Genesis 25 (BOGWICC)

1 Abrahamu anakwatira mkazi wina dzina lake Ketura. 2 Iyeyu anamubalira Zimurani, Yokisani, Medani, Midiyani, Isibaki ndi Suwa. 3 Yokisani anabereka Seba ndi Dedani ndipo zidzukulu za Dedani ndiwo Aasuri, Aletusi, ndi Aleumi. 4 Ana aamuna a Midiyani anali, Efai, Eferi, Hanoki, Abida ndi Elida. Onsewa anali zidzukulu za Ketura. 5 Abrahamu anasiyira Isake chilichonse anali nacho. 6 Koma pamene anali ndi moyo, Abrahamu anapereka mphatso kwa ana aakazi ake ena onse. Kenaka anawatumiza ku dziko la kummawa kuti akhale kutali ndi mwana wake Isake. 7 Abrahamu anakhala ndi moyo zaka 175. 8 Abrahamu anamwalira atakalamba kwambiri ndipo anakakhala ndi anthu a mtundu wake. 9 Ana ake, Isake ndi Ismaeli anamuyika mʼphanga la Makipela pafupi ndi Mamre, mʼmunda umene kale unali wa Efroni mwana wa Zohari Mhiti, 10 uwu ndi munda umene Abrahamu anagula kwa Ahiti. Kumeneko Abrahamu anakayikidwa pamodzi ndi mkazi wake Sara. 11 Atamwalira Abrahamu, Mulungu anadalitsa mwana wake Isake, amene ankakhala pafupi ndi Beeri-lahai-roi (chitsime cha Wamoyo Wondipenya). 12 Nazi zidzukulu za Ismaeli, mwana wa Abrahamu amene wantchito wa Sara, Hagara Mwigupto uja, anaberekera Abrahamu. 13 Awa ndi mayina a ana a Ismaeli monga mwa mndandanda wa mabadwidwe awo: Nebayoti ndiye anali mwana woyamba wa Ismaeli; kenaka Kedara, Adibeeli, Mibisamu, 14 Misima, Duma, Masa, 15 Hadadi, Tema, Yeturi, Nafisi ndi Kedema; 16 Amenewa ndi ana a Ismaeli ndi mayina awo monga mwa midzi ndi misasa yawo. Anali olamulira mafuko khumi ndi awiri. 17 Ismaeli anakhala ndi moyo zaka 137. Iye anamwalira ndipo anakakhala ndi anthu a mtundu wake. 18 Zidzukulu za Ismaeli zinkakhala mʼdera la pakati pa Havila ndi Suri, kummwera kwa Igupto, mukamapita cha ku Asuri. Choncho anakhala kummawa kwa abale awo. 19 Iyi ndi mbiri ya Isake mwana wa Abrahamu. Abrahamu anabereka Isake 20 ndipo Isake anali ndi zaka makumi anayi pamene anakwatira Rebeka mwana wa Betueli Mwaramu wa ku Padanaramu mlongo wa Labani Mwaramu. 21 Isake anapempherera mkazi wake kwa Yehova popeza iye anali wosabereka. Yehova anayankha pemphero lake ndipo mkazi wake Rebeka anatenga pathupi. 22 Koma pamene anawo amalimbana mʼmimba mwake, iye anati, “Bwanji zikundichitikira zoterezi?” Choncho anapita kukafunsa kwa Yehova. 23 Yehova anati kwa iye,“Udzabala mafuko awiri a anthu olimbana,ndipo magulu awiri a anthu ochokera mwa iwe adzasiyana;fuko limodzi lidzakhala la mphamvu kuposa linzake,ndipo wamkulu adzatumikira wamngʼono.” 24 Pamene nthawi inakwana yakuti abeleke, Rebeka anaberekadi mapasa. 25 Woyamba kubadwa anali wofiira, ndipo thupi lake lonse linali ngati chovala cha ubweya; choncho anamutcha Esau. 26 Kenaka mʼbale wake anabadwa atagwira chidendene cha Esau; choncho anamutcha Yakobo. Isake anali ndi zaka 60 pamene Rebeka anabereka mapasawa. 27 Anyamatawo anakula ndipo Esau anakhala katswiri wosaka, munthu wamʼthengo, pamene Yakobo anali munthu wofatsa, wokonda kukhala pa nyumba. 28 Isake ankakonda Esau chifukwa cha nyama za kutchire zomwe ankakonda kudya, koma Rebeka ankakonda Yakobo. 29 Tsiku lina pamene Yakobo ankaphika chakudya, Esau anabwera kuchokera kuthengo ali wolefuka ndi njala. 30 Iye anati kwa Yakobo, “Tandipatsako phala lofiiralo, ndimwe! Ndalefuka ndi njala.” (Nʼchifukwa chake amatchedwanso Edomu). 31 Yakobo anayankha, “Choyamba undigulitse ukulu wako.” 32 Esau anati, “Chabwino, ine ndatsala pangʼono kufa, ukulu undithandiza chiyani?” 33 Koma Yakobo anati, “Lumbira kwa ine choyamba.” Kotero Esau analumbiradi, ndipo anagulitsa ukulu wake kwa Yakobo. 34 Choncho Yakobo anamupatsa Esau buledi ndi phala lofiira lija. Iye anadya ndi kumwa, nanyamuka kumapita.Motero Esau anapeputsa ukulu wake wachisamba uja.

In Other Versions

Genesis 25 in the ANGEFD

Genesis 25 in the ANTPNG2D

Genesis 25 in the AS21

Genesis 25 in the BAGH

Genesis 25 in the BBPNG

Genesis 25 in the BBT1E

Genesis 25 in the BDS

Genesis 25 in the BEV

Genesis 25 in the BHAD

Genesis 25 in the BIB

Genesis 25 in the BLPT

Genesis 25 in the BNT

Genesis 25 in the BNTABOOT

Genesis 25 in the BNTLV

Genesis 25 in the BOATCB

Genesis 25 in the BOATCB2

Genesis 25 in the BOBCV

Genesis 25 in the BOCNT

Genesis 25 in the BOECS

Genesis 25 in the BOHCB

Genesis 25 in the BOHCV

Genesis 25 in the BOHLNT

Genesis 25 in the BOHNTLTAL

Genesis 25 in the BOICB

Genesis 25 in the BOILNTAP

Genesis 25 in the BOITCV

Genesis 25 in the BOKCV

Genesis 25 in the BOKCV2

Genesis 25 in the BOKHWOG

Genesis 25 in the BOKSSV

Genesis 25 in the BOLCB

Genesis 25 in the BOLCB2

Genesis 25 in the BOMCV

Genesis 25 in the BONAV

Genesis 25 in the BONCB

Genesis 25 in the BONLT

Genesis 25 in the BONUT2

Genesis 25 in the BOPLNT

Genesis 25 in the BOSCB

Genesis 25 in the BOSNC

Genesis 25 in the BOTLNT

Genesis 25 in the BOVCB

Genesis 25 in the BOYCB

Genesis 25 in the BPBB

Genesis 25 in the BPH

Genesis 25 in the BSB

Genesis 25 in the CCB

Genesis 25 in the CUV

Genesis 25 in the CUVS

Genesis 25 in the DBT

Genesis 25 in the DGDNT

Genesis 25 in the DHNT

Genesis 25 in the DNT

Genesis 25 in the ELBE

Genesis 25 in the EMTV

Genesis 25 in the ESV

Genesis 25 in the FBV

Genesis 25 in the FEB

Genesis 25 in the GGMNT

Genesis 25 in the GNT

Genesis 25 in the HARY

Genesis 25 in the HNT

Genesis 25 in the IRVA

Genesis 25 in the IRVB

Genesis 25 in the IRVG

Genesis 25 in the IRVH

Genesis 25 in the IRVK

Genesis 25 in the IRVM

Genesis 25 in the IRVM2

Genesis 25 in the IRVO

Genesis 25 in the IRVP

Genesis 25 in the IRVT

Genesis 25 in the IRVT2

Genesis 25 in the IRVU

Genesis 25 in the ISVN

Genesis 25 in the JSNT

Genesis 25 in the KAPI

Genesis 25 in the KBT1ETNIK

Genesis 25 in the KBV

Genesis 25 in the KJV

Genesis 25 in the KNFD

Genesis 25 in the LBA

Genesis 25 in the LBLA

Genesis 25 in the LNT

Genesis 25 in the LSV

Genesis 25 in the MAAL

Genesis 25 in the MBV

Genesis 25 in the MBV2

Genesis 25 in the MHNT

Genesis 25 in the MKNFD

Genesis 25 in the MNG

Genesis 25 in the MNT

Genesis 25 in the MNT2

Genesis 25 in the MRS1T

Genesis 25 in the NAA

Genesis 25 in the NASB

Genesis 25 in the NBLA

Genesis 25 in the NBS

Genesis 25 in the NBVTP

Genesis 25 in the NET2

Genesis 25 in the NIV11

Genesis 25 in the NNT

Genesis 25 in the NNT2

Genesis 25 in the NNT3

Genesis 25 in the PDDPT

Genesis 25 in the PFNT

Genesis 25 in the RMNT

Genesis 25 in the SBIAS

Genesis 25 in the SBIBS

Genesis 25 in the SBIBS2

Genesis 25 in the SBICS

Genesis 25 in the SBIDS

Genesis 25 in the SBIGS

Genesis 25 in the SBIHS

Genesis 25 in the SBIIS

Genesis 25 in the SBIIS2

Genesis 25 in the SBIIS3

Genesis 25 in the SBIKS

Genesis 25 in the SBIKS2

Genesis 25 in the SBIMS

Genesis 25 in the SBIOS

Genesis 25 in the SBIPS

Genesis 25 in the SBISS

Genesis 25 in the SBITS

Genesis 25 in the SBITS2

Genesis 25 in the SBITS3

Genesis 25 in the SBITS4

Genesis 25 in the SBIUS

Genesis 25 in the SBIVS

Genesis 25 in the SBT

Genesis 25 in the SBT1E

Genesis 25 in the SCHL

Genesis 25 in the SNT

Genesis 25 in the SUSU

Genesis 25 in the SUSU2

Genesis 25 in the SYNO

Genesis 25 in the TBIAOTANT

Genesis 25 in the TBT1E

Genesis 25 in the TBT1E2

Genesis 25 in the TFTIP

Genesis 25 in the TFTU

Genesis 25 in the TGNTATF3T

Genesis 25 in the THAI

Genesis 25 in the TNFD

Genesis 25 in the TNT

Genesis 25 in the TNTIK

Genesis 25 in the TNTIL

Genesis 25 in the TNTIN

Genesis 25 in the TNTIP

Genesis 25 in the TNTIZ

Genesis 25 in the TOMA

Genesis 25 in the TTENT

Genesis 25 in the UBG

Genesis 25 in the UGV

Genesis 25 in the UGV2

Genesis 25 in the UGV3

Genesis 25 in the VBL

Genesis 25 in the VDCC

Genesis 25 in the YALU

Genesis 25 in the YAPE

Genesis 25 in the YBVTP

Genesis 25 in the ZBP