Udzakhala chenjezo ndi chinthu choopsa kwa anthu a mitundu ina amene akuzungulira ndikadzakulanga mokwiya ndi mwaukali ndi kugamula mlandu wako mokwiya. Ine Yehova ndayankhula. 16 Pamene ndidzakulasa ndi njala yolasa ngati mivi yoopsa ndi yosakaza ndidzatero nʼcholinga choti ndikuwonongeni. Ndidzagwetsa njalayo pa iwe mowirikiza pochepetsa chakudya chako cha tsiku ndi tsiku. 17 Ndidzatumiza njala ndi zirombo za kuthengo, ndipo zidzakulanda ana ako. Mliri ndi kuphana zidzakhala pakati pako, ndipo ndidzakubweretsera nkhondo. Ine Yehova ndayankhula.”
In Other Versions
Ezekiel 5 in the ANGEFD
Ezekiel 5 in the ANTPNG2D
Ezekiel 5 in the AS21
Ezekiel 5 in the BAGH
Ezekiel 5 in the BBPNG
Ezekiel 5 in the BBT1E
Ezekiel 5 in the BDS
Ezekiel 5 in the BEV
Ezekiel 5 in the BHAD
Ezekiel 5 in the BIB
Ezekiel 5 in the BLPT
Ezekiel 5 in the BNT
Ezekiel 5 in the BNTABOOT
Ezekiel 5 in the BNTLV
Ezekiel 5 in the BOATCB
Ezekiel 5 in the BOATCB2
Ezekiel 5 in the BOBCV
Ezekiel 5 in the BOCNT
Ezekiel 5 in the BOECS
Ezekiel 5 in the BOHCB
Ezekiel 5 in the BOHCV
Ezekiel 5 in the BOHLNT
Ezekiel 5 in the BOHNTLTAL
Ezekiel 5 in the BOICB
Ezekiel 5 in the BOILNTAP
Ezekiel 5 in the BOITCV
Ezekiel 5 in the BOKCV
Ezekiel 5 in the BOKCV2
Ezekiel 5 in the BOKHWOG
Ezekiel 5 in the BOKSSV
Ezekiel 5 in the BOLCB
Ezekiel 5 in the BOLCB2
Ezekiel 5 in the BOMCV
Ezekiel 5 in the BONAV
Ezekiel 5 in the BONCB
Ezekiel 5 in the BONLT
Ezekiel 5 in the BONUT2
Ezekiel 5 in the BOPLNT
Ezekiel 5 in the BOSCB
Ezekiel 5 in the BOSNC
Ezekiel 5 in the BOTLNT
Ezekiel 5 in the BOVCB
Ezekiel 5 in the BOYCB
Ezekiel 5 in the BPBB
Ezekiel 5 in the BPH
Ezekiel 5 in the BSB
Ezekiel 5 in the CCB
Ezekiel 5 in the CUV
Ezekiel 5 in the CUVS
Ezekiel 5 in the DBT
Ezekiel 5 in the DGDNT
Ezekiel 5 in the DHNT
Ezekiel 5 in the DNT
Ezekiel 5 in the ELBE
Ezekiel 5 in the EMTV
Ezekiel 5 in the ESV
Ezekiel 5 in the FBV
Ezekiel 5 in the FEB
Ezekiel 5 in the GGMNT
Ezekiel 5 in the GNT
Ezekiel 5 in the HARY
Ezekiel 5 in the HNT
Ezekiel 5 in the IRVA
Ezekiel 5 in the IRVB
Ezekiel 5 in the IRVG
Ezekiel 5 in the IRVH
Ezekiel 5 in the IRVK
Ezekiel 5 in the IRVM
Ezekiel 5 in the IRVM2
Ezekiel 5 in the IRVO
Ezekiel 5 in the IRVP
Ezekiel 5 in the IRVT
Ezekiel 5 in the IRVT2
Ezekiel 5 in the IRVU
Ezekiel 5 in the ISVN
Ezekiel 5 in the JSNT
Ezekiel 5 in the KAPI
Ezekiel 5 in the KBT1ETNIK
Ezekiel 5 in the KBV
Ezekiel 5 in the KJV
Ezekiel 5 in the KNFD
Ezekiel 5 in the LBA
Ezekiel 5 in the LBLA
Ezekiel 5 in the LNT
Ezekiel 5 in the LSV
Ezekiel 5 in the MAAL
Ezekiel 5 in the MBV
Ezekiel 5 in the MBV2
Ezekiel 5 in the MHNT
Ezekiel 5 in the MKNFD
Ezekiel 5 in the MNG
Ezekiel 5 in the MNT
Ezekiel 5 in the MNT2
Ezekiel 5 in the MRS1T
Ezekiel 5 in the NAA
Ezekiel 5 in the NASB
Ezekiel 5 in the NBLA
Ezekiel 5 in the NBS
Ezekiel 5 in the NBVTP
Ezekiel 5 in the NET2
Ezekiel 5 in the NIV11
Ezekiel 5 in the NNT
Ezekiel 5 in the NNT2
Ezekiel 5 in the NNT3
Ezekiel 5 in the PDDPT
Ezekiel 5 in the PFNT
Ezekiel 5 in the RMNT
Ezekiel 5 in the SBIAS
Ezekiel 5 in the SBIBS
Ezekiel 5 in the SBIBS2
Ezekiel 5 in the SBICS
Ezekiel 5 in the SBIDS
Ezekiel 5 in the SBIGS
Ezekiel 5 in the SBIHS
Ezekiel 5 in the SBIIS
Ezekiel 5 in the SBIIS2
Ezekiel 5 in the SBIIS3
Ezekiel 5 in the SBIKS
Ezekiel 5 in the SBIKS2
Ezekiel 5 in the SBIMS
Ezekiel 5 in the SBIOS
Ezekiel 5 in the SBIPS
Ezekiel 5 in the SBISS
Ezekiel 5 in the SBITS
Ezekiel 5 in the SBITS2
Ezekiel 5 in the SBITS3
Ezekiel 5 in the SBITS4
Ezekiel 5 in the SBIUS
Ezekiel 5 in the SBIVS
Ezekiel 5 in the SBT
Ezekiel 5 in the SBT1E
Ezekiel 5 in the SCHL
Ezekiel 5 in the SNT
Ezekiel 5 in the SUSU
Ezekiel 5 in the SUSU2
Ezekiel 5 in the SYNO
Ezekiel 5 in the TBIAOTANT
Ezekiel 5 in the TBT1E
Ezekiel 5 in the TBT1E2
Ezekiel 5 in the TFTIP
Ezekiel 5 in the TFTU
Ezekiel 5 in the TGNTATF3T
Ezekiel 5 in the THAI
Ezekiel 5 in the TNFD
Ezekiel 5 in the TNT
Ezekiel 5 in the TNTIK
Ezekiel 5 in the TNTIL
Ezekiel 5 in the TNTIN
Ezekiel 5 in the TNTIP
Ezekiel 5 in the TNTIZ
Ezekiel 5 in the TOMA
Ezekiel 5 in the TTENT
Ezekiel 5 in the UBG
Ezekiel 5 in the UGV
Ezekiel 5 in the UGV2
Ezekiel 5 in the UGV3
Ezekiel 5 in the VBL
Ezekiel 5 in the VDCC
Ezekiel 5 in the YALU
Ezekiel 5 in the YAPE
Ezekiel 5 in the YBVTP
Ezekiel 5 in the ZBP