Jeremiah 40 (BOGWICC)
1 Yehova anayankhula ndi Yeremiya pamene Nebuzaradani mtsogoleri wa asilikali olonda mfumu anamasula Yeremiyayo ku Rama. Anamupeza Yeremiya ali womangidwa ndi unyolo pamodzi ndi amʼndende ena onse a ku Yerusalemu ndi a ku Yuda amene ankapita nawo ku ukapolo ku Babuloni. 2 Mtsogoleriyu anamupeza Yeremiya, anamuwuza kuti, “Yehova Mulungu wako analengeza kale zakuti malo ano adzawonongedwa. 3 Ndipo tsopano Yehova wachitadi zimenezi monga mmene ananenera. Izi zonse zachitika chifukwa anthu inu munachimwira Yehova ndipo simunamumvere. 4 Koma tsopano taona, lero ndikukumasula unyolo umene unali mʼmanja mwako. Ngati ukufuna kupita nane ku Babuloni, tiye ndipo adzakusamala bwino. Koma ngati sukufuna kupita, ndiye usapite. Dziko ndi limeneli monga ukulioneramo. Uli ndi ufulu kupita kulikonse kumene ukufuna.” 5 Yeremiya asanayankhe, Nebuzaradani anamuwuzanso kuti, “Ngati supita ndiye pita, ubwerere kwa Gedaliya, mwana wa Ahikamu, mdzukulu wa Safani, amene mfumu ya ku Babuloni inamusankha kuti akhale bwanamkubwa wa Yuda. Ukakhale naye pakati pa anthu, kapena upite kulikonse ukufuna.”Ndipo mtsogoleri uja anamupatsa Yeremiya chakudya ndi mphatso zina ndi kumulola kuti apite. 6 Motero Yeremiya anapita kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu ku Mizipa ndipo anakakhala naye kumeneko pakati pa anthu amene anatsala mʼdzikomo. 7 Panali atsogoleri ena a nkhondo ndi anthu awo amene sanadzipereke nawo. Iwowa anamva kuti mfumu ya ku Babuloni inasankha Gedaliya mwana wa Ahikamu kukhala bwanamkubwa wa dzikolo ndipo kuti yamuyika kukhala wolamulira amuna, akazi ndi ana amene anali osauka kwambiri mʼdzikomo, amene sanawagwire ukapolo kupita nawo ku Babuloni. 8 Iwowa anapita ku Mizipa kwa Gedaliya. Amene anapitawo ndi awa: Ismaeli mwana wa Netaniya, Yohanani ndi Yonatani ana a Kareya, Seraya mwana wa Tanihumeti, ana a Efai a ku Netofa, ndi Yezaniya mwana wa Maaka, iwowo pamodzi ndi anthu awo. 9 Gedaliya mwana wa Ahikamu, mdzukulu wa Safani, anawalonjeza iwo pamodzi ndi anthuwo mwalumbiro. Ndipo anati, “Musaope kuwatumikira Ababuloni. Khalani mʼdziko muno, tumikirani mfumu ya ku Babuloni, ndipo zinthu zidzakuyenderani bwino. 10 Ine ndidzakhala ku Mizipa kuti ndizikuyimirirani kwa Ababuloni amene azidzabwera kwa ife, koma inu muzikolola vinyo wanu, zipatso zanu, mafuta anu ndi kuzisunga mʼmitsuko yanu, nʼkumakhala mʼmizinda imene mwalandayo.” 11 Nawonso Ayuda onse a ku Mowabu, ku Amoni, ku Edomu ndi a ku mayiko ena onse anamva kuti mfumu ya ku Babuloni inasiyako anthu ena ku Yuda ndipo kuti inasankha Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani, kukhala bwanamkubwa wawo. 12 Tsono Ayuda onsewo anabwerera ku Yuda, ku Mizipa kwa Gedaliya, kuchokera ku mayiko onse kumene anabalalikira. Ndipo anakolola zipatso zochuluka ndi vinyo wambiri. 13 Yohanani mwana wa Kareya ndi atsogoleri a ankhondo onse amene sanadzipereke aja anabwera ku Mizipa kwa Gedaliya 14 ndipo anamufunsa kuti, “Kodi sukudziwa kuti Baalisi mfumu ya Aamoni watuma Ismaeli mwana wa Netaniya kuti akuphe?” Koma Gedaliya mwana wa Ahikamu sanawankhulupirire. 15 Tsono Yohanani mwana wa Kareya, mwamseri anawuza Gedaliya ku Mizipa kuti, “Loleni ndipite ndikaphe Ismaeli mwana wa Netaniya, ndipo palibe amene ati adziwe. Akuphereninji ndi kuchititsa Ayuda onse, amene akuzungulirani kuti abalalike ndi kuti otsala a ku Yuda awonongeke?” 16 Koma Gedaliya mwana wa Ahikamu anawuza Yohanani mwana wa Kareya kuti, “Usachite zimenezo! Zimene ukunena za Ismaeli ndi zabodza.”
In Other Versions
Jeremiah 40 in the ANGEFD
Jeremiah 40 in the ANTPNG2D
Jeremiah 40 in the AS21
Jeremiah 40 in the BAGH
Jeremiah 40 in the BBPNG
Jeremiah 40 in the BBT1E
Jeremiah 40 in the BDS
Jeremiah 40 in the BEV
Jeremiah 40 in the BHAD
Jeremiah 40 in the BIB
Jeremiah 40 in the BLPT
Jeremiah 40 in the BNT
Jeremiah 40 in the BNTABOOT
Jeremiah 40 in the BNTLV
Jeremiah 40 in the BOATCB
Jeremiah 40 in the BOATCB2
Jeremiah 40 in the BOBCV
Jeremiah 40 in the BOCNT
Jeremiah 40 in the BOECS
Jeremiah 40 in the BOHCB
Jeremiah 40 in the BOHCV
Jeremiah 40 in the BOHLNT
Jeremiah 40 in the BOHNTLTAL
Jeremiah 40 in the BOICB
Jeremiah 40 in the BOILNTAP
Jeremiah 40 in the BOITCV
Jeremiah 40 in the BOKCV
Jeremiah 40 in the BOKCV2
Jeremiah 40 in the BOKHWOG
Jeremiah 40 in the BOKSSV
Jeremiah 40 in the BOLCB
Jeremiah 40 in the BOLCB2
Jeremiah 40 in the BOMCV
Jeremiah 40 in the BONAV
Jeremiah 40 in the BONCB
Jeremiah 40 in the BONLT
Jeremiah 40 in the BONUT2
Jeremiah 40 in the BOPLNT
Jeremiah 40 in the BOSCB
Jeremiah 40 in the BOSNC
Jeremiah 40 in the BOTLNT
Jeremiah 40 in the BOVCB
Jeremiah 40 in the BOYCB
Jeremiah 40 in the BPBB
Jeremiah 40 in the BPH
Jeremiah 40 in the BSB
Jeremiah 40 in the CCB
Jeremiah 40 in the CUV
Jeremiah 40 in the CUVS
Jeremiah 40 in the DBT
Jeremiah 40 in the DGDNT
Jeremiah 40 in the DHNT
Jeremiah 40 in the DNT
Jeremiah 40 in the ELBE
Jeremiah 40 in the EMTV
Jeremiah 40 in the ESV
Jeremiah 40 in the FBV
Jeremiah 40 in the FEB
Jeremiah 40 in the GGMNT
Jeremiah 40 in the GNT
Jeremiah 40 in the HARY
Jeremiah 40 in the HNT
Jeremiah 40 in the IRVA
Jeremiah 40 in the IRVB
Jeremiah 40 in the IRVG
Jeremiah 40 in the IRVH
Jeremiah 40 in the IRVK
Jeremiah 40 in the IRVM
Jeremiah 40 in the IRVM2
Jeremiah 40 in the IRVO
Jeremiah 40 in the IRVP
Jeremiah 40 in the IRVT
Jeremiah 40 in the IRVT2
Jeremiah 40 in the IRVU
Jeremiah 40 in the ISVN
Jeremiah 40 in the JSNT
Jeremiah 40 in the KAPI
Jeremiah 40 in the KBT1ETNIK
Jeremiah 40 in the KBV
Jeremiah 40 in the KJV
Jeremiah 40 in the KNFD
Jeremiah 40 in the LBA
Jeremiah 40 in the LBLA
Jeremiah 40 in the LNT
Jeremiah 40 in the LSV
Jeremiah 40 in the MAAL
Jeremiah 40 in the MBV
Jeremiah 40 in the MBV2
Jeremiah 40 in the MHNT
Jeremiah 40 in the MKNFD
Jeremiah 40 in the MNG
Jeremiah 40 in the MNT
Jeremiah 40 in the MNT2
Jeremiah 40 in the MRS1T
Jeremiah 40 in the NAA
Jeremiah 40 in the NASB
Jeremiah 40 in the NBLA
Jeremiah 40 in the NBS
Jeremiah 40 in the NBVTP
Jeremiah 40 in the NET2
Jeremiah 40 in the NIV11
Jeremiah 40 in the NNT
Jeremiah 40 in the NNT2
Jeremiah 40 in the NNT3
Jeremiah 40 in the PDDPT
Jeremiah 40 in the PFNT
Jeremiah 40 in the RMNT
Jeremiah 40 in the SBIAS
Jeremiah 40 in the SBIBS
Jeremiah 40 in the SBIBS2
Jeremiah 40 in the SBICS
Jeremiah 40 in the SBIDS
Jeremiah 40 in the SBIGS
Jeremiah 40 in the SBIHS
Jeremiah 40 in the SBIIS
Jeremiah 40 in the SBIIS2
Jeremiah 40 in the SBIIS3
Jeremiah 40 in the SBIKS
Jeremiah 40 in the SBIKS2
Jeremiah 40 in the SBIMS
Jeremiah 40 in the SBIOS
Jeremiah 40 in the SBIPS
Jeremiah 40 in the SBISS
Jeremiah 40 in the SBITS
Jeremiah 40 in the SBITS2
Jeremiah 40 in the SBITS3
Jeremiah 40 in the SBITS4
Jeremiah 40 in the SBIUS
Jeremiah 40 in the SBIVS
Jeremiah 40 in the SBT
Jeremiah 40 in the SBT1E
Jeremiah 40 in the SCHL
Jeremiah 40 in the SNT
Jeremiah 40 in the SUSU
Jeremiah 40 in the SUSU2
Jeremiah 40 in the SYNO
Jeremiah 40 in the TBIAOTANT
Jeremiah 40 in the TBT1E
Jeremiah 40 in the TBT1E2
Jeremiah 40 in the TFTIP
Jeremiah 40 in the TFTU
Jeremiah 40 in the TGNTATF3T
Jeremiah 40 in the THAI
Jeremiah 40 in the TNFD
Jeremiah 40 in the TNT
Jeremiah 40 in the TNTIK
Jeremiah 40 in the TNTIL
Jeremiah 40 in the TNTIN
Jeremiah 40 in the TNTIP
Jeremiah 40 in the TNTIZ
Jeremiah 40 in the TOMA
Jeremiah 40 in the TTENT
Jeremiah 40 in the UBG
Jeremiah 40 in the UGV
Jeremiah 40 in the UGV2
Jeremiah 40 in the UGV3
Jeremiah 40 in the VBL
Jeremiah 40 in the VDCC
Jeremiah 40 in the YALU
Jeremiah 40 in the YAPE
Jeremiah 40 in the YBVTP
Jeremiah 40 in the ZBP