Jeremiah 33 (BOGWICC)
1 Yeremiya akanali mʼndende mʼbwalo la alonda, Yehova anayankhula nayenso kachiwiri nati: 2 “Yehova amene analenga dziko lapansi, kuliwumba ndi kulikhazikitsa; amene dzina lake ndi Yehova, akuti, 3 ‘Unditame mopemba ndipo ndidzakuyankha. Ndidzakuwuza zinsinsi zazikulu zimene suzidziwa.’ 4 Yehova Mulungu wa Israeli akunenapo pa za nyumba za mu mzinda muno ndiponso pa za nyumba za mafumu a Yuda. Zidzagwetsedwa, ndipo palibe chifukwa cholimbana ndi mitumbira ya nkhondo ya Ababuloni. 5 Ababuloni akubwera kudzawuthira nkhondo mzindawu ndipo nyumba zake zidzadzaza ndi mitembo ya anthu amene ndidzawapha mokwiya ndi mwaukali. Ndawufulatira mzinda uno chifukwa cha zoyipa zake zonse. 6 “ ‘Pambuyo pake mzindawu ndidzawupatsanso moyo ndi kuwuchiritsa; ndidzachiritsa anthu anga ndi kuwapatsa chitetezo ndi mtendere weniweni. 7 Ndidzawakhazikanso Ayuda ndi Aisraeli ku dziko lawo, ndipo ndidzawabwezera monga mmene analili poyamba. 8 Ndidzawayeretsa pochotsa zoyipa zonse zimene anandichitira, ndiponso ndidzawakhululukira machimo onse amene anachita pondiwukira. 9 Mzinda wa Yerusalemu udzandipatsa chimwemwe, chiyamiko ndi ulemerero. Anthu a mitundu yonse adzanditamanda akadzamva za zabwino zonse zimene ndawuchitira mzindawu. Iwo adzachita mantha ndi kunjenjemera poona madalitso ochuluka ndi mtendere zimene ndapereka kwa mzinda umenewu.’ 10 “Yehova akuti, ‘Inu mumanena za malo ano kuti ndi bwinja,’ malo opandamo anthu kapena nyama. Komatu mizinda ya Yuda ndi mʼmisewu ya mu Yerusalemu mʼmene tsopano muli zii mudzamvekanso 11 mfuwu wachimwemwe ndi mawu achisangalalo, mawu a mkwatibwi ndi mkwati. Mʼnyumba ya Mulungu mudzamvekanso nyimbo za anthu amene akudzapereka nsembe zothokoza Yehova. Azidzati,“Yamikani Yehova Wamphamvuzonse,popeza Iye ndi wabwino;pakuti chifundo chake nʼchamuyaya.”Pakuti ndidzabwezeretsa zinthu zabwino za dziko lino monga zinalili poyamba, akutero Yehova. 12 “Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Malo ano, a chipululu ndi wopanda anthu kapena nyama, mʼmizinda yake yonse mudzakhala msipu umene abusa adzadyetserako nkhosa zawo. 13 Ku mizinda ya kumapiri, ya kuchigwa, ya ku Negevi, ya ku dera la Benjamini, ku dziko lozungulira Yerusalemu, ndi ku mizinda ya Yuda, nkhosa zidzadutsanso pamaso pa munthu woziwerenga,’ akutero Yehova. 14 “ ‘Taonani masiku akubwera,’ akutero Yehova, ‘pamene ndidzachitadi zokoma zimene ndinalonjeza Aisraeli ndi nyumba ya Yuda. 15 “ ‘Mʼmasiku amenewo ndi pa nthawi imeneyondidzaphukitsa Nthambi yolungama kuchokera ku banja la Davide;munthuyo adzachita zolungama ndi zabwino mʼdziko. 16 Mʼmasiku amenewo Yuda adzapulumukandipo Yerusalemu adzakhala mwamtendere.Dzina limene mzindawu udzadziwike nalo ndi ili:Yehova Chilungamo Chathu.’ 17 Yehova akunena kuti, ‘Davide sadzasowa mdzukulu wolowa mʼmalo mwake pa mpando waufumu wa Israeli, 18 ngakhale ansembe, amene ndi Alevi, sadzasowanso munthu woyima pamaso panga nthawi zonse wopereka nsembe zopsereza, nsembe zaufa ndi nsembe zina.’ ” 19 Yehova anawuza Yeremiya kuti: 20 Mawu anga ndi awa. Ine ndinachita pangano ndi usana ndi usiku kuti zizibwera pa nthawi yake. Pangano limeneli inu simungaliphwanye. 21 Ndinachitanso pangano ndi Davide, mtumiki wanga kuti nthawi zonse adzakhala ndi mdzukulu wodzakhala pa mpando wake waufumu. Ndinachitanso pangano ndi Alevi kuti iwonso adzanditumikira nthawi zonse. Mapangano amenewa sadzaphwanyidwa nthawi zonse. 22 Ndidzachulukitsa ngati nyenyezi zamlengalenga ndiponso ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja zidzukulu za mtumiki wanga Davide ndiponso za Alevi amene amanditumikira Ine. 23 Yehova anafunsa Yeremiya kuti, 24 “Kodi sunamve mmene anthu ena akumanenera kuti, ‘Yehova wakana maufumu awiriwa amene Iye anawasankha.’ Kotero anthuwo akunyoza anthu anga ndipo sakuwayesanso mtundu wa anthu. 25 ‘Koma Ine Yehova ndinachita pangano ndi usana ndi usiku. Ndinakhazikitsanso malamulo oyendetsa dziko lakumwamba ndi dziko lapansi, 26 monga ndachita zimenezi motsimikiza, choncho ndidzasunga pangano limene ndinachita ndi zidzukulu za Yakobo ndi Davide mtumiki wanga. Ndidzasankha mmodzi mwa ana a Davide kuti alamulire zidzukulu za Abrahamu, Isake ndi Yakobo. Komatu ndidzawamvera chifundo ndi kuwakhazikanso pabwino.’ ”