Genesis 17 (BOGWICC)
1 Pamene Abramu anali ndi zaka 99, Yehova anamuonekera nati, “Ine ndine Mulungu Wamphamvuzonse. Ukhale munthu wochita zolungama nthawi zonse. 2 Ndipo Ine ndikulonjeza kuti ndidzakupatsa zidzukulu zambiri.” 3 Pomwepo Abramu anadziponya pansi ndipo Mulungu anati kwa iye, 4 “Pangano langa ndi iwe ndi ili: Udzakhala kholo la mitundu yambiri ya anthu. 5 Sudzatchedwanso Abramu; dzina lako lidzakhala Abrahamu, chifukwa ndakusandutsa kukhala kholo la mitundu yambiri ya anthu. 6 Ndidzakupatsa zidzukulu zambiri motero kuti mitundu yambiri ya anthu idzatuluka mwa iwe. Mafumunso adzatuluka mwa iwe. 7 Pangano langa ndi iwe pamodzi ndi zidzukulu za mibado ya mʼtsogolo lidzakhala la muyaya. Ndidzakhala Mulungu wako ndi Mulungu wa zidzukulu zako. 8 Dziko lonse la Kanaani, limene iwe ukukhala tsopano, ndalipereka kwa iwe ndi kwa zidzukulu zako kuti likhale chuma chanu mpaka muyaya. Ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wa zidzukulu zako.” 9 Kenaka Mulungu anati kwa Abrahamu, “Koma iwe pamodzi ndi zidzukulu zako zobwera pambuyo pako mʼmibado ya mʼtsogolomo, sungani pangano langali. 10 Iwe pamodzi ndi zidzukulu zako zobwera pambuyo pako muzisunga pangano ili loti mwamuna aliyense pakati panupa azichita mdulidwe. 11 Kuyambira tsopano muzichita mdulidwe ndipo ichi chidzakhala chizindikiro cha pangano langa ndi iwe. 12 Kuyambira tsopano mpaka mibado ya mʼtsogolomo mwana wamwamuna aliyense pakati panu amene wakwana masiku asanu ndi atatu ayenera kuchita mdulidwe. Awa ndi ana obadwa mʼbanja lako, kapena akapolo ochita kugula ndi ndalama, mlendo osakhala wa mʼmbumba yako. 13 Achite mdulidwe ndithu mwana wamwamuna aliyense, mbadwa ngakhale kapolo wochita kugula ndi ndalama, ndipo ichi chidzakhala chizindikiro pa thupi lanu cha pangano langa lamuyaya. 14 Mwamuna aliyense amene adzakhala wosachita mdulidwe adzachotsedwa pakati pa anthu ake chifukwa sanasunge pangano langa.” 15 Mulungu anatinso kwa Abrahamu, “Sarai mkazi wako, sudzamutchanso Sarai; dzina lake lidzakhala Sara. 16 Ndidzamudalitsa ndipo adzakubalira mwana wamwamuna. Ndidzamudalitsa kuti akhale mayi wa mitundu ya anthu; mafumu a anthuwo adzachokera mwa iye.” 17 Abrahamu anadzigwetsa pansi pamaso pa Yehova, Iye anaseka nati, “Kodi munthu wa zaka 100 nʼkubala mwana? Kodi Sara adzabereka mwana pa msinkhu wa zaka makumi asanu ndi anayi?” 18 Ndipo Abrahamu anati kwa Mulungu, “Bwanji mumudalitse Ismaeli.” 19 Koma Mulungu anati, “Ayi, koma mkazi wako Sara adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha Isake. Ndidzasunga pangano langa losatha ndi iyeyu komanso ndi zidzukulu zobwera pambuyo pake. 20 Koma za Ismaeli, ndamva. Ndidzamudalitsadi, ndipo adzakhala ndi zidzukulu zambiri. Iye adzakhala kholo la mafumu khumi ndi awiri ndipo mwa iye mudzatuluka mtundu waukulu wa anthu. 21 Koma ndidzasunga pangano langali ndi Isake amene Sara adzakubalira pofika nthawi ngati ino chaka chamawa.” 22 Atatha kuyankhula, Mulungu anamuchokera Abrahamu. 23 Tsono Abrahamu anachita mdulidwe mwana wake Ismaeli ndi onse amene anali mʼbanja lake, mbadwa ngakhale kapolo ochita kugula ndi ndalama, monga mmene Mulungu analamulira. 24 Abrahamu anali ndi zaka 99 pamene anachita mdulidwe, 25 ndipo mwana wake Ismaeli anali ndi zaka khumi ndi zitatu; 26 Onse, Abrahamu ndi mwana wake Ismaeli, anachita mdulidwe tsiku limodzi. 27 Aliyense wamwamuna wa pa banja pa Abrahamu, kuphatikizapo iwo amene anabadwira pa banja pomwepo kapena akapolo ogula ndi ndalama kwa alendo, anachita mdulidwe.
In Other Versions
Genesis 17 in the ANGEFD
Genesis 17 in the ANTPNG2D
Genesis 17 in the AS21
Genesis 17 in the BAGH
Genesis 17 in the BBPNG
Genesis 17 in the BBT1E
Genesis 17 in the BDS
Genesis 17 in the BEV
Genesis 17 in the BHAD
Genesis 17 in the BIB
Genesis 17 in the BLPT
Genesis 17 in the BNT
Genesis 17 in the BNTABOOT
Genesis 17 in the BNTLV
Genesis 17 in the BOATCB
Genesis 17 in the BOATCB2
Genesis 17 in the BOBCV
Genesis 17 in the BOCNT
Genesis 17 in the BOECS
Genesis 17 in the BOHCB
Genesis 17 in the BOHCV
Genesis 17 in the BOHLNT
Genesis 17 in the BOHNTLTAL
Genesis 17 in the BOICB
Genesis 17 in the BOILNTAP
Genesis 17 in the BOITCV
Genesis 17 in the BOKCV
Genesis 17 in the BOKCV2
Genesis 17 in the BOKHWOG
Genesis 17 in the BOKSSV
Genesis 17 in the BOLCB
Genesis 17 in the BOLCB2
Genesis 17 in the BOMCV
Genesis 17 in the BONAV
Genesis 17 in the BONCB
Genesis 17 in the BONLT
Genesis 17 in the BONUT2
Genesis 17 in the BOPLNT
Genesis 17 in the BOSCB
Genesis 17 in the BOSNC
Genesis 17 in the BOTLNT
Genesis 17 in the BOVCB
Genesis 17 in the BOYCB
Genesis 17 in the BPBB
Genesis 17 in the BPH
Genesis 17 in the BSB
Genesis 17 in the CCB
Genesis 17 in the CUV
Genesis 17 in the CUVS
Genesis 17 in the DBT
Genesis 17 in the DGDNT
Genesis 17 in the DHNT
Genesis 17 in the DNT
Genesis 17 in the ELBE
Genesis 17 in the EMTV
Genesis 17 in the ESV
Genesis 17 in the FBV
Genesis 17 in the FEB
Genesis 17 in the GGMNT
Genesis 17 in the GNT
Genesis 17 in the HARY
Genesis 17 in the HNT
Genesis 17 in the IRVA
Genesis 17 in the IRVB
Genesis 17 in the IRVG
Genesis 17 in the IRVH
Genesis 17 in the IRVK
Genesis 17 in the IRVM
Genesis 17 in the IRVM2
Genesis 17 in the IRVO
Genesis 17 in the IRVP
Genesis 17 in the IRVT
Genesis 17 in the IRVT2
Genesis 17 in the IRVU
Genesis 17 in the ISVN
Genesis 17 in the JSNT
Genesis 17 in the KAPI
Genesis 17 in the KBT1ETNIK
Genesis 17 in the KBV
Genesis 17 in the KJV
Genesis 17 in the KNFD
Genesis 17 in the LBA
Genesis 17 in the LBLA
Genesis 17 in the LNT
Genesis 17 in the LSV
Genesis 17 in the MAAL
Genesis 17 in the MBV
Genesis 17 in the MBV2
Genesis 17 in the MHNT
Genesis 17 in the MKNFD
Genesis 17 in the MNG
Genesis 17 in the MNT
Genesis 17 in the MNT2
Genesis 17 in the MRS1T
Genesis 17 in the NAA
Genesis 17 in the NASB
Genesis 17 in the NBLA
Genesis 17 in the NBS
Genesis 17 in the NBVTP
Genesis 17 in the NET2
Genesis 17 in the NIV11
Genesis 17 in the NNT
Genesis 17 in the NNT2
Genesis 17 in the NNT3
Genesis 17 in the PDDPT
Genesis 17 in the PFNT
Genesis 17 in the RMNT
Genesis 17 in the SBIAS
Genesis 17 in the SBIBS
Genesis 17 in the SBIBS2
Genesis 17 in the SBICS
Genesis 17 in the SBIDS
Genesis 17 in the SBIGS
Genesis 17 in the SBIHS
Genesis 17 in the SBIIS
Genesis 17 in the SBIIS2
Genesis 17 in the SBIIS3
Genesis 17 in the SBIKS
Genesis 17 in the SBIKS2
Genesis 17 in the SBIMS
Genesis 17 in the SBIOS
Genesis 17 in the SBIPS
Genesis 17 in the SBISS
Genesis 17 in the SBITS
Genesis 17 in the SBITS2
Genesis 17 in the SBITS3
Genesis 17 in the SBITS4
Genesis 17 in the SBIUS
Genesis 17 in the SBIVS
Genesis 17 in the SBT
Genesis 17 in the SBT1E
Genesis 17 in the SCHL
Genesis 17 in the SNT
Genesis 17 in the SUSU
Genesis 17 in the SUSU2
Genesis 17 in the SYNO
Genesis 17 in the TBIAOTANT
Genesis 17 in the TBT1E
Genesis 17 in the TBT1E2
Genesis 17 in the TFTIP
Genesis 17 in the TFTU
Genesis 17 in the TGNTATF3T
Genesis 17 in the THAI
Genesis 17 in the TNFD
Genesis 17 in the TNT
Genesis 17 in the TNTIK
Genesis 17 in the TNTIL
Genesis 17 in the TNTIN
Genesis 17 in the TNTIP
Genesis 17 in the TNTIZ
Genesis 17 in the TOMA
Genesis 17 in the TTENT
Genesis 17 in the UBG
Genesis 17 in the UGV
Genesis 17 in the UGV2
Genesis 17 in the UGV3
Genesis 17 in the VBL
Genesis 17 in the VDCC
Genesis 17 in the YALU
Genesis 17 in the YAPE
Genesis 17 in the YBVTP
Genesis 17 in the ZBP