Jeremiah 35 (BOGWICC)
1 Yehova anayankhula ndi Yeremiya nthawi ya ulamuliro wa Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya Yuda, kuti: 2 “Pita ku banja la Arekabu ndipo ukawayitane kuti abwere mʼchipinda chimodzi cha Nyumba ya Yehova ndipo akafika uwapatse vinyo kuti amwe.” 3 Choncho ndinakatenga Yaazaniya (mwana wa Yeremiya winanso amene anali mwana wa Habaziniya), abale ake, ana ake onse aamuna ndi banja lonse la Arekabu. 4 Ndinabwera nawo ku Nyumba ya Yehova, ku chipinda cha ophunzira a mneneri Hanani mwana wa Igidaliya, munthu wa Mulungu. Chipinda chimenechi chinali pafupi ndi chipinda cha akuluakulu, chimene chinali pamwamba pa chipinda cha Maaseya mwana wa Salumu, mlonda wa pa khomo. 5 Kenaka ndinayika mabotolo odzaza ndi vinyo ndi zikho zake pamaso pa Arekabu ndipo ndinawawuza kuti, “Imwani vinyoyu.” 6 Koma iwo anayankha kuti, “Ife sitimwa vinyo, chifukwa kholo lathu Yehonadabu mwana wa Rekabu anatilamula kuti, ‘Inuyo ngakhale zidzukulu zanu, musadzamwe vinyo mpaka kalekale. 7 Musadzamange nyumba kapena kufesa mbewu, kapena kulima minda ya mpesa; musadzakhale ndi zinthu zimenezi. Mʼmalo mwake muzidzakhale mʼmatenti. Mukadzatero mudzakhala nthawi yayitali mʼdziko limene mukukhalamo.’ 8 Ife takhala tikumvera zonse zimene kholo lathu Yehonadabu mwana wa Rekabu anatilamula. Ife ngakhale akazi athu kapena ana athu aamuna ndi aakazi sitinamwepo vinyo 9 kapena kumanga nyumba kuti tizikhalamo kapenanso kukhala ndi minda ya mpesa, minda ina iliyonse kapena mbewu. 10 Koma takhala mʼmatenti ndipo tamvera kwathunthu chilichonse chimene kholo lathu Yehonadabu anatilamula. 11 Koma pamene Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anathira nkhondo dziko lino, ife tinati, ‘Tiyeni tichoke, tipite ku Yerusalemu kuti tithawe magulu ankhondo a Akasidi ndi Aaramu.’ Kotero ife takhala tikukhala mu Yerusalemu.” 12 Yehova anayankhulanso ndi Yeremiya kuti, 13 “Iyeyu, Yehova Mulungu wa Israeli anawuza Yeremiya kuti: Pita ukawawuze anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu kuti, ‘Kodi simungatengeko phunziro ndi kumvera mawu anga?’ akutero Yehova. 14 ‘Yehonadabu mwana wa Rekabu analamula ana ake kuti asamwe vinyo ndipo lamulo limeneli alisunga. Mpaka lero lino iwo samwa vinyo, chifukwa akumvera lamulo la kholo lawo. Koma Ine ndakhala ndikuyankhula nanu kawirikawiri kukuchenjezani, koma inu simunandimvere Ine. 15 Kawirikawiri ndakhala ndikutumiza atumiki anga, aneneri, kwa inu. Iwo akhala akukuwuzani kuti, ‘Aliyense wa inu asiye ntchito zake zoyipa ndi kukonza makhalidwe ake; musatsatire milungu ina ndi kumayitumikira. Pamenepo mudzakhala mʼdziko limene ndinakupatsani ndi makolo anu.’ Komabe inu simunasamale zimenezi kapena kundimvera Ine. 16 Zidzukulu za Yehonadabu mwana wa Rekabu zakhala zikumvera lamulo limene kholo lawo anazilamula, koma inuyo simunandimvere Ine. 17 “Nʼchifukwa chake Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ndidzagwetsera pa Yuda ndi pa onse okhala mu Yerusalemu masautso onse amene ndinakonza chifukwa sanandimvere. Ndinawayitana koma iwo sanayankhe.’ ” 18 Yeremiya anawuza banja la Arekabu mawu onse a Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, kuti, “Munamvera lamulo la kholo lanu Yehonadabu ndipo mwatsatira malangizo ake onse ndi kuchita chilichonse chimene anakulamulani.” 19 Tsono Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, “Yehonadabu mwana wa Rekabu sadzasowa munthu wonditumikira Ine nthawi zonse.”
In Other Versions
Jeremiah 35 in the ANGEFD
Jeremiah 35 in the ANTPNG2D
Jeremiah 35 in the AS21
Jeremiah 35 in the BAGH
Jeremiah 35 in the BBPNG
Jeremiah 35 in the BBT1E
Jeremiah 35 in the BDS
Jeremiah 35 in the BEV
Jeremiah 35 in the BHAD
Jeremiah 35 in the BIB
Jeremiah 35 in the BLPT
Jeremiah 35 in the BNT
Jeremiah 35 in the BNTABOOT
Jeremiah 35 in the BNTLV
Jeremiah 35 in the BOATCB
Jeremiah 35 in the BOATCB2
Jeremiah 35 in the BOBCV
Jeremiah 35 in the BOCNT
Jeremiah 35 in the BOECS
Jeremiah 35 in the BOHCB
Jeremiah 35 in the BOHCV
Jeremiah 35 in the BOHLNT
Jeremiah 35 in the BOHNTLTAL
Jeremiah 35 in the BOICB
Jeremiah 35 in the BOILNTAP
Jeremiah 35 in the BOITCV
Jeremiah 35 in the BOKCV
Jeremiah 35 in the BOKCV2
Jeremiah 35 in the BOKHWOG
Jeremiah 35 in the BOKSSV
Jeremiah 35 in the BOLCB
Jeremiah 35 in the BOLCB2
Jeremiah 35 in the BOMCV
Jeremiah 35 in the BONAV
Jeremiah 35 in the BONCB
Jeremiah 35 in the BONLT
Jeremiah 35 in the BONUT2
Jeremiah 35 in the BOPLNT
Jeremiah 35 in the BOSCB
Jeremiah 35 in the BOSNC
Jeremiah 35 in the BOTLNT
Jeremiah 35 in the BOVCB
Jeremiah 35 in the BOYCB
Jeremiah 35 in the BPBB
Jeremiah 35 in the BPH
Jeremiah 35 in the BSB
Jeremiah 35 in the CCB
Jeremiah 35 in the CUV
Jeremiah 35 in the CUVS
Jeremiah 35 in the DBT
Jeremiah 35 in the DGDNT
Jeremiah 35 in the DHNT
Jeremiah 35 in the DNT
Jeremiah 35 in the ELBE
Jeremiah 35 in the EMTV
Jeremiah 35 in the ESV
Jeremiah 35 in the FBV
Jeremiah 35 in the FEB
Jeremiah 35 in the GGMNT
Jeremiah 35 in the GNT
Jeremiah 35 in the HARY
Jeremiah 35 in the HNT
Jeremiah 35 in the IRVA
Jeremiah 35 in the IRVB
Jeremiah 35 in the IRVG
Jeremiah 35 in the IRVH
Jeremiah 35 in the IRVK
Jeremiah 35 in the IRVM
Jeremiah 35 in the IRVM2
Jeremiah 35 in the IRVO
Jeremiah 35 in the IRVP
Jeremiah 35 in the IRVT
Jeremiah 35 in the IRVT2
Jeremiah 35 in the IRVU
Jeremiah 35 in the ISVN
Jeremiah 35 in the JSNT
Jeremiah 35 in the KAPI
Jeremiah 35 in the KBT1ETNIK
Jeremiah 35 in the KBV
Jeremiah 35 in the KJV
Jeremiah 35 in the KNFD
Jeremiah 35 in the LBA
Jeremiah 35 in the LBLA
Jeremiah 35 in the LNT
Jeremiah 35 in the LSV
Jeremiah 35 in the MAAL
Jeremiah 35 in the MBV
Jeremiah 35 in the MBV2
Jeremiah 35 in the MHNT
Jeremiah 35 in the MKNFD
Jeremiah 35 in the MNG
Jeremiah 35 in the MNT
Jeremiah 35 in the MNT2
Jeremiah 35 in the MRS1T
Jeremiah 35 in the NAA
Jeremiah 35 in the NASB
Jeremiah 35 in the NBLA
Jeremiah 35 in the NBS
Jeremiah 35 in the NBVTP
Jeremiah 35 in the NET2
Jeremiah 35 in the NIV11
Jeremiah 35 in the NNT
Jeremiah 35 in the NNT2
Jeremiah 35 in the NNT3
Jeremiah 35 in the PDDPT
Jeremiah 35 in the PFNT
Jeremiah 35 in the RMNT
Jeremiah 35 in the SBIAS
Jeremiah 35 in the SBIBS
Jeremiah 35 in the SBIBS2
Jeremiah 35 in the SBICS
Jeremiah 35 in the SBIDS
Jeremiah 35 in the SBIGS
Jeremiah 35 in the SBIHS
Jeremiah 35 in the SBIIS
Jeremiah 35 in the SBIIS2
Jeremiah 35 in the SBIIS3
Jeremiah 35 in the SBIKS
Jeremiah 35 in the SBIKS2
Jeremiah 35 in the SBIMS
Jeremiah 35 in the SBIOS
Jeremiah 35 in the SBIPS
Jeremiah 35 in the SBISS
Jeremiah 35 in the SBITS
Jeremiah 35 in the SBITS2
Jeremiah 35 in the SBITS3
Jeremiah 35 in the SBITS4
Jeremiah 35 in the SBIUS
Jeremiah 35 in the SBIVS
Jeremiah 35 in the SBT
Jeremiah 35 in the SBT1E
Jeremiah 35 in the SCHL
Jeremiah 35 in the SNT
Jeremiah 35 in the SUSU
Jeremiah 35 in the SUSU2
Jeremiah 35 in the SYNO
Jeremiah 35 in the TBIAOTANT
Jeremiah 35 in the TBT1E
Jeremiah 35 in the TBT1E2
Jeremiah 35 in the TFTIP
Jeremiah 35 in the TFTU
Jeremiah 35 in the TGNTATF3T
Jeremiah 35 in the THAI
Jeremiah 35 in the TNFD
Jeremiah 35 in the TNT
Jeremiah 35 in the TNTIK
Jeremiah 35 in the TNTIL
Jeremiah 35 in the TNTIN
Jeremiah 35 in the TNTIP
Jeremiah 35 in the TNTIZ
Jeremiah 35 in the TOMA
Jeremiah 35 in the TTENT
Jeremiah 35 in the UBG
Jeremiah 35 in the UGV
Jeremiah 35 in the UGV2
Jeremiah 35 in the UGV3
Jeremiah 35 in the VBL
Jeremiah 35 in the VDCC
Jeremiah 35 in the YALU
Jeremiah 35 in the YAPE
Jeremiah 35 in the YBVTP
Jeremiah 35 in the ZBP