Genesis 3 (BOGWICC)
1 Ndipo njoka inali yochenjera kuposa nyama yakuthengo iliyonse imene Yehova Mulungu anapanga. Njokayo inati kwa mkaziyo, “Kodi Mulungu ananenadi kuti, ‘Inu musadye zipatso za mtengo uliwonse mʼmundamu?’ ” 2 Mkaziyo anati kwa njokayo, “Tikhoza kudya zipatso za mʼmitengo ya mʼmundawu, 3 koma Mulungu anati, ‘Musadye zipatso za mu mtengo umene uli pakati pa munda, ndipo musadzawukhudze kuti mungadzafe.’ ” 4 “Ndithudi simudzafa,” inatero njokayo kwa mkaziyo. 5 “Pakuti Mulungu akudziwa kuti tsiku limene mudzadye zipatso za mu mtengowo, maso anu adzatsekuka, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wodziwa zabwino ndi zoyipa.” 6 Pamene mkaziyo anaona kuti mtengowo unali wabwino kudya ndi wokongola ndi kuti unali wopatsa nzeru, anatengako zipatso zake nadya. Zina anamupatsako mwamuna wake amene anali naye pomwepo ndipo naye anadyanso. 7 Kenaka maso awo anatsekuka, ndipo anazindikira kuti anali maliseche. Choncho anasoka masamba a mkuyu nadzipangira zovala. 8 Kenaka munthu uja ndi mkazi wake anamva mtswatswa wa Yehova Mulungu akuyendayenda mʼmundamo madzulo a tsikulo, ndipo iwo anabisala pamaso pa Yehova Mulungu pakati pa mitengo ya mʼmundamo. 9 Yehova Mulungu anayitana munthu uja kuti, “Uli kuti?” 10 Iye anayankha, “Ndinakumvani mʼmundamo, ndipo ndimaopa chifukwa ndinali maliseche; choncho ndinabisala.” 11 Ndipo anamufunsa, “Ndani anakuwuza kuti uli maliseche? Kodi wadya zipatso za mtengo umene ndinakulamulira kuti usadye?” 12 Koma munthu uja anati, “Mkazi amene munandipatsa kuti ndizikhala nayeyu anandipatsako chipatso cha mtengowo ndipo ndinadya.” 13 Tsono Yehova Mulungu anati kwa mkaziyo, “Wachitachi nʼchiyani?”Mkaziyo anati, “Njoka inandinamiza, ndipo ndinadya.” 14 Choncho Yehova Mulungu anati kwa njokayo, “Popeza wachita zimenezi,“Ndiwe wotembereredwa kuposa ziweto zonsendi nyama zakuthengo zonse.Udzayenda chafufumimbandipo udzadya fumbimasiku onse a moyo wako. 15 Ndipo ndidzayika chidanipakati pa iwe ndi mkaziyo,pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake;Iye adzaphwanya mutu wakondipo iwe udzaluma chidendene chake.” 16 Kwa mkaziyo Iye anati,“Ndidzachulukitsa ululu wako kwambiri pamene uli ndi pakati;ndipo udzamva ululu pa nthawi yako yobereka ana.Udzakhumba mwamuna wako,ndipo adzakulamulira.” 17 Ndipo kwa Adamu Mulungu anati, “Chifukwa wamvera mkazi wako ndipo wadya zipatso za mu mtengo umene ndinakulamulira kuti, ‘Usadye.’“Nthaka yatembereredwa chifukwa cha iwe,movutikira udzadya zochokera mʼnthakamomasiku onse a moyo wako. 18 Mʼnthakamo mudzamera minga ndi nthulandipo udzadya zomera zakuthengo. 19 Kuti upeze chakudya udzayenerakukhetsa thukuta,mpaka utabwerera ku nthakapakuti unachokera kumeneko;pakuti ndiwe fumbiku fumbi komweko udzabwerera.” 20 Munthu uja anatcha mkazi wake Hava, chifukwa iyeyu adzakhala mayi wa anthu onse amoyo. 21 Yehova Mulungu anapangira Adamu ndi mkazi wake zovala zachikopa ndipo anawaveka. 22 Ndipo Yehova Mulungu anati, “Tsopano munthu uyu wasanduka mmodzi wa ife, wodziwa zabwino ndi zoyipa. Iyeyu asaloledwe kutambasula dzanja ndi kutengako zipatso za mu mtengo wopatsa moyo uja kuti angakhale ndi moyo mpaka muyaya.” 23 Kotero Yehova Mulungu anatulutsa Adamu Mʼmunda wa Edeni kuti azilima mʼnthaka imene anachokera. 24 Atamuthamangitsa munthu uja, Yehova anayika Akerubi mbali ya kummawa kwa Munda wa Edeni ndi lupanga lamoto limene limayendayenda ponsepo, kuteteza njira ya ku mtengo wopatsa moyo.
In Other Versions
Genesis 3 in the ANGEFD
Genesis 3 in the ANTPNG2D
Genesis 3 in the AS21
Genesis 3 in the BAGH
Genesis 3 in the BBPNG
Genesis 3 in the BBT1E
Genesis 3 in the BDS
Genesis 3 in the BEV
Genesis 3 in the BHAD
Genesis 3 in the BIB
Genesis 3 in the BLPT
Genesis 3 in the BNT
Genesis 3 in the BNTABOOT
Genesis 3 in the BNTLV
Genesis 3 in the BOATCB
Genesis 3 in the BOATCB2
Genesis 3 in the BOBCV
Genesis 3 in the BOCNT
Genesis 3 in the BOECS
Genesis 3 in the BOHCB
Genesis 3 in the BOHCV
Genesis 3 in the BOHLNT
Genesis 3 in the BOHNTLTAL
Genesis 3 in the BOICB
Genesis 3 in the BOILNTAP
Genesis 3 in the BOITCV
Genesis 3 in the BOKCV
Genesis 3 in the BOKCV2
Genesis 3 in the BOKHWOG
Genesis 3 in the BOKSSV
Genesis 3 in the BOLCB
Genesis 3 in the BOLCB2
Genesis 3 in the BOMCV
Genesis 3 in the BONAV
Genesis 3 in the BONCB
Genesis 3 in the BONLT
Genesis 3 in the BONUT2
Genesis 3 in the BOPLNT
Genesis 3 in the BOSCB
Genesis 3 in the BOSNC
Genesis 3 in the BOTLNT
Genesis 3 in the BOVCB
Genesis 3 in the BOYCB
Genesis 3 in the BPBB
Genesis 3 in the BPH
Genesis 3 in the BSB
Genesis 3 in the CCB
Genesis 3 in the CUV
Genesis 3 in the CUVS
Genesis 3 in the DBT
Genesis 3 in the DGDNT
Genesis 3 in the DHNT
Genesis 3 in the DNT
Genesis 3 in the ELBE
Genesis 3 in the EMTV
Genesis 3 in the ESV
Genesis 3 in the FBV
Genesis 3 in the FEB
Genesis 3 in the GGMNT
Genesis 3 in the GNT
Genesis 3 in the HARY
Genesis 3 in the HNT
Genesis 3 in the IRVA
Genesis 3 in the IRVB
Genesis 3 in the IRVG
Genesis 3 in the IRVH
Genesis 3 in the IRVK
Genesis 3 in the IRVM
Genesis 3 in the IRVM2
Genesis 3 in the IRVO
Genesis 3 in the IRVP
Genesis 3 in the IRVT
Genesis 3 in the IRVT2
Genesis 3 in the IRVU
Genesis 3 in the ISVN
Genesis 3 in the JSNT
Genesis 3 in the KAPI
Genesis 3 in the KBT1ETNIK
Genesis 3 in the KBV
Genesis 3 in the KJV
Genesis 3 in the KNFD
Genesis 3 in the LBA
Genesis 3 in the LBLA
Genesis 3 in the LNT
Genesis 3 in the LSV
Genesis 3 in the MAAL
Genesis 3 in the MBV
Genesis 3 in the MBV2
Genesis 3 in the MHNT
Genesis 3 in the MKNFD
Genesis 3 in the MNG
Genesis 3 in the MNT
Genesis 3 in the MNT2
Genesis 3 in the MRS1T
Genesis 3 in the NAA
Genesis 3 in the NASB
Genesis 3 in the NBLA
Genesis 3 in the NBS
Genesis 3 in the NBVTP
Genesis 3 in the NET2
Genesis 3 in the NIV11
Genesis 3 in the NNT
Genesis 3 in the NNT2
Genesis 3 in the NNT3
Genesis 3 in the PDDPT
Genesis 3 in the PFNT
Genesis 3 in the RMNT
Genesis 3 in the SBIAS
Genesis 3 in the SBIBS
Genesis 3 in the SBIBS2
Genesis 3 in the SBICS
Genesis 3 in the SBIDS
Genesis 3 in the SBIGS
Genesis 3 in the SBIHS
Genesis 3 in the SBIIS
Genesis 3 in the SBIIS2
Genesis 3 in the SBIIS3
Genesis 3 in the SBIKS
Genesis 3 in the SBIKS2
Genesis 3 in the SBIMS
Genesis 3 in the SBIOS
Genesis 3 in the SBIPS
Genesis 3 in the SBISS
Genesis 3 in the SBITS
Genesis 3 in the SBITS2
Genesis 3 in the SBITS3
Genesis 3 in the SBITS4
Genesis 3 in the SBIUS
Genesis 3 in the SBIVS
Genesis 3 in the SBT
Genesis 3 in the SBT1E
Genesis 3 in the SCHL
Genesis 3 in the SNT
Genesis 3 in the SUSU
Genesis 3 in the SUSU2
Genesis 3 in the SYNO
Genesis 3 in the TBIAOTANT
Genesis 3 in the TBT1E
Genesis 3 in the TBT1E2
Genesis 3 in the TFTIP
Genesis 3 in the TFTU
Genesis 3 in the TGNTATF3T
Genesis 3 in the THAI
Genesis 3 in the TNFD
Genesis 3 in the TNT
Genesis 3 in the TNTIK
Genesis 3 in the TNTIL
Genesis 3 in the TNTIN
Genesis 3 in the TNTIP
Genesis 3 in the TNTIZ
Genesis 3 in the TOMA
Genesis 3 in the TTENT
Genesis 3 in the UBG
Genesis 3 in the UGV
Genesis 3 in the UGV2
Genesis 3 in the UGV3
Genesis 3 in the VBL
Genesis 3 in the VDCC
Genesis 3 in the YALU
Genesis 3 in the YAPE
Genesis 3 in the YBVTP
Genesis 3 in the ZBP