Isaiah 36 (BOGWICC)
1 Chaka cha khumi ndi chinayi cha ulamuliro wa Mfumu Hezekiya, Senakeribu mfumu ya ku Asiriya anathira nkhondo mizinda yonse yotetezedwa ya ku Yuda, nayilanda. 2 Kenaka mfumu ya ku Asiriya inatuma kazembe wake wankhondo pamodzi ndi gulu lalikulu lankhondo kuchokera ku Lakisi kupita kwa mfumu Hezekiya ku Yerusalemu. Tsono kazembeyo anayima pafupi ndi ngalande yamadzi yochokera ku Dziwe lakumtunda pa msewu wopita ku malo a munda wa mmisiri wochapa zovala. 3 Panali anthu atatu. Woyamba anali Eliyakimu mwana wa Hilikiya komanso ndiye woyangʼanira nyumba ya mfumu. Wachiwiri anali Sebina amene anali mlembi wa bwalo; ndipo wachitatu anali Yowa mwana wa Asafu komanso anali wolemba zochitika. Anthu awa anatuluka kukakumana ndi kazembe wa ankhondo uja. 4 Kazembe wa ankhondo anawawuza kuti, “Kamuwuzeni Hezekiya kuti,“Mfumu yayikulu, mfumu ya ku Asiriya ikunena kuti, Kodi chikukulimbitsa mtima ndi chiyani? 5 Iwe ukuti uli ndi luso ndiponso mphamvu pa nkhondo, komatu ukuyankhula mawu opanda pake. Kodi tsono iwe ukudalira yani kuti undiwukire ine? 6 Taona tsono, iwe ukudalira Igupto, bango lothyokalo, limene limalasa mʼmanja mwa munthu ngati waliyesa ndodo yoyendera! Umo ndi mmene Farao mfumu ya ku Igupto imachitira aliyense amene akuyidalira. 7 Ndipo ngati ukunena kwa ine kuti, ‘Ife tikudalira Yehova Mulungu wathu,’ kodi si Mulungu yemweyo amene nyumba zake ndi maguwa ake, Hezekiya anachotsa, nawuza anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu kuti, ‘Muzipembedza pa guwa lansembe ili?’ 8 “Ndipo tsopano bwera udzakambirane ndi mbuye wanga, mfumu ya ku Asiriya: Ine ndidzakupatsa akavalo 2,000 ngati ungathe kupeza okwerapo! 9 Iwe ungathe bwanji kugonjetsa ngakhale mmodzi mwa akazembe angʼonoangʼono a mbuye wanga, pamene ukudalira Igupto kuti akupatse magaleta ndi anthu okwera pa akavalo. 10 Kuwonjezera pamenepa, kodi ine ndabwera kudzathira nkhondo ndi kuwononga dziko lino popanda chilolezo cha Yehova? Yehova mwini ndiye anandiwuza kuti ndidzathire nkhondo ndi kuwononga dziko lino.” 11 Pamenepo Eliyakimu, Sebina ndi Yowa anawuza kazembeyo kuti, “Chonde yankhulani kwa atumiki anufe mʼChiaramu, popeza timachimva. Musayankhule nafe mu Chihebri kuopa kuti anthu onse amene ali pa khomapa angamve.” 12 Koma kazembeyo anayankha kuti, “Kodi mbuye wanga wandituma kuti ndidzanene zinthu izi kwa mbuye wanu yekha ndi inu nokha basi? Ayi, komanso kwa anthu amene akhala pa khomawa. Iwowa adzadya chimbudzi chawo chomwe ndi kumwa mkodzo wawo womwe monga momwe mudzachitire inuyonso.” 13 Tsono kazembeyo anayimirira nafuwula mu Chihebri kuti, “Imvani mawu a mfumu yayikulu, mfumu ya ku Asiriya! 14 Zimene mfumu ikunena ndi izi: Musalole kuti Hezekiya akunamizeni. Iye sangakupulumutseni! 15 Hezekiya asakukakamizeni kudalira Yehova ndi mawu akuti, ‘Ndithu, Yehova adzatipulumutsa; ndipo sadzapereka mzindawu mʼdzanja la mfumu ya ku Asiriya.’ 16 “Musamumvere Hezekiya. Zimene mfumu ya ku Asiriya ikunena ndi izi: Pangani mtendere ndi ine ndipo mutuluke mu mzinda. Mukatero aliyense wa inu adzadya mphesa ndi nkhuyu za mʼmunda mwake ndiponso adzamwa madzi a mʼchitsime chake, 17 mpaka mfumuyo itabwera kudzakutengani kupita ku dziko lofanana ndi lanulo, dziko limene lili ndi tirigu ndi vinyo watsopano, dziko loyenda mkaka ndi uchi. 18 “Inu musalole kuti Hezekiya akusocheretseni pamene iye akuti, ‘Yehova adzatipulumutsa.’ Kodi alipo mulungu wa anthu a mtundu wina amene anapulumutsa dziko lake mʼdzanja la mfumu ya ku Asiriya? 19 Kodi ili kuti milungu ya Hamati ndi Aripadi? Ili kuti milungu ya Sefaravaimu? Kodi inapulumutsa Samariya mʼdzanja langa? 20 Kodi ndi milungu iti mwa milungu yonse ya mayiko awa amene anapulumutsa dziko lake mʼdzanja? Nanga tsono Yehova adzapulumutsa Yerusalemu mʼdzanja langa motani?” 21 Koma anthu anakhala chete ndipo sanayankhepo kanthu, chifukwa mfumu inawalamula kuti, “Musayankhe.” 22 Pamenepo anthu atatu aja Eliyakimu, mwana wa Hilikiya amene ankayangʼanira nyumba ya mfumu; Sebina mlembi wa bwalo; ndi Yowa, mwana wa Asafu mlembi wa zochitika anapita kwa Hezekiya atangʼamba zovala zawo ndipo anamuwuza zonse zimene anayankhula kazembe uja.