Genesis 4 (BOGWICC)
1 Adamu anagona malo amodzi ndi Hava mkazi wake ndipo mkaziyo anakhala woyembekezera nabala Kaini, ndipo anati, “Ndi thandizo la Yehova ndapeza mwana wamwamuna.” 2 Kenaka anabereka mʼbale wake Abele.Abele anali woweta nkhosa ndipo Kaini anali mlimi. 3 Patapita nthawi, Kaini anatenga zipatso za ku munda nakazipereka kwa Yehova monga nsembe. 4 Nayenso Abele anatenga ana ankhosa oyamba kubadwa pamodzi ndi mafuta ake nakazipereka ngati nsembe kwa Yehova. Yehova anakondwera ndi Abele ndi nsembe yake. 5 Koma sanakondwere ndi Kaini ndi nsembe yake. Kotero Kaini anakwiya kwambiri ndipo nkhope yake inagwa. 6 Choncho Yehova anati kwa Kaini, “Chifukwa chiyani wakwiya ndipo bwanji nkhope yako yagwa? 7 Ukanachita zabwino sindikanakulandira kodi? Koma tsopano wachita zoyipa ndipo tchimo likukudikira pa khomo pako, likufuna kukugwira; koma iwe uyenera kugonjetsa tchimolo.” 8 Tsiku lina Kaini anati kwa mʼbale wake Abele, “Tiye tipite ku munda.” Ndipo ali ku mundako, Kaini anawukira mʼbale wake namupha. 9 Ndipo Yehova anamufunsa Kaini kuti, “Ali kuti mʼbale wako Abele?”Iye anayankha kuti, “Sindikudziwa. Kodi ine ndine wosunga mʼbale wanga?” 10 Yehova anati, “Kodi wachita chiyani? Tamvera! Magazi a mʼbale wako akulirira kwa Ine kuchokera mʼnthaka. 11 Ndipo tsopano ndiwe wotembereredwa ndipo wachotsedwa mʼdziko limene nthaka yake inatsekula pakamwa pake kulandira magazi a mʼbale wako amene unakhetsa. 12 Udzalima munda koma nthakayo sidzakupatsanso zokolola zake. Udzakhala wosakhazikika; womangoyendayenda pa dziko lapansi.” 13 Kaini anati kwa Yehova, “Chilango changa ndi chachikulu kuposera mphamvu zanga. 14 Lero mukundipirikitsa pa dziko ndi pamaso panu; ndidzakhala wosakhazikika, woyendayenda, ndipo aliyense amene adzandipeze adzandipha.” 15 Koma Yehova anamuwuza kuti, “Sizidzatero ayi; aliyense amene adzaphe Kaini adzalangidwa ndi kulipiritsidwa kasanu ndi kawiri.” Pamenepo Yehova anayika chizindikiro pa Kaini kuti aliyense womupeza asamuphe. 16 Ndipo Kaini anachoka pamaso pa Yehova nakakhala ku dziko la Nodi, kummawa kwa Edeni. 17 Kaini anagona malo amodzi ndi mkazi wake ndipo mkaziyo anakhala woyembekezera nabala Enoki. Kaini nthawi imeneyo nʼkuti akumanga mzinda ndipo anawutcha dzina la mwana wake Enoki. 18 Enoki anabereka Iradi; Iradi anabereka Mehuyaeli, ndipo Mehuyaeli anabereka Metusela, ndipo Metusela anabereka Lameki. 19 Lameki anakwatira akazi awiri, wina dzina lake linali Ada ndi winayo dzina lake linali Zila. 20 Ada anabereka Yabala; iyeyu anali kholo la onse okhala mʼmatenti ndi oweta ziweto. 21 Dzina la mʼbale wake linali Yubala; iyeyu anali kholo la onse oyimba zeze ndi chitoliro. 22 Zila nayenso anali ndi mwana wamwamuna, dzina lake Tubala-Kaini. Iyeyu anali kholo la amisiri onse osula zida za mkuwa ndi chitsulo. Mlongo wake wa Tubala-Kaini anali Naama. 23 Lameki anawuza akazi akewo kuti,“Ada ndi Zila, ndimvereni;inu akazi anga imvani mawu anga.Ine ndinapha munthu chifukwa anandipweteka.Ndinapha mnyamatayo chifukwa anandimenya. 24 Ngati wopha Kaini amulipsira kasanu nʼkawiri,ndiye kuti wopha ine Lameki adzamulipsira kokwanira 77.” 25 Adamu anagonanso malo amodzi ndi mkazi wake, ndipo anabereka mwana wamwamuna namutcha Seti, kutanthauza kuti, “Mulungu wandipatsa mwana wina mʼmalo mwa Abele, popeza Kaini anamupha.” 26 Seti naye anali ndi mwana wa mwamuna, ndipo anamutcha Enosi.Pa nthawi imeneyi anthu anayamba kupemphera mʼdzina la Yehova.
In Other Versions
Genesis 4 in the ANGEFD
Genesis 4 in the ANTPNG2D
Genesis 4 in the AS21
Genesis 4 in the BAGH
Genesis 4 in the BBPNG
Genesis 4 in the BBT1E
Genesis 4 in the BDS
Genesis 4 in the BEV
Genesis 4 in the BHAD
Genesis 4 in the BIB
Genesis 4 in the BLPT
Genesis 4 in the BNT
Genesis 4 in the BNTABOOT
Genesis 4 in the BNTLV
Genesis 4 in the BOATCB
Genesis 4 in the BOATCB2
Genesis 4 in the BOBCV
Genesis 4 in the BOCNT
Genesis 4 in the BOECS
Genesis 4 in the BOHCB
Genesis 4 in the BOHCV
Genesis 4 in the BOHLNT
Genesis 4 in the BOHNTLTAL
Genesis 4 in the BOICB
Genesis 4 in the BOILNTAP
Genesis 4 in the BOITCV
Genesis 4 in the BOKCV
Genesis 4 in the BOKCV2
Genesis 4 in the BOKHWOG
Genesis 4 in the BOKSSV
Genesis 4 in the BOLCB
Genesis 4 in the BOLCB2
Genesis 4 in the BOMCV
Genesis 4 in the BONAV
Genesis 4 in the BONCB
Genesis 4 in the BONLT
Genesis 4 in the BONUT2
Genesis 4 in the BOPLNT
Genesis 4 in the BOSCB
Genesis 4 in the BOSNC
Genesis 4 in the BOTLNT
Genesis 4 in the BOVCB
Genesis 4 in the BOYCB
Genesis 4 in the BPBB
Genesis 4 in the BPH
Genesis 4 in the BSB
Genesis 4 in the CCB
Genesis 4 in the CUV
Genesis 4 in the CUVS
Genesis 4 in the DBT
Genesis 4 in the DGDNT
Genesis 4 in the DHNT
Genesis 4 in the DNT
Genesis 4 in the ELBE
Genesis 4 in the EMTV
Genesis 4 in the ESV
Genesis 4 in the FBV
Genesis 4 in the FEB
Genesis 4 in the GGMNT
Genesis 4 in the GNT
Genesis 4 in the HARY
Genesis 4 in the HNT
Genesis 4 in the IRVA
Genesis 4 in the IRVB
Genesis 4 in the IRVG
Genesis 4 in the IRVH
Genesis 4 in the IRVK
Genesis 4 in the IRVM
Genesis 4 in the IRVM2
Genesis 4 in the IRVO
Genesis 4 in the IRVP
Genesis 4 in the IRVT
Genesis 4 in the IRVT2
Genesis 4 in the IRVU
Genesis 4 in the ISVN
Genesis 4 in the JSNT
Genesis 4 in the KAPI
Genesis 4 in the KBT1ETNIK
Genesis 4 in the KBV
Genesis 4 in the KJV
Genesis 4 in the KNFD
Genesis 4 in the LBA
Genesis 4 in the LBLA
Genesis 4 in the LNT
Genesis 4 in the LSV
Genesis 4 in the MAAL
Genesis 4 in the MBV
Genesis 4 in the MBV2
Genesis 4 in the MHNT
Genesis 4 in the MKNFD
Genesis 4 in the MNG
Genesis 4 in the MNT
Genesis 4 in the MNT2
Genesis 4 in the MRS1T
Genesis 4 in the NAA
Genesis 4 in the NASB
Genesis 4 in the NBLA
Genesis 4 in the NBS
Genesis 4 in the NBVTP
Genesis 4 in the NET2
Genesis 4 in the NIV11
Genesis 4 in the NNT
Genesis 4 in the NNT2
Genesis 4 in the NNT3
Genesis 4 in the PDDPT
Genesis 4 in the PFNT
Genesis 4 in the RMNT
Genesis 4 in the SBIAS
Genesis 4 in the SBIBS
Genesis 4 in the SBIBS2
Genesis 4 in the SBICS
Genesis 4 in the SBIDS
Genesis 4 in the SBIGS
Genesis 4 in the SBIHS
Genesis 4 in the SBIIS
Genesis 4 in the SBIIS2
Genesis 4 in the SBIIS3
Genesis 4 in the SBIKS
Genesis 4 in the SBIKS2
Genesis 4 in the SBIMS
Genesis 4 in the SBIOS
Genesis 4 in the SBIPS
Genesis 4 in the SBISS
Genesis 4 in the SBITS
Genesis 4 in the SBITS2
Genesis 4 in the SBITS3
Genesis 4 in the SBITS4
Genesis 4 in the SBIUS
Genesis 4 in the SBIVS
Genesis 4 in the SBT
Genesis 4 in the SBT1E
Genesis 4 in the SCHL
Genesis 4 in the SNT
Genesis 4 in the SUSU
Genesis 4 in the SUSU2
Genesis 4 in the SYNO
Genesis 4 in the TBIAOTANT
Genesis 4 in the TBT1E
Genesis 4 in the TBT1E2
Genesis 4 in the TFTIP
Genesis 4 in the TFTU
Genesis 4 in the TGNTATF3T
Genesis 4 in the THAI
Genesis 4 in the TNFD
Genesis 4 in the TNT
Genesis 4 in the TNTIK
Genesis 4 in the TNTIL
Genesis 4 in the TNTIN
Genesis 4 in the TNTIP
Genesis 4 in the TNTIZ
Genesis 4 in the TOMA
Genesis 4 in the TTENT
Genesis 4 in the UBG
Genesis 4 in the UGV
Genesis 4 in the UGV2
Genesis 4 in the UGV3
Genesis 4 in the VBL
Genesis 4 in the VDCC
Genesis 4 in the YALU
Genesis 4 in the YAPE
Genesis 4 in the YBVTP
Genesis 4 in the ZBP