Ezra 5 (BOGWICC)

1 Nthawi imeneyo aneneri Hagai ndi Zekariya, mwana wa Ido, ankayankhula kwa Ayuda okhala mʼdziko la Yuda ndi mu Yerusalemu mʼdzina la Mulungu wa Israeli, amene anali nawo. 2 Pambuyo pake Zerubabeli mwana wa Sealatieli ndi Yesuwa mwana wa Yozadaki ananyamuka nakayambanso kumanga Nyumba ya Mulungu mu Yerusalemu. Ndipo aneneri a Mulungu anali nawo pamodzi, kuwathandiza. 3 Pa nthawi imeneyo Tatenai, bwanamkubwa wa chigawo cha patsidya pa Yufurate pamodzi ndi Setari-Bozenai ndi anzawo anapita kwa iwo ndi kukawafunsa kuti, “Anakulolani ndani kuti mumangenso Nyumba imeneyi ndi kutsiriza khoma lake?” 4 Anawafunsanso kuti, “Kodi anthu amene akumanga nyumbayi mayina awo ndani?” 5 Koma Mulungu wawo amayangʼanira atsogoleri Ayuda, motero kuti anthu aja anaganiza kuti asawaletse kumanga Nyumbayo mpaka atalembera mfumu Dariyo kalata ndi kulandira yankho lake. 6 Iyi ndi kalata imene Tatenai bwanamkubwa wa dera la patsidya pa Yufurate, ndiponso Setari-Bozenai ndi anzake, akazembe amene anali mʼchigawo cha patsidya pa Yufurate, anatumiza kwa mfumu Dariyo 7 Analemba kalatayo motere:Kwa mfumu Dariyo:Mukhale ndi mtendere wonse. 8 Amfumu mudziwe kuti ife tinapita ku dziko la Yuda ku Nyumba ya Mulungu wamkulu. Nyumbayo ikumangidwa ndi miyala ikuluikulu ndipo akuyala matabwa pa makoma. Ntchitoyi ikugwiridwa mwachangu ndipo ikuyenda bwino kwambiri mwautsogoleri wawo. 9 Ndipo tinawafunsa atsogoleriwo kuti, “Anakulolezani kuti mumangenso Nyumbayi ndi kutsiriza makoma ake ndani?” 10 Tinawafunsanso mayina a atsogoleri awo, kuti tikalemba mayina atsogoleriwo tidzakudziwitseni kuti muwadziwe. 11 Yankho limene anatipatsa ndi ili: “Ife ndife atumiki a Mulungu wa kumwamba ndi wa dziko lapansi, ndipo tikumanganso Nyumba imene mfumu ina yamphamvu ya Israeli inamanga ndi kuyitsiriza zaka zambiri zapitazo. 12 Koma chifukwa chakuti makolo athu anakwiyitsa Mulungu wakumwamba, Iye anawapereka kwa Nebukadinezara Mkalideya, mfumu ya Babuloni, amene anawononga Nyumbayi ndi kutenga anthu onse kupita nawo ku ukapolo ku Babuloni. 13 “Komabe chaka choyamba cha Koresi, mfumu ya ku Babuloni, mfumu Koresiyo anapereka lamulo lakuti Nyumba ya Mulunguyi imangidwenso. 14 Ndipo ziwiya zagolide ndi zasiliva za ku Nyumba ya Mulungu zimene Nebukadinezara anazitenga mʼNyumba ya Mulungu ku Yerusalemu ndi kukaziyika mʼnyumba ya milungu ya ku Babuloni, anakazichotsa ku nyumba ya milungu ya ku Babuloniko ndi kuzipereka kwa Sesibazara, amene mfumu inamusankha kukhala bwanamkubwa. 15 Tsono mfumuyo inamuwuza kuti, ‘Tenga ziwiyazi ukaziyike mʼNyumba ya Mulungu ku Yerusalemu. Ndipo Nyumba ya Mulunguyo ikamangidwenso pa maziko ake akale.’ 16 “Choncho Sesibazarayo anabwera ndi kumanga maziko a Nyumba ya Mulunguyo mu Yerusalemu. Kuyambira tsiku limenelo mpaka lero yakhala ikumangidwa ndipo sinathebe.” 17 Nʼchifukwa chake ngati chingakukomereni amfumu, pachitike kafukufuku mʼnyumba yaufumu mosungira chuma ndi mabuku okhudza mbiri ya Babuloni kuti tione ngati mfumu Koresi inalamuladi za kumanganso Nyumba ya Mulungu mu Yerusalemu. Kenaka amfumu mutiwuze zomwe zikukondweretsani kuti mugamule pa nkhani imeneyi.

In Other Versions

Ezra 5 in the ANGEFD

Ezra 5 in the ANTPNG2D

Ezra 5 in the AS21

Ezra 5 in the BAGH

Ezra 5 in the BBPNG

Ezra 5 in the BBT1E

Ezra 5 in the BDS

Ezra 5 in the BEV

Ezra 5 in the BHAD

Ezra 5 in the BIB

Ezra 5 in the BLPT

Ezra 5 in the BNT

Ezra 5 in the BNTABOOT

Ezra 5 in the BNTLV

Ezra 5 in the BOATCB

Ezra 5 in the BOATCB2

Ezra 5 in the BOBCV

Ezra 5 in the BOCNT

Ezra 5 in the BOECS

Ezra 5 in the BOHCB

Ezra 5 in the BOHCV

Ezra 5 in the BOHLNT

Ezra 5 in the BOHNTLTAL

Ezra 5 in the BOICB

Ezra 5 in the BOILNTAP

Ezra 5 in the BOITCV

Ezra 5 in the BOKCV

Ezra 5 in the BOKCV2

Ezra 5 in the BOKHWOG

Ezra 5 in the BOKSSV

Ezra 5 in the BOLCB

Ezra 5 in the BOLCB2

Ezra 5 in the BOMCV

Ezra 5 in the BONAV

Ezra 5 in the BONCB

Ezra 5 in the BONLT

Ezra 5 in the BONUT2

Ezra 5 in the BOPLNT

Ezra 5 in the BOSCB

Ezra 5 in the BOSNC

Ezra 5 in the BOTLNT

Ezra 5 in the BOVCB

Ezra 5 in the BOYCB

Ezra 5 in the BPBB

Ezra 5 in the BPH

Ezra 5 in the BSB

Ezra 5 in the CCB

Ezra 5 in the CUV

Ezra 5 in the CUVS

Ezra 5 in the DBT

Ezra 5 in the DGDNT

Ezra 5 in the DHNT

Ezra 5 in the DNT

Ezra 5 in the ELBE

Ezra 5 in the EMTV

Ezra 5 in the ESV

Ezra 5 in the FBV

Ezra 5 in the FEB

Ezra 5 in the GGMNT

Ezra 5 in the GNT

Ezra 5 in the HARY

Ezra 5 in the HNT

Ezra 5 in the IRVA

Ezra 5 in the IRVB

Ezra 5 in the IRVG

Ezra 5 in the IRVH

Ezra 5 in the IRVK

Ezra 5 in the IRVM

Ezra 5 in the IRVM2

Ezra 5 in the IRVO

Ezra 5 in the IRVP

Ezra 5 in the IRVT

Ezra 5 in the IRVT2

Ezra 5 in the IRVU

Ezra 5 in the ISVN

Ezra 5 in the JSNT

Ezra 5 in the KAPI

Ezra 5 in the KBT1ETNIK

Ezra 5 in the KBV

Ezra 5 in the KJV

Ezra 5 in the KNFD

Ezra 5 in the LBA

Ezra 5 in the LBLA

Ezra 5 in the LNT

Ezra 5 in the LSV

Ezra 5 in the MAAL

Ezra 5 in the MBV

Ezra 5 in the MBV2

Ezra 5 in the MHNT

Ezra 5 in the MKNFD

Ezra 5 in the MNG

Ezra 5 in the MNT

Ezra 5 in the MNT2

Ezra 5 in the MRS1T

Ezra 5 in the NAA

Ezra 5 in the NASB

Ezra 5 in the NBLA

Ezra 5 in the NBS

Ezra 5 in the NBVTP

Ezra 5 in the NET2

Ezra 5 in the NIV11

Ezra 5 in the NNT

Ezra 5 in the NNT2

Ezra 5 in the NNT3

Ezra 5 in the PDDPT

Ezra 5 in the PFNT

Ezra 5 in the RMNT

Ezra 5 in the SBIAS

Ezra 5 in the SBIBS

Ezra 5 in the SBIBS2

Ezra 5 in the SBICS

Ezra 5 in the SBIDS

Ezra 5 in the SBIGS

Ezra 5 in the SBIHS

Ezra 5 in the SBIIS

Ezra 5 in the SBIIS2

Ezra 5 in the SBIIS3

Ezra 5 in the SBIKS

Ezra 5 in the SBIKS2

Ezra 5 in the SBIMS

Ezra 5 in the SBIOS

Ezra 5 in the SBIPS

Ezra 5 in the SBISS

Ezra 5 in the SBITS

Ezra 5 in the SBITS2

Ezra 5 in the SBITS3

Ezra 5 in the SBITS4

Ezra 5 in the SBIUS

Ezra 5 in the SBIVS

Ezra 5 in the SBT

Ezra 5 in the SBT1E

Ezra 5 in the SCHL

Ezra 5 in the SNT

Ezra 5 in the SUSU

Ezra 5 in the SUSU2

Ezra 5 in the SYNO

Ezra 5 in the TBIAOTANT

Ezra 5 in the TBT1E

Ezra 5 in the TBT1E2

Ezra 5 in the TFTIP

Ezra 5 in the TFTU

Ezra 5 in the TGNTATF3T

Ezra 5 in the THAI

Ezra 5 in the TNFD

Ezra 5 in the TNT

Ezra 5 in the TNTIK

Ezra 5 in the TNTIL

Ezra 5 in the TNTIN

Ezra 5 in the TNTIP

Ezra 5 in the TNTIZ

Ezra 5 in the TOMA

Ezra 5 in the TTENT

Ezra 5 in the UBG

Ezra 5 in the UGV

Ezra 5 in the UGV2

Ezra 5 in the UGV3

Ezra 5 in the VBL

Ezra 5 in the VDCC

Ezra 5 in the YALU

Ezra 5 in the YAPE

Ezra 5 in the YBVTP

Ezra 5 in the ZBP