Judges 2 (BOGWICC)
1 Mngelo wa Yehova anapita ku Bokimu kuchokera ku Giligala ndipo anati kwa Aisraeli, “Ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto ndikukulowetsani mʼdziko limene ndinalumbira kwa makolo anu. Ndinati ‘Sindidzaswa pangano langa ndi inu, 2 ndipo inu musadzachite pangano ndi anthu a dziko lino, koma mudzaphwanye maguwa awo ansembe.’ Koma inu simunamvere lamulo langa. Chifukwa chiyani mwachita zimenezi? 3 Ndikukuwuzani tsopano kuti sindithamangitsa nzikazo pamene inu mukufika. Ndidzawasandutsa kukhala adani anu ndipo milungu yawo idzakhala ngati msampha kwa inu.” 4 Mngelo wa Mulungu atayankhula izi kwa Aisraeli, onse analira mokweza, 5 ndipo anatcha malowo kuti Bokimu (kutanthauza kuti Olira). Pamenepo anapereka nsembe kwa Yehova. 6 Yoswa atawuza Aisraeli kuti achoke, iwo anapita kukatenga dzikolo, aliyense dera lake. 7 Anthuwo anatumikira Yehova masiku onse a moyo wa Yoswa. Atamwalira Yoswa, Aisraeli anatumikirabe Yehova nthawi yonse ya moyo wa akuluakulu amene anaona zazikulu zimene Yehova anawachitira. 8 Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Yehova, anamwalira ali ndi zaka 110. 9 Ndipo anamuyika mʼmanda a mʼdziko lake, ku Timnati-Heresi mʼdziko la mapiri la Efereimu, kumpoto kwa phiri la Gaasi. 10 Mʼbado onse utapita kukakhala ndi anthu a mtundu awo, kenaka panauka mʼbado wina umene sunadziwe Yehova ngakhale ntchito zazikulu zimene Yehova anachitira Aisraeli. 11 Choncho Aisraeli anayamba kuchita zinthu zoyipa pamaso pa Yehova ndipo anatumikira Abaala. 12 Iwo anasiya Yehova Mulungu wa makolo awo, amene anawatulutsa ku Igupto. Ndipo anatsatira ndi kupembedza milungu yosiyanasiyana ya anthu amene anawazungulira. Motero Aisraeli anakwiyitsa Yehova. 13 Iwo anasiya Yehova ndi kumatumikira Baala ndi Asiteroti. 14 Yehova anapsera mtima Aisraeli ndipo anawapereka mʼmanja mwa anthu ofunkha amene ankasakaza zinthu zawo. Ndipo analola kuti adani awo owazungulira amene sanathenso kulimbana nawo, awagonjetse. 15 Nthawi zonse Aisraeli ankati akapita ku nkhondo, Yehova amalimbana nawo kuti agonjetsedwe, monga ananenera molumbira kuti zidzaterodi. Choncho iwo anali pa mavuto aakulu. 16 Choncho Yehova anawawutsira atsogoleri amene ankawapulumutsa mʼmanja mwa anthu amene ankasakaza zinthu zawo. 17 Komabe iwo sanawamvere atsogoleri awowo popeza ankapembedza milungu ina ndi kumayigwadira. Iwo anapatuka msangamsanga mu njira imene ankayendamo makolo awo. Iwo aja ankamvera malamulo a Yehova, koma mʼbado uwu ayi. 18 Nthawi zonse Yehova akawautsira mtsogoleri, Iye amakhala naye, ndipo mtsogoleriyo ankawapulumutsa Aisraeliwo mʼmanja mwa adani awo mʼnthawi imene anali moyo. Yehova ankawamvera chisoni Aisraeli pamene ankabuwula chifukwa cha anthu owazunza ndi kuwasautsa. 19 Koma nthawi zonse mtsogoleri akamwalira, Aisraeli ankabwerera mʼmbuyo. Iwo amadzisandutsa oyipa kupambana makolo awo popeza ankatsata milungu ina, kuyitumikira ndi kumayigwadira. Anakana kusiya makhalidwe awo oyipa ndi njira zawo zamakani. 20 Choncho Yehova anawapsera mtima Aisraeli ndipo anati, “Chifukwa mtundu uwu waswa pangano limene ndinakhazikitsa ndi makolo awo ndipo sanandimvere, 21 Inenso sindidzapirikitsanso mtundu uli wonse wa anthu amene Yoswa anawasiya pomwalira. 22 Ndidzatero kuti ndiwayese Aisraeli ndi kuona ngati adzasamala kuyenda mʼnjira ya Ine Yehova monga momwe ankachitira makolo awo.” 23 Choncho Yehova anayileka mitundu imeneyi ndipo sanayithamangitse kapena kuyipereka mʼmanja mwa Yoswa.
In Other Versions
Judges 2 in the ANGEFD
Judges 2 in the ANTPNG2D
Judges 2 in the AS21
Judges 2 in the BAGH
Judges 2 in the BBPNG
Judges 2 in the BBT1E
Judges 2 in the BDS
Judges 2 in the BEV
Judges 2 in the BHAD
Judges 2 in the BIB
Judges 2 in the BLPT
Judges 2 in the BNT
Judges 2 in the BNTABOOT
Judges 2 in the BNTLV
Judges 2 in the BOATCB
Judges 2 in the BOATCB2
Judges 2 in the BOBCV
Judges 2 in the BOCNT
Judges 2 in the BOECS
Judges 2 in the BOHCB
Judges 2 in the BOHCV
Judges 2 in the BOHLNT
Judges 2 in the BOHNTLTAL
Judges 2 in the BOICB
Judges 2 in the BOILNTAP
Judges 2 in the BOITCV
Judges 2 in the BOKCV
Judges 2 in the BOKCV2
Judges 2 in the BOKHWOG
Judges 2 in the BOKSSV
Judges 2 in the BOLCB
Judges 2 in the BOLCB2
Judges 2 in the BOMCV
Judges 2 in the BONAV
Judges 2 in the BONCB
Judges 2 in the BONLT
Judges 2 in the BONUT2
Judges 2 in the BOPLNT
Judges 2 in the BOSCB
Judges 2 in the BOSNC
Judges 2 in the BOTLNT
Judges 2 in the BOVCB
Judges 2 in the BOYCB
Judges 2 in the BPBB
Judges 2 in the BPH
Judges 2 in the BSB
Judges 2 in the CCB
Judges 2 in the CUV
Judges 2 in the CUVS
Judges 2 in the DBT
Judges 2 in the DGDNT
Judges 2 in the DHNT
Judges 2 in the DNT
Judges 2 in the ELBE
Judges 2 in the EMTV
Judges 2 in the ESV
Judges 2 in the FBV
Judges 2 in the FEB
Judges 2 in the GGMNT
Judges 2 in the GNT
Judges 2 in the HARY
Judges 2 in the HNT
Judges 2 in the IRVA
Judges 2 in the IRVB
Judges 2 in the IRVG
Judges 2 in the IRVH
Judges 2 in the IRVK
Judges 2 in the IRVM
Judges 2 in the IRVM2
Judges 2 in the IRVO
Judges 2 in the IRVP
Judges 2 in the IRVT
Judges 2 in the IRVT2
Judges 2 in the IRVU
Judges 2 in the ISVN
Judges 2 in the JSNT
Judges 2 in the KAPI
Judges 2 in the KBT1ETNIK
Judges 2 in the KBV
Judges 2 in the KJV
Judges 2 in the KNFD
Judges 2 in the LBA
Judges 2 in the LBLA
Judges 2 in the LNT
Judges 2 in the LSV
Judges 2 in the MAAL
Judges 2 in the MBV
Judges 2 in the MBV2
Judges 2 in the MHNT
Judges 2 in the MKNFD
Judges 2 in the MNG
Judges 2 in the MNT
Judges 2 in the MNT2
Judges 2 in the MRS1T
Judges 2 in the NAA
Judges 2 in the NASB
Judges 2 in the NBLA
Judges 2 in the NBS
Judges 2 in the NBVTP
Judges 2 in the NET2
Judges 2 in the NIV11
Judges 2 in the NNT
Judges 2 in the NNT2
Judges 2 in the NNT3
Judges 2 in the PDDPT
Judges 2 in the PFNT
Judges 2 in the RMNT
Judges 2 in the SBIAS
Judges 2 in the SBIBS
Judges 2 in the SBIBS2
Judges 2 in the SBICS
Judges 2 in the SBIDS
Judges 2 in the SBIGS
Judges 2 in the SBIHS
Judges 2 in the SBIIS
Judges 2 in the SBIIS2
Judges 2 in the SBIIS3
Judges 2 in the SBIKS
Judges 2 in the SBIKS2
Judges 2 in the SBIMS
Judges 2 in the SBIOS
Judges 2 in the SBIPS
Judges 2 in the SBISS
Judges 2 in the SBITS
Judges 2 in the SBITS2
Judges 2 in the SBITS3
Judges 2 in the SBITS4
Judges 2 in the SBIUS
Judges 2 in the SBIVS
Judges 2 in the SBT
Judges 2 in the SBT1E
Judges 2 in the SCHL
Judges 2 in the SNT
Judges 2 in the SUSU
Judges 2 in the SUSU2
Judges 2 in the SYNO
Judges 2 in the TBIAOTANT
Judges 2 in the TBT1E
Judges 2 in the TBT1E2
Judges 2 in the TFTIP
Judges 2 in the TFTU
Judges 2 in the TGNTATF3T
Judges 2 in the THAI
Judges 2 in the TNFD
Judges 2 in the TNT
Judges 2 in the TNTIK
Judges 2 in the TNTIL
Judges 2 in the TNTIN
Judges 2 in the TNTIP
Judges 2 in the TNTIZ
Judges 2 in the TOMA
Judges 2 in the TTENT
Judges 2 in the UBG
Judges 2 in the UGV
Judges 2 in the UGV2
Judges 2 in the UGV3
Judges 2 in the VBL
Judges 2 in the VDCC
Judges 2 in the YALU
Judges 2 in the YAPE
Judges 2 in the YBVTP
Judges 2 in the ZBP