Jeremiah 39 (BOGWICC)
1 Mzinda wa Yerusalemu anawulanda motere: Mʼchaka chachisanu ndi chinayi cha Zedekiya mfumu ya Yuda, mwezi wakhumi, Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni anabwera ndi gulu lake lonse kudzathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu ndipo anawuzinga mzindawo. 2 Ndipo pa tsiku lachisanu ndi chinayi la mwezi wachinayi wa chaka cha khumi ndi chimodzi cha Zedekiya, malinga a mzindawo anabowoledwa. 3 Pamenepo akuluakulu onse a mfumu ya ku Babuloni anabwera nakakhala pa Chipata Chapakati. Akuluwo ndi awa: Nerigali-Sarezeri, Samugara Nebo, Sarisekimu mkulu wa nduna, Nerigali-Sarezeri winanso mlangizi wa mfumu ndi akuluakulu onse a mfumu ya ku Babuloni. 4 Zedekiya mfumu ya Yuda pamodzi ndi ankhondo ake atawaona, anathawa mu mzindawo usiku podzera ku munda wa mfumu, kudutsa chipata cha pakati pa makoma awiri. Anathawira ku Araba. 5 Koma gulu la ankhondo la ku Babuloni linalondola ndi kumupeza Zedekiyayo mʼchigwa cha ku Yeriko. Anamugwira napita naye kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni ku Ribula mʼdziko la Hamati kumene anagamula mlandu wake. 6 Ku Ribulako, mfumu ya ku Babuloni inapha ana aamuna a Zedekiya iyeyo akuona. Inaphanso anthu olemekezeka onse a ku Yuda. 7 Kenaka inakolowola maso a Zedekiya ndi kumumanga ndi maunyolo a mkuwa nʼkupita naye ku Babuloni. 8 Ababuloni anatentha nyumba ya mfumu ndi nyumba za anthu, ndiponso anagwetsa malinga a Yerusalemu. 9 Nebuzaradani, mtsogoleri wa alonda ankhondo a mfumu, anatenga ukapolo anthu onse otsala mu mzindamo kupita nawo ku Babuloni, pamodzi ndi amene anadzipereka kale kwa iye. 10 Koma Nebuzaradani, mtsogoleri wa alonda ankhondo anasiya mʼdziko la Yuda anthu ena osauka, amene analibe chilichonse; ndipo anawapatsa minda ya mpesa ndi minda inanso. 11 Tsono Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni inatuma mawu kwa Nebuzaradani mtsogoleri wa alonda ankhondo a mfumu za Yeremiya. Iye anati: 12 “Mutenge, umusamale bwino, ndipo usamuvute koma umuchitire zimene afuna.” 13 Choncho Nebuzaradani mtsogoleri wa alonda, Nebusazibani mkulu wa nduna, Nerigali-Sarezeri mlangizi wamkulu wa mfumu ndi akuluakulu onse a mfumu ya ku Babuloni 14 anatuma anthu nakamutulutsa Yeremiya mʼbwalo la alonda. Anakamupereka kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani, kuti amutumize ku nyumba yake. Ndipo Yeremiya anakhala pakati pa abale ake. 15 Yeremiya ali mʼndende ku bwalo la alonda, Yehova anayankhula naye: 16 “Pita ukamuwuze Ebedi-Meleki, Mkusi, kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Zidzachitikadi zimene ndinanena zokhudza mzinda uno; ndipo zidzakhala zoyipa osati zabwino ayi. Zimenezi zidzachitika pa nthawi yake iwe ukuona. 17 Koma ndidzakupulumutsa pa tsiku limenelo, akutero Yehova; sudzaperekedwa kwa anthu amene umawaopa. 18 Ndithu ndidzakupulumutsa; sudzaphedwa pa nkhondo koma udzapulumuka, chifukwa wadalira Ine, akutero Yehova.’ ”
In Other Versions
Jeremiah 39 in the ANGEFD
Jeremiah 39 in the ANTPNG2D
Jeremiah 39 in the AS21
Jeremiah 39 in the BAGH
Jeremiah 39 in the BBPNG
Jeremiah 39 in the BBT1E
Jeremiah 39 in the BDS
Jeremiah 39 in the BEV
Jeremiah 39 in the BHAD
Jeremiah 39 in the BIB
Jeremiah 39 in the BLPT
Jeremiah 39 in the BNT
Jeremiah 39 in the BNTABOOT
Jeremiah 39 in the BNTLV
Jeremiah 39 in the BOATCB
Jeremiah 39 in the BOATCB2
Jeremiah 39 in the BOBCV
Jeremiah 39 in the BOCNT
Jeremiah 39 in the BOECS
Jeremiah 39 in the BOHCB
Jeremiah 39 in the BOHCV
Jeremiah 39 in the BOHLNT
Jeremiah 39 in the BOHNTLTAL
Jeremiah 39 in the BOICB
Jeremiah 39 in the BOILNTAP
Jeremiah 39 in the BOITCV
Jeremiah 39 in the BOKCV
Jeremiah 39 in the BOKCV2
Jeremiah 39 in the BOKHWOG
Jeremiah 39 in the BOKSSV
Jeremiah 39 in the BOLCB
Jeremiah 39 in the BOLCB2
Jeremiah 39 in the BOMCV
Jeremiah 39 in the BONAV
Jeremiah 39 in the BONCB
Jeremiah 39 in the BONLT
Jeremiah 39 in the BONUT2
Jeremiah 39 in the BOPLNT
Jeremiah 39 in the BOSCB
Jeremiah 39 in the BOSNC
Jeremiah 39 in the BOTLNT
Jeremiah 39 in the BOVCB
Jeremiah 39 in the BOYCB
Jeremiah 39 in the BPBB
Jeremiah 39 in the BPH
Jeremiah 39 in the BSB
Jeremiah 39 in the CCB
Jeremiah 39 in the CUV
Jeremiah 39 in the CUVS
Jeremiah 39 in the DBT
Jeremiah 39 in the DGDNT
Jeremiah 39 in the DHNT
Jeremiah 39 in the DNT
Jeremiah 39 in the ELBE
Jeremiah 39 in the EMTV
Jeremiah 39 in the ESV
Jeremiah 39 in the FBV
Jeremiah 39 in the FEB
Jeremiah 39 in the GGMNT
Jeremiah 39 in the GNT
Jeremiah 39 in the HARY
Jeremiah 39 in the HNT
Jeremiah 39 in the IRVA
Jeremiah 39 in the IRVB
Jeremiah 39 in the IRVG
Jeremiah 39 in the IRVH
Jeremiah 39 in the IRVK
Jeremiah 39 in the IRVM
Jeremiah 39 in the IRVM2
Jeremiah 39 in the IRVO
Jeremiah 39 in the IRVP
Jeremiah 39 in the IRVT
Jeremiah 39 in the IRVT2
Jeremiah 39 in the IRVU
Jeremiah 39 in the ISVN
Jeremiah 39 in the JSNT
Jeremiah 39 in the KAPI
Jeremiah 39 in the KBT1ETNIK
Jeremiah 39 in the KBV
Jeremiah 39 in the KJV
Jeremiah 39 in the KNFD
Jeremiah 39 in the LBA
Jeremiah 39 in the LBLA
Jeremiah 39 in the LNT
Jeremiah 39 in the LSV
Jeremiah 39 in the MAAL
Jeremiah 39 in the MBV
Jeremiah 39 in the MBV2
Jeremiah 39 in the MHNT
Jeremiah 39 in the MKNFD
Jeremiah 39 in the MNG
Jeremiah 39 in the MNT
Jeremiah 39 in the MNT2
Jeremiah 39 in the MRS1T
Jeremiah 39 in the NAA
Jeremiah 39 in the NASB
Jeremiah 39 in the NBLA
Jeremiah 39 in the NBS
Jeremiah 39 in the NBVTP
Jeremiah 39 in the NET2
Jeremiah 39 in the NIV11
Jeremiah 39 in the NNT
Jeremiah 39 in the NNT2
Jeremiah 39 in the NNT3
Jeremiah 39 in the PDDPT
Jeremiah 39 in the PFNT
Jeremiah 39 in the RMNT
Jeremiah 39 in the SBIAS
Jeremiah 39 in the SBIBS
Jeremiah 39 in the SBIBS2
Jeremiah 39 in the SBICS
Jeremiah 39 in the SBIDS
Jeremiah 39 in the SBIGS
Jeremiah 39 in the SBIHS
Jeremiah 39 in the SBIIS
Jeremiah 39 in the SBIIS2
Jeremiah 39 in the SBIIS3
Jeremiah 39 in the SBIKS
Jeremiah 39 in the SBIKS2
Jeremiah 39 in the SBIMS
Jeremiah 39 in the SBIOS
Jeremiah 39 in the SBIPS
Jeremiah 39 in the SBISS
Jeremiah 39 in the SBITS
Jeremiah 39 in the SBITS2
Jeremiah 39 in the SBITS3
Jeremiah 39 in the SBITS4
Jeremiah 39 in the SBIUS
Jeremiah 39 in the SBIVS
Jeremiah 39 in the SBT
Jeremiah 39 in the SBT1E
Jeremiah 39 in the SCHL
Jeremiah 39 in the SNT
Jeremiah 39 in the SUSU
Jeremiah 39 in the SUSU2
Jeremiah 39 in the SYNO
Jeremiah 39 in the TBIAOTANT
Jeremiah 39 in the TBT1E
Jeremiah 39 in the TBT1E2
Jeremiah 39 in the TFTIP
Jeremiah 39 in the TFTU
Jeremiah 39 in the TGNTATF3T
Jeremiah 39 in the THAI
Jeremiah 39 in the TNFD
Jeremiah 39 in the TNT
Jeremiah 39 in the TNTIK
Jeremiah 39 in the TNTIL
Jeremiah 39 in the TNTIN
Jeremiah 39 in the TNTIP
Jeremiah 39 in the TNTIZ
Jeremiah 39 in the TOMA
Jeremiah 39 in the TTENT
Jeremiah 39 in the UBG
Jeremiah 39 in the UGV
Jeremiah 39 in the UGV2
Jeremiah 39 in the UGV3
Jeremiah 39 in the VBL
Jeremiah 39 in the VDCC
Jeremiah 39 in the YALU
Jeremiah 39 in the YAPE
Jeremiah 39 in the YBVTP
Jeremiah 39 in the ZBP