Ezra 3 (BOGWICC)
1 Utafika mwezi wa chisanu ndi chiwiri Aisraeli atakhala kale mʼmidzi yawo, anthu anasonkhana ku Yerusalemu ndi cholinga chimodzi. 2 Kenaka Yesuwa mwana wa Yozadaki ndi ansembe anzake pamodzi ndi Zerubabeli mwana wa Sealatieli ndi abale ake anayamba kumanga guwa lansembe la Mulungu wa Israeli. Anatero pofuna kuti aziperekapo nsembe zopsereza monga analembera mʼbuku la Mose, munthu wa Mulungu uja. 3 Ndi mantha ndi mantha chifukwa cha anthu a mʼmayikomo, iwo anamanga guwalo pa maziko ake akale, ndipo anapereka nsembe zopsereza kwa Mulungu pa guwapo mmawa ndi madzulo. 4 Ankasunga tsiku la chikondwerero cha misasa monga momwe zinalembedwera. Ankaperekanso nsembe za tsiku ndi tsiku monga mwa chiwerengero chake potsata mwambo wake wa tsiku ndi tsiku monga zinalembedwa. 5 Pambuyo pake, ankapereka nsembe zopsereza, nsembe zopereka pa nthawi ya mwezi watsopano ndi za pa masiku onse a chikondwerero oyikidwa kutamandira Yehova, kudzanso nsembe zaufulu zopereka kwa Yehova. 6 Kuyambira pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri, iwo anayambanso kupereka nsembe zopsereza kwa Yehova, ngakhale kuti maziko a Nyumba ya Yehova anali asanamangidwe. 7 Ndipo anapereka ndalama kwa amisiri a miyala ndi kwa amisiri a matabwa, ndi chakudya, chakumwa ndi mafuta kwa anthu a ku Sidoni ndi a ku Turo, kuti abweretse mitengo ya mkungudza pa nyanja kuchokera ku Lebanoni mpaka ku Yopa. Zonsezi anachita malinga ndi chilolezo chimene analandira kuchokera kwa Koresi, mfumu ya Peresiya. 8 Tsono mu chaka chachiwiri atabwera ku Yerusalemu, ku malo akale a Nyumba ya Yehova, mwezi wachiwiri Zerubabeli mwana wa Sealatieli, Yesuwa mwana wa Yozadaki pamodzi ndi abale awo onse, ansembe, Alevi ndi onse amene anabwera ku Yerusalemu kuchokera ku ukapolo, anayamba kugwira ntchito. Iwo anasankha Alevi a zaka zoyambira makumi awiri kuti aziyangʼanira ntchito ya kumanga Nyumba ya Yehova. 9 Yesuwa ndi ana ake aamuna kudzanso abale ake, Kadimieli ndi ana ake (ana a Yuda) onse pamodzi anasenza udindo woyangʼanira antchito ku Nyumba ya Mulungu, kuphatikizanso ana a Henadadi komanso Alevi, ana awo ndi abale awo. 10 Amisiri omanga nyumba atamanga maziko a Nyumba ya Yehova, ansembe anabwera akuyimba malipenga, atavala zovala zaunsembe. Ndipo Alevi, zidzukulu za Asafu, anadza akuyimba matambolini ndi kutenga udindo wawo wotamanda Yehova, potsata malangizo a Davide mfumu ya Aisraeli. 11 Iwo ankayimba motamanda ndi mothokoza Yehova nyimbo iyi:“Yehova ndi wabwino;chikondi chake pa Israeli ndi chamuyaya.”Ndipo anthu onse ankafuwula kwambiri kumutamanda Yehova, chifukwa maziko a Nyumba ya Yehova anali kumangidwa. 12 Koma ambiri mwa ansembe, Alevi ndiponso atsogoleri amabanja, akuluakulu amene anaona Nyumba ya Yehova yakale, analira mokweza pamene anaona maziko a nyumbayi akumangidwa. Komanso ena ambiri ankafuwula mosangalala. 13 Choncho panalibe amene ankatha kusiyanitsa liwu lofuwula mokondwerera ndi liwu la anthu olira, chifukwa anthuwo ankafuwula kwambiri. Ndipo liwu lofuwulalo limamveka kutali.
In Other Versions
Ezra 3 in the ANGEFD
Ezra 3 in the ANTPNG2D
Ezra 3 in the AS21
Ezra 3 in the BAGH
Ezra 3 in the BBPNG
Ezra 3 in the BBT1E
Ezra 3 in the BDS
Ezra 3 in the BEV
Ezra 3 in the BHAD
Ezra 3 in the BIB
Ezra 3 in the BLPT
Ezra 3 in the BNT
Ezra 3 in the BNTABOOT
Ezra 3 in the BNTLV
Ezra 3 in the BOATCB
Ezra 3 in the BOATCB2
Ezra 3 in the BOBCV
Ezra 3 in the BOCNT
Ezra 3 in the BOECS
Ezra 3 in the BOHCB
Ezra 3 in the BOHCV
Ezra 3 in the BOHLNT
Ezra 3 in the BOHNTLTAL
Ezra 3 in the BOICB
Ezra 3 in the BOILNTAP
Ezra 3 in the BOITCV
Ezra 3 in the BOKCV
Ezra 3 in the BOKCV2
Ezra 3 in the BOKHWOG
Ezra 3 in the BOKSSV
Ezra 3 in the BOLCB
Ezra 3 in the BOLCB2
Ezra 3 in the BOMCV
Ezra 3 in the BONAV
Ezra 3 in the BONCB
Ezra 3 in the BONLT
Ezra 3 in the BONUT2
Ezra 3 in the BOPLNT
Ezra 3 in the BOSCB
Ezra 3 in the BOSNC
Ezra 3 in the BOTLNT
Ezra 3 in the BOVCB
Ezra 3 in the BOYCB
Ezra 3 in the BPBB
Ezra 3 in the BPH
Ezra 3 in the BSB
Ezra 3 in the CCB
Ezra 3 in the CUV
Ezra 3 in the CUVS
Ezra 3 in the DBT
Ezra 3 in the DGDNT
Ezra 3 in the DHNT
Ezra 3 in the DNT
Ezra 3 in the ELBE
Ezra 3 in the EMTV
Ezra 3 in the ESV
Ezra 3 in the FBV
Ezra 3 in the FEB
Ezra 3 in the GGMNT
Ezra 3 in the GNT
Ezra 3 in the HARY
Ezra 3 in the HNT
Ezra 3 in the IRVA
Ezra 3 in the IRVB
Ezra 3 in the IRVG
Ezra 3 in the IRVH
Ezra 3 in the IRVK
Ezra 3 in the IRVM
Ezra 3 in the IRVM2
Ezra 3 in the IRVO
Ezra 3 in the IRVP
Ezra 3 in the IRVT
Ezra 3 in the IRVT2
Ezra 3 in the IRVU
Ezra 3 in the ISVN
Ezra 3 in the JSNT
Ezra 3 in the KAPI
Ezra 3 in the KBT1ETNIK
Ezra 3 in the KBV
Ezra 3 in the KJV
Ezra 3 in the KNFD
Ezra 3 in the LBA
Ezra 3 in the LBLA
Ezra 3 in the LNT
Ezra 3 in the LSV
Ezra 3 in the MAAL
Ezra 3 in the MBV
Ezra 3 in the MBV2
Ezra 3 in the MHNT
Ezra 3 in the MKNFD
Ezra 3 in the MNG
Ezra 3 in the MNT
Ezra 3 in the MNT2
Ezra 3 in the MRS1T
Ezra 3 in the NAA
Ezra 3 in the NASB
Ezra 3 in the NBLA
Ezra 3 in the NBS
Ezra 3 in the NBVTP
Ezra 3 in the NET2
Ezra 3 in the NIV11
Ezra 3 in the NNT
Ezra 3 in the NNT2
Ezra 3 in the NNT3
Ezra 3 in the PDDPT
Ezra 3 in the PFNT
Ezra 3 in the RMNT
Ezra 3 in the SBIAS
Ezra 3 in the SBIBS
Ezra 3 in the SBIBS2
Ezra 3 in the SBICS
Ezra 3 in the SBIDS
Ezra 3 in the SBIGS
Ezra 3 in the SBIHS
Ezra 3 in the SBIIS
Ezra 3 in the SBIIS2
Ezra 3 in the SBIIS3
Ezra 3 in the SBIKS
Ezra 3 in the SBIKS2
Ezra 3 in the SBIMS
Ezra 3 in the SBIOS
Ezra 3 in the SBIPS
Ezra 3 in the SBISS
Ezra 3 in the SBITS
Ezra 3 in the SBITS2
Ezra 3 in the SBITS3
Ezra 3 in the SBITS4
Ezra 3 in the SBIUS
Ezra 3 in the SBIVS
Ezra 3 in the SBT
Ezra 3 in the SBT1E
Ezra 3 in the SCHL
Ezra 3 in the SNT
Ezra 3 in the SUSU
Ezra 3 in the SUSU2
Ezra 3 in the SYNO
Ezra 3 in the TBIAOTANT
Ezra 3 in the TBT1E
Ezra 3 in the TBT1E2
Ezra 3 in the TFTIP
Ezra 3 in the TFTU
Ezra 3 in the TGNTATF3T
Ezra 3 in the THAI
Ezra 3 in the TNFD
Ezra 3 in the TNT
Ezra 3 in the TNTIK
Ezra 3 in the TNTIL
Ezra 3 in the TNTIN
Ezra 3 in the TNTIP
Ezra 3 in the TNTIZ
Ezra 3 in the TOMA
Ezra 3 in the TTENT
Ezra 3 in the UBG
Ezra 3 in the UGV
Ezra 3 in the UGV2
Ezra 3 in the UGV3
Ezra 3 in the VBL
Ezra 3 in the VDCC
Ezra 3 in the YALU
Ezra 3 in the YAPE
Ezra 3 in the YBVTP
Ezra 3 in the ZBP